Yeremiya 52 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 52:1-34

Kuwonongeka kwa Yerusalemu

1Zedekiya anali wa zaka 21 pamene analowa ufumu, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Amayi ake anali Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina. 2Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Yehoyakimu. 3Chifukwa cha zonse zimene zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yuda Yehova anakwiyira anthu ake mpaka kuwachotsa pamaso pake.

Tsono Zedekiya anawukira mfumu ya ku Babuloni.

4Choncho mʼchaka cha chisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa Zedekiya, mwezi wakhumi, pa tsiku la khumi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anabwera ndi ankhondo ake onse kudzathira nkhondo Yerusalemu. Anamanga misasa ndi mitumbira yankhondo kunja kuzungulira mzindawo. 5Mzindawo unazingidwa mpaka chaka cha khumi ndi chimodzi cha ulamuliro wa Mfumu Zedekiya.

6Pa tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi wachinayi njala inakula kwambiri mu mzindamo kotero kuti munalibe chakudya choti anthu nʼkudya. 7Tsono linga la mzindawo linabowoledwa, ndipo ankhondo onse anathawa. Iwo anatuluka mu mzindamo usiku kudzera pa chipata cha pakati pa makoma awiri a pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababuloni anali atazinga mzindawo. Ndipo anathawira ku Araba, 8koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola mfumu Zedekiya ndi kumupeza mʼchigwa cha ku Yeriko. Ankhondo onse anamusiya yekha nabalalika.

9Anagwidwa napita naye kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula mʼdziko la Hamati, kumene anagamula mlandu wake. 10Ku Ribulako mfumu ya ku Babuloni inapha ana aamuna a Zedekiya iyeyo akuona; ndiponso inapha akuluakulu onse a ku Yuda. 11Ndipo inamukolowola maso Zedekiya, ndi kumumanga ndi maunyolo a mkuwa nʼkupita naye ku Babuloni kumene inakamuyika mʼndende kuti akhalemo moyo wake wonse.

12Mwezi wachisanu, pa tsiku lakhumi, chaka cha 19 cha ulamuliro wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo a mfumu, amene amatumikira mfumu ya ku Babuloni, anabwera ku Yerusalemu. 13Ndipo anatentha Nyumba ya Yehova, nyumba ya mfumu ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu. Anatentha nyumba iliyonse. 14Tsono gulu lonse lankhondo la Ababuloni limene linali ndi mtsogoleri wa ankhondo a mfumu uja linagwetsa malinga onse ozungulira Yerusalemu. 15Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo anatenga anthu amene anatsala mu mzindamo, anthu aluso pamodzi ndi amene anadzipereka kale kwa mfumu ya ku Babuloni kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. 16Komabe Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo anasiya anthu ena onse osaukitsitsa a mʼdzikomo kuti azigwira ntchito mʼminda ya mpesa ndi minda ina.

17Ababuloni anaphwanya nsanamira za mkuwa, maphaka ndi chimbiya chamkuwa zimene zinali mʼNyumba ya Yehova. Anatenga mkuwa wonsewo nʼkupita nazo ku Babuloni. 18Ankhondowo anatenganso mbiya, zochotsera phulusa, zozimitsira nyale, mbale zofukizira lubani, zikho pamodzi ndi ziwiya zina zonse za mkuwa zimene ankagwiritsira ntchito mʼNyumba ya Yehova. 19Nebuzaradani uja anatenganso mabeseni, ziwiya zosonkhapo moto, mbale zowazira madzi, zoyikapo nyale, zipande zofukizira lubani ndi zikho ndi zina zonse zagolide ndi siliva.

20Nsanamira ziwiri zija, chimbiya, maphaka ndi ngʼombe khumi ndi ziwiri za mkuwa zochirikizira chimbiyacho zimene mfumu Solomoni anapangira Nyumba ya Yehova kulemera kwake kunali kosawerengeka. 21Nsanamira imodzi kutalika kwake kunali mamita asanu ndi atatu, akazunguliza chingwe inali mamita asanu ndi theka; mʼkati mwake munali bowo ndipo kuchindikala kwake kunali zala zinayi. 22Pamwamba pa nsanamira iliyonse panali mutu wamkuwa umene kutalika kwake kunali mamita awiri. Pozungulira pake panali ukonde ndi makangadza, zonsezo za mkuwa. Nsanamira inayo inalinso ndi makangadza ake ndipo inali yofanana ndi inzake ija. 23Mʼmbali mwake munali makangadza 96; makangadza onse pamodzi analipo 100 kuzungulira ukonde onse.

24Mtsogoleri wa ankhondo uja, anagwira Seraya mkulu wa ansembe ndi Zefaniya, wachiwiri wa mkulu wa ansembe ndi alonda atatu apachipata. 25Mu mzindamo anagwiramo mkulu amene ankalamulira ankhondo, ndi alangizi amfumu asanu ndi awiri. Anagwiranso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo, amene ankalemba anthu mʼdzikomo, pamodzi ndi anthu ena 60 amene anali mu mzindamo. 26Nebuzaradani, mtsogoleri wa ankhondoyo anawatenga onse napita nawo kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula. 27Ku Ribulako, mʼdziko la Hamati, mfumu ya ku Babuloniyo inalamula kuti anthuwo aphedwe.

Motero anthu a ku Yuda anapita ku ukapolo, kutali ndi dziko lawo. 28Chiwerengero cha anthu amene Nebukadinezara anawatenga kupita nawo ku ukapolo ndi ichi:

Mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri cha ulamuliro wake, anatenga Ayuda 3,023;

29mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Nebukadinezara,

anatenga anthu 832 kuchokera mu Yerusalemu;

30mʼchaka cha 23 cha ulamuliro wa Nebukadinezara,

Nebuzaradani, mtsogoleri wa ankhondo a mfumu anagwira Ayuda 745 kupita ku ukapolo.

Onse pamodzi analipo anthu 4,600.

Kumasulidwa kwa Yehoyakini

31Mʼchaka chimene Evili-Merodaki analowa ufumu wa Babuloni, iye anakomera mtima Yehoyakini mfumu ya ku Yuda, namutulutsa mʼndende. Izi zinachitika pa tsiku la 25 la mwezi wa khumi ndi chiwiri zitatha zaka 37 chitengedwere Yehoyakimu ku ukapolo. 32Evili-Merodaki anakomera mtima Yehoyakini, namupatsa malo aulemu kuposa mafumu ena amene anali naye ku Babuloni. 33Choncho Yehoyakini analoledwa kuvula zovala zake za ku ndende ndipo tsiku ndi tsiku ankadya ndi mfumu pa moyo wake wonse. 34Tsiku ndi tsiku mfumu ya ku Babuloni inkamupatsa Yehoyakini phoso lake nthawi yonse ya moyo wake, mpaka pa nthawi ya imfa yake.

Bibelen på hverdagsdansk

Jeremiasʼ Bog 52:1-34

Historisk oversigt over Jerusalems fald

1Zidkija var 21 år gammel, da han blev konge, og han regerede i Jerusalem i 11 år. Hans mor hed Hamutal og var datter af Jirmeja fra byen Libna. 2Han gjorde, hvad der var ondt i Herrens øjne, ligesom Jojakim havde gjort. 3Til sidst var Jerusalems og Judas oprør og ugudelighed blevet så voldsom, at Herren var nødt til at straffe dem og sende dem i eksil. Det varede ikke længe, før Zidkija gjorde oprør imod den babyloniske konge.

4Derfor mobiliserede kong Nebukadnezar igen sin hær og drog mod Jerusalem. I kong Zidkijas niende regeringsår, på den tiende dag i den tiende måned, begyndte den babyloniske hær en svær belejring af byen. De byggede angrebsramper op imod bymuren. 5Belejringen varede til kong Zidkijas 11. regeringsår. 6På den niende dag i den fjerde måned af det år var alt spiseligt sluppet op og befolkningen totalt udsultet. 7På det tidspunkt brød fjenden hul gennem bymuren og den judæiske hær prøvede at flygte. Nogle forlod byen om natten gennem paladsets have, igennem en korridor mellem to mure, ud af en port i bymuren og videre i retning af Jordandalen. Men de babyloniske tropper holdt vagt rundt omkring byen, 8og de satte efter kong Zidkija og indhentede ham på sletten ved Jeriko. Hans soldater flygtede i alle retninger, 9men han selv blev fanget og ført til den babyloniske konge i byen Ribla i Hamat-området, hvor han blev anklaget og dømt. 10Han blev tvunget til at overvære sine sønners og nærmeste embedsmænds henrettelse, 11hvorefter hans øjne blev stukket ud. Så blev han lagt i lænker og ført til Babylon, hvor han blev holdt fængslet til sin død.

12På den tiende dag i den femte måned i kong Nebukadnezars 19. regeringsår kom Nebuzaradan til Jerusalem fra Babylon. Nebuzaradan var chef for den babyloniske konges livvagt. 13Han nedbrændte Herrens tempel, kongens palads og alle byens mest betydningsfulde bygninger, 14hvorefter han beordrede sine tropper til at rive Jerusalems bymur ned. 15Så samlede han resten af byens indbyggere, håndværkerne og de, der havde overgivet sig, for at føre dem til Babylon i eksil. 16Kun de fattigste lod Nebuzaradan blive tilbage, så der var nogen til at dyrke jorden og passe vingårdene.

17Babylonierne slog templets bronzesøjler, bronzehavet og alle rullebordene i stykker og tog alt metallet med sig hjem til Babylon. 18De tog alt, hvad der var lavet af bronze: askebakkerne, skovlene, vægesaksene, fadene, skålene og de bronzeredskaber der blev brugt ved ofringerne i templet. 19Nebuzaradan tog selv, hvad der var af guld og sølvting: skålene, bakkerne til gløder, stænkeskålene, fadene, lysestagerne og de forskellige drikofferskåle. 20Det hele blev vejet, undtagen de to søjler, bronzehavet, de 12 bronzetyre og rullebordene, som kong Salomon i sin tid havde ladet fremstille til Herrens tempel. De var for store til at blive vejet. 21Søjlerne var 8,1 m høje og 5,4 m i omkreds. De var hule med en tykkelse på fire fingre. 22Foroven havde de et søjlehoved på 2,25 m med en dekoration af fletværk og granatæbler i bronze. 23På siderne var der 96 granatæbler og øverst på søjlehovedet yderligere 100 granatæbler hele vejen rundt.

24Af tempelpersonalet tog Nebuzaradan følgende krigsfanger: Ypperstepræsten Seraja, andenpræsten Zefanja og de tre dørvogtere. 25Fra byen tog han den øverstkommanderende officer, en rekrutteringsofficer, syv af kongens tidligere rådgivere og 60 andre betydningsfulde mænd, som var gået under jorden. 26Han førte disse mænd til den babyloniske konge i Ribla i Hamat-området, 27hvor de alle blev henrettet. Judas folk var nu ført bort fra deres land og måtte leve i eksil.

28I Nebukadnezars syvende regeringsår blev i alt 3023 judæere ført i eksil, 29i hans 18. regeringsår yderligere 832 fanger fra Jerusalem, 30og i hans 23. regeringsår bortførte Nebuzaradan 745 fanger fra Juda, alt i alt 4600 fanger.

Jojakin får bedre forhold under sit fangenskab

31Mange år senere kom der en ny konge på tronen i Babylon, som hed Evil-Merodak. Han besluttede at benåde Jojakin og løslade ham fra fængslet. Det skete den 27. dag i den 12. måned i Jojakins 37. år i fangenskab. 32Den nye konge behandlede Jojakin venligt, bedre end de andre konger, som også var i fangenskab. 33Jojakin fik nyt tøj i stedet for fangedragten, og han spiste i kongens palads indtil sin dødsdag. 34Så længe han levede, gav kongen ham fra dag til dag, hvad han havde brug for.