Yehova Asankha Yoswa Kukhala Mtsogoleri
1Atamwalira Mose mtumiki wa Mulungu, Yehova anati kwa Yoswa mwana wa Nuni mthandizi wa Mose: 2“Mose mtumiki wanga wamwalira. Ndipo iwe ndi anthu onsewa, tsopano konzekani kuwoloka mtsinje wa Yorodani kupita ku dziko limene ndiwapatse Aisraeli onse. 3Paliponse pamene phazi lanu liponde, ndikupatsani monga momwe ndinalonjezera Mose. 4Dziko lanu lidzayambira ku chipululu kummwera mpaka ku mapiri a Lebanoni kumpoto, kuchokeranso ku mtsinje waukulu wa Yufurate kummawa, mpaka dziko lonse la Ahiti, kukafika ku Nyanja Yayikulu ya kumadzulo. 5Palibe munthu amene adzatha kukugonjetsa masiku onse a moyo wako. Monga Ine ndinakhalira ndi Mose, chomwechonso ndidzakhala nawe. Sindidzakusiya kapena kukataya.
6“Ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima, chifukwa iwe udzatsogolera anthu awa kukalandira dziko limene Ine ndinalonjeza makolo awo kuti ndidzawapatsa. 7Ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima kwambiri. Usamale ndithu kuti umvere malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakupatsa. Usachoke pa malamulo anga ndipo kulikonse kumene udzapite udzapambana. 8Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana. 9Paja ndinakulamula kuti ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima. Choncho usamachite mantha kapena kutaya mtima popeza Ine Yehova Mulungu wako ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”
10Tsono Yoswa analamula atsogoleri a Aisraeli nawawuza kuti, 11“Pitani ku misasa yonse ndipo muwuze anthu kuti, ‘Konzekani, mangani katundu wanu, popeza pakapita masiku atatu kuyambira lero mudzawoloka Yorodani kupita kukatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.’ ”
12Koma Yoswa anawuza fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti, 13“Kumbukirani zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani kuti, ‘Yehova Mulungu wanu akukupatsani mpumulo, ndi dziko ili kuti likhale lanu.’ 14Tsono akazi anu, ana anu ndi ziweto zanu zitsale mʼdziko lino limene Mose anakupatsani kummawa kwa Yorodani. Koma ankhondo anu okha ndiwo awoloke atatenga zida zawo ndi kupita patsogolo pa abale anu kukawathandiza. 15Abale anuwo akadzalandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akuwapatsa monga inu mwachitira, inu mudzabwerera kudzakhazikika mʼdziko lanu limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya la kummawa kwa Yorodani.”
16Kenaka iwo anayankha Yoswa kuti, “Ife tidzachita chilichonse chimene mwatilamula, ndipo kulikonse kumene mudzatitume tidzapita. 17Monga momwe tinamvera Mose kwathunthu, chomwechonso tidzakumvera iwe. Yehova Mulungu wanu akhale nanu monga momwe anachitira ndi Mose. 18Aliyense wotsutsana ndi inu kapena wosamvera zimene mutilamula adzaphedwa. Inu mukhale wamphamvu ndi wolimba mtima!”
主对约书亚的吩咐
1耶和华的仆人摩西死了以后,耶和华对摩西的助手——嫩的儿子约书亚说: 2“我的仆人摩西已经死了,现在你和全体以色列人要准备渡过约旦河,到我要赐给你们的地方去。 3我已把你们脚掌将踏之地都赐给了你们,正如我对摩西的应许。 4从南部的旷野直到北部的黎巴嫩,从东部的幼发拉底大河直到西部的地中海,包括赫人居住的全境,都将是你们的领土。 5在你有生之年,没有人能够抵挡你。过去我怎样与摩西同在,也必照样与你同在,我必不离开你,也不丢弃你。 6你要刚强勇敢,因为你要带领这些人占领我起誓赐给他们祖先的土地。 7你只要刚强勇敢,谨遵我仆人摩西所吩咐你的一切律法,毫不偏离,就可以无往不利。 8你要常常诵读这律法书,昼夜不断地思想,以便谨遵律法书上的一切指示。这样,你必亨通、顺利。 9我再次吩咐你,要刚强勇敢!不要害怕,也不要灰心,因为你无论走到哪里,你的上帝耶和华必与你同在。”
10于是,约书亚吩咐民众的首领说: 11“你们要走遍全营,吩咐大家预备好食物。因为三天之内,你们就要过约旦河,去占领你们的上帝耶和华赐给你们的土地。”
12约书亚又对吕便支派、迦得支派和玛拿西半个支派的人说: 13“你们要牢记耶和华的仆人摩西吩咐你们的话,他说你们的上帝耶和华要把约旦河东面的土地赐给你们,让你们安居。 14你们的妻子儿女和牲畜可以留在约旦河东岸摩西分给你们的土地上,但你们当中所有的勇士要带着兵器先过约旦河,帮助你们的弟兄。 15要等到你们的上帝耶和华使你们的弟兄像你们一样得到祂所赐的土地,安居以后,你们才可以回到约旦河东,在耶和华的仆人摩西分给你们的土地上定居。” 16他们回答约书亚说:“凡你命令我们的,我们一定遵行。无论你派我们去哪里,我们一定去。 17我们在一切的事上怎样服从摩西,也必照样服从你,愿你的上帝耶和华与你同在,像与摩西同在一样。 18任何人违抗你的命令,不照你的吩咐去做,都要被处死。你要刚强勇敢!”