Amosi 3 – The Word of God in Contemporary Chichewa CCL

The Word of God in Contemporary Chichewa

Amosi 3:1-15

Mboni Zotsutsa Israeli

1Inu Aisraeli, imvani mawu awa amene Yehova wayankhula kutsutsana nanu, kutsutsana ndi banja lonse limene analitulutsa mu Igupto:

2“Inu nokha ndi amene ndinakusankhani

pakati pa mabanja onse a dziko lapansi;

nʼchifukwa chake ndidzakulangani

chifukwa cha machimo anu onse.”

3Kodi anthu awiri nʼkuyendera limodzi

asanapangane?

4Kodi mkango umabangula mʼnkhalango

usanagwire nyama?

Kodi msona wamkango umalira mʼphanga mwake

pamene sunagwire kanthu?

5Kodi mbalame nʼkutera pa msampha

pamene palibe nyambo yake?

Kodi msampha umafwamphuka

usanakole kanthu?

6Kodi pamene lipenga la nkhondo lalira mu mzinda,

anthu sanjenjemera?

Pamene tsoka lafika mu mzinda,

kodi si Yehova amene wachititsa zimenezo?

7Zoonadi Ambuye Yehova sachita kanthu

asanawulule zimene akufuna kuchita

kwa atumiki ake, aneneri.

8Mkango wabangula,

ndani amene sachita mantha?

Ambuye Yehova wayankhula,

ndani amene sanganenere?

9Lengezani zimenezi ku nyumba zaufumu za ku Asidodi

ndiponso ku nyumba zaufumu za ku Igupto:

“Sonkhanani ku mapiri a ku Samariya;

onani chisokonezo pakati pake

ndiponso kuponderezana pakati pa anthu ake.”

10“Iwo sadziwa kuchita zolungama,

ndipo amadzaza malo awo otetezedwa ndi zinthu zolanda ku nkhondo ndi zakuba,” akutero Yehova.

11Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akunena izi:

“Mdani adzalizungulira dzikoli;

iye adzagwetsa malinga ako,

ndi kufunkha nyumba zako zaufumu.”

12Yehova akuti,

“Monga mʼbusa amalanditsa mʼkamwa mwa mkango

miyendo iwiri yokha kapena msonga yokha ya khutu,

moteronso ndimo mmene adzapulumukire Aisraeli

amene amakhala mu Samariya

pa msonga za mabedi awo,

ndi ku Damasiko pa akakhutagona awo.”

13“Imvani izi ndipo mupereke umboni wotsutsa nyumba ya Yakobo,” akutero Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.

14“Pa tsiku limene ndidzalange Israeli chifukwa cha machimo ake,

ndidzagumula maguwa ansembe a ku Beteli;

nyanga za guwa zidzathyoka

ndipo zidzagwa pansi.

15Ndidzagwetsa nyumba ya pa nthawi yozizira

pamodzi ndi nyumba ya pa nthawi yotentha;

nyumba zokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu zidzawonongedwa

ndipo nyumba zikuluzikulu zidzaphwasulidwa,”

akutero Yehova.