Yeremiya 51 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 51:1-64

1Yehova akuti,

“Taonani, ndidzadzutsa mphepo yowononga

kuti iwononge Babuloni pamodzi ndi anthu a ku Lebi Kamai.

2Ndidzatuma alendo ku Babuloni

kudzamupeta ndi kuwononga dziko lake kotheratu.

Iwo adzalimbana naye ku mbali zonse

pa tsiku la masautso ake.

3Okoka uta musawalekerere

kapena wonyadira chovala chawo chankhondo.

Musawasiye anyamata ake kuti akhale ndi moyo;

koma muwononge ankhondo ake kotheratu.

4Adzavulazidwa ndi kufera mʼdziko la Babuloni

lomwelo ndi mʼmisewu yawo yomwe.

5Pakuti Yuda ndi Israeli sanasiyidwe ngati amasiye

ndi Mulungu wawo, Yehova Wamphamvuzonse,

koma ngakhale dziko la Babuloni ndi lodzaza ndi machimo

pamaso pa Woyerayo wa Israeli.

6“Thawaniko ku Babuloni!

Aliyense apulumutse moyo wake!

Musawonongeke naye pamodzi chifukwa cha machimo ake.

Imeneyi ndi nthawi yoti Yehova amulange;

Yehova adzamulipsira.

7Babuloni anali ngati chikho cha golide mʼdzanja la Yehova;

kuti aledzeretse dziko lonse lapansi.

Mitundu yambiri ya anthu inamwa vinyo wake;

nʼchifukwa chake tsopano inachita misala.

8Babuloni wagwa mwadzidzidzi ndi kusweka.

Mulireni!

Mfunireni mankhwala opha ululu wake;

mwina iye nʼkuchira.”

9Ena anati, “ ‘Ife tinayesa kumupatsa mankhwala Babuloni,

koma sanachire;

tiyeni timusiye ndipo aliyense apite ku dziko la kwawo,

pakuti mlandu wake wafika mpaka mlengalenga,

wafika mpaka kumwamba.’

10“ ‘Yehova waonetsa poyera kuti ndife osalakwa;

tiyeni tilengeze mu Ziyoni

zimene Yehova Mulungu wathu wachita.’

11“Yehova wadzutsa mitima ya mafumu a Amedi,

popeza cholinga chake ndi kuwononga Babuloni.

Motero adzalipsira Ababuloni

chifukwa chowononga Nyumba yake.

Ndiye Yehova akuti,

‘Nolani mivi, tengani zishango.’

12Kwezani mbendera yankhondo kuti muwononge malinga a Babuloni!

Limbitsani oteteza,

ikani alonda pa malo awo,

konzekerani kulalira.

Pakuti Yehova watsimikiza

ndipo adzachitadi zomwe ananena za anthu a ku Babuloni.

13Inu muli ndi mitsinje yambiri

ndi chuma chambiri.

Koma chimaliziro chanu chafika,

moyo wanu watha.

14Yehova Wamphamvuzonse analumbira pali Iye mwini kuti:

Ndidzakutumizira adani ochuluka ngati dzombe,

kuti adzakuthire nkhondo ndipo adzafuwula kuonetsa kuti apambana.

15“Yehova analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake;

Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zake

ndipo anayala thambo mwaluso lake.

16Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba.

Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.

Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvula

ndi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene amasungira.

17“Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru;

mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake.

Mafano akewo ndi abodza;

alibe moyo mʼkati mwawo.

18Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo.

Pamene anthuwo azidzaweruzidwa mafanowo adzawonongedwa.

19Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo.

Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse,

kuphatikizapo mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake.

Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.

20“Iwe Babuloni ndi ndodo yanga,

chida changa chankhondo.

Ndi iwe ndimaphwanya mitundu ya anthu,

ndi iwe ndimawononga maufumu,

21ndi iwe ndimaphwanya kavalo ndi wokwerapo,

ndi iwe ndimaphwanya galeta ndi woyendetsa wake.

22Ndi iwe ndimaphwanya mwamuna ndi mkazi,

ndi iwe ndimaphwanya nkhalamba ndi wachinyamata,

ndi iwe ndimaphwanya mnyamata ndi namwali.

23Ndi iwe ndimaphwanya mʼbusa ndi ziweto,

ndi iwe ndimaphwanya mlimi ndi ngʼombe,

ndi iwe ndimaphwanya abwanamkubwa ndi atsogoleri a ankhondo.

24“Inu mukuona ndidzalanga Babuloni ndi onse amene amakhala mʼdziko la Babuloni chifukwa cha zolakwa zonse anachita ku Ziyoni,” akutero Yehova.

25“Taonani, ndikukuzenga mlandu, iwe phiri lowononga,

amene umawononga dziko lonse lapansi,”

akutero Yehova.

“Ndidzatambalitsa dzanja langa pofuna kukulanga,

kukugubuduzira pansi kuchokera pa matanthwe ako,

ndi kukusandutsa kukhala phiri lopserera.

26Palibe ngakhale ndi mwala wako umodzi umene anthu adzawutenga

kuti awugwiritse ntchito kumangira nyumba,

chifukwa iwe udzakhala chipululu mpaka muyaya,”

akutero Yehova.

27“Kwezani mbendera ya nkhondo mʼdziko!

Lizani lipenga pakati pa mitundu ya anthu!

Konzekeretsani mitundu ya anthu kuti ikamuthire nkhondo;

itanani maufumu awa:

Ararati, Mini ndi Asikenazi kuti adzamuthire nkhondo.

Ikani mtsogoleri wankhondo kuti amenyane naye;

tumizani akavalo ochuluka ngati magulu a dzombe.

28Konzekeretsani mitundu ya anthu.

Amenewa ndiwo mafumu a Amedi,

abwanamkubwa awo, atsogoleri a ankhondo,

ndiponso ankhondo a mayiko amene amawalamulira, kuti idzathire nkhondo Babuloni.

29Dziko likunjenjemera ndi kunthunthumira,

chifukwa zidzachitikadi zimene Yehova wakonzera Babuloni;

kusakaza dziko la Babuloni

kuti musapezeke wokhalamo.

30Ankhondo a ku Babuloni aleka kuchita nkhondo;

iwo angokhala mʼmalinga awo.

Mphamvu zawo zatheratu;

ndipo akhala ngati akazi.

Malo ake wokhala atenthedwa;

mipiringidzo ya zipata zake yathyoka.

31Othamanga akungopezanapezana,

amithenga akungotsatanatsatana

kudzawuza mfumu ya ku Babuloni

kuti alande mzinda wake wonse.

32Madooko onse alandidwa,

malo onse obisalamo alonda atenthedwa ndi moto,

ndipo ankhondo onse asokonezeka.”

33Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,

“Babuloni wokongola uja wakhala ngati malo opunthirapo tirigu

pa nthawi yake yopuntha tirigu; A ku Yerusalemu akuti,

Posachedwapa nthawi yake yomukolola ifika.”

34A ku Yerusalemu akuti, “Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni watiwononga,

watiphwanya,

ndi kutitaya ngati mbiya yopanda kanthu.

Watimeza ngati ngʼona,

wakhuta ndi zakudya zathu zokoma,

kenaka nʼkutilavula.”

35Anthu a ku Ziyoni anene kuti,

“Zankhanza zimene anatichitira ife ziwabwerere Ababuloni.”

Anthu okhala mu Yerusalemu anene kuti,

“Magazi athu amene anakhetsedwa akhale pa amene akukhala ku Babuloni.”

36Nʼchifukwa chake Yehova akuti,

“Taona, ndidzakumenyera nkhondo

ndi kukulipsirira;

ndidzawumitsa nyanja yake

ndipo akasupe ake adzaphwa.

37Motero Babuloni adzasanduka mulu wa nyumba zogumuka,

malo okhala nkhandwe,

malo ochititsa mantha ndi onyozedwa,

malo wopanda aliyense wokhalamo.

38Anthu ake onse adzabangula ngati mkango,

adzadzuma ngati ana amkango.

39Ngati achita dyera

ndiye ndidzawakonzera madyerero

ndi kuwaledzeretsa,

kotero kuti adzasangalala,

kenaka nʼkugona tulo mpaka muyaya ndipo sadzadzukanso,”

akutero Yehova.

40“Ine ndidzawatenga

kuti akaphedwe ngati ana ankhosa onenepa,

ngati nkhosa zazimuna ndi mbuzi.

41“Ndithu Babuloni walandidwa,

mzinda umene dziko lonse lapansi limanyadira wagwidwa!

Taonani, mmene Babuloni wasandukira chinthu chochititsa mantha

pakati pa mitundu ya anthu!

42Nyanja yakwera ndi kumiza Babuloni;

mafunde ake okokoma aphimba Babuloni.

43Mizinda yake yasanduka bwinja,

dziko lowuma ndi lachipululu,

dziko losakhalamo wina aliyense,

dziko losayendamo munthu aliyense.

44Ndidzalanga Beli mulungu wa Ababuloni,

ndidzamusanzitsa zimene anameza.

Mitundu ya anthu sidzapitanso kwa iye.

Malinga a Babuloni agwa.

45“Tulukani mʼBabuloni anthu anga!

Pulumutsani miyoyo yanu!

Thawani mkwiyo woopsa wa Yehova.

46Musataye mtima kapena kuchita mantha

pamene mphekesera zikumveka mʼdziko mwanu.

Chaka ndi chaka pamabuka mphekesera

za ziwawa mʼdziko lapansi,

ndiponso yakuti mfumu yakuti ikuthira nkhondo mfumu ina.

47Pakuti taonani, nthawi ikubwera ndithu

pamene ndidzalanga mafano a ku Babuloni;

dziko lake lonse lidzachita manyazi

ndi ophedwa ake onse adzakhala ngundangunda pakati pake.

48Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo

zidzayimba mokondwa chifukwa cha kugwa kwa Babuloni.

Anthu owononga ochokera kumpoto

adzamuthira nkhondo,”

akutero Yehova.

49“Babuloni anapha anthu ambiri pa dziko lapansi.

Tsono, nawo anthu a ku Babuloni ayenera kuphedwa

chifukwa anapha anthu a ku Yerusalemu.

50Inu amene munapulumuka ku nkhondo ya Babuloni,

chokani pano ndipo musazengereze!

Kumbukirani Yehova ngakhale muli ku mayiko akutali,

ganizirani za Yerusalemu.”

51Inu mukuti, “Tikuchita manyazi,

chifukwa tanyozedwa

ndipo nkhope zathu zili ndi manyazi,

chifukwa anthu achilendo alowa

malo opatulika a Nyumba ya Yehova.”

52Nʼchifukwa chake Yehova akuti,

“Masiku akubwera pamene ndidzalanga mafano ake,

ndipo mʼdziko lake lonse

anthu ovulala adzabuwula.

53Ngakhale Babuloni atadzikweza mpaka mlengalenga

ndi kulimbitsa nsanja zake,

ndidzatuma anthu owononga kudzamenyana naye,”

akutero Yehova.

54“Imvani mfuwu wolira kuchokera ku Babuloni.

Imvani phokoso lachiwonongeko chachikulu

kuchokera mʼdziko la Babuloni.

55Pakuti Yehova akuwononga Babuloni,

ndipo akuthetsa phokoso lake lalikulu.

Mfuwu wa adani ukumveka ngati mkokomo wa madzi ambiri.

Phokoso lawo likunka likwererakwerera.

56Pakuti wowononga wafika kudzamenyana ndi Babuloni,

ankhondo ake agwidwa,

ndipo mauta awo athyoka.

Paja Yehova ndi Mulungu wobwezera chilango;

adzabwezera kwathunthu.

57Ndidzaledzeretsa akuluakulu ake pamodzi ndi anzeru ake,

abwanamkubwa ake, atsogoleri a ankhondo pamodzinso ndi ankhondo;

adzagona kwamuyaya osadzukanso,”

akutero Mfumu, amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.

58Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Malinga aakulu a Babuloni adzasalazidwa

ndipo zipata zake zazitali zidzatenthedwa;

mitundu ya anthu inangogwira ntchito pachabe.

Anthu anatopa ndi kumanga zimene tsopano zikupsa ndi moto.”

59Zedekiya mfumu ya Yuda inali ndi phungu wake wamkulu amene dzina lake linali Seraya mwana wa Neriya chidzukulu cha Maseya. Mʼchaka chachinayi cha ulamuliro wake, Zedekiya anapita ndi Seraya ku Babuloni. Tsono mneneri Yeremiya anamupatsirako uthenga Serayayo. 60Yeremiya anali atalemba mʼbuku za masautso onse amene adzafike pa Babuloni ndi zina zonse zokhudza Babuloni. 61Yeremiya anawuza Seraya kuti, “Ukakafika ku Babuloni, ukaonetsetse kuti wawawerengera anthu onse mawu onsewa. 62Ndipo ukanene kuti, ‘Inu Yehova, mwanena kuti mudzawononga malo ano, kotero kuti simudzatsala munthu kapena nyama mʼdziko muno; lidzakhala chipululu mpaka muyaya.’ 63Ukakatha kuwerenga bukuli, ukalimangirire ku mwala ndipo ukaliponye pakati pa mtsinje wa Yufurate. 64Ndipo ukanene kuti, ‘Umu ndi mmene adzamirire Babuloni ndipo sadzadzukanso chifukwa cha masautso amene adzamugwere.’ ”

Mawu a Yeremiya athera pamenepa.

Bibelen på hverdagsdansk

Jeremiasʼ Bog 51:1-64

1Herren siger: „Jeg sender et ødelæggende stormvejr ind over Babylonien, en voldsom vind midt ind i landet. 2Befolkningen skal blæses bort som avner, når man renser korn. Fremmede vil angribe fra alle sider, indtil landet er tomt og øde. 3Når katastrofen rammer dem, vil ingen kunne nå at få rustning på eller spænde buen. Ingen bliver skånet, både unge og ældre bliver dræbt. 4De faldne ligger overalt i landet, og døde kroppe hober sig op i byernes gader, 5for jeg er Herren, den Almægtige, og jeg svigter ikke Israel og Juda. Babylonierne bliver straffet for deres mange synder imod Israels hellige Gud.”

6Flygt fra Babylonien, alle I fremmede, som blev holdt i fangenskab. Bring jer i sikkerhed, så I ikke også bliver dræbt, når Herren hævner sig på babylonierne og giver dem, hvad de har fortjent. 7Babylon var som et guldbæger i Herrens hånd, og de fremmede fra alverdens lande blev betaget og beruset af dets storhed. Derfor er de lamslåede og siger: 8„Pludselig er Babylon faldet og knust. Græd over hendes skæbne. Skaf hende lægende salver, måske er der endnu håb. 9Vi ville gerne hjælpe hende, hvis vi kunne, men nu kan intet redde hende. Derfor må vi lade hende være og vende hjem til vores eget land. Den straf, Herren sendte mod hende fra Himlen, er så stor, at den ikke kan måles.”

10Og Judas folk siger: „Herren har givet os oprejsning. Kom, lad os vende hjem til Jerusalem og fortælle om alt, hvad Herren, vores Gud, har gjort.”

11„Gør pilene spidse og fyld jeres koggere!” siger Herren, for han har gjort medernes konger opsatte på at erobre og ødelægge Babylonien. Det er Herrens hævn over dem, der vanærede hans tempel. 12„Giv signal til angreb på Babylons mure! Sæt vagter ved portene og hele vejen rundt om muren, så ingen slipper væk. Gør klar til bagholdsangreb.”

Herren vil nu udføre sin plan og gøre alvor af sine trusler. 13Du prægtige by ved de mange vandområder, du blomstrende handelscentrum, nu er timen kommet, hvor du får din straf. 14Herren den Almægtige har givet et højtideligt løfte: Jeg vil lade dine fjender oversvømme dig, som var de græshopper, og de vil udstøde vældige sejrsråb.

15Det var Herren, der med sin vældige styrke, visdom og snilde grundlagde universet, skabte jorden og udspændte himmelhvælvingen. 16Med sin tordnende røst får han regnen til at styrte ned. Han samler skyerne fra horisonten, skaber lyn og regn, og slipper vinden løs.

17Alle afgudsdyrkerne er tåbelige, de forstår ingenting. Guldsmedene vil engang skamme sig over at have lavet afgudsbilleder, som er det rene svindel og bedrag. Der er jo ikke gnist af liv i deres afguder. 18De er nytteløse og latterlige, og en skønne dag bliver de ødelagt.

19Men Jakobs Gud er helt anderledes. Han er verdens Skaber, og Israel er hans udvalgte folk. Han er den almægtige Gud.

20„Babylonien, du var mit våben, min kølle,” siger Herren. „Med dig knuste jeg folkeslag og ødelagde riger. 21Med dig knuste jeg heste og ryttere, stridsvogne og vognkæmpere. 22Med dig knuste jeg gamle og unge, mænd og kvinder, 23hyrder og fåreflokke, bønder og kvæg, regenter og guvernører. 24I judæere har oplevet deres grusomhed i Jerusalem, men I vil nu få at se, hvordan jeg straffer Babylon og det babyloniske folk for deres ondskab.

25Nu er jeg blevet din fjende, du vældige bjerg, der knuste jordens nationer. Jeg løfter min hånd imod dig og styrter dig ned fra din høje plads, så der kun er en afsvedet bakketop tilbage. 26Du skal fra nu af ligge øde og forladt, og dine murbrokker vil aldrig blive genbrugt til fundamenter for nye huse, siger Herren.

27Kald på de andre nationer, så de kan gå i krig mod Babylonien. Lad krigsråbet lyde, tilkald hære fra landene Ararat, Minni og Ashkenaz. Udpeg en angrebsleder, og lad hestene storme frem som sultne græshopper. 28Lad de mediske konger gøre sig klar til kamp og sende besked til alle guvernørerne i det mediske storrige. Alle hære i hele riget skal mobiliseres.

29Babylon skælver og vrider sig i smerte, for Herren vil nu gennemføre sin plan, og han giver ikke op, før byen er raseret og lagt øde. 30Babylons krigere vil opgive at gøre modstand. De gemmer sig i deres fæstninger og ryster som skræmte kvinder. Byens porte vil blive sprængt og husene brændt ned. 31Fra alle sider kommer der løbere med bud til kongen om, at slaget er tabt. 32Alle flodovergange er spærrede, marsken står i lys lue, og alle krigerne er panikslagne.”

33Herren, den Almægtige, Israels Gud, siger: „Babylon er som en tærskeplads, der er stampet til og gjort klar. Om kort tid begynder høsten.”

34„Kong Nebukadnezar faldt over os,” siger judæerne. „Som et mægtigt havuhyre kom han og slugte os og fyldte sin vom med vores rigdomme. Han åd os rub og stub og slikkede tallerkenen ren. 35Lad nu Babylon få betalt for de grusomme lidelser, han påførte os. Lad byens befolkning betale prisen for alle dem hos os, der mistede livet.”

36„Jeg vil kæmpe for jer,” siger Herren til Jerusalem. „Jeg vil føre jeres sag og skaffe jer hævn. Jeg udtørrer Babylons bassiner og stopper byens vandforsyning. 37Jeg gør Babylon til en ruinbunke, et hjemsted for sjakaler, et eksempel til skræk og advarsel.

38Babylon plejede at brøle som en løve på rov og knurre som sultne løveunger. 39Men nu skal den få lov at tømme min vredes bæger, så den drikker sig fra sans og samling. Den vil segne bevidstløs om og aldrig vågne igen, siger Herren. 40Jeg fører dens befolkning til slagtebænken, som var de får eller geder.

41Tænk, Babylon er faldet, den store, stolte by, som alle jordens lande beundrede. Babylons undergang har rystet hele verden. 42Et hav af krigere skyllede hen over Babylon og jævnede den med jorden. 43Nu ligger alle bydele i ruiner. De er øde og forladte som en ørken, hvor ingen bor, og hvor ingen rejser igennem. 44Jeg straffer Bel, Babylons gud, og river byttet ud af gabet på ham. Folkeslagene skal ikke længere komme langvejsfra for at dyrke ham. Babylons mure er faldet.

45Mit folk, flygt ud af Babylon. Bring jer i sikkerhed. Søg i dækning for den straf, jeg vil ramme byen med. 46Men lad jer ikke skræmme af de rygter, I hører. Der vil hele tiden være nye rygter, år efter år, om voldelige begivenheder og lande, der bekriger hinanden. 47Snart vil jeg straffe babylonierne og deres afguder. Hele landet vil blive ydmyget, og de faldne vil fylde gaderne. 48Himlen og jorden skal fryde sig, når hærene fra nord vælter ind over landet, siger Herren. 49Babyloniens hær dræbte Israels folk og andre folkeslag ud over jorden. Nu står Babylonien selv for tur. 50Flygt fra krigens rædsler, mit folk. Stands ikke op for se på det. Tænk på jeres Gud, skønt I er i et fjernt land, og glem ikke Jerusalem.

51I siger, at I er blevet hånet og ydmyget, fordi fremmede folkeslag vanærede Herrens hellige tempel. 52Ja, men snart vil jeg hævne mig på Babyloniens afguder, og der skal lyde stønnen fra sårede over hele landet. 53Selv om Babylon forsøger at klatre op på den højeste tinde og befæster sine forsvarsværker, vil jeg sende en hær imod byen, som vil udslette den,” siger Herren.

54Hør! Dødsskriget stiger op fra Babylon, hele Babyloniens land er brudt sammen. 55Det er Herren, som angriber Babylons befolkning og lukker munden på deres praleri. Fjendehære skyller ind over landet som brusende bølger, og der høres krigslarm i byen. 56Ødelæggelsen trænger ind i byen, overrumpler dens stolte krigere og brækker deres buer, for Herren er en Gud, som straffer mennesker for deres ondskab.

57„Alle landets ledere og vismænd skal tømme min vredes bæger,” siger Kongen, Herren, den Almægtige. „Alle guvernører, stormænd og krigere får min vrede at føle. De segner om for aldrig at vågne igen. 58Babylons brede bymur skal jævnes med jorden, og de høje porte skal brænde ned til grunden. Folkenes slid er forgæves, for det hele bliver flammernes bytte.”

Jeremias’ budskaber bliver sendt til Babylonien

59-61Kong Zidkija af Juda blev i sit fjerde regeringsår kaldt til Babylon, og hans kvartermester Seraja, søn af Nerija, som var søn af Maseja, skulle ledsage ham. Jeremias skrev så alle domsprofetierne om Babylon ned, gav bogrullen til Seraja og sagde til ham: „Så snart du kommer til Babylon, skal du oplæse ordene i bogrullen for folk der 62og fremsige følgende ord: ‚Herre, du har sagt, at du vil jævne Babylon med jorden, så den fremover skal ligge ubeboet hen.’ 63Når du har læst hele bogrullen op, skal du kaste den i Eufratfloden 64og sige: ‚Sådan skal det gå Babylon: Hun skal synke og aldrig komme op til overfladen igen, for Herren har besluttet at straffe hende.’ ”

Her slutter Jeremias’ budskaber.