Yoswa 10 – CCL & CARS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 10:1-43

Kuyimitsidwa kwa Dzuwa

1Adoni-Zedeki mfumu ya ku Yerusalemu inamva kuti Yoswa wagonjetsa ndi kuwononga kotheratu mzinda wa Ai pamodzi ndi mfumu yake, monga anachitira ndi Yeriko ndi mfumu yake. Inamvanso kuti anthu a ku Gibiyoni anachita pangano la mtendere ndi Israeli ndipo amakhala pakati pawo. 2Choncho iye ndi anthu ake anachita mantha aakulu, chifukwa Gibiyoni unali mzinda waukulu kwambiri, monga mzinda uliwonse wokhala ndi mfumu. Unali waukulu ndipo ankhondo ake anali olimba mtima. 3Chotsatira chake Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu inatuma uthenga kwa Hohamu mfumu ya Hebroni, Piramu mfumu ya Yarimuti, Yafiya mfumu ya Lakisi ndi Debri mfumu ya Egiloni. 4Iye anatumiza mawu kuti, “Bwerani mudzandithandize kumenyana ndi Gibiyoni, chifukwa anthu ake achita pangano la mtendere ndi Yoswa ndi Aisraeli.”

5Mafumu asanu a Aamori aja, mfumu ya Yerusalemu, mfumu ya Hebroni, mfumu ya Yarimuti, mfumu ya Lakisi ndi mfumu ya Egiloni, anagwirizana. Iwo anasonkhanitsa ankhondo awo nazungulira mzinda wa Gibiyoni ndi kuwuthira nkhondo.

6Koma anthu a ku Gibiyoni anatumiza uthenga kwa Yoswa ku misasa ya ku Giligala nati, “Musawataye anthu anu! Bwerani msanga mudzatipulumutse! Dzatithandizeni chifukwa mafumu a Aamori ochokera ku dziko la ku mapiri agwirizana kuti adzatithire nkhondo.”

7Choncho Yoswa ananyamuka kuchoka ku Giligala ndi gulu lake la ankhondo pamodzi ndi anthu ake olimba mtima. 8Yehova anati kwa Yoswa, “Usawaope, Ine ndawapereka mʼdzanja lako. Palibe ndi mmodzi mwa amenewa amene adzalimbe.”

9Atayenda usiku wonse kuchokera ku Giligala, Yoswa anawathira nkhondo mwadzidzidzi. 10Yehova anachititsa mantha adani aja atangoona gulu lankhondo la Israeli. Choncho Aisraeli anagonjetsa Aamori ku Gibiyoni ndipo anawathamangitsa mu msewu wopita ku Beti-Horoni ndi kuwapha njira yonse yopita ku Azeka ndi Makeda. 11Pamene ankathawa pamaso pa Israeli pa njira yochokera ku Beti-Horoni mpaka ku Azeka, Yehova anawagwetsera matalala akuluakulu kuchokera kumwamba ndipo ambiri mwa iwo anafa ndi matalala kuposa amene anaphedwa ndi lupanga la Israeli.

12Pa tsiku limene Yehova anapereka Aamori mʼmanja mwa Israeli, Yoswa ananena kwa Yehova pamaso pa Israeli kuti,

“Iwe dzuwa, ima pamwamba pa Gibiyoni,

mwezi ima pamwamba pa chigwa cha Ayaloni.”

13Choncho dzuwa linayima,

mwezinso unayima,

mpaka dziko la Israeli litagonjetsa adani ake.

Zimenezi zalembedwa mʼbuku la Yasari.

Dzuwa linayima pamodzimodzi pakati pa thambo mlengalenga, osayendanso kwa tsiku lathunthu. 14Sipanakhaleponso tsiku ngati limeneli kuyambira kale, tsiku limene Yehova anamvera munthu. Izi zinatero chifukwa Yehova ankamenyera nkhondo Aisraeli.

15Kenaka Yoswa anabwerera pamodzi ndi Aisraeli onse ku misasa ku Giligala.

Kuphedwa kwa Mafumu Asanu a Aamori

16Mafumu asanu aja anathawa ndi kukabisala ku phanga la Makeda. 17Koma Yoswa anamva kuti mafumu asanu awapeza akubisala ku phanga la Makeda. 18Tsono Yoswa analamula kuti, “Mugubuduzire miyala ikuluikulu pa khomo la phangalo, ndipo muyike anthu ena kuti azilondera. 19Koma inu musakhaleko! Thamangitsani adani anu, muwathire nkhondo kuchokera kumbuyo ndipo musawalole kuti akafike ku mizinda yawo, pakuti Yehova Mulungu wanu wawapereka mʼmanja mwanu.”

20Kotero Yoswa ndi Aisraeli anapha anthu aja, kupatulapo ochepa amene anathawa nakabisala ku mizinda yawo. 21Kenaka gulu lonse la ankhondo linabwerera bwinobwino kwa Yoswa ku misasa ya ku Makeda, palibe aliyense mu mzindamo amene anaputanso Aisraeli.

22Yoswa anati, “Tsekulani khomo la phangalo ndipo muwabweretse kwa ine mafumu asanuwo.” 23Pamenepo mafumu asanu aja anatulutsidwa, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yarimuti, mfumu ya ku Lakisi, ndi mfumu ya ku Egiloni. 24Atabwera nawo kwa Yoswa, iye anayitana Aisraeli onse. Ndipo analamula akuluakulu ake amene anapita naye limodzi kuti, “Bwerani kuno ndipo apondeni pakhosi mafumuwa.”

25Yoswa anawawuza kuti, “Musaope kapena kutaya mtima. Khalani amphamvu ndi olimba mtima popeza umo ndi mmene Yehova adzachitire ndi adani anu onse amene mudzamenyana nawo.” 26Kenaka Yoswa anawabaya ndi kuwapha mafumuwo ndipo anawapachika pa mitengo isanu ndipo anakhala pamenepo mpaka madzulo.

27Dzuwa litalowa, Yoswa analamula kuti awachotse pa mitengo ija ndi kuwaponya mʼphanga limene ankabisalamo. Pa khomo pa phangalo anayikapo miyala ikuluikulu imene ilipo mpaka lero.

28Tsiku lomwelo Yoswa analanda mzinda wa Makeda. Iye anapha anthu a mu mzindamo ndi mfumu yake ndipo sanasiye aliyense wamoyo. Yoswa anachita ndi mfumu ya ku Makeda monga anachitira ndi mfumu ya Yeriko.

Agonjetsa Mizinda ya Kummwera

29Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anapitirira kuchokera ku Makeda nakafika ku Libina ndi kuthira nkhondo mzindawo. 30Yehova anaperekanso mzindawo ndi mfumu yake mʼmanja mwa Aisraeli. Ndipo Yoswa anapha onse amene anali mu mzindamo. Palibe amene anatsala wamoyo. Ndipo Yoswa anachita ndi mfumu ya Libina monga anachitira ndi mfumu ya Yeriko.

31Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anapitirira kuchokera ku Libina kupita ku Lakisi. Iye anazungulira mzindawo ndi kuwuthira nkhondo. 32Yehova anapereka Lakisi kwa Israeli; ndipo Yoswa anawulanda pa tsiku lachiwiri. Monga anachita ndi mzinda wa Libina, Yoswa anapha anthu onse okhala mu mzinda wa Lakisi, ndipo palibe amene anatsala ndi moyo. 33Nthawi imeneyi nʼkuti Horamu mfumu ya Gezeri itabwera kudzathandiza Lakisi koma Yoswa anamugonjetsa pamodzi ndi asilikali ake ndipo palibe anatsala wamoyo.

34Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anapitirira kuchokera ku Lakisi nakafika ku Egiloni. Iwo anazungulira mzindawo ndi kuwuthira nkhondo. 35Anawulanda tsiku lomwelo ndipo anapha aliyense amene anali mu mzindawo monga momwe anachitira ku Lakisi.

36Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anachoka ku Egiloni nakafika ku Hebroni ndi kukawuthira nkhondo. 37Iwo analanda mzindawo napha ndi lupanga mfumu yake pamodzi ndi onse amene ankakhala mʼmenemo. Monga anachita ndi mzinda wa Egiloni, kuti sanasiye aliyense ndi moyo, anachitanso chimodzimodzi ndi mzinda wa Hebroni.

38Pambuyo pake Yoswa ndi Aisraeli onse anatembenukira mzinda wa Debri ndi kukawuthira nkhondo. 39Iwo analanda mzindawo ndi midzi ndi kupha mfumu yake pamodzi ndi onse okhala mʼmenemo. Anachita ndi mzinda wa Debri pamodzi ndi mfumu yake zofanana ndi zimene anachita ndi mzinda wa Libina ndi wa Hebroni.

40Motero Yoswa anagonjetsa dziko lonselo. Anapha mafumu onse a dera la kumapiri, dera la kummawa, dera la kumadzulo mʼmphepete mwa phiri, ndiponso dera la ku magomo, kummwera. Iye sanasiye wina aliyense wamoyo. Anapha onse amene anali moyo monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli analamulira. 41Yoswa anawagonjetsa iwo kuyambira ku Kadesi Barinea mpaka ku Gaza, ndiponso kuchokera ku chigawo chonse cha Goseni mpaka ku Gibiyoni. 42Yoswa anagonjetsa mafumu onsewa ndi kulanda dziko lawo kamodzinʼkamodzi chifukwa Yehova Mulungu wa Israeli anawamenyera nkhondo.

43Pambuyo pake Yoswa ndi Aisraeli onse anabwerera ku misasa yawo ku Giligala.

Священное Писание

Иешуа 10:1-43

Битва с аморреями. Остановленное солнце

1Когда Адони-Цедек, царь Иерусалима, услышал о том, что Иешуа захватил Гай и полностью уничтожил его, сделав с Гаем и его царём то же, что он сделал с Иерихоном и его царём, и о том, что жители Гаваона заключили с Исраилом мир и живут среди них, 2он очень испугался, потому что Гаваон был такой же большой город, как один из царских городов. Он был больше Гая, и все его жители были храбрыми воинами. 3И Адони-Цедек, царь Иерусалима, послал Гогаму, царю Хеврона, Пираму, царю Иармута, Иафие, царю Лахиша, и Девиру, царю Эглона, весть:

4– Придите и помогите мне напасть на Гаваон, – говорил он, – потому что он заключил мир с Иешуа и исраильтянами.

5Пять аморрейских царей – цари Иерусалима, Хеврона, Иармута, Лахиша и Эглона – объединили силы. Они вышли со всеми своими воинами, расположились станом напротив Гаваона и напали на него. 6Тогда гаваонитяне послали сказать Иешуа в гилгалский лагерь:

– Не оставь своих рабов! Скорее приходи к нам и спаси нас! Помоги нам, потому что все аморрейские цари с нагорий объединили свои силы против нас.

7Иешуа выступил из Гилгала со всем своим войском, со всеми лучшими воинами. 8Вечный сказал Иешуа:

– Не бойся их. Я отдал их в твои руки. Никто из них не сможет противостоять тебе.

9Иешуа шёл из Гилгала всю ночь и захватил своих врагов врасплох. 10Вечный привёл их в смятение перед Исраилом, который разбил их, одержав при Гаваоне великую победу. Исраильтяне гнались за ними по дороге, поднимающейся в Бет-Хорон, и разили их до Азеки и Маккеды. 11Когда аморреи бежали от исраильтян по склону Бет-Хорона в Азеку, Вечный забросал их с неба огромными градинами, и от града погибло больше народа, чем от мечей исраильтян.

12-13Иешуа воззвал к Вечному в тот день, когда Вечный отдал аморреев исраильтянам, и он сказал в присутствии Исраила (как и написано в «Книге Праведного»10:12-13 Букв.: «Книга Иашара». Эта древняя книга, не вошедшая в состав Священного Писания, не сохранилась до наших времён.):

«Стой, солнце, над Гаваоном,

и ты, луна, – над долиною Аялон!»

И солнце остановилось,

и стояла луна,

пока народ не отомстил своим врагам.

Солнце стояло посреди неба и медлило садиться почти целый день. 14Никогда не было такого дня ни прежде, ни потом – дня, когда Вечный послушался человека. Ведь Вечный сражался за Исраил.

15После этого Иешуа вернулся со всем Исраилом в гилгалский лагерь.

Казнь пяти аморрейских царей

16А пять царей бежали и укрылись в пещере в Маккеде. 17Когда Иешуа доложили, что пятерых царей обнаружили прячущимися в пещере в Маккеде, 18он сказал:

– Привалите к входу пещеры большие камни и приставьте к ней стражу. 19Но не останавливайтесь! Преследуйте своих врагов, атакуйте их сзади и не дайте им добраться до своих городов, потому что Вечный, ваш Бог, отдал их в ваши руки.

20Иешуа и исраильтяне истребили их полностью, не оставив в живых почти никого, и лишь немногие уцелевшие добрались до своих укреплённых городов. 21После этого всё войско благополучно вернулось к Иешуа в лагерь в Маккеде, и никто не посмел даже рта раскрыть против исраильтян.

22Иешуа сказал:

– Откройте пещеру и выведите ко мне тех пятерых царей!

23И к нему вывели из пещеры пятерых царей – царей Иерусалима, Хеврона, Иармута, Лахиша и Эглона. 24Когда к Иешуа вывели этих пятерых царей, он призвал всех исраильтян и сказал военачальникам, которые ходили с ним:

– Подойдите и поставьте ваши ноги на шеи этих царей.

Они подошли и поставили ноги на шеи царей.

25Иешуа сказал им:

– Не бойтесь и не теряйте присутствия духа! Будьте тверды и мужественны! Вечный поступит так со всеми врагами, с которыми вы будете воевать.

26Затем Иешуа поразил и умертвил царей и повесил их на пяти деревьях, и они висели на деревьях до вечера. 27На закате Иешуа приказал, и их сняли с деревьев и бросили в пещеру, где они укрывались. К входу в пещеру привалили большие камни, которые там и по сегодняшний день.

28В тот день Иешуа взял Маккеду. Он предал город и его царя мечу и полностью истребил всех жителей. Он никого не оставил в живых. Он сделал с царём Маккеды то же, что и с царём Иерихона.

Захват южных городов

29Затем Иешуа, и с ним весь Исраил, пошёл из Маккеды к Ливне и напал на неё. 30Вечный отдал в руки Исраила и этот город вместе с его царём. Город и всех, кто в нём был, Иешуа предал мечу. Он никого не оставил там в живых. Он сделал с его царём то же, что и с царём Иерихона.

31Затем Иешуа, и с ним весь Исраил, пошёл из Ливны к Лахишу. Он поставил напротив него стан и напал на него. 32Вечный отдал Лахиш Исраилу, и Иешуа взял его на второй день. Город и всех в нём он предал мечу, как он сделал это в Ливне. 33Тем временем Хорам, царь Гезера, пришёл Лахишу на помощь, но Иешуа разбил его и его войско, никого не оставив в живых.

34Затем Иешуа, и с ним весь Исраил, пошёл из Лахиша в Эглон. Они поставили напротив него стан и напали на него. 35Они взяли его в тот же день и предали его мечу. Иешуа полностью истребил всех, кто в нём был, как он сделал это с Лахишем.

36Затем Иешуа, и с ним весь Исраил, пошёл из Эглона в Хеврон и напал на него. 37Исраильтяне взяли город и предали его мечу вместе с его царём, его поселениями и всеми, кто в нём был. Они никого не оставили в живых. Как и в Эглоне, Иешуа полностью уничтожил и город, и всех, кто в нём был.

38Затем Иешуа, и с ним весь Исраил, повернул назад к Девиру и напал на него. 39Они взяли город, его царя и селения и предали их мечу. Они полностью истребили всех, кто в нём был, никого не оставив в живых. Иешуа сделал с Девиром то же, что и с Ливной и её царём и с Хевроном.

40Так Иешуа покорил всю ту область – нагорья и Негев, западные предгорья и горные склоны, и всех её царей. Он никого не оставил в живых. Он полностью истребил всё живое, как повелел Вечный, Бог Исраила. 41Иешуа покорил земли от Кадеш-Барни до Газы и всю область Гошен10:41 Гошен – эту область нужно отличать от Гошена в Египте (см., напр., Нач. 47:27). до Гаваона. 42Всех этих царей и их земли Иешуа взял за один поход, потому что Вечный, Бог Исраила, сражался за Исраил.

43Затем Иешуа и весь Исраил вернулись в гилгалский лагерь.