Masalimo 86 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 86:1-17

Salimo 86

Pemphero la Davide.

1Ndimvereni Yehova ndipo mundiyankhe,

pakuti ndine wosauka ndi wosowa.

2Yangʼanirani moyo wanga, pakuti ndine wodzipereka kwa Inu.

Inu ndinu Mulungu wanga;

pulumutsani mtumiki wanu amene amadalira Inu.

Inu ndinu Mulungu wanga.

3Mundichitire chifundo, Inu Ambuye,

pakuti ndikuyitana Inu tsiku lonse.

4Bweretsani chimwemwe kwa mtumiki wanu, Ambuye,

pakuti ndimadalira Inu.

5Inu Ambuye, ndinu wokhululuka ndi wabwino,

wodzaza ndi chikondi kwa onse amene amayitana Inu.

6Yehova imvani pemphero langa;

mvetserani kulira kwanga kofuna chifundo.

7Pa tsiku la mavuto anga ndidzayitana Inu,

pakuti Inu mudzandiyankha.

8Pakati pa milungu palibe wina wofanana nanu Ambuye;

palibe ntchito zolingana ndi ntchito zanu.

9Mitundu yonse ya anthu imene munayipanga

idzabwera ndi kudzalambira pamaso panu Ambuye;

iwo adzabweretsa ulemerero pa dzina lanu.

10Pakuti ndinu wamkulu ndipo mumachita zodabwitsa;

Inu nokha ndiye Mulungu.

11Ndiphunzitseni njira yanu Yehova,

ndipo ndidzayenda mʼchoonadi chanu;

patseni mtima wosagawikana

kuti ndilemekeze dzina lanu.

12Ndidzakutamandani Ambuye Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse;

ndidzalemekeza dzina lanu kwamuyaya.

13Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu kwa ine;

mwandipulumutsa ku malo ozama a manda.

14Inu Mulungu wanga, anthu odzikuza akundithira nkhondo;

anthu ankhanza akufuna kundipha,

amene salabadira za Inu.

15Koma Ambuye ndinu Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima,

wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi ndi wokhulupirika.

16Tembenukirani kwa ine ndipo ndichitireni chifundo;

perekani mphamvu zanu kwa mtumiki wanu

ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.

17Mundionetse chizindikiro cha ubwino wanu

kuti adani achione ndi kuchititsidwa manyazi,

pakuti Yehova mwandithandiza ndi kunditonthoza.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

詩篇 86:1-17

第 86 篇

祈求上帝施恩

大衛的祈禱。

1耶和華啊,我窮苦無助,

求你垂聽我的禱告,應允我。

2求你保護我的性命,

因為我忠於你。

你是我的上帝,我信靠你,

求你拯救僕人。

3主啊,我終日向你呼求,

求你憐憫我。

4主啊,我的心仰望你,

求你賜我歡樂。

5主啊,你良善仁慈,樂意赦免,

以無限的慈愛待一切求告你的人。

6耶和華啊,求你聽我的禱告,

垂聽我的懇求。

7患難之時,我要向你呼求,

因為你必應允我。

8主啊,

眾神明中沒有一位能與你相比,

你的作為無與倫比。

9主啊,

你創造的萬國都要來敬拜你,

將榮耀歸給你的名。

10因為你偉大無比,行事奇妙,

唯有你是上帝。

11耶和華啊,求你教我行你的道,

我要行在你的真理中,

求你使我一心敬畏你。

12主——我的上帝啊,

我要全心全意地讚美你,

我要永遠將榮耀歸給你的名。

13因為你深愛我,

從陰間的深處拯救了我。

14上帝啊,狂傲的人攻擊我,

一群兇殘之徒要殺害我,

他們藐視你。

15但主啊,

你是有憐憫和恩典的上帝,

不輕易發怒,充滿慈愛,

無比信實。

16求你垂顧我,憐憫我,

賜力量給你的僕人,

拯救你婢女的兒子。

17求你賜下恩待我的憑據,

使那些恨我的人見狀就抱愧蒙羞,

因為你耶和華幫助我、安慰我。