Yeremiya 50 – CCL & NIV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 50:1-46

Uthenga Wonena za Babuloni

1Uthenga umene Yehova anayankhula ndi mneneri Yeremiya wonena za mzinda wa Babuloni ndi anthu ake ndi uwu:

2“Lengeza ndi kulalika pakati pa anthu a mitundu ina,

kweza mbendera ndipo ulengeze;

usabise kanthu, koma uwawuze kuti,

‘Babuloni wagwa;

mulungu wawo Beli wachititsidwa manyazi,

nayenso Mariduku wagwidwa ndi mantha.

Milungu yake yagwidwa ndi mantha

ndipo mafano ake adzagwidwa ndi mantha.’

3Mtundu wa anthu wochokera kumpoto wadzathira nkhondo Babuloni

ndi kusandutsa bwinja dziko lake.

Kumeneko sikudzakhalanso

munthu kapena nyama.

4“Masiku amenewo, nthawi imeneyo,”

akutero Yehova,

“anthu a ku Israeli ndi anthu a ku Yuda

onse pamodzi adzabwera akulira. Adzafunitsitsa kuchita zimene Yehova Mulungu wawo akufuna.

5Adzafunsa njira ya ku Ziyoni

ndi kuyamba ulendo wopita kumeneko.

Iwo adzadzipereka kwa Yehova

pochita naye pangano lamuyaya

limene silidzayiwalika.

6“Anthu anga ali ngati nkhosa zotayika;

abusa awo

anawasocheretsa mʼmapiri.

Iwo anayendayenda mʼmapiri ndi mʼzitunda

mpaka kuyiwala kwawo.

7Aliyense amene anawapeza anawawononga;

adani awo anati, ‘Ife si olakwa,

chifukwa iwo anachimwira Yehova, amene ali mpumulo wawo weniweni

ndi amene makolo awo anamukhulupirira.’

8“Thawaniko ku Babuloni;

chokani mʼdziko la Ababuloni.

Muyambe inu kutuluka ngati atonde amene amatsogolera ziweto.

9Taonani, ndidzaukitsa gulu lankhondo lamphamvu la mitundu ina

ndi kubwera nalo kuchokera kumpoto

kudzamenyana ndi Babuloni.

Iwo adzandandalika ankhondo awo ndi kugonjetsa Babuloni.

Mivi yawo ili ngati ya ankhondo aluso,

yosapita padera.

10Motero Ababuloni adzafunkhidwa;

ndipo onse omufunkha adzakhuta,”

akutero Yehova.

11“Inu Ababuloni, munawononga anthu anga osankhika.

Ndiye pano mukukondwa, mukusangalala.

Mukulumphalumpha mokondwa ngati mwana wangʼombe wopuntha tirigu

ndiponso mukulira monyada ngati ngʼombe zazimuna.

12Koma mzinda wanu udzachititsidwa manyazi kwambiri.

Mzinda umene uli ngati mayi wanu udzanyazitsidwa.

Babuloni adzasanduka chitsirizira cha anthu onse.

Mzinda wawo udzakhala ngati thengo, ngati dziko lowuma lachipululu.

13Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova Babuloni adzakhala wopanda anthu

ndipo adzakhala chipululu chokhachokha.

Onse odutsa kumeneko adzachita mantha ndipo azidzangotsonya

chifukwa cha chiwonongeko chake chachikulu.

14“Inu okoka uta,

konzekani kuti muthire nkhondo mzinda wa Babuloni mbali zonse.

Muponyereni mivi yanu yonse

chifukwa anachimwira Yehova.

15Mufuwulireni mbali zonse pakuti wagonja.

Nsanja zake zagwa.

Malinga ake agwetsedwa.

Kumeneku ndiko kulipsira kwa Yehova.

Mulipsireni,

mumuchite zomwe iye anachitira anthu ena.

16Chotsani ku Babuloni munthu wofesa mbewu aliyense,

ndiponso wodula tirigu ndi chikwakwa chake pa nthawi yokolola.

Poona lupanga la ozunza anzawo,

aliyense adzabwerera kwa anthu ake;

adzathawira ku dziko la kwawo.

17“Aisraeli ali ngati nkhosa zomwe zabalalika

pothamangitsidwa ndi mikango.

Mfumu ya ku Asiriya ndiye inayamba kuwapha Aisraeliwo.

Wotsiriza anali Nebukadinezara

mfumu ya ku Babuloni

amene anachita ngati kuphwanya mafupa ake.”

18Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,

“Ndidzalanga mfumu ya ku Babuloni pamodzi ndi dziko lake

monga momwe ndinalangira mfumu ya ku Asiriya.

19Koma ndidzabwezera Israeli ku msipu wake

ndipo adzadya mʼminda ya ku Karimeli ndi Basani;

adzadya nakhuta ku mapiri

a ku Efereimu ndi Giliyadi.

20Masiku amenewo, nthawi imeneyo,”

akutero Yehova,

“anthu adzafunafuna zolakwa za Israeli

koma sadzapeza nʼchimodzi chomwe,

ndipo adzafufuza machimo a Yuda,

koma sadzapeza ndi limodzi lomwe,

chifukwa otsala amene ndawasiya ndidzawakhululukira.

21“Lithireni nkhondo dziko la Merataimu

ndi anthu okhala ku Pekodi.

Muwaphe ndi lupanga ndi kuwawonongeratu,”

akutero Yehova.

“Chitani zonse monga momwe ndakulamulani.

22Mʼdziko muli phokoso la nkhondo,

phokoso la chiwonongeko chachikulu!

23Taonani mʼmene waphwanyikira ndi kuwonongekera

uja amati ndi nyundo ya dziko lonse lapansi.

Mzinda wa Babuloni wasanduka chinthu chochititsa mantha

pakati pa mitundu ina!

24Ndinakutchera msampha, iwe Babuloni,

ndipo wakodwamo iwe wosazindikira kanthu;

unapezeka ndiponso unakodwa

chifukwa unalimbana ndi Yehova.

25Yehova watsekula nyumba ya zida zake

ndipo watulutsa zida za ukali wake,

pakuti Ambuye Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ntchito yoti agwire

mʼdziko la Ababuloni.

26Mumenyane naye Babuloni mbali zonse.

Anthu ake muwawunjike

ngati milu ya tirigu.

Muwawononge kotheratu

ndipo pasakhale wopulumuka ndi mmodzi yemwe.

27Iphani ankhondo ake onse.

Onse aphedwe ndithu.

Tsoka lawagwera

pakuti tsiku lawo lachilango lafika.

28Tikumva anthu othawa nkhondo ochokera ku Babuloni

akulengeza mu Yerusalemu

za kulipsira kwa Yehova Mulungu wathu.

Iye akulipsira chifukwa chowononga Nyumba yake.

29“Itanani anthu oponya mivi kudzathira nkhondo Babuloni.

Muyitanenso onse amene amakoka mauta.

Mangani misasa ya nkhondo momuzungulira;

musalole munthu aliyense kuthawa.

Muchiteni monga momwe

iye anachitira anthu ena.

Iyeyu ananyoza

Yehova, Woyera wa Israeli.

30Nʼchifukwa chake, anyamata ake adzaphedwa mʼmabwalo ake;

ankhondo ake onse adzaphedwa tsiku limenelo,”

akutero Yehova.

31“Taona, ndikukuthira nkhondo, iwe wodzikuzawe,”

akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse,

“chifukwa tsiku lako lafika,

nthawi yoti ndikulange yakwana.

32Wodzikuzawe udzapunthwa nʼkugwa

ndipo palibe amene adzakudzutse;

ndidzayatsa moto mʼmizinda yake

umene udzanyeketsa onse amene amuzungulira.”

33Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Anthu a ku Israeli akuzunzidwa,

pamodzi ndi anthu a ku Yuda,

ndipo onse amene anawagwira ukapolo awagwiritsitsa,

akukana kuwamasula.

34Koma Mpulumutsi wawo ndi wamphamvu;

dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.

Iye adzawateteza molimba pa mlandu wawo

nʼcholinga choti abweretse mtendere mʼdziko lawo,

koma adzavutitsa okhala ku Babuloni.”

35Yehova akuti,

“Imfa yalunjika pa Ababuloni,

pa akuluakulu ake

ndi pa anthu ake a nzeru!

36Imfa yalunjika pa aneneri abodza

kuti asanduke zitsiru.

Imfa yalunjika pa ankhondo ake

kuti agwidwe ndi mantha aakulu.

37Imfa ilunjike pa akavalo ake ndi magaleta ake.

Ilunjikanso pa magulu ankhondo achilendo amene ali pakati pawo

kuti asanduke ngati akazi.

Chiwonongeko chilunjikenso pa chuma chake

kuti chidzafunkhidwe.

38Chilala chilunjike pa madzi ake

kuti aphwe.

Babuloni ndi dziko la mafano,

ndipo anthu afika poyaluka nawo mafanowo.

39“Nʼchifukwa chake nyama zakuthengo ndi afisi zidzakhala kumeneko

ndipo kudzakhalanso akadzidzi.

Kumeneko sikudzapezekako anthu,

ndithu anthu sadzakhalako pa mibado yonse.

40Monga momwe Mulungu anawonongera Sodomu ndi Gomora

pamodzi ndi mizinda yonse yozungulira,”

akutero Yehova,

“momwemonso palibe amene adzakhale kumeneko;

anthu sadzayendanso mʼmenemo.

41“Taonani! Gulu lankhondo likubwera kuchokera kumpoto;

mtundu wa anthu amphamvu pamodzi ndi mafumu ambiri,

wanyamuka kuchokera kumathero a dziko lapansi.

42Atenga mauta ndi mikondo;

ndi anthu ankhanza ndipo alibe chifundo.

Phokoso lawo likumveka ngati mkokomo wa nyanja.

Akwera pa akavalo awo,

ndipo akonzekera kudzakuthira nkhondo

iwe Babuloni.

43Mfumu ya ku Babuloni yamva za mbiri yawo,

ndipo yalobodokeratu.

Ikuda nkhawa,

ikumva ululu ngati wa mayi pa nthawi yake yochira.

44Taonani, monga mkango wochokera ku nkhalango ya ku Yorodani

kupita ku msipu wobiriwira,

momwemonso ine ndidzapirikitsa Babuloni mʼdziko lake mwadzidzidzi.

Pambuyo pake ndidzawayikira wowalamulira amene ndamufuna Ine.

Wofanana nane ndani ndipo ndani amene angalimbane nane?

Ndi mtsogoleri wa dziko uti amene anganditengere ku bwalo la milandu?”

45Nʼchifukwa chake imvani.

Izi ndi zimene Ine Yehova ndakonza zolangira anthu a ku Babuloni.

Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolo

ndipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo.

46Akadzagwa Babuloni padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera,

ndipo kulira kwawo kudzamveka pakati pa mitundu yonse ya anthu.

New International Version

Jeremiah 50:1-46

A Message About Babylon

1This is the word the Lord spoke through Jeremiah the prophet concerning Babylon and the land of the Babylonians50:1 Or Chaldeans; also in verses 8, 25, 35 and 45:

2“Announce and proclaim among the nations,

lift up a banner and proclaim it;

keep nothing back, but say,

‘Babylon will be captured;

Bel will be put to shame,

Marduk filled with terror.

Her images will be put to shame

and her idols filled with terror.’

3A nation from the north will attack her

and lay waste her land.

No one will live in it;

both people and animals will flee away.

4“In those days, at that time,”

declares the Lord,

“the people of Israel and the people of Judah together

will go in tears to seek the Lord their God.

5They will ask the way to Zion

and turn their faces toward it.

They will come and bind themselves to the Lord

in an everlasting covenant

that will not be forgotten.

6“My people have been lost sheep;

their shepherds have led them astray

and caused them to roam on the mountains.

They wandered over mountain and hill

and forgot their own resting place.

7Whoever found them devoured them;

their enemies said, ‘We are not guilty,

for they sinned against the Lord, their verdant pasture,

the Lord, the hope of their ancestors.’

8“Flee out of Babylon;

leave the land of the Babylonians,

and be like the goats that lead the flock.

9For I will stir up and bring against Babylon

an alliance of great nations from the land of the north.

They will take up their positions against her,

and from the north she will be captured.

Their arrows will be like skilled warriors

who do not return empty-handed.

10So Babylonia50:10 Or Chaldea will be plundered;

all who plunder her will have their fill,”

declares the Lord.

11“Because you rejoice and are glad,

you who pillage my inheritance,

because you frolic like a heifer threshing grain

and neigh like stallions,

12your mother will be greatly ashamed;

she who gave you birth will be disgraced.

She will be the least of the nations—

a wilderness, a dry land, a desert.

13Because of the Lord’s anger she will not be inhabited

but will be completely desolate.

All who pass Babylon will be appalled;

they will scoff because of all her wounds.

14“Take up your positions around Babylon,

all you who draw the bow.

Shoot at her! Spare no arrows,

for she has sinned against the Lord.

15Shout against her on every side!

She surrenders, her towers fall,

her walls are torn down.

Since this is the vengeance of the Lord,

take vengeance on her;

do to her as she has done to others.

16Cut off from Babylon the sower,

and the reaper with his sickle at harvest.

Because of the sword of the oppressor

let everyone return to their own people,

let everyone flee to their own land.

17“Israel is a scattered flock

that lions have chased away.

The first to devour them

was the king of Assyria;

the last to crush their bones

was Nebuchadnezzar king of Babylon.”

18Therefore this is what the Lord Almighty, the God of Israel, says:

“I will punish the king of Babylon and his land

as I punished the king of Assyria.

19But I will bring Israel back to their own pasture,

and they will graze on Carmel and Bashan;

their appetite will be satisfied

on the hills of Ephraim and Gilead.

20In those days, at that time,”

declares the Lord,

“search will be made for Israel’s guilt,

but there will be none,

and for the sins of Judah,

but none will be found,

for I will forgive the remnant I spare.

21“Attack the land of Merathaim

and those who live in Pekod.

Pursue, kill and completely destroy50:21 The Hebrew term refers to the irrevocable giving over of things or persons to the Lord, often by totally destroying them; also in verse 26. them,”

declares the Lord.

“Do everything I have commanded you.

22The noise of battle is in the land,

the noise of great destruction!

23How broken and shattered

is the hammer of the whole earth!

How desolate is Babylon

among the nations!

24I set a trap for you, Babylon,

and you were caught before you knew it;

you were found and captured

because you opposed the Lord.

25The Lord has opened his arsenal

and brought out the weapons of his wrath,

for the Sovereign Lord Almighty has work to do

in the land of the Babylonians.

26Come against her from afar.

Break open her granaries;

pile her up like heaps of grain.

Completely destroy her

and leave her no remnant.

27Kill all her young bulls;

let them go down to the slaughter!

Woe to them! For their day has come,

the time for them to be punished.

28Listen to the fugitives and refugees from Babylon

declaring in Zion

how the Lord our God has taken vengeance,

vengeance for his temple.

29“Summon archers against Babylon,

all those who draw the bow.

Encamp all around her;

let no one escape.

Repay her for her deeds;

do to her as she has done.

For she has defied the Lord,

the Holy One of Israel.

30Therefore, her young men will fall in the streets;

all her soldiers will be silenced in that day,”

declares the Lord.

31“See, I am against you, you arrogant one,”

declares the Lord, the Lord Almighty,

“for your day has come,

the time for you to be punished.

32The arrogant one will stumble and fall

and no one will help her up;

I will kindle a fire in her towns

that will consume all who are around her.”

33This is what the Lord Almighty says:

“The people of Israel are oppressed,

and the people of Judah as well.

All their captors hold them fast,

refusing to let them go.

34Yet their Redeemer is strong;

the Lord Almighty is his name.

He will vigorously defend their cause

so that he may bring rest to their land,

but unrest to those who live in Babylon.

35“A sword against the Babylonians!”

declares the Lord

“against those who live in Babylon

and against her officials and wise men!

36A sword against her false prophets!

They will become fools.

A sword against her warriors!

They will be filled with terror.

37A sword against her horses and chariots

and all the foreigners in her ranks!

They will become weaklings.

A sword against her treasures!

They will be plundered.

38A drought on50:38 Or A sword against her waters!

They will dry up.

For it is a land of idols,

idols that will go mad with terror.

39“So desert creatures and hyenas will live there,

and there the owl will dwell.

It will never again be inhabited

or lived in from generation to generation.

40As I overthrew Sodom and Gomorrah

along with their neighboring towns,”

declares the Lord,

“so no one will live there;

no people will dwell in it.

41“Look! An army is coming from the north;

a great nation and many kings

are being stirred up from the ends of the earth.

42They are armed with bows and spears;

they are cruel and without mercy.

They sound like the roaring sea

as they ride on their horses;

they come like men in battle formation

to attack you, Daughter Babylon.

43The king of Babylon has heard reports about them,

and his hands hang limp.

Anguish has gripped him,

pain like that of a woman in labor.

44Like a lion coming up from Jordan’s thickets

to a rich pastureland,

I will chase Babylon from its land in an instant.

Who is the chosen one I will appoint for this?

Who is like me and who can challenge me?

And what shepherd can stand against me?”

45Therefore, hear what the Lord has planned against Babylon,

what he has purposed against the land of the Babylonians:

The young of the flock will be dragged away;

their pasture will be appalled at their fate.

46At the sound of Babylon’s capture the earth will tremble;

its cry will resound among the nations.