Yoswa 3 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 3:1-17

Aisraeli Awoloka Yorodani

1Yoswa ndi Aisraeli onse anadzuka mmamawa nanyamuka ku Sitimu kupita ku Yorodani. Iwo anagona kumeneko asanawoloke mtsinje wa Yorodaniwo. 2Patatha masiku atatu, atsogoleri anayendera misasa yonse, 3kulangiza anthu kuti, “Mukaona ansembe a Chilevi atanyamula Bokosi la Chipangano la Yehova Mulungu wanu, inu munyamuke pa malo ano ndi kumalitsatira. 4Potero mudzadziwa njira yoti mudzere, popeza simunayendepo njira ino nʼkale lomwe. Koma musaliyandikire. Pakati pa inu ndi bokosilo pakhale mtunda pafupifupi kilomita imodzi.”

5Yoswa anawuza anthu kuti, “Dzipatuleni tsono pakuti mawa Yehova adzachita zodabwitsa pakati panu.”

6Mmawa mwake Yoswa ananena kwa ansembe kuti, “Nyamulani Bokosi la Chipangano muwoloke ndipo mukhale patsogolo pa anthu.” Motero iwo analinyamula ndi kupita patsogolo pawo.

7Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, “Lero Ine ndidzayamba kukukweza pamaso pa Aisraeli onse kuti adziwe kuti ndili nawe monga ndinalili ndi Mose. 8Ansembe amene akunyamula Bokosi la Chipangano uwalamule kuti, ‘Mukafika ku mtsinje wa Yorodani mulowe mu mtsinjemo ndi kuyima mʼmphepete.’ ”

9Yoswa anati kwa Aisraeli, “Bwerani pano mudzamve mawu a Yehova Mulungu wanu. 10Umu ndi mmene mudzadziwira kuti Mulungu wamoyo ali pakati panu. Inu mukamadzapita patsogolo Iye adzathamangitsa Akanaani, Ahiti, Ahivi, Aperezi, Agirigasi, Aamori ndi Ayebusi. 11Pamenepo, Bokosi la Chipangano la Mbuye wa dziko lonse lapansi lidzawoloka mu Yorodani patsogolo panu. 12Musankhe amuna khumi ndi awiri kuchokera ku fuko lililonse la Israeli. 13Mapazi a ansembe onyamula Bokosi la Yehova, Mbuye wa dziko lapansi, akadzangoponda mu Yorodani, madzi ake onse ochokera ku mtunda adzaleka kuyenda ndipo adzayima ngati chipupa.”

14Tsono Aisraeli anachoka ku misasa yawo kukawoloka mtsinje wa Yorodani. Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano ndiwo anatsogolera anthuwo. 15Nyengo imeneyi inali yokolola ndipo mtsinje wa Yorodani umakhala wodzaza. Komabe, ansembe onyamula Bokosi la Chipangano anafika ku Yorodani, ndipo atangoponda mʼmadzimo, 16madzi ochokera ku mtunda anasiya kuyenda. Madzi a Yorodani ochokera ku mtunda anawunjikana pamodzi ngati khoma lalitali pa mtunda wautali ndithu ndi mzinda wa Adama chapafupi ndi mzinda wa Zaretani. Madzi othamangira ku nyanja ya Araba, ngakhalenso amene amachokera kuti Nyanja ya Mchere amathera pamenepo. Choncho anthu anawoloka tsidya lina moyangʼanana ndi Yeriko. 17Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano la Yehova anali chiyimire powuma, pakati pa Yorodani pamene Aisraeli amawoloka mpaka gulu lonse linamaliza kuwoloka powuma.

Bibelen på hverdagsdansk

Josvabogen 3:1-17

Israelitterne går over Jordanfloden

1Tidligt næste morgen brød Josva og Israels folk op fra lejren ved Shittim og kom ned til Jordanfloden. Der slog de lejr, indtil de var parat til at gå over floden.

2Tre dage senere gik lederne rundt i lejren 3med følgende besked til folket: „Når I ser præsterne bryde op og gå af sted med pagtens ark, skal I følge efter. 4De vil gå foran jer og vise vej. Men der skal være en afstand på en kilometer3,4 På hebraisk 2000 alen, ca. 900 meter. mellem jer og arken. I må ikke komme for tæt på den.”

5Derefter sagde Josva til folket: „Sørg for at være rituelt rene, for i morgen vil Herren gøre undere iblandt jer.”

6Til præsterne sagde han: „I skal tage pagtens ark og gå i spidsen for folket.” Og de accepterede at tage pagtens ark og gå foran folket.

7Om natten sagde Herren til Josva: „I dag vil jeg sørge for, at du vinder stor respekt blandt Israels folk. Alle skal få at se, at jeg er med dig, ligesom jeg var med Moses. 8Sig til præsterne, som skal bære pagtens ark: Når I kommer til flodens bred, skal I gå et skridt ud i den og blive stående.”

9Næste morgen kaldte Josva folket sammen og sagde: „Hør efter, hvad Herren, jeres Gud, siger. 10I dag vil I se et bevis på, at den levende Gud er midt iblandt jer. Det vil give jer mod til at tro på, at han også vil drive landets indbyggere på flugt foran jer—alle kana’anæerne, hittitterne, hivvitterne, perizzitterne, girgashitterne, amoritterne og jebusitterne. 11Arken, der tilhører Herren—hele jordens Herre—skal bane vej for jer gennem floden. 12I skal udvælge 12 mænd, en fra hver stamme. 13Så snart præsterne med arken træder ud i floden, vil vandstrømmen nordfra standse og hobe sig op som en vold.”

14-15Så brød folket op for at gå over floden, og præsterne, som bar pagtens ark, gik foran dem. Det var i høsttiden, hvor Jordanfloden går over sine bredder. Men da præsterne trådte ud i floden, 16standsede vandet, som kom nordfra, hobede sig op og stod som en vold ved byen Adam nær Saretan, mens vandet på sydsiden flød bort i retning af Det Døde Hav, indtil flodlejet var tørt, så folket kunne gå over lige ved Jeriko. 17Mens folket gik over, stod præsterne med arken midt ude i det udtørrede flodleje.