Deuteronomo 7 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 7:1-26

Apirikitsa Mitundu Ina ya Anthu

1Pamene Yehova Mulungu wanu wakufikitsani mʼdziko limene mukukalowa ndi kulilanda ndi kuthamangitsa pamaso panu mitundu ya anthu iyi: Ahiti, Agirigasi, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi; yomwe ndi mitundu isanu ndi iwiri yayikulu ndi yamphamvu kuposa inu; 2Yehova Mulungu wanu akadzawapereka mʼmanja mwanu, ndipo inu mukadzawagonjetsa, mudzawawononge kwathunthu. Musadzachite mgwirizano ndi anthuwo ndiponso musadzawachitire chifundo. 3Musadzakwatirane nawo. Musadzapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna kapena kutenga ana anu aamuna ndi kuwapereka kwa ana awo aakazi. 4Mukadzatero, iwo adzasocheretsa ana anu aamuna kuti asanditsatire ndi kutumikira milungu ina. Motero Yehova adzakukwiyirani ndi kukuwonongani mwachangu. 5Koma mukachite izi: Mukagumule maguwa awo ansembe, mukaswe miyala yawo yachipembedzo, mukadule mitengo yawo ya Asera, ndi kutentha mafano awo pa moto. 6Pakuti inu ndinu anthu opatulika kwa Yehova Mulungu wanu. Yehova Mulungu wanu anakusankhani pakati pa anthu onse pa dziko lapansi kuti mukhale ake, chuma chake cha mtengo wapatali.

7Yehova sanakukondeni chifukwa choti munali ochuluka kuposa ena pakuti inuyo ndiye munali ochepetsetsa mwa anthu onse. 8Koma chifukwa chakuti Yehova anakukondani nasunga lumbiro lake limene analumbira kwa makolo anu. Ndi chifukwa chake anakutulutsani ndi mphamvu yake yopanda malire ndi kukupulumutsani ku dziko la ukapolo, kuchoka mʼmanja mwa Farao mfumu ya ku Igupto. 9Choncho dziwani kuti Yehova Mulungu wanu, ndi Mulungu. Iye ndi Mulungu wokhulupirika, wosunga pangano lake la chikondi chosasinthika ku mibadomibado, kwa iwo amene amamukonda nasunga malamulo ake. 10Koma

iwo amene amamuda adzawabwezera powawononga pamaso pawo;

sadzachedwa kuwabwezera iwo amene amadana naye.

11Choncho muziyesetsa kusunga malamulo, malangizo ndi maphunziro amene ndikukulamulani lero lino kuti muchite.

12Mukamvera malamulo amenewa, ndi kusamala kuwatsata, ndiye kuti Yehova Mulungu wanu adzasunga pangano lake la chikondi chosasinthika ndi inu, monga analumbira kwa makolo anu. 13Iye adzakukondani nakudalitsani ndi kukuchulukitsani. Adzadalitsa chipatso cha mʼmimba mwanu, zokolola za mʼdziko mwanu, tirigu wanu, vinyo wanu ndi mafuta anu, ana angʼombe zanu ndi ana ankhosa zanu mʼdziko limene analumbirira kwa makolo anu kuti akupatseni inu. 14Inu mudzadalitsika kuposa mtundu wina uliwonse wa anthu ndipo palibe mwamuna kapena mkazi aliyense pakati panu amene adzakhale wosabereka. Ziweto zanu nazonso, sipadzapezeka zosabereka. 15Yehova adzakupewetsani ku matenda aliwonse. Sadzakugwetserani matenda owopsa aja munawadziwa ku Igupto, koma adzawagwetsera pa odana nanu. 16Muwononge anthu onse amene Yehova Mulungu wanu awapereka kwa inu. Musawamvere chisoni ndipo musatumikire milungu yawo pakuti umenewo udzakhala msampha kwa inu.

17Mukhoza kunena kuti, “Anthu awa ndi amphamvu kuposa ifeyo. Nanga tingawapirikitse bwanji?” 18Koma musachite nawo mantha, kumbukirani bwino zimene Yehova Mulungu wanu anachita ndi Farao pamodzi ndi Igupto yense. 19Munadzionera nokha ndi maso anu mayesero aakulu, zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa, mphamvu yake yopanda malire imene Yehova Mulungu wanu anakutulutsirani. Yehova Mulungu adzachita zimenezo ndi anthu onse amene muwaopa tsopano. 20Kuwonjezera apo, Yehova Mulungu wanu adzatumiza mavu pakati pawo mpaka atamaliza onse amene adzakubisalirani. 21Musaopsedwe nawo pakuti Yehova Mulungu wanu, amene ali pakati panu, ndi Mulungu wamkulu ndi woopsa. 22Yehova Mulungu wanu adzapirikitsa anthu a mitundu yonse pamaso panu, pangʼonopangʼono. Sadzakulolani kuti muwathe nthawi imodzi, kuti nyama zakuthengo zingadzaswane mokuzungulirani. 23Koma Yehova Mulungu wanu adzawapereka kwa inu, adzawasokoneza kufikira atawonongedwa. 24Iye adzapereka mafumu awo mʼdzanja lanu, ndipo adzafafaniza mayina awo pa dziko lapansi. Palibe amene adzalimbana nanu, inu mudzawawononga. 25Muwawotche pa moto mafano a milungu yawo. Musasirire siliva ndi golide amene ali pa mafanoyo. Musamutenge kuti akhale wanu chifukwa mukatero mudzakodwa naye ngati msampha, pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa nazo. 26Musabweretse chinthu chonyansa mʼnyumba mwanu kuopa kuwonongedwa ngati chonyasacho. Muziyipidwa ndi kunyansidwa nacho kwambiri pakuti chidzawonongedwanso.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

申命记 7:1-26

做上帝的子民

1“你们的上帝耶和华带领你们进入将要占领的土地时,会为你们赶走人、革迦撒人、亚摩利人、迦南人、比利洗人、希未人和耶布斯人这七个比你们强大的民族。 2当你们的上帝耶和华把他们交在你们手里、使你们打败他们后,你们必须彻底毁灭他们。不可与他们立约,不可怜悯他们。 3不可与他们通婚,不可让你们的儿女与他们的儿女通婚, 4因为他们会让你们的儿女离弃耶和华去拜其他神明,以致耶和华向你们发怒,迅速毁灭你们。 5你们要拆毁他们的祭坛,打碎他们的神柱,砍下他们的亚舍拉神像,焚烧他们的偶像。 6因为你们属于你们的上帝耶和华,是圣洁的民族,祂从天下万族中拣选了你们做祂的子民——祂宝贵的产业。

7“耶和华喜爱你们、拣选你们,不是因为你们的人口比别的民族多——其实你们在万族中是最小的—— 8而是因为祂爱你们,遵守祂向你们祖先所起的誓。因此,祂用大能的手把你们从受奴役的地方领出来,从埃及王法老手中救赎了你们。 9所以你们要知道,你们的上帝耶和华是真神,是信实的真神,祂向爱祂、遵守祂诫命的人守约、施慈爱直到千代。 10但祂必毫不迟延地报应、毁灭那些恨祂的人。 11所以,你们要遵行我今天吩咐你们的诫命、律例和典章。

遵守诫命必蒙福

12“如果你们听从并谨遵这一切,你们的上帝耶和华就会信守祂给你们祖先的誓约,以慈爱待你们。 13祂会爱你们,赐福给你们,使你们在祂向你们祖先起誓要赐给你们的土地上子孙昌盛,牛羊成群,收获丰富的谷物、新酒和油。 14天下万族之中,你们是最蒙福的,你们的男人、女人和牲畜没有不能生育的。 15耶和华要使你们免患疾病,免遭你们在埃及所见的恶疾,祂要把那些恶疾降在一切憎恶你们的人身上。 16你们必须灭绝你们的上帝耶和华交在你们手里的各族,不可怜悯他们,不可拜他们的神明,因为那样会使你们陷入网罗。

17“也许你们心里会说,‘这些民族都比我们强大,我们怎能赶走他们呢?’ 18不要怕他们,要牢记你们的上帝耶和华曾如何对付埃及和法老, 19你们亲眼目睹祂如何降下大灾难、行神迹奇事、伸出臂膀和大能的手领你们离开埃及,祂也要这样对付你们所惧怕的各族。 20你们的上帝耶和华还要派黄蜂去攻击他们,直到躲藏起来的残存者也全部灭亡。 21不要惧怕他们,因为你们的上帝耶和华住在你们当中,祂是伟大而可畏的上帝。 22你们的上帝耶和华将在你们前面渐渐地赶走那些民族,你们不可急速地灭尽他们,否则你们周围的野兽会大增,危害你们。 23你们的上帝耶和华要将他们交给你们,使他们惊恐万状,直到被灭绝。 24祂要将他们的王交在你们手中,无人能抵挡你们,你们要毁灭他们,使他们的名字从世上绝迹。 25你们要烧毁他们的神像,不可贪图神像上的金银,不可将那些金银据为己有,免得你们因此陷入网罗;因为那是你们的上帝耶和华所憎恶的。 26不可把可憎之物带到家里,否则你们会像它们一样被毁灭。你们要极其憎恶、厌弃它们,因为它们是当毁灭之物。