Miyambo 20 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 20:1-30

1Vinyo amachititsa munthu kukhala wonyoza ndipo chakumwa choledzeretsa chimachititsa munthu kukhala wolongolola;

aliyense wosochera nazo zimenezi alibe nzeru.

2Ukali wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango;

amene amawuputa mkwiyowo amataya moyo wake.

3Nʼchaulemu kwa munthu kupewa mikangano,

koma chitsiru chilichonse chimafulumira kulongolola.

4Munthu waulesi satipula mʼmunda pa nthawi yoyenera;

kotero pa nthawi yokolola adzafunafuna zinthu koma sadzapeza kanthu kalikonse.

5Zolinga za mtima wa munthu zili ngati madzi akuya,

munthu womvetsa zinthu ndiye yekha angawatunge.

6Anthu ambiri amayankhula za kukhulupirika kwawo,

koma munthu wokhulupirika angamupeze ndani?

7Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino;

odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake.

8Mfumu ikhala pa mpando wake wa chiweruzo,

imapeta ndi maso ake anthu onse oyipa.

9Ndani amene anganene kuti, “Ndawuyeretsa mtima wanga;

ndilibe tchimo lililonse?”

10Masikelo ndi miyeso ya zinthu imene ili yachinyengo

zonsezi Yehova zimamunyansa.

11Ngakhale mwana amadziwika ndi zochita zake,

ngati zochita zake zili zoyera ndi zoyenera.

12Makutu amene amamva ndi maso amene amaona,

zonsezi anazilenga ndi Yehova.

13Usakonde tulo ungasauke;

khala maso ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.

14Munthu wogula chinthu amati, “Sichabwino, sichabwino.”

Koma akagula nʼkuchokapo amayamba kudzitama.

15Pali golide ndi miyala yamtengowapatali,

koma milomo yoyankhula zanzeru ndi yamtengowapatali koposa zonsezi.

16Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole;

kuti chikhale chikole chako chifukwa waperekera chikole munthu wachilendo.

17Chakudya chochipeza mwachinyengo chimukomera munthu,

koma pa mapeto pake chimasanduka ngati mchenga mʼkamwa mwake.

18Zokonzekera zimapindula utafunsira uphungu;

ndipo usanamenye nkhondo yamba wapempha malangizo oyenera.

19Amene amanka nanena miseche amawulula zachinsinsi.

Choncho usamagwirizane naye munthu woyankhula zopusayo.

20Ngati munthu atemberera abambo ake kapena amayi ake,

moyo wake udzazimitsidwa ngati nyale mu mdima wandiweyani.

21Cholowa chochipeza mofulumira poyamba,

sichidzakhala dalitso pa mapeto pake.

22Usanene kuti, “Ine ndidzabwezera choyipa chimenechi!”

Dikira Yehova, ndipo Iye adzakupulumutsa.

23Miyeso yosintha imamunyansa Yehova;

ndipo masikelo onyenga si abwino.

24Mayendedwe a munthu amawalamulira ndi Yehova,

tsono munthu angadziwe bwanji njira yake?

25Ndi msampha kwa munthu kuyankhula mofulumira kuti “Chinthu ichi nʼchopatulika kwa Yehova,”

popeza mwina atha kusintha maganizo utalumbira kale.

26Mfumu ya nzeru imapeta kwathunthu

anthu oyipa.

27Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Yehova;

imafufuza ziwalo zake zonse zamʼkati.

28Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu;

chilungamo chimalimbikitsa mpando wake waufumu.

29Ulemerero wa achinyamata uli mu mphamvu zawo,

imvi ndi ulemerero wa anthu okalamba.

30Mikwingwirima yopweteka ndiyo imachotsa zoyipa,

ndipo mikwapulo ndiyo imachotsa zamʼkatikati mwa munthu.

New Russian Translation

Притчи 20:1-30

1Вино глумливо, хмельное питье неистово;

кто дает им себя обмануть, не мудр.

2Ярость царя подобна львиному реву;

досадивший ему поплатится жизнью.

3Честь для человека – удерживаться от раздоров,

а всякий глупец скор на ссору.

4Ленивый не пашет вовремя;

возьмется искать в пору жатвы – и нет ничего.

5Замыслы в человеческом сердце – глубокие воды,

но разумный сможет их вычерпать.

6Многие зовут себя преданными,

но где найти человека, кому бы довериться?

7Праведник живет беспорочной жизнью,

блаженны после него его дети.

8Когда царь садится на судейский престол,

он глазами способен все зло развеять.

9Кто может сказать: «Я очистил сердце,

я чист и безгрешен»?

10Неверные весы и неверные гири –

и то и другое мерзко для Господа.

11Даже ребенка узнают по его делам,

по тому, чисты ли поступки его, правильны ли.

12Уши, которые слышат, и глаза, которые видят, –

и то и другое создал Господь.

13Не люби спать, не то обнищаешь;

бодрствуй, и будешь досыта есть.

14«Плохо, плохо», – говорит покупатель,

а когда отойдет, то покупкой хвастает.

15Есть золото и много драгоценных камней,

но уста ученые – редкая драгоценность.

16Забери одежду20:16 Верхнюю одежду брали в залог у бедняков (см. Исх. 22:26-27; Втор. 24:10-13). у поручившегося за незнакомца,

удержи залог у ручавшегося за чужую жену.

17Сладка человеку пища, добытая обманом,

но после нее рот будет полон песка.

18Строй замыслы, обсуждая их с другими;

если ведешь войну, ищи мудрого совета.

19Сплетня доверие предает,

так что избегай человека, который болтлив.

20У проклинающего отца или мать

светильник погаснет во тьме кромешной.

21Наследство, поспешно захваченное вначале,

в конце не принесет благословения.

22Не говори: «Я отплачу за обиду!»

Положись на Господа – Он спасет тебя.

23Мерзость для Господа гири неправильные,

и весы нечестные Ему неугодны.

24Шаги человека направляет Господь.

Как же может человек путь свой постичь?

25Ловушка для человека – поспешно посвящать что-либо Богу

и только после обдумывать свой обет.

26Мудрый царь провеивает нечестивых;

он гонит по ним молотильное колесо.

27Дух человека – светильник Господень,

исследующий все глубины его существа.

28Любовь20:28 Или: «милость». и истина20:28 Или: «верность». хранят царя;

милостью он утверждает престол свой.

29Слава юношей в силе их,

седина – украшение старости.

30Удары, что ранят, очищают от зла,

и битье очищает глубины сердца.