Masalimo 119 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 119:1-176

Salimo 119

Alefu

1Odala ndi amene moyo wawo ulibe cholakwa,

amene amayenda monga mwa malamulo a Yehova.

2Odala ndi amene amasunga malamulo ake,

amene amafunafuna Iyeyo ndi mtima wawo wonse.

3Sachita cholakwa chilichonse;

amayenda mʼnjira zake.

4Inu mwapereka malangizo

ndipo ayenera kutsatidwa kwathunthu.

5Aa! Ndikanakonda njira zanga zikanakhala zokhazikika

pa kumvera zophunzitsa zanu!

6Pamenepo ine sindikanachititsidwa manyazi,

poganizira malamulo anu onse.

7Ndidzakutamandani ndi mtima wolungama,

pamene ndikuphunzira malamulo anu olungama.

8Ndidzamvera zophunzitsa zanu;

musanditaye kwathunthu.

Beti

9Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake?

Akawasamala potsata mawu anu.

10Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse;

musalole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu.

11Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga

kuti ndisakuchimwireni.

12Mutamandike Inu Yehova;

phunzitseni malamulo anu.

13Ndi milomo yanga ndimafotokoza malamulo anu onse

amene amachokera pakamwa panu.

14Ndimakondwera potsatira malamulo anu

monga momwe munthu amakondwera akakhala ndi chuma chambiri.

15Ndimalingalira malangizo anu

ndipo ndimaganizira njira zanu.

16Ndimakondwera ndi malamulo anu;

sindidzayiwala konse mawu anu.

Gimeli

17Chitirani zokoma mtumiki wanu, ndipo ndidzakhala ndi moyo;

kuti tsono ndisunge mawu anu.

18Tsekulani maso anga kuti ndithe kuona

zinthu zodabwitsa mʼmalamulo anu.

19Ine ndine mlendo pa dziko lapansi;

musandibisire malamulo anu.

20Moyo wanga wafowoka polakalaka

malamulo anu nthawi zonse.

21Inu mumadzudzula onyada, otembereredwa,

amene achoka pa malamulo anu.

22Mundichotsere chitonzo ndi mnyozo

pakuti ndimasunga malamulo anu.

23Ngakhale mafumu akhale pamodzi kundinyoza,

mtumiki wanu adzalingalirabe zophunzitsa zanu.

24Malamulo anu amandikondweretsa;

ndiwo amene amandilangiza.

Daleti

25Moyo wanga wakangamira fumbi;

tsitsimutseni molingana ndi mawu anu.

26Ndinafotokoza njira zanga ndipo Inu munandiyankha;

phunzitseni malamulo anu.

27Mundidziwitse chiphunzitso cha malangizo anu;

pamenepo ndidzalingalira zodabwitsa zanu.

28Moyo wanga wafowoka ndi chisoni;

limbikitseni monga mwa mawu anu.

29Mundichotse mʼnjira zachinyengo;

mundikomere mtima pondiphunzitsa malamulo anu.

30Ndasankha njira ya choonadi;

ndayika malamulo anu pa mtima panga.

31Ndagwiritsitsa umboni wanu, Inu Yehova;

musalole kuti ndichititsidwe manyazi.

32Ndimathamanga mʼnjira ya malamulo anu,

pakuti Inu mwamasula mtima wanga.

He

33Yehova, phunzitseni kutsatira zophunzitsa zanu;

ndipo ndidzazisunga mpaka kumapeto.

34Mundipatse mtima womvetsa zinthu ndipo ndidzasunga malamulo anu

ndi kuwamvera ndi mtima wanga wonse.

35Munditsogolere mʼnjira ya malamulo anu,

pakuti mʼmenemo ndimapezamo chikondwerero changa.

36Tembenuzani mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu,

osati chuma.

37Tembenuzani maso anga kuchoka ku zinthu zachabechabe;

sungani moyo wanga monga mwa mawu anu.

38Kwaniritsani lonjezo lanu kwa mtumiki wanu,

kuti Inu muopedwe.

39Mundichotsere chipongwe chimene ndikuchiopa,

pakuti malamulo anu ndi abwino.

40Taonani, ndimalakalakatu malangizo anu!

Sungani moyo wanga mʼchilungamo chanu.

Wawi

41Chikondi chanu chosasinthika chibwere kwa ine, Inu Yehova,

chipulumutso chanu monga mwa lonjezo lanu;

42ndipo ndidzayankha amene amandinyoza,

popeza ndimadalira mawu anu.

43Musakwatule mawu a choonadi mʼkamwa mwanga,

pakuti ndakhazikitsa chiyembekezo changa mʼmalamulo anu.

44Ndidzasunga malamulo anu nthawi zonse,

ku nthawi za nthawi.

45Ndidzayendayenda mwaufulu,

chifukwa ndinafunafuna malangizo anu.

46Ndidzayankhula za umboni wanu pamaso pa mfumu

ndipo sindidzachititsidwa manyazi,

47popeza ndimakondwera ndi malamulo anu

chifukwa ndimawakonda.

48Ndikweza manja anga ku malamulo anu, ku malamulo amene ndimawakonda,

ndipo ndimalingalira malangizo anu.

Zayini

49Kumbukirani mawu anu kwa mtumiki wanu,

popeza mwandipatsa chiyembekezo.

50Chitonthozo changa pa masautso anga ndi ichi:

lonjezo lanu limasunga moyo wanga.

51Odzikuza amandinyoza popanda chowaletsa,

koma sindichoka pa malamulo anu.

52Ndimakumbukira malamulo anu Yehova akalekale,

ndipo mwa iwo ndimapeza chitonthozo.

53Ndayipidwa kwambiri chifukwa cha oyipa

amene ataya malamulo anu.

54Zophunzitsa zanu ndi mitu ya nyimbo yanga

kulikonse kumene ndigonako.

55Usiku ndimakumbukira dzina lanu Yehova,

ndipo ndidzasunga malamulo anu.

56Ichi ndicho ndakhala ndikuchita:

ndimasunga malangizo anu.

Heti

57Yehova, Inu ndiye gawo langa;

ndalonjeza kumvera mawu anu.

58Ndimafunafuna nkhope yanu ndi mtima wanga wonse;

mundikomere mtima monga mwa lonjezo lanu.

59Ndinalingalira za njira zanga

ndipo ndatembenuza mayendedwe anga kutsatira umboni wanu.

60Ndidzafulumira ndipo sindidzazengereza

kumvera malamulo anu.

61Ngakhale oyipa andimange ndi zingwe,

sindidzayiwala lamulo lanu.

62Ndimadzuka pakati pa usiku kuyamika Inu

chifukwa cha malamulo anu olungama.

63Ine ndine bwenzi la onse amene amakukondani,

kwa onse amene amatsatira malangizo anu.

64Dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chanu chosasinthika,

phunzitseni malamulo anu.

Teti

65Inu Yehova, chitirani chabwino mtumiki wanu

molingana ndi mawu anu.

66Phunzitseni nzeru ndi chiweruzo chabwino,

pakuti ndimakhulupirira malamulo anu.

67Ndisanayambe kuzunzika ndinasochera,

koma tsopano ndimamvera mawu anu.

68Inu ndinu abwino ndipo zimene mumachita ndi zabwino;

phunzitseni malamulo anu.

69Ngakhale odzikuza andipaka mabodza,

ine ndimasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.

70Mitima yawo ndi yowuma ndi yosakhudzidwa,

koma ine ndimakondwera ndi malamulo anu.

71Ndi bwino kuti ndinasautsidwa

kuti ndithe kuphunzira malamulo anu.

72Lamulo lochokera mʼkamwa mwanu limandikomera kwambiri

kuposa ndalama zambirimbiri za siliva ndi golide.

Yodi

73Manja anu anandilenga ndi kundiwumba;

patseni nzeru zomvetsa zinthu kuti ndiphunzire malamulo anu.

74Iwo amene amakuopani akondwere akandiona,

chifukwa chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.

75Ine ndikudziwa, Inu Yehova, kuti malamulo anu ndi olungama

ndipo mwandizunza chifukwa cha kukhulupirika kwanu.

76Chikondi chanu chosasinthika chikhale chitonthozo changa,

molingana ndi lonjezo lanu kwa mtumiki wanu.

77Chifundo chanu chindifikire kuti ndikhale ndi moyo,

popeza malamulo anu ndiye chikondwerero changa.

78Odzikuza achititsidwe manyazi chifukwa cha kundilakwira popanda chifukwa;

koma ine ndidzalingalira malangizo anu.

79Iwo amene amakuopani atembenukire kwa ine,

iwo amene amamvetsetsa umboni wanu.

80Mtima wanga ukhale wopanda cholakwa pa chiphunzitso chanu

kuti ndisachititsidwe manyazi.

Kafu

81Moyo wanga wafowoka ndi kufunafuna chipulumutso chanu,

koma chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.

82Maso anga alefuka pofunafuna lonjezo lanu;

Ine ndikuti, “Kodi mudzanditonthoza liti?”

83Ngakhale ndili ngati thumba lachikopa la vinyo pa utsi

sindiyiwala zophunzitsa zanu.

84Kodi mtumiki wanu ayenera kudikira mpaka liti?

Kodi mudzawalanga liti amene amandizunza?

85Anthu osalabadira za Mulungu,

odzikuza amandikumbira dzenje motsutsana ndi malamulo anu.

86Malamulo anu onse ndi odalirika;

thandizeni, pakuti anthu akundizunza popanda chifukwa.

87Iwo anatsala pangʼono kundichotsa pa dziko lapansi

koma sindinataye malangizo anu.

88Sungani moyo wanga molingana ndi chikondi chanu chosasinthika,

ndipo ndidzamvera umboni wa pakamwa panu.

Lamedi

89Mawu anu Yehova ndi amuyaya;

akhazikika kumwambako.

90Kukhulupirika kwanu kumakhala mpaka ku mibado yonse;

Inu munakhazikitsa dziko lapansi ndipo lilipobe.

91Malamulo anu alipobe mpaka lero lino,

pakuti zinthu zonse zimatumikira Inu.

92Malamulo anu akanapanda kukhala chikondwerero changa,

ndikanawonongeka mʼmasautso anga.

93Ine sindidzayiwala konse malangizo anu,

pakuti ndi malangizo anuwo munasunga moyo wanga.

94Ndine wanu, ndipulumutseni;

pakuti ndasamala malangizo anu.

95Anthu oyipa akudikira kuti andiwononge,

koma ndidzalingalira umboni wanu.

96Ndadziwa kuti zinthu zonse zili ndi malire,

koma malamulo anu alibe malire konse.

Memu

97Ndithu, ine ndimakonda malamulo anu!

Ndimalingaliramo tsiku lonse.

98Malamulo anu amachititsa kuti ndikhale wanzeru kuposa adani anga,

popeza malamulowo ali ndi ine nthawi zonse.

99Ndimamvetsa zinthu kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse

popeza ndimalingalira umboni wanu.

100Ndili ndi nzeru zochuluka zomvetsera zinthu kuposa anthu okalamba,

popeza ndimamvera malangizo anu.

101Ndimaletsa miyendo yanga kuyenda mʼnjira iliyonse yoyipa

kuti ndithe kumvera mawu anu.

102Sindinapatuke kuchoka pa malamulo anu,

pakuti Inu mwini munandiphunzitsa.

103Mawu anu ndi otsekemera ndikawalawa,

otsekemera kuposa uchi mʼkamwa mwanga!

104Ndimapeza nzeru zodziwira zinthu kuchokera mʼmalangizo anu;

kotero ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.

Nuni

105Mawu anu ndi nyale ya kumapazi kwanga

ndi kuwunika kwa pa njira yanga.

106Ndalumbira ndipo ndatsimikiza,

kuti ndidzatsatira malamulo anu olungama.

107Ndazunzika kwambiri;

Inu Yehova, sungani moyo wanga molingana ndi mawu anu.

108Inu Yehova, landirani matamando aufulu ochokera pakamwa panga,

ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.

109Ngakhale moyo wanga umakhala mʼzoopsa nthawi ndi nthawi,

sindidzayiwala malamulo anu.

110Anthu oyipa anditchera msampha,

koma sindinasochere kuchoka pa malangizo anu.

111Umboni wanu ndiye cholowa changa kwamuyaya;

Iwo ndiye chimwemwe cha mtima wanga.

112Mtima wanga wakhazikika pa kusunga zophunzitsa zanu

mpaka kumapeto kwenikweni.

Samekhi

113Ndimadana ndi anthu apawiripawiri,

koma ndimakonda malamulo anu.

114Inu ndinu pothawirapo panga ndi chishango changa;

chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.

115Chokani kwa ine, inu anthu ochita zoyipa,

kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga!

116Mundichirikize molingana ndi lonjezo lanu, ndipo ndidzakhala ndi moyo;

musalole kuti chiyembekezo changa chipite pachabe.

117Gwirizizeni, ndipo ndidzapulumutsidwa;

nthawi zonse ndidzasamalira zophunzitsa zanu.

118Inu mumakana onse amene amasochera kuchoka pa zophunzitsa zanu,

pakuti chinyengo chawo ndi chopanda phindu.

119Anthu onse oyipa a pa dziko lapansi mumawayesa ngati zinthu zakudzala;

nʼchifukwa chake ndimakonda umboni wanu.

120Thupi langa limanjenjemera chifukwa cha kuopa Inu;

ndimachita mantha ndi malamulo anu.

Ayini

121Ndachita zolungama ndi zabwino;

musandisiye mʼmanja mwa ondizunza.

122Onetsetsani kuti mtumiki wanu akukhala bwino,

musalole kuti anthu odzikuza andipondereze.

123Maso anga alefuka, kufunafuna chipulumutso chanu,

kufunafuna lonjezo lanu lolungama.

124Muchite naye mtumiki wanu molingana ndi chikondi chanu chosasinthika,

ndipo mundiphunzitse malamulo anu.

125Ine ndine mtumiki wanu; patseni mzimu wondizindikiritsa,

kuti ndimvetsetse umboni wanu.

126Yehova, ndi nthawi yoti muchitepo kanthu;

malamulo anu akuswedwa.

127Chifukwa choti ndimakonda malamulo anu

kuposa golide, kuposa golide woyengeka bwino,

128ndiponso chifukwa choti ndimaona kuti malangizo anu onse ndi wowongoka,

ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.

Pe

129Maumboni anu ndi odabwitsa

nʼchifukwa chake ndimawamvera.

130Mawu anu akamaphunzitsidwa amapereka kuwunika;

ngakhale anthu wamba amamvetsetsa.

131Ndimatsekula pakamwa panga ndi kupuma wefuwefu,

kufunafuna malamulo anu.

132Tembenukirani kwa ine ndipo mundichitire chifundo,

monga mumachitira nthawi zonse kwa iwo amene amakonda dzina lanu.

133Tsogolerani mayendedwe anga molingana ndi mawu anu;

musalole kuti tchimo lizindilamulira.

134Ndiwomboleni mʼdzanja la anthu ondizunza,

kuti ndithe kumvera malangizo anu.

135Nkhope yanu iwalire mtumiki wanu

ndipo mundiphunzitse malamulo anu.

136Mitsinje ya misozi ikuyenda kuchoka mʼmaso mwanga,

chifukwa anthu sakumvera malamulo anu.

Tsade

137Yehova ndinu wolungama,

ndipo malamulo anu ndi abwino.

138Maumboni amene munatipatsa ndi olungama;

ndi odalirika ndithu.

139Ndikusautsidwa kwambiri mʼkati mwanga

chifukwa adani anu amanyalanyaza mawu anu.

140Mawu anu ndi woyera kwambiri

nʼchifukwa chake mtumiki wanune ndimawakonda.

141Ngakhale ndili wamngʼono ndi wonyozeka,

sindiyiwala malangizo anu.

142Chilungamo chanu nʼchamuyaya,

ndipo malamulo anu nʼchoona.

143Mavuto ndi masautso zandigwera,

koma ndimakondwera ndi malamulo anu.

144Umboni wanu ndi wabwino nthawi zonse;

patseni nzeru zomvetsa zinthu kuti ine ndikhale ndi moyo.

Kofu

145Ndimayitana ndi mtima wanga wonse; ndiyankheni Inu Yehova,

ndipo ndidzamvera zophunzitsa zanu.

146Ndikuyitana kwa Inu; pulumutseni

ndipo ndidzasunga umboni wanu.

147Ndimadzuka tambala asanalire kuti ndipemphe thandizo;

chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.

148Maso anga amakhala chipenyere nthawi yonse ya usiku,

kuti ndithe kulingalira malonjezo anu.

149Imvani mawu anga molingana ndi chikondi chanu chosasinthika;

Yehova sungani moyo wanga, molingana ndi malamulo anu.

150Iwo amene amakonza njira zoyipa andiyandikira,

koma ali kutali ndi malamulo anu.

151Koma Inu Yehova muli pafupi,

malamulo anu onse ndi woona.

152Ndinaphunzira kalekale kuchokera mʼmaumboni anu

kuti maumboni amene munakhazikitsawo ndi amuyaya.

Reshi

153Yangʼanani masautso anga ndipo mundipulumutse,

pakuti sindinayiwale malamulo anu.

154Mundiyimirire pa mlandu wanga ndi kundiwombola;

sungani moyo wanga molingana ndi lonjezo lanu.

155Chipulumutso chili kutali ndi anthu oyipa,

pakuti iwowo safunafuna zophunzitsa zanu.

156Chifundo chanu Yehova nʼchachikulu;

sungani moyo wanga molingana ndi malamulo anu.

157Adani amene akundizunza ndi ambiri,

koma ine sindinatembenuke kuchoka pa umboni wanu.

158Ndimawayangʼana monyansidwa anthu opanda chikhulupiriro,

popeza samvera mawu anu.

159Onani momwe ndimakondera malangizo anu;

sungani moyo wanga, Inu Yehova, molingana ndi chikondi chanu chosanthika.

160Mawu anu onse ndi owona;

malamulo anu onse olungama ndi amuyaya.

Sini ndi Shini

161Olamulira amandizunza popanda chifukwa,

koma mtima wanga umanjenjemera ndi mawu anu.

162Ine ndimakondwa ndi lonjezo lanu,

ngati munthu amene wapeza chuma chambiri.

163Ndimadana ndi chinyengo, kwambiri ndimanyansidwa nacho,

koma ndimakonda malamulo anu.

164Ndimakutamandani kasanu ndi kawiri pa tsiku

pakuti malamulo anu ndi olungama.

165Amene amakonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu,

ndipo palibe chimene chingawapunthwitse

166Ndikudikira chipulumutso chanu, Inu Yehova,

ndipo ndimatsatira malamulo anu.

167Ndimamvera umboni wanu

pakuti ndimawukonda kwambiri.

168Ndimamvera malangizo anu ndi umboni wanu,

pakuti njira zanga zonse ndi zodziwika pamaso panu.

Tawu

169Kulira kwanga kufike pamaso panu Yehova;

patseni nzeru zomvetsa zinthu molingana ndi mawu anu.

170Kupempha kwanga kufike pamaso panu;

pulumutseni molingana ndi lonjezo lanu.

171Matamando asefukire pa milomo yanga,

pakuti Inu mumandiphunzitsa malamulo anu.

172Lilime langa liyimbe mawu anu,

popeza malamulo anu onse ndi olungama.

173Dzanja lanu likhale lokonzeka kundithandiza

pakuti ndasankha malangizo anu.

174Ndikufunitsitsa chipulumutso chanu Yehova,

ndipo ndimakondwera ndi malamulo anu.

175Loleni kuti ndikhale ndi moyo kuti ndikutamandeni,

ndipo malamulo anu andichirikize.

176Ndasochera ngati nkhosa yotayika,

funafunani mtumiki wanu,

pakuti sindinayiwale malamulo anu.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

诗篇 119:1-176

第 119 篇

上帝的律法

1行为正直、遵行耶和华律法的人有福了!

2遵守祂的法度、全心寻求祂的人有福了!

3他们不做不义的事,

只照祂的旨意而行。

4耶和华啊,你已经赐下法则,

叫我们竭力遵行。

5我渴望坚定地遵从你的律例。

6我重视你的一切命令,

便不致羞愧。

7我学习你公义的法令时,

要存着正直的心来称谢你。

8我要遵守你的律例,

求你不要弃绝我。

9青年如何保持纯洁呢?

就是要遵守你的话。

10我全心全意地寻求你,

求你不要让我偏离你的命令。

11我把你的话珍藏在心中,

免得我得罪你。

12耶和华啊,你当受称颂!

求你将你的律例教导我。

13我宣扬你口中所出的一切法令。

14我喜爱你的法度如同人们喜爱财富。

15我要默想你的法则,

思想你的旨意。

16我以遵行你的律例为乐,

我不忘记你的话语。

17求你以厚恩待我,

使我能活着,并遵守你的话语。

18求你开我的眼睛,

使我能明白你律法中的奥妙。

19我在世上是过客,

求你不要向我隐藏你的命令。

20我的心时刻切慕你的法令。

21你斥责受咒诅、不听从你命令的狂傲人。

22求你除去我所受的羞辱和藐视,

因为我遵从你的法度。

23虽然权贵们坐着毁谤我,

仆人仍要默想你的律例。

24你的法度是我的喜乐,

是我的谋士。

25我几乎性命不保,

求你照你的应许救我的性命。

26我陈明自己的行为,

你就回应了我;

求你将你的律例教导我。

27求你使我明白你的法则,

我要思想你的奇妙作为。

28我伤心欲绝,

求你照你的应许使我坚强起来。

29求你使我远离恶道,

开恩将你的律法教导我。

30我已经选择了真理之路,

决心遵行你的法令。

31我持守你的法度,耶和华啊,

求你不要使我蒙羞。

32我竭力遵守你的命令,

因为你使我更有悟性。

33耶和华啊,

求你将你的律例教导我,

我必遵守到底。

34求你叫我明白你的律法,

使我可以全心遵守。

35求你引导我遵行你的命令,

因为这是我喜爱的。

36求你使我的心爱慕你的法度而非不义之财。

37求你使我的眼目远离虚空之事,

按你的旨意更新我的生命。

38求你实现你给仆人的应许,

就是你给敬畏你之人的应许。

39求你除去我所害怕的羞辱,

因为你的法令是美善的。

40我渴望遵行你的法则,

求你按你的公义更新我的生命。

41耶和华啊!

愿你的慈爱临到我,

愿你的拯救临到我,

正如你的应许,

42好叫我能面对嘲笑我的人,

因为我信靠你的话。

43求你使真理不离我的口,

因为你的法令是我的盼望。

44我要持守你的律法,

直到永永远远。

45我要自由地生活,

因为我寻求你的法则。

46我要在君王面前讲论你的法度,

我不以此为耻。

47我以遵行你的命令为乐,

我喜爱你的命令。

48我尊崇你的命令,

我喜爱你的命令,

我要默想你的律例。

49求你顾念你对仆人的应许,

你的话带给我盼望。

50你的应许是我生命的支柱,

是我患难中的安慰。

51狂傲人肆意嘲讽我,

但我仍然没有偏离你的律法。

52耶和华啊,

我牢记你古时赐下的法令,

你的法令是我的安慰。

53我见恶人丢弃你的律法,

就怒火中烧。

54我在世寄居的日子,

你的律例就是我的诗歌。

55耶和华啊,我在夜间思想你,

我要遵守你的律法。

56我向来乐于遵行你的法则。

57耶和华啊,你是我的福分!

我决心遵行你的话语。

58我一心求你施恩,

求你照着你的应许恩待我。

59我思想自己走过的路,

就决定归向你的法度。

60我毫不迟疑地遵守你的命令。

61虽然恶人用绳索捆绑我,

我仍不忘记你的律法。

62我半夜起来称谢你公义的法令。

63我与所有敬畏你、遵守你法则的人为友。

64耶和华啊,

你的慈爱遍及天下,

求你将你的律例教导我。

65耶和华啊,

你信守诺言,善待了仆人。

66求你赐我知识,教我判别是非,

因为我信靠你的命令。

67从前我没有受苦的时候走迷了路,

现在我要遵行你的话。

68你是美善的,

你所行的都是美善的,

求你将你的律例教导我。

69傲慢人毁谤我,

但我一心遵守你的法则。

70他们执迷不悟,

但我喜爱你的律法。

71我受苦对我有益,

使我可以学习你的律例。

72你赐的律法对我而言比千万金银更宝贵。

73你亲手造我、塑我,

求你赐我悟性好明白你的命令。

74敬畏你的人见我就欢喜,

因为我信靠你的话。

75耶和华啊,

我知道你的法令公义,

你是凭信实管教我。

76求你照着你给仆人的应许,

用慈爱来安慰我。

77求你怜悯我,使我可以存活,

因为你的律法是我的喜乐。

78愿狂傲人受辱,

因他们诋毁我;

但我要思想你的法则。

79愿敬畏你的人到我这里来,

好明白你的法度。

80愿我能全心遵守你的律例,

使我不致羞愧。

81我的心迫切渴慕你的拯救,

你的话语是我的盼望。

82我期盼你的应许实现,

望眼欲穿。

我说:“你何时才安慰我?”

83我形容枯槁,好像烟熏的皮袋,

但我仍然没有忘记你的律例。

84你仆人还要等多久呢?

你何时才会惩罚那些迫害我的人呢?

85违背你律法的狂傲人挖陷阱害我。

86你的一切命令都可靠,

他们无故地迫害我,

求你帮助我。

87他们几乎置我于死地,

但我仍然没有背弃你的法则。

88求你施慈爱保护我的性命,

我好遵守你赐下的法度。

89耶和华啊,

你的话与天同存,亘古不变。

90你的信实万代长存;

你创造了大地,使它恒久不变。

91天地照你的法令一直存到今日,

因为万物都是你的仆役。

92如果没有你的律法给我带来喜乐,

我早已死在苦难中了。

93我永不忘记你的法则,

因你借着法则救了我的生命。

94我属于你,求你拯救我,

因为我努力遵守你的法则。

95恶人伺机害我,

但我仍然思想你的法度。

96我看到万事都有尽头,

唯有你的命令无边无界。

97我多么爱慕你的律法,

终日思想。

98我持守你的命令,

你的命令使我比仇敌有智慧。

99我比我的老师更有洞见,

因为我思想你的法度。

100我比长者更明智,

因为我遵守你的法则。

101我听从你的话,

拒绝走恶道。

102我从未偏离你的法令,

因为你教导过我。

103你的话语品尝起来何等甘甜,

在我口中胜过蜂蜜。

104我从你的法则中得到智慧,

我厌恶一切诡诈之道。

105你的话是我脚前的灯,

是我路上的光。

106我曾经起誓,我必信守诺言:

我要遵行你公义的法令。

107我饱受痛苦,耶和华啊,

求你照你的话保护我的性命。

108耶和华啊,

求你悦纳我由衷的赞美,

将你的法令教导我。

109我的生命时刻面临危险,

但我不会忘记你的律法。

110恶人为我设下网罗,

但我没有偏离你的法则。

111你的法度永远是我的宝贵产业,

是我喜乐的泉源。

112我决心遵行你的律例,

一直到底。

113我厌恶心怀二意的人,

我爱慕你的律法。

114你是我的藏身之所,

是我的盾牌,

你的话语是我的盼望。

115你们这些恶人离开我吧,

我要顺从上帝的命令。

116耶和华啊,

求你按你的应许扶持我,

使我存活,

不要使我的盼望落空。

117求你扶持我,使我得救,

我要时刻默想你的律例。

118你弃绝一切偏离你律例的人,

他们的诡计无法得逞。

119你铲除世上的恶人,

如同除掉渣滓,

因此我喜爱你的法度。

120我因敬畏你而战抖,

我惧怕你的法令。

121我做事公平正直,

求你不要把我交给欺压我的人。

122求你保障仆人的福祉,

不要让傲慢的人欺压我。

123我望眼欲穿地期盼你拯救我,

实现你公义的应许。

124求你以慈爱待你的仆人,

将你的律例教导我。

125我是你的仆人,

求你赐我悟性可以明白你的法度。

126耶和华啊,人们违背你的律法,

是你惩罚他们的时候了。

127我爱你的命令胜于爱金子,

胜于爱纯金。

128我遵行你一切的法则,

我憎恨一切恶道。

129你的法度奇妙,我一心遵守。

130你的话语一解明,

就发出亮光,

使愚人得到启迪。

131我迫切地渴慕你的命令。

132求你眷顾我、怜悯我,

像你素来恩待那些爱你的人一样。

133求你照你的应许引导我的脚步,

不要让罪恶辖制我。

134求你救我脱离恶人的欺压,

好使我能顺服你的法则。

135求你笑颜垂顾仆人,

将你的律例教导我。

136我泪流成河,

因为人们不遵行你的律法。

137耶和华啊,你是公义的,

你的法令是公正的。

138你定的法度公义,完全可信。

139我看见仇敌漠视你的话语,

就心急如焚。

140你仆人喜爱你的应许,

因为你的应许可靠。

141我虽然卑微、受人藐视,

但我铭记你的法则。

142你的公义常存,

你的律法是真理。

143我虽然遭遇困苦患难,

但你的命令是我的喜乐。

144你的法度永远公正,

求你帮助我明白你的法度,

使我可以存活。

145耶和华啊,我迫切向你祷告,

求你应允我,

我必遵守你的律例。

146我向你呼求,求你救我,

我必持守你的法度。

147天不亮,

我就起来呼求你的帮助,

你的话语是我的盼望。

148我整夜不睡,思想你的应许。

149耶和华啊,你充满慈爱,

求你垂听我的呼求,

照你的法令保护我的性命。

150作恶多端的人逼近了,

他们远离你的律法。

151但耶和华啊,你就在我身边,

你的一切命令都是真理。

152我很早就从你的法度中知道,

你的法度永远长存。

153求你眷顾苦难中的我,搭救我,

因为我没有忘记你的律法。

154求你为我申冤,救赎我,

照着你的应许保护我的性命。

155恶人不遵守你的律例,

以致得不到拯救。

156耶和华啊,

你有无比的怜悯之心,

求你照你的法令保护我的性命。

157迫害我的仇敌众多,

但我却没有偏离你的法度。

158我厌恶这些背弃你的人,

因为他们不遵行你的话。

159耶和华啊,

你知道我多么爱你的法则,

求你施慈爱保护我的生命。

160你的话都是真理,

你一切公义的法令永不改变。

161权贵无故迫害我,

但我的心对你的话充满敬畏。

162我喜爱你的应许,

如获至宝。

163我厌恶虚假,

喜爱你的律法。

164因你公义的法令,

我要每天七次赞美你。

165喜爱你律法的人常有平安,

什么也不能使他跌倒。

166耶和华啊,我等候你的拯救,

我遵行你的命令。

167我深爱你的法度,一心遵守。

168我遵守你的法则和法度,

你知道我做的每一件事。

169耶和华啊,求你垂听我的祷告,

照你的话赐我悟性。

170求你垂听我的祈求,

照你的应许拯救我。

171愿我的口涌出赞美,

因你将你的律例教导了我。

172愿我的舌头歌颂你的应许,

因为你一切的命令尽都公义。

173愿你的手随时帮助我,

因为我选择了你的法则。

174耶和华啊,我盼望你的拯救,

你的律法是我的喜乐。

175求你让我存活,我好赞美你,

愿你的法令成为我的帮助。

176我像只迷途的羊,

求你来寻找仆人,

因为我没有忘记你的命令。