Yoswa 9 – CCL & CARS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 9:1-27

Chinyengo cha Agibiyoni

1Mafumu onse okhala kumadzulo kwa Yorodani atamva zimenezi pamodzi ndi mafumu okhala ku mayiko a ku mapiri, mu zigwa, mʼmbali mwa Nyanja yayikulu mpaka ku Lebanoni (mafumu a Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi, ndi Ayebusi), 2anapangana kuti achite nkhondo ndi Yoswa ndi Israeli.

3Koma Ahivi ena a ku Gibiyoni atamva zomwe Yoswa anachitira mizinda ya Yeriko ndi Ai, 4anaganiza zochita zachinyengo. Anapita nasenzetsa abulu awo chakudya mʼmatumba akalekale ndiponso matumba a vinyo achikopa ongʼambikangʼambika. 5Anthuwa anavala nsapato zakutha ndi zazigamba ndiponso anavala sanza. Buledi wawo yense anali wowuma ndi wowola. 6Ndipo anapita kwa Yoswa ku msasa ku Giligala ndikumuwuza kuti, pamodzi ndi Aisraeli onse, “Ife tachokera ku dziko lakutali, ndipo tikufuna kuti muchite mgwirizano ndi ife.”

7Koma Aisraeli anayankha Ahiviwo kuti, “Mwinatu inu mukukhala pafupi ndi ife. Tsono ife tingachite bwanji mgwirizano ndi inu?”

8Iwo anati kwa Yoswa, “Ife ndife akapolo anu.”

Tsono Yoswa anawafunsa kuti, “Inu ndinu yani ndipo mukuchokera kuti?”

9Iwo anayankha kuti, “Akapolo anufe tachokera ku dziko lakutali chifukwa tamva za Yehova Mulungu wanu. Tamva mbiri yonse ya zimene Iye anachita ku Igupto, 10ndi zonse zimene anachita kwa mafumu awiri a Aamori kummawa kwa Yorodani, mfumu Sihoni ya Hesiboni ndi Ogi mfumu ya Basani amene amalamulira ku Asiteroti. 11Tsono akuluakulu athu ndi onse amene akukhala mʼdziko lathu anati kwa ife. Tengani chakudya cha pa ulendo wanu. Pitani mukakumane nawo ndipo mukati kwa iwo, ‘Ife ndife akapolo anu, ndipo tikufuna kuti mugwirizane nafe za mtendere.’ ” 12Buledi wathuyu anali wotentha pamene timanyamuka ku mudzi kubwera kwa inu. Koma tsopano taonani ali gwaa ndiponso wawola. 13Zikopa zimene tinathiramo vinyozi zinali zatsopano, koma taonani zathetheka. Zovala zathu ndi nsapato zathu zatha chifukwa cha kutalika kwa ulendo.

14Aisraeli anatengako chakudya chawo koma sanafunse kwa Yehova. 15Choncho Yoswa anapangana nawo za mtendere kuti sadzawapha, ndipo atsogoleri a gulu anavomereza pochita lumbiro.

16Patatha masiku atatu atachita mgwirizano wa mtendere ndi Agibiyoni, Aisraeli anamva kuti anali anansi awo, anthu amene amakhala nawo pafupi. 17Tsono Aisraeli ananyamuka ulendo ndipo tsiku lachitatu anafika ku mizinda ya Gibiyoni, Kefira, Beeroti ndi Kiriati-Yearimu. 18Koma Aisraeli sanawaphe anthuwo chifukwa atsogoleri awo anali atalonjeza mʼdzina la Yehova Mulungu wa Israeli za Agibiyoniwo.

Koma anthu onse anatsutsana ndi atsogoleriwo. 19Koma atsogoleriwo anayankha kuti, “Ife tinawalonjeza mʼdzina la Yehova, Mulungu wa Israeli, ndipo tsopano sitingawaphe. 20Chimene tidzachita nawo ndi ichi: Tidzawasiya akhale ndi moyo kuti mkwiyo wa Yehova usatigwere chifukwa chophwanya lonjezo limene tinawalonjeza.” 21Anapitiriza kunena kuti “Asiyeni akhale ndi moyo, komabe akhale otidulira mitengo ndi kutitungira madzi ogwiritsa ntchito pa chipembedzo.” Lonjezo la atsogoleriwo linasungidwa.

22Kenaka Yoswa anayitanitsa Agibiyoni aja nawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani inu munatinyenga ponena kuti mumachokera kutali pamene zoona zake nʼzoti mumakhala pafupi pomwe pano? 23Tsopano popeza mwachita izi, Mulungu wakutembererani ndipo palibe wina mwa inu amene akhale mfulu. Nthawi zonse inu muzidzatidulira nkhuni ndi kutitungira madzi ku Nyumba ya Yehova.”

24Iwo anayankha Yoswa kuti, “Ife akapolo anufe tinachita zimenezi chifukwa tinamva bwino lomwe kuti Yehova Mulungu wanu analamula Mose mtumiki wake kuti adzakupatsani dziko lonseli ndi kuti anthu onse okhalamo adzaphedwe. Tsono ife tinachita mantha aakulu ndipo tinachita zimenezi pofuna kupulumutsa miyoyo yathu. 25Tsopanotu ife tili mʼmanja mwanu, ndipo inu chitani nafe monga kukukomerani.”

26Tsono Yoswa anawapulumutsa mʼmanja mwa Aisraeli ndipo sanawaphe. 27Kuyambira tsiku limenelo Agibiyoni aja anasanduka odula nkhuni zaguwa lansembe la Yehova ndiponso otunga madzi. Mpaka lero lino iwo akuchitabe zimenezi kulikonse kumene Yehova anasankha.

Священное Писание

Иешуа 9:1-27

Обман исраильтян гаваонитянами

1Когда об этом услышали все цари к западу от Иордана – в нагорьях, в западных предгорьях и по всему побережью Средиземного моря9:1 Букв.: «Великого моря». до самого Ливана (цари хеттов, аморреев, хананеев, перизеев, хивеев и иевусеев), 2они собрались вместе, чтобы воевать с Иешуа и Исраилом.

3Но жители Гаваона, услышав о том, что Иешуа сделал с Иерихоном и Гаем, 4прибегли к хитрости: они пошли, и собрали в дорогу еды, и нагрузили своих ослов ветхими мешками и ветхими бурдюками для вина, изорванными и заплатанными. 5На ногах у них были поношенные и залатанные сандалии, их одежда также была очень ветхой. Весь хлеб, что они взяли с собой, был чёрствым и заплесневелым. 6Они пришли к Иешуа в гилгалский лагерь и сказали ему и исраильтянам:

– Мы пришли из далёкой страны. Заключите с нами союз.

7Исраильтяне сказали хивеям:

– А вдруг вы живёте рядом с нами? Как же нам тогда заключать с вами союз?

8– Мы твои рабы, – сказали они Иешуа.

Но Иешуа спросил:

– Кто вы такие и откуда вы пришли?

9Они ответили:

– Твои рабы пришли из очень далёкой страны, узнав о славе Вечного, твоего Бога. Мы слышали о Нём: обо всём, что Он сделал в Египте, 10и обо всём, что Он сделал с двумя царями аморреев к востоку от Иордана – с Сигоном, царём Хешбона, и Огом, царём Башана, который правил в Аштароте. 11Наши старейшины и все жители нашей страны сказали нам: «Соберите в дорогу пищу, идите, встретьтесь с ними и скажите им: „Мы ваши рабы, заключите с нами союз“». 12Вот наш хлеб. Он был ещё тёплым, когда, отправляясь к вам, мы дома запасались им в дорогу. Но посмотрите теперь, как он зачерствел и заплесневел. 13А эти бурдюки для вина, когда мы их наполняли, были новыми, но посмотрите, как они изорвались теперь. А наша одежда и сандалии совсем износились за долгую дорогу.

14Исраильтяне в знак мира взяли и ели из их припасов, но не спросили Вечного. 15И Иешуа заключил с ними мир, охраняя их жизни договором, а вожди народа скрепили его клятвой.

16Спустя три дня после того, как они заключили союз с гаваонитянами, исраильтяне узнали, что это их соседи, живущие рядом. 17Тогда исраильтяне отправились в путь и на третий день пришли к их городам – Гаваону, Кефире, Беэроту и Кириат-Иеариму. 18Но исраильтяне не напали на них, потому что вожди народа поклялись им Вечным, Богом Исраила. Весь народ роптал против вождей, 19но они ответили:

– Мы поклялись им Вечным, Богом Исраила, и не можем теперь тронуть их. 20Вот что мы сделаем с ними: мы оставим их в живых, чтобы на нас не обрушился гнев за нарушение клятвы, которую мы им дали.

21И вожди народа продолжили:

– Пусть они живут, но будут дровосеками и водоносами для всего нашего общества.

Так обещание вождей не было нарушено.

22Иешуа призвал гаваонитян и сказал:

– Почему вы обманули нас, сказав: «Мы живём далеко от вас», тогда как вы живёте рядом с нами? 23Теперь вы прокляты. Вы всегда будете работать дровосеками и водоносами для дома моего Бога9:23 Позже это наказание обратилось в благословение: в начале царствования Сулеймана в Гаваоне находился священный шатёр (см. 2 Лет. 1:3), где через свою работу гаваонитяне могли служить истинному Богу..

24Они ответили Иешуа:

– Твои рабы узнали наверняка, что Вечный, твой Бог, повелел Своему рабу Мусе отдать вам всю эту землю и истребить перед вами всех её жителей. Мы очень испугались за свою жизнь и потому поступили так. 25Теперь мы в твоих руках. Поступай с нами, как сочтёшь лучшим и справедливым.

26И Иешуа защитил их от исраильтян, и те не убили их. 27В тот день он сделал гаваонитян дровосеками и водоносами для народа и для жертвенника Вечного на том месте, какое бы Вечный ни избирал. Они делают это и до сих пор.