New International Version

Ephesians 2

Made Alive in Christ

1As for you, you were dead in your transgressions and sins, in which you used to live when you followed the ways of this world and of the ruler of the kingdom of the air, the spirit who is now at work in those who are disobedient. All of us also lived among them at one time, gratifying the cravings of our flesh[a] and following its desires and thoughts. Like the rest, we were by nature deserving of wrath. But because of his great love for us, God, who is rich in mercy, made us alive with Christ even when we were dead in transgressions—it is by grace you have been saved. And God raised us up with Christ and seated us with him in the heavenly realms in Christ Jesus, in order that in the coming ages he might show the incomparable riches of his grace, expressed in his kindness to us in Christ Jesus. For it is by grace you have been saved, through faith—and this is not from yourselves, it is the gift of God— not by works, so that no one can boast. 10 For we are God’s handiwork, created in Christ Jesus to do good works, which God prepared in advance for us to do.

Jew and Gentile Reconciled Through Christ

11 Therefore, remember that formerly you who are Gentiles by birth and called “uncircumcised” by those who call themselves “the circumcision” (which is done in the body by human hands)— 12 remember that at that time you were separate from Christ, excluded from citizenship in Israel and foreigners to the covenants of the promise, without hope and without God in the world. 13 But now in Christ Jesus you who once were far away have been brought near by the blood of Christ.

14 For he himself is our peace, who has made the two groups one and has destroyed the barrier, the dividing wall of hostility, 15 by setting aside in his flesh the law with its commands and regulations. His purpose was to create in himself one new humanity out of the two, thus making peace, 16 and in one body to reconcile both of them to God through the cross, by which he put to death their hostility. 17 He came and preached peace to you who were far away and peace to those who were near. 18 For through him we both have access to the Father by one Spirit.

19 Consequently, you are no longer foreigners and strangers, but fellow citizens with God’s people and also members of his household, 20 built on the foundation of the apostles and prophets, with Christ Jesus himself as the chief cornerstone. 21 In him the whole building is joined together and rises to become a holy temple in the Lord. 22 And in him you too are being built together to become a dwelling in which God lives by his Spirit.

Footnotes

  1. Ephesians 2:3 In contexts like this, the Greek word for flesh (sarx) refers to the sinful state of human beings, often presented as a power in opposition to the Spirit.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Aefeso 2

Amene anali Akufa Alandira Moyo

1Kunena za inu, kale munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu ndi machimo anu, mmene inu munkakhalamo pamene munkatsatira njira za dziko lapansi ndi za ulamuliro waufumu wa mlengalenga, mzimu umene ukugwira ntchito tsopano mwa amene samvera. Nthawi ina tonsefe tinalinso ndi moyo wonga wawo, tinkachitanso zilizonse zimene matupi ndi maganizo athu ankafuna. Mwachibadwa chathu, tinali oyenera chilango monga anthu ena onse. Koma chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife, Mulungu amene ndi olemera mʼchifundo, anatipanga kukhala amoyo ndi Khristu ngakhale pamene ife tinali akufa mu zolakwa zathu. Koma tinapulumutsidwa mwachisomo. Ndipo Mulungu anatiukitsa pamodzi ndi Khristu ndi kutikhazika pamodzi ndi Iye mmwamba mwa Khristu Yesu, ndi cholinga chakuti mʼnthawi imene ikubwera, Iyeyo adzaonetse chuma choposa cha chisomo chake, choonetsedwa mwa kukoma mtima kwake kwa ife mwa Khristu Yesu. Pakuti mwapulumutsidwa mwachisomo, kudzera mʼchikhulupiriro ndipo izi sizochokera mwa inu eni, koma ndi mphatso ya Mulungu, osati ndi ntchito, kuti wina aliyense asadzitamandire. 10 Pakuti ndife ntchito ya Mulungu, olengedwa mwa Khristu Yesu kuti tichite ntchito zabwino, zimene Mulungu anazikonzeratu kale kuti tizichite.

Umodzi mwa Khristu

11 Chifukwa chake kumbukirani kuti poyamba inu amene munali anthu a mitundu ina mwachibadwa ndipo munkatchedwa “osachita mdulidwe” ndi amene amadzitcha okha “a mdulidwe” (zimene zinachitika mʼthupi ndi manja a anthu). 12 Kumbukirani kuti nthawi imene inu munali wopanda Khristu, simunkawerengedwa ngati nzika za Israeli ndipo munali alendo pa pangano la lonjezo, wopanda chiyembekezo ndi opanda Mulungu mʼdziko lapansi. 13 Koma tsopano mwa Khristu Yesu, inu amene nthawi ina munali kutali, mwabweretsedwa pafupi kudzera mʼmagazi a Khristu.

14 Pakuti Iye mwini ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti awiri akhale mmodzi ndipo anagumula chotchinga, khoma la udani lotilekanitsa, 15 pothetsa mʼthupi lake lamulo pamodzi ndi zolamulira zake ndi malangizo. Cholinga chake chinali chakuti alenge mwa Iye mwini, munthu mmodzi watsopano kuchokera kwa abwino, motero nʼkupanga mtendere, 16 ndi kuyanjanitsa onse awiriwa mʼthupi lake kwa Mulungu, kudzera pa mtanda, umene Iye anaphapo udani wawo. 17 Iye anabwera ndipo analalikira mtendere kwa inu amene munali kutali ndi mtendere ndiponso kwa iwonso amene anali pafupi. 18 Pakuti mwa Iye, ife tonse titha kufika kwa Atate mwa Mzimu mmodzi.

19 Kotero kuti, inu sindinunso alendo ndi adani, koma nzika pamodzi ndi anthu a Mulungu ndiponso a mʼbanja la Mulungu. 20 Ndinu okhazikika pa maziko a atumwi ndi a aneneri, pamodzi ndi Khristu Yesu mwini ngati mwala wa pa ngodya. 21 Mwa Iyeyo, nyumba yonse yalumikizidwa pamodzi ndipo yakwezedwa kukhala Nyumba yoyera mwa Ambuye. 22 Ndipo mwa Iye, inunso mukamangidwa pamodzi ndi ena onse kukhala nyumba yokhalamo imene Mulungu amakhala mwa Mzimu wake.