Mkwiyo wa Yona ndi Chifundo cha Yehova
1Koma Yona anakhumudwa kwambiri ndipo anakwiya. 2Iye anapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, kodi izi si zimene ndinanena ndikanali kwathu? Nʼchifukwa chaketu ine ndinafulumira kuthawa kupita ku Tarisisi. Ine ndinadziwa kuti ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chopanda malire, Mulungu amene mumaleka kubweretsa tsoka. 3Ndipo tsopano, Inu Yehova, ingondiphani basi, pakuti ndi bwino kuti ndife kupambana nʼkukhala ndi moyo.”
4Koma Yehova anayankha kuti, “Kodi nʼkoyenera kuti iwe ukwiye?”
5Yona anatuluka mu mzindamo nakakhala pansi cha kummawa kwa mzindawo. Kumeneko anadzimangira chithando nakhala mʼmenemo mu mthunzi, kudikira kuti aone zimene zichitikire mzindawo. 6Tsono Yehova Mulungu anameretsa msatsi ndi kuyikulitsa kuti ipereke mthunzi kwa Yona kuchotsa mavuto ake; ndipo Yona anasangalala kwambiri chifukwa cha msatsiyo. 7Koma tsiku linalo mmawa, Mulungu anabweretsa mbozi imene inadya msatsiyo ndipo inafota. 8Dzuwa litatuluka, Yehova anabweretsa mphepo yotentha yochokera kummawa, ndipo dzuwa linatentha pamutu pa Yona kotero analenguka nalo. Iye anangofuna atafa, ndipo anati, “Ndi bwino kuti ndife kupambana nʼkukhala ndi moyo.”
9Koma Mulungu anati kwa Yona, “Kodi nʼkoyenera kuti iwe ukwiye chifukwa cha msatsi?”
Iye anayankha kuti, “Inde nʼkoyenera. Kukwiya kwanga nʼkofuna kufa nako.”
10Koma Yehova anati, “Iwe ukumvera chisoni msatsiwo, ngakhale kuti sunawugwirire ntchito kapena kuwukulitsa. Inamera pa usiku umodzi ndipo inafanso pa usiku umodzi. 11Koma mu Ninive muli anthu opitirira 120,000 amene sadziwa kusiyanitsa kuti chabwino nʼchiti ndipo choyipa nʼchiti, mulinso ziweto zochuluka. Kodi sindiyenera kumvera chisoni mzinda waukulu ngati uwu?”