Habakuku 1 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Habakuku 1:1-17

1Uthenga umene mneneri Habakuku analandira mʼmasomphenya.

Dandawulo la Habakuku

2Kodi inu Yehova, ndidzakhala ndikukupemphani thandizo kwa nthawi yayitali motani,

koma wosayankha?

Kapena kufuwulira kwa inu kuti, “Chiwawa kuno!”

koma wosatipulumutsa?

3Chifukwa chiyani mukundionetsa zinthu zoyipa?

Chifukwa chiyani mukundionetsa mavutowa?

Ndikuona chiwonongeko ndi chiwawa;

pali ndewu ndi kukangana kwambiri.

4Kotero malamulo anu atha mphamvu,

ndipo chilungamo sichikugwira ntchito.

Anthu oyipa aposa olungama,

kotero apotoza chilungamo.

Yankho la Yehova

5“Yangʼanani pakati pa mitundu ya anthu, ndipo penyetsetsani,

ndipo muthedwe nazo nzeru.

Pakuti ndidzachitadi zinthu pa nthawi yanu

zimene inu simudzazikhulupirira,

ngakhale wina atakufotokozerani.

6Pakuti taonani, Ine ndikuwutsa Ababuloni,

anthu ankhanza ndiponso amphamvu,

amene amapita pa dziko lonse lapansi

kukalanda malo amene si awo.

7Iwowa ndi anthu ochititsa mantha, ndipo ndi owopsa;

amadzipangira okha malamulo

ndi kudzipezera okha ulemu.

8Akavalo awo ndi aliwiro kwambiri kupambana akambuku

ndi owopsa kupambana mimbulu yolusa nthawi ya madzulo.

Okwerapo awo akuthamanga molunjika;

a pa akavalo awo ndi ochokera kutali,

akuwuluka ngati chiwombankhanga chofuna kugwira nyama;

9onse akubwera atakonzekera zachiwawa.

Gulu la ankhondo likubwera ngati mphepo ya mʼchipululu

ndi kugwira akapolo ochuluka ngati mchenga.

10Akunyoza mafumu

ndiponso kuchitira chipongwe olamulira.

Akupeputsa mizinda yonse yotetezedwa;

akumanga mitumbira ndi kulanda mizindayo.

11Kenaka amasesa mofulumira ngati mphepo nʼkumangopitirirabe,

anthu ochimwa, amene mphamvu zawo ndiye mulungu wawo.”

Dandawulo Lachiwiri la Habakuku

12Inu Yehova, kodi sindinu wachikhalire?

Mulungu wanga, Woyera wanga, ife sitidzafa.

Inu Yehova, munawasankha anthuwo kuti abweretse chiweruzo;

Inu Thanthwe, munawayika iwowo kuti atilange.

13Maso anu ndi oyera kwambiri safuna kuona choyipa;

Inu simulekerera cholakwa.

Chifukwa chiyani nanga mukulekerera anthu ochita zachinyengowa?

Chifukwa chiyani muli chete pamene anthu oyipa

akuwononga anthu olungama kupambana iwowo?

14Mwasandutsa anthu kukhala ngati nsomba zamʼnyanja,

ngati zolengedwa zamʼnyanja zimene zilibe wolamulira.

15Mdani wawo woyipa amakoka anthu onse ndi mbedza,

amawakola mu ukonde wake,

amawasonkhanitsa mu khoka lake;

kotero iyeyo amakondwa ndi kusangalala.

16Choncho iye amaperekera nsembe ukonde wake

ndiponso kufukizira lubani khoka lake,

popeza ukonde wakewo ndiye umamubweretsera moyo wapamwamba

ndipo amadya chakudya chabwino kwambiri.

17Kodi iye azipitirabe kugwiritsa ntchito makoka akewo,

kuwononga mitundu ya anthu mopanda chifundo?

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

哈巴谷书 1:1-17

1以下是哈巴谷先知得到的启示。

哈巴谷的抱怨

2耶和华啊,

我要向你呼救到何时,

你才垂听呢?

暴虐横行,我向你呼求,

你却不拯救。

3你为何让我目睹罪恶?

你为何容忍邪恶?

我眼前尽是毁灭和暴力,

到处是纷争和冲突。

4因此律法失效,

正义不彰,

恶人包围义人,

正义被扭曲。

耶和华的答复

5耶和华说:“你们环顾列国,

仔细察看,

必惊奇不已,

因为我要在你们的时代行一件事,

即使你们听说了也不会相信。

6我要使凶残、暴虐的迦勒底人兴起。

他们要席卷天下,

强占别人的家园。

7他们任意妄为,

令人胆战心惊。

8“他们的马比豹子还快,

比夜狼还猛。

他们的骑兵从远方飞驰而来,

如鹰扑食。

9他们残暴成性,

像狂风一样扑来,

抓获的俘虏多如尘沙。

10他们嘲笑君王,讥讽首领,

对一切坚城嗤之以鼻,

修筑高台将其攻取。

11他们如狂风横扫而过,

这些有罪的人把自己的力量奉为神明。”

哈巴谷再次抱怨

12耶和华,

我的上帝,我的圣者啊,

你从亘古就存在,

你永不消逝1:12 你永不消逝”另有希伯来文抄本作“我们不会死”。

耶和华啊,你派迦勒底人来审判;

磐石啊,你立他们作施罚者。

13你的眼目极为清洁,

见不得邪恶,

也不能容忍罪恶。

但你为何容忍奸恶之人呢?

恶人吞灭比他们公义的人,

你为何默然不语呢?

14你为何使人像海里的鱼,

像没有首领的爬虫呢?

15迦勒底人用钩子钩住他们,

用渔网网住他们,

用拖网把他们聚在一起,

并因此而欢喜快乐。

16迦勒底人向渔网献祭,

向渔网烧香,

因为他们靠渔网而富裕,

食物充足。

17难道他们要无休止地撒网,

无情地毁灭列国吗?