Oweruza 11 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 11:1-40

1Yefita wa ku Giliyadi anali wankhondo wa mphamvu. Iyeyu amayi ake anali mkazi wachiwerewere, ndipo abambo ake anali Giliyadi. 2Mkazi wake wa Giliyadi anabereka naye ana aamuna. Tsono ana amenewa atakula anapirikitsa Yefita ndi kumuwuza kuti, “Sudzalandirako cholowa mʼnyumba ya abambo athu chifukwa ndiwe mwana wa mkazi wina.” 3Choncho Yefita anathawa kuchoka kwa abale ake ndi kukakhala mʼdziko la Tobu. Kumeneko anakakopa ndi kusonkhanitsa anthu achabechabe ndipo anatuluka pamodzi kukasakaza zinthu.

4Patapita nthawi Aamoni anadzachita nkhondo ndi Israeli. 5Tsono pamene Aamoni ankathira nkhondo Aisraeli, akuluakulu a ku Giliyadi anapita kukamutenga Yefita ku dziko la Tobu. 6Iwo anati kwa iye, “Bwera ukhale mkulu wathu wankhondo kuti timenyane ndi Amoni.”

7Yefita anawawuza Agiliyadi kuti, “Kodi inu suja munkadana nane ndi kundithamangitsa ku nyumba ya abambo anga? Nʼchifukwa chiyani lero mwabwera kwa ine pamene muli pa mavuto?”

8Akuluakulu a ku Giliyadi aja anamuyankha kuti, “Chimene tabwerera kwa iwe ndi chakuti upite nafe kukamenyana ndi Aamoni, ndipo udzakhala wolamulira wa onse okhala mu Giliyadi.”

9Yefita anawayankha akuluakulu a ku Giliyadi kuti, “Ngati mundibwezeranso kwathu kuti ndikachite nkhondo ndi Aamoni ndipo Yehova nʼkukandithandiza kuwagonjetsa, ndidzakhaladi wokulamulirani?”

10Akuluakulu a ku Giliyadi anamuyankha kuti, “Yehova akhale mboni pakati pa inu ndi ife, ngati sitidzachita monga mwa mawu anu.” 11Choncho Yefita anapita nawo akuluakulu a ku Giliyadi aja, ndipo anthu a kumeneko anamusandutsa kukhala wowalamulira ndi mkulu wankhondo. Tsono Yefita anabwerezanso mawu omwewa pamaso pa Yehova ku Mizipa.

12Kenaka Yefita anatuma amithenga kwa mfumu ya Aamoni ndi funso lakuti, “Kodi ife takuchimwirani chiyani kuti muzichita nkhondo ndi dziko langa?”

13Ndipo mfumu ya Aamoni inayankha amithenga a Yefita aja kuti, “Pamene Israeli amatuluka kuchokera mu Igupto, analanda dziko langa kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki mpakanso ku mtsinje wa Yorodani. Tsopano mundibwezere dziko langa mwamtendere.”

14Yefita anatumizanso amithenga akewo kwa mfumu ya Aamoni 15kukanena kuti,

Yefita akuti, “Israeli sanalande dziko la Mowabu kapena dziko la Aamoni. 16Koma pamene Aisraeli ankachoka ku Igupto anadzera njira ya ku chipululu mpaka ku Nyanja Yofiira nakafika ku Kadesi. 17Kenaka Israeli anatumiza amithenga kwa mfumu ya ku Edomu kuti, ‘Chonde tiloleni kuti tidutse mʼdziko lanu,’ Koma mfumu ya ku Edomu sinamvere zimenezo. Aisraeli anatumizanso amithenga kwa mfumu ya ku Mowabu, ndipo iyo inakananso. Choncho Israeli anakhala ku Kadesi.

18“Pambuyo pake, Aisraeli ananyamuka ulendo kudzera ku chipululu nazungulira dziko la Edomu ndi dziko la Mowabu, ndipo anafika ku mmawa kwa dziko la Mowabu ndi kumanga zinthando zawo ku mbali ina ya mtsinje wa Arinoni. Iwo sanalowe mʼdziko la Mowabu, chifukwa mtsinje wa Arinoni ndiwo unali malire a dziko la Mowabu.

19“Pambuyo pake Israeli anatumiza amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, amene amalamulira ku Hesiboni ndipo anati kwa iye, ‘Chonde tiloleni kuti tidutse mʼdziko lanu popita kwathu.’ 20Koma Sihoni sanalole Israeli kuti adzere mʼdziko mwake. Mʼmalo mwake Sihoni anasonkhanitsa ankhondo ake onse nakamanga msasa ku Yahazi ndipo anachita nkhondo ndi Israeli.

21“Koma Yehova Mulungu wa Israeli anamupereka Sihoni pamodzi ndi anthu ake onse mʼmanja mwa Israeli, ndipo anawagonjetsa. Choncho Aisraeli analanda dziko lonse la Aamori amene amakhala mʼdzikolo. 22Analanda dziko lonse kuchokera ku Arinoni mpaka ku Yaboki ndiponso kuchokera ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yorodani.

23“Ndiye kuti Yehova Mulungu wa Aisraeli ndiye analanda dziko la Aamori, kuwalandirira anthu ake. Kodi inu mukufuna kutilanda dzikolo? 24Bwanji inu osakhazikika mʼdziko limene Kemosi mulungu wanu anakupatsani, ifenso tikhazikike mʼdziko limene Yehova Mulungu wathu anatipatsa? 25Kodi ndinu abwino kuposa Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu? Kodi iye anakanganapo kapena kuchita nkhondo ndi Israeli? 26Pamene Aisraeli ankakhala mʼdziko la Hesiboni ndi mʼmidzi yake, mʼdziko la Aroeri ndi midzi yake, komanso mʼmizinda yonse imene ili mʼmbali mwa mtsinje wa Arinoni kwa zaka 300, nʼchifukwa chiyani inu simunalande malowo nthawi imeneyo? 27Choncho ine sindinakuchimwireni. Koma inu mukundilakwira pomenyana nane. Yehova woweruza, ndiye aweruze lero mlandu wa pakati pa Aisraeli ndi Aamoni.”

28Koma mfumu ya Aamori, sinasamale mawu amene Yefita anatumiza kwa iyo.

29Tsono Mzimu wa Yehova unatsikira pa Yefita. Ndipo iye ananyamuka nadzera ku Giliyadi ndi ku Manase. Anafika ku Mizipa mʼdziko la Giliyadi, ndipo kuchokera kumeneko anapita kukalimbana ndi Aamoni. 30Yefita analumbira kwa Yehova kuti, “Ngati mupereka Aamoni mʼmanja mwanga, 31aliyense amene atuluke pa khomo la nyumba yanga kudzandichingamira pobwerera nditagonjetsa Aamoni adzakhala wake wa Yehova, ndipo ndidzamupereka kuti akhale nsembe yopsereza.”

32Kenaka Yefita anawolokera kwa Aamoni kukamenya nawo nkhondo, ndipo Yehova anawaperekadi mʼmanja mwake. 33Iye anawononga mizinda makumi awiri kuchokera ku Ariori mpaka pafupi ndi mzinda wa Miniti. Anapitirira mpaka ku Abeli-Keranimu. Choncho Aisraeli anagonjetsa Aamoni.

34Pambuyo pake Yefita anabwerera ku nyumba yake. Tsono anangoona mwana wake wamkazi akutuluka kudzamuchingamira akuyimba ngʼoma ndi kuvina. Uyu anali mwana yekhayo wa Yefita. Analibenso mwana wina wamwamuna kapena wamkazi. 35Yefita ataona mwana wake uja, anangʼamba zovala zake ndi kulira, “Kalanga ine! Mwana wanga! Wandivulaza kwambiri ndipo iwe ndi gwero la mavuto anga. Ine ndinalumbira kwa Yehova ndi pakamwa pangapa ndipo sindingathe kubweza malumbiro angawo.”

36Mwanayo anayankha kuti, “Abambo, ngati munalonjeza kwa Yehova ndi pakamwa panu, chitani zimene munalonjezera pakuti Yehova wakuthandizani kulipsira adani anu Amowabu.” 37Anatinso kwa abambo ake, “Ndikupempheni chinthu ichi: Mundilole ndikayendeyende ku mapiri miyezi iwiri ndizikalira pamodzi ndi anzanga chifukwa ndikufa ndikanali namwali wosadziwa mwamuna.”

38Yefita anamuyankha kuti, “Pita.” Ndipo anamulola kuti apite miyezi iwiri. Tsono anapita kumapiri ndi atsikana anzake kukalira chifukwa cha unamwali wake. 39Miyezi iwiri itatha iye anabwerera kwa abambo ake, ndipo anachitadi zimene analonjeza.

Motero unakhala mwambo wa Aisraeli, 40kuti atsikana a Israeli ankapita chaka chilichonse kukalira maliro a mwana wa mkazi wa Yefita, Mgiliyadi uja masiku makumi anayi pa chaka.

Bibelen på hverdagsdansk

Dommerbogen 11:1-40

1Jefta var en modig kriger fra Gileads land. Han var søn af en mand ved navn Gilead, men hans mor var en prostitueret kvinde. 2Gileads kone fødte ham også en del sønner, og da de blev voksne, jog de deres halvbror Jefta bort. „Du er et uægte barn!” sagde de til ham. „Du skal ikke have del i arven efter vores far!”

3Så flygtede Jefta fra sit hjem og slog sig ned i landet Tob, hvor en flok omstrejfende banditter sluttede sig til ham. 4-5Det var omkring det tidspunkt, at ammonitterne gjorde sig klar til at angribe israelitterne. Da sendte lederne i Gilead bud efter Jefta i Tob. 6„Kom og vær vores anfører i krigen mod ammonitterne,” sagde de. 7Men Jefta svarede: „Var det ikke jer, som hadede mig og jog mig væk fra mit barndomshjem? Hvorfor kommer I så for at få hjælp fra mig nu, hvor I er i vanskeligheder?” 8„Fordi vi har brug for dig,” svarede de. „Hvis du vil være vores hærfører mod ammonitterne, vil vi bagefter gøre dig til overhoved for Gilead!” 9Jefta fortsatte: „Hvis jeg vender tilbage, og hvis Herren giver mig sejr i kampen mod ammonitterne, så vil jeg være jeres leder.” 10„Det sværger vi på for Herrens ansigt!” svarede de.

11Så tog Jefta imod tilbuddet og fulgte med dem. Han blev udnævnt til leder og hærfører for folket, og han blev officielt indsat som leder over dem i Herrens nærvær i Mitzpa. 12Derefter sendte Jefta bud til Ammons konge for at få at vide, hvorfor han angreb Israel. 13Kongen svarede: „Da israelitterne kom fra Egypten stjal de mit land, hele området mellem Arnonfloden, Jabbokfloden og Jordanfloden. Giv os nu frivilligt vores land tilbage.”

14-15Jefta sendte besked tilbage: „Israel har aldrig stjålet land fra ammonitterne eller moabitterne. 16Da Israels folk ankom til Kadesh, efter at de havde forladt Egypten og var gået igennem Det Røde Hav, 17sendte de bud til Edoms konge for at få tilladelse til at gå igennem hans land, men Edoms konge nægtede dem tilladelse. Det samme gjorde Moabs konge, da de henvendte sig til ham. Derfor blev israelitterne i Kadesh.

18Da israelitterne senere brød op, gik de gennem ørkenen i en bue uden om Edom og Moab langs den østlige grænse, indtil de havde passeret Moab, og nåede til Arnonfloden. Men de overskred aldrig grænsen til Moab. 19Derfra sendte de bud til amoritterkongen Sihon i Heshbon for at bede om tilladelse til at rejse gennem hans land og videre til deres bestemmelsessted.

20Men kong Sihon troede ikke på, at israelitterne ville rejse fredeligt igennem hans land. Derfor samlede han sin hær ved Jahatz og rykkede ud imod dem. 21-22Herren, vores Gud, gav imidlertid Israel sejr over kong Sihon og hans hær, så de overtog amoritternes område fra Arnonfloden i syd til Jabbokfloden i nord, og fra ørkenen mod øst til Jordanfloden i vest.

23Du ser altså, at det var Herren, Israels Gud, der tog landet fra amoritterne og gav det til Israels folk. Hvorfor skulle vi så give det tilbage til dig? 24Beholder du ikke, hvad din gud Kemosh har givet dig? Vi gør krav på ethvert område, som Herren, vores Gud, gav os held til at erobre! 25Er du bedre end kong Balak, Moabs konge, der aldrig gjorde krav på landet, efter at israelitterne havde taget det fra ham? 26Nu er der gået 300 år, og så kommer du og vil have området tilbage! I al den tid har det tilhørt israelitterne, der har slået sig ned langs Arnonfloden og i området fra Heshbon i nord til Aroer i syd. Hvorfor har I ikke for længst gjort noget for at få området tilbage? 27Nej, jeg er i min fulde ret til at beholde området, og det er dig, som gør mig uret ved at erklære mig krig. Lad nu Herren være vores dommer og afgøre hvem af os, der har ret, Israel eller Ammon.”

28Den besked gjorde imidlertid ikke indtryk på ammonitterkongen.

29Da kom Herrens Ånd over Jefta, og han drog gennem Gilead og Manasse og tilbage til Mitzpa i Gilead for at samle en hær, hvorefter han gjorde klar til at rykke ud mod ammonitterne. 30-31Jefta gav Herren det løfte, at hvis Herren ville hjælpe ham til at besejre ammonitterne og vende uskadt tilbage, ville han til gengæld bringe det første, han traf på, når han kom hjem, som et brændoffer til Herren.

32Jefta førte nu hæren til angreb på ammonitterne, som han ved Herrens hjælp besejrede. 33Han fældede ammonitterne i en frygtelig massakre lige fra Aroer til Minnit og løb 20 byer over ende, helt til Abel-Keramim. Ammonitterne led således et afgørende nederlag til israelitterne.

34Da Jefta vendte tilbage til sit hus i Mitzpa,11,34 Mitzpa betyder „vagttårn”, og flere byer er kendt under det samme navn. Det er uklart, om det drejer sig om byen Mitzpa syd for Betel eller en by i Gilead. kom hans datter—hans eneste barn—ham dansende i møde, mens hun spillede på tamburin. 35Da han fik øje på hende, flængede han sit tøj i dyb fortvivlelse.

„Åh, min datter!” udbrød han. „Du har knust mit hjerte, for jeg har givet Herren et løfte, som jeg umuligt kan trække tilbage.” 36Da hun fik at vide, hvad det var, svarede hun: „Far, du må holde dit løfte til Herren, for han har givet dig sejr over dine fjender. 37Men giv mig først lov til at gå op i bjergene i to måneder, så jeg sammen med mine veninder kan sørge over, at jeg skal dø så ung og som ugift.”

38Det gav han hende lov til, og hun gik op i bjergene for sammen med sine veninder at sørge over sin skæbne. 39Derefter vendte hun tilbage til sin far, der indfriede sit løfte, og derfor nåede hun ikke at blive gift. Efter den tid blev det skik i Israel, 40at unge piger hvert år tager væk i fire dage for at begræde den skæbne, der ramte Jeftas datter.