Yoswa 15 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 15:1-63

Dziko Limene Yuda Analandira

1Chigawo cha dzikolo chimene mabanja a fuko la Yuda analandira chinafika ku malire ndi Edomu mpaka ku chipululu cha Zini kummwera kwenikweni.

2Malire awo a kummwera anayambira kummwera kwenikweni kwa Nyanja ya Mchere, 3kudutsa cha kummwera ku Akirabimu, nʼkupitirira mpaka ku Zini. Kuchokera pamenepo nʼkumapita cha kummwera kwa Kadesi Barinea, kudutsa Hezironi mpaka ku Adari ndi kutembenuka mpaka ku Karika. 4Anapitirira mpaka ku Azimoni motsata mtsinje umene uli malire a Igupto mpaka ku nyanja. Awa ndiwo malire awo a kummwera.

5Malire a kummawa anali Nyanja Yakufa mpaka kumene Yorodani amathira mu Nyanja ya Mchere.

Malire a kumpoto anayambira kumene Yorodani amathirira nyanjayo, 6napitirira mpaka ku Beti-Hogila ndi kupitirira kumpoto mpaka ku Beti-Araba. Anapitirira mpaka anakafika ku Mwala wa Bohani. 7Ndipo malirewo anachokeranso ku chigwa cha Akori mpaka ku Debri, kuchokera ku chigwa cha Akori ndi kutembenukira kumpoto ku Giligala, dera limene linayangʼanana ndi msewu wa Adumimu kummwera kwa chigwa. Anapitirira mpaka ku madzi a ku Eni Semesi ndi kutulukira ku Eni Rogeli. 8Ndipo anapitirira mpaka ku chigwa cha Hinomu mbali ya kummwera kwa mzinda wa Ayebusi (mzinda wa Yerusalemu). Kuchokera kumeneko anakwera mpaka pamwamba pa phiri kumadzulo kwa chigwa cha Hinomu cha kumpoto kwenikweni kwa chigwa cha Refaimu. 9Ndipo anachokeranso pamwamba pa phiri, kukafika mpaka ku akasupe a ku Nepitowa, nadzatulukira ku mizinda ya phiri la Efroni, ndi kutsikira ku Baalahi (ndiye Kiriati Yearimu). 10Kuchokera kumeneko anazungulira cha kumadzulo ku Baalahi mpaka ku phiri la Seiri. Anapitirira cha kumpoto kutsata phiri la Yearimu (lomwe ndi Kesaloni). Anapitirirabe kutsika ku Beti Semesi ndi kuwolokera ku Timna. 11Malirewo anapitirira kumatsitso a mapiri chakumpoto kwa Ekroni, ndi kukhotera ku Sikeroni. Malirewo anadutsa phiri la Baalahi ndi kufika ku Yabineeli. Malirewo anathera ku nyanja.

12Malire a mbali ya kumadzulo anali Nyanja Yayikulu.

Awa ndi malire ozungulira malo amene anapatsidwa kwa mabanja a fuko la Yuda.

13Potsata lamulo la Yehova, Yoswa anapereka kwa Kalebe mwana wa Yefune gawo lina la dziko la Yuda dera la Kiriati Ariba, limene ndi Hebroni. (Ariba anali gogo wa Aanaki). 14Kuchokera ku Hebroni, Kalebe anathamangitsamo mafuko a Aanaki awa: Sesai, Ahimani ndi Talimai, zidzukulu za Aanaki. 15Kuchokera kumeneko, Kalebe anakathira nkhondo anthu amene ankakhala ku Debri (mzindawu poyamba unkatchedwa Kiriati Seferi). 16Tsono Kalebe anati, “Munthu amene angathire nkhondo mzinda wa Kiriati Seferi ndi kuwulanda, ndidzamupatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.” 17Otanieli, mwana wa mʼbale wa Kalebe, Kenazi, ndiye anawulanda. Choncho Kalebe anamupatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake.

18Tsiku lina atafika Akisayo, Otanieli anamuwumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe abambo ake. Pamene Akisa anatsika pa bulu wake, Kalebe anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna ndikuchitire chiyani.”

19Iye anayankha kuti “Mundikomere mtima. Popeza mwandipatsa ku Negevi, kumalo kumene kulibe madzi, mundipatsenso akasupe amadzi.” Choncho Kalebe anamupatsa akasupe a kumtunda ndi a kumunsi.

20Dziko limene mabanja a fuko la Yuda analandira ngati cholowa chawo ndi ili:

21Mizinda yakummwera kwenikweni kwa fuko la Yuda yoyandikana ndi malire a Edomu anali:

Kabizeeli, Ederi, Yaguri 22Kina, Dimona, Adada 23Kedesi, Hazori, Itinani 24Zifi, Telemu, Bealoti, 25Hazori-Hadata, Keriyoti Hezironi (ndiye kuti Hazori) 26Amamu, Sema, Molada 27Hazari-Gada, Hesimoni, Beti-Peleti 28Hazari-Suwali, Beeriseba, Biziotiya, 29Baalahi, Iyimu, Ezemu 30Elitoladi, Kesili, Horima 31Zikilagi, Madimena, Sanisana, 32Lebaoti, Silihimu, Aini ndi Rimoni. Mizinda yonse inalipo 29 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.

33Mizinda ya ku chigwa cha kumadzulo ndi iyi:

Esitaoli, Zora, Asina 34Zanowa, Eni-Ganimu, Tapuwa, Enamu, 35Yarimuti, Adulamu, Soko, Azeka, 36Saaraimu, Aditaimu, ndi Gederi (kapena Gederotaimu). Mizinda yonse inalipo 14 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.

37Mizinda ina inali iyi: Zenani, Hadasa, Migidali-Gadi, 38Dileani, Mizipa, Yokiteeli, 39Lakisi, Bozikati, Egiloni, 40Kaboni, Lahimasi, Kitilisi, 41Gederoti, Beti-Dagoni, Naama ndi Makeda. Mizinda yonse pamodzi inalipo 16 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.

42Mizinda ina inali iyi: Libina, Eteri, Asani, 43Ifita, Asina, Nezibu, 44Keila, Akizibu ndi Maresa, mizinda isanu ndi inayi pamodzi ndi midzi yake.

45Panalinso Ekroni pamodzi ndi midzi yake; 46komanso yonse imene inali mʼmbali mwa Asidodi ndi midzi yake kuyambira ku Ekroni mpaka ku Nyanja Yayikulu. 47Panalinso mizinda ya Asidodi ndi Gaza pamodzi ndi midzi yawo. Malire ake anafika ku mtsinje wa Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu.

48Mizinda ya kumapiri inali:

Samiri, Yatiri, Soko, 49Dana, Kiriati-Sana, (ndiye kuti Debri) 50Anabu, Esitemo, Animu, 51Goseni, Holoni ndi Gilo. Mizinda yonse pamodzi inali khumi ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake.

52Analandiranso mizinda iyi: Arabu, Duma, Esani, 53Yanumu, Beti-Tapuwa, Afeki 54Humita, Kiriati-Ariba (ndiye kuti Hebroni) ndi Ziori, mizinda isanu ndi inayi pamodzi ndi midzi yake.

55Panalinso Maoni, Karimeli, Zifi, Yuta 56Yezireeli, Yokideamu, Zanowa, 57Kaini, Gibeya ndi Timna, mizinda khumi ndi midzi yake.

58Mizinda ina inali: Halihuli, Beti Zuri, Gedori, 59Maarati, Beti-Anoti ndi Elitekoni, mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake

60Panalinso Kiriati Baala (ndiye kuti Kiriati Yearimu) ndi Raba; mizinda iwiri pamodzi ndi midzi yake.

61Mizinda ya ku chipululu inali iyi:

Beti-Araba, Midini, Sekaka, 62Nibisani, Mzinda wa Mchere ndi Eni Gedi, mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake.

63Koma Yuda sanathe kuthamangitsa Ayebusi amene amakhala ku Yerusalemu, ndipo mpaka lero Ayebusi akukhala komweko pamodzi ndi Ayudawo.

New Russian Translation

Навин 15:1-63

Надел Иуды

(Суд. 1:11-15)

1Жребий рода Иуды по их кланам простирался до земель Эдома, до пустыни Цин на самом юге.

2Их южная граница начиналась от залива, что на южной оконечности Соленого моря, 3проходила южнее Скорпионовой возвышенности15:3 Или: «возвышенности Акраббим»., продолжалась к Цину и поднималась к югу от Кадеш-Барнеа. Затем она шла мимо Хецрона к Аддару и поворачивала к Каркае. 4Далее она проходила Ацмон, выходила к египетскому потоку и оканчивалась у моря. Вот их15:4 Букв.: «ваша». южная граница.

5Восточная граница – это Соленое море до устья Иордана.

Северная граница начиналась от залива в море при устье Иордана, 6поднималась к Бет-Хогле и продолжалась севернее Бет-Аравы до камня Богана, сына Рувима. 7Затем граница поднималась к Давиру из долины Ахор и поворачивала на север к Гилгалу, что напротив возвышенности Адуммим к югу от потока. Она тянулась к водам Эн-Шемеша и заканчивалась у Эн-Рогела. 8Затем она поднималась к долине Бен-Гинном по южному склону иевусейского города (то есть Иерусалима). Оттуда она восходила на вершину горы к западу от долины Гинном в северном конце долины Рефаим. 9С вершины горы граница тянулась к источнику вод Нефтоах, оттуда – к городам горы Эфрон, а затем поворачивала к Баале (то есть Кирьят-Иеариму). 10Затем она поворачивала к западу от Баалы к горе Сеир, проходила по северному склону горы Иарим (то есть Кесалон), спускалась к Бет-Шемешу и проходила через Тимну. 11Она шла к северному склону Экрона, поворачивала к Шикарону, проходила к горе Баала, достигала Иавнеила, и заканчивалась у моря.

12Западная граница – это побережье Великого моря.

Таковы границы вокруг народа Иуды по его кланам.

13По повелению Господа, Иисус дал Халеву, сыну Иефоннии, земельный надел среди народа Иуды – Кирьят-Арбу, то есть Хеврон. (Арба был отцом Анака). 14Из Хеврона Халев прогнал трех анакитов – Шешая, Ахимана и Талмая, потомков Анака. 15Оттуда он пошел на жителей Давира (который прежде назывался Кирьят-Сефер). 16Халев сказал:

– Я отдам свою дочь Ахсу в жены тому, кто нападет на Кирьят-Сефер и возьмет его.

17Отниил, сын Кеназа, брата Халева15:17 Или: «Отниил, потомок Кеназа, брат Халева»., взял его, и Халев отдал ему в жены свою дочь Ахсу.

18В день, когда была назначена свадьба, она говорила с Отниилом, чтобы просить у ее отца поле. Когда она слезла со своего осла, Халев спросил ее:

– Чего ты хочешь?

19Она ответила:

– Окажи мне особую милость. Ты дал мне землю в Негеве – так дай мне и источники воды.

И Халев дал ей верхние и нижние источники.

20Вот удел рода Иуды по их кланам:

21Города рода Иуды на самом юге, в Негеве по направлению к границе Эдома:

Кавцеил, Едер, Иагур, 22Кина, Димона, Адада, 23Кедеш, Хацор, Ифнан, 24Зиф, Телем, Валоф, 25Хацор-Хадафа, Кериот-Хецрон (то есть Хацор), 26Амам, Шема, Молада, 27Хацар-Гадда, Хешмон, Бет-Пелет, 28Хацар-Шуал, Вирсавия, Визиофея, 29Баала, Иим, Ецем, 30Элтолад, Кесил, Хорма, 31Циклаг, Мадманна, Сансана, 32Леваоф, Шилхим, Аин и Риммон – всего двадцать девять городов с окрестными поселениями15:32 То, что число городов в списке превышает двадцать девять, может иметь два объяснения: 1) возможно некоторые города были добавлены в список позже; 2) в тексте стоит число двадцать девять, так как семь из перечисленных городов позднее были отданы роду Симеона (см. 19:1-7)..

33В западных предгорьях:

Эштаол, Цора, Ашна, 34Заноах, Эн-Ганним, Таппуах, Энам, 35Ярмут, Адуллам, Сохо, Азека, 36Шаараим, Адифаим, Гедера (или Гедерофаим)15:36 Или: «Гедера и Гедерофаим». – четырнадцать городов с окрестными поселениями.

37Ценан, Хадаша, Мигдал-Гад, 38Дилеан, Мицпе, Иоктеил, 39Лахиш, Боцкат, Эглон, 40Каббон, Лахмас, Хитлиш, 41Гедероф, Бет-Дагон, Наама и Македа – шестнадцать городов с окрестными поселениями. 42Ливна, Ефер, Ашан, 43Ифтах, Ашна, Нецив, 44Кеила, Ахзив и Мареша – девять городов с окрестными поселениями.

45Экрон, с окрестными деревнями и поселениями; 46к западу от Экрона – все, что рядом с Ашдодом вместе с их селами; 47Ашдод с окрестными деревнями и селами; Газа с ее деревнями и поселениями до египетского потока и побережья Великого моря.

48В нагорьях:

Шамир, Иаттир, Сохо, 49Данна, Кирьят-Санна (то есть Давир), 50Анав, Эштемо, Аним, 51Гошен, Холон и Гило – одинадцать городов с окрестными поселениями.

52Арав, Дума, Ешан, 53Ианум, Бет-Таппуах, Афека, 54Хумта, Кирьят-Арба (то есть Хеврон) и Цигор – девять городов с окрестными поселениями.

55Маон, Кармил, Зиф, Ютта, 56Изреель, Иокдам, Заноах, 57Каин, Гива и Тимна – десять городов с окрестными поселениями.

58Халхул, Бет-Цур, Гедор, 59Маараф, Бет-Аноф и Элтекон – шесть городов с окрестными поселениями15:59 В древнем переводе список продолжается: «Текоа, Ефрафа (то есть Вифлеем), Пеор, Етам, Кулон, Татам, Шореш, Керем, Галлим, Бет-Эр и Манахат – одинадцать городов с окрестными поселениями»..

60Кирьят-Баал (то есть Кирьят-Иеарим) и Равва – два города с окрестными поселениями.

61В пустыне:

Бет-Арава, Миддин, Секаха, 62Нившан, Ир-Мелах и Эн-Геди – шесть городов с окрестными поселениями.

63Иуда не смог выселить иевусеев, которые жили в Иерусалиме; до сегодняшнего дня иевусеи живут там вместе с народом Иуды.