Deuteronomo 5 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 5:1-33

Malamulo Khumi

1Mose anayitanitsa Aisraeli onse nati:

Tamverani inu Aisraeli, malangizo ndi malamulo amene ndikuwuzeni lero. Muwaphunzire ndi kuonetsetsa kuti mukuwatsata. 2Yehova Mulungu wathu anachita pangano ndi ife ku Horebu. 3Yehova sanachite pangano ndi makolo athu koma ndi ife, tonse amene tili moyo lero. 4Yehova anayankhula nanu maso ndi maso kuchokera mʼmoto pa phiri paja. 5(Pa nthawi imeneyo ine ndinayimirira pakati pa Yehova ndi inu kuti ndikuwuzeni mawu a Yehova, chifukwa inu munkachita mantha ndi moto ndipo simunakwere ku phiri). Ndipo Iye anati:

6“Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo.

7“Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.

8“Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. 9Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane, 10koma ndimaonetsa chikondi chosasinthika ku mibado miyandamiyanda ya anthu amene amandikonda ndi kusunga malamulo anga.

11“Usagwiritse ntchito molakwika dzina la Yehova Mulungu wako, pakuti Yehova adzamutenga kukhala wochimwa aliyense amene akugwiritsa ntchito dzina lakelo molakwika.

12“Uzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika monga momwe Yehova Mulungu wako anakulamulira. 13Uzigwira ntchito zako zonse masiku asanu ndi limodzi, 14koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi kapena wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu kapena ngʼombe yanu kapena bulu wanu kapena ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu, motero ndiye kuti wantchito wanu wamwamuna ndi wantchito wanu wamkazi adzapumula monga inuyo. 15Kumbukira kuti unali kapolo ku Igupto ndipo Yehova Mulungu wako anakutulutsa kumeneko ndi dzanja lamphamvu ndi lotambasuka. Choncho Yehova Mulungu wako akukulamula kuti uzisunga tsiku la Sabata.

16“Lemekeza abambo ako ndi amayi ako monga Yehova Mulungu wako wakulamulira iwe kuti ukhale ndi moyo wautali ndi kuti zikuyendere bwino mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.

17“Usaphe.

18“Usachite chigololo.

19“Usabe.

20“Usapereke umboni womunamizira mnzako.

21“Usasirire mkazi wa mnzako. Usasirire nyumba ya mnzako kapena munda wake, wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”

22Awa ndi malamulo amene Yehova anayankhula ndi mawu okweza kwa gulu lanu lonse pa phiri paja mʼmoto, mtambo ndi mdima woopsa, sanawonjezerepo kanthu. Ndipo anawalemba pa mapale awiri amiyala ndi kundipatsa.

23Mutamva mawu kuchokera mu mdimawo, phiri lili moto lawilawi, atsogoleri onse a mafuko anu ndi akuluakulu anu anabwera kwa ine. 24Ndipo munati, “Yehova Mulungu wathu wationetsa ulemerero ndi ukulu wake, ndipo tamva mawu ake kuchokera mʼmoto. Lero taona kuti munthu akhoza kukhala ndi moyo ngakhale Mulungu atayankhula naye. 25Koma tsopano tife chifukwa chiyani? Moto waukuluwu utinyeketsa, ndipo tifa tikapitirirabe kumva mawu a Yehova Mulungu wathu. 26Pakuti ndi munthu uti wolengedwa amene anamvapo mawu a Mulungu wamoyo akuyankhula kuchokera mʼmoto, monga tachitiramu, nakhala ndi moyo? 27Pita pafupi kuti ukamvetsere zonse zimene Yehova Mulungu wathu akunena. Kenaka udzatiwuze chilichonse chimene Yehova Mulungu wathu akunena ndipo tidzamvera ndi kuchita.”

28Yehova anakumvani pamene munkayankhula kwa ine ndipo Yehova anati kwa ine, “Ndamva zimene anthuwa anena kwa iwe. Chilichonse chimene anena ndi chabwino. 29Zikanakhala bwino akanakhala ndi mtima wondiopa ndi kusunga malamulo anga nthawi zonse kuti zinthu ziziwayendera bwino, iwowo pamodzi ndi ana awo kwamuyaya.

30“Pita uwawuze kuti abwerere ku matenti awo. 31Koma iwe ukhale kuno ndi ine kuti ndikupatse malamulo, malangizo ndi ziphunzitso zimene azitsatira mʼdziko limene ndiwapatse kuti alitenge.”

32Choncho samalirani kuchita zimene Yehova Mulungu wanu akukulamulirani inu, musapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere. 33Muyende mʼnjira yonse imene Yehova Mulungu wanu wakulamulirani kuti mukhale ndi moyo ndi kupambana, ndi kuti masiku anu achuluke mʼdziko limene mudzatengelo.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

申命记 5:1-33

十诫

1摩西把所有的以色列人召来,对他们说:“以色列人啊,要留心听我今天对你们宣讲的律例和典章,要学习并谨慎遵行。 2我们的上帝耶和华曾在何烈山与我们立约, 3这约不是与我们祖先立的,乃是与我们今天还活着的人立的。 4耶和华在山上的烈火中面对面跟你们说话。 5那时,因为你们害怕那烈火,没有到山上去,我就站在耶和华和你们中间,把耶和华的话传给你们。耶和华说,

6“‘我是你的上帝耶和华,曾把你领出埃及,使你不再受奴役。

7“‘除我以外,你不可有别的神。

8“‘不可为自己雕刻神像,不可仿照任何飞禽走兽或水族的样子造神像, 9不可跪拜它们,也不可供奉它们,因为我——你的上帝耶和华痛恨不贞,我必追讨背弃我之人的罪,从父到子直到三四代。 10但那些爱我、遵守我诫命的人,我必以慈爱待他们,直到千代。

11“‘不可妄用你上帝耶和华的名,违者必被耶和华定罪。

12“‘要遵照你的上帝耶和华的吩咐守安息日为圣日。 13你一周可工作六天, 14但第七天是你的上帝耶和华的安息日,你和儿女、仆婢、牛驴等牲畜以及你那里的外族人在这一天不可做任何工,好让仆婢和你一样得到休息。 15要记住,你曾在埃及做奴隶,你的上帝耶和华伸出臂膀,用大能的手把你从那里领出来。因此,你的上帝耶和华吩咐你守安息日。

16“‘要遵照你的上帝耶和华的吩咐孝敬父母,以便在你的上帝耶和华要赐给你的土地上享长寿,蒙祝福。

17“‘不可杀人。

18“‘不可通奸。

19“‘不可偷盗。

20“‘不可作伪证陷害人。

21“‘不可贪恋别人的妻子,不可贪图别人的房屋、田地、仆婢、牛驴或其他任何物品。’

22“这是耶和华在山上的烈火、乌云和幽暗中高声颁布给你们全体会众的诫命。此外,祂没有说别的。祂把这些话写在两块石版上交给我。 23当时,山上燃烧着烈焰,你们听见声音从黑暗中传来。你们各支派的首领和长老都到我跟前, 24说,‘看啊,我们的上帝耶和华向我们彰显了祂的荣耀和威严,我们听见了祂从火中发出的声音。今天我们已经看见,人听见上帝说话后还能活着。 25但我们何必冒死,被这烈火吞噬呢?我们若再次听到我们的上帝耶和华的声音,必然丧命。 26世上有谁像我们一样听见永活上帝从火中说话后还能活着呢? 27你去听听我们上帝耶和华所说的话,然后回来告诉我们,我们必听从、遵行。’

28“耶和华听见了你们的话,就对我说,‘我听见了众人对你说的话,他们所说的都对。 29但愿他们常常敬畏我,遵从我的一切诫命,以便他们和他们的子孙世世代代可以蒙福。 30你吩咐他们回到自己的帐篷, 31然后你再回到我这里来,我要把所有的诫命、律例和典章都赐给你,你要把这些传授给众人,使他们可以在我要赐给他们的土地上遵行。’ 32所以,你们要谨遵你们上帝耶和华的吩咐,不可偏离左右。 33这样,你们便得享长寿,并且可以在你们将要占领的土地上兴盛。