Deuteronomo 27 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 27:1-26

Guwa Lansembe ku Phiri la Ebala

1Mose ndi akuluakulu a Israeli analamula anthu kuti, “Sungani malamulo onse amene ndikukupatsani lero lino. 2Mukawoloka mtsinje wa Yorodani kulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, muyimiritse miyala ingapo ikuluikulu ndi kuyikulungiza. 3Mulembepo mawu onse a malamulo amenewa pamene muwoloka kulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani. 4Ndipo mukawoloka Yorodani muyimike miyala iyi pa Phiri la Ebala monga momwe ndikukulamulirani lero lino ndipo muyikulungize. 5Pamenepo mumange guwa lansembe la miyala la Yehova Mulungu wanu. Musagwiritse ntchito chida chilichonse chachitsulo pa miyalapo. 6Mumange guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu ndi miyala yakutchire ndi kuperekerapo nsembe yopsereza kwa Yehova Mulungu wanu. 7Muperekerepo nsembe zopereka za chiyanjano, muzidye ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 8Ndipo pa miyalapo mudzalembepo mawu onse a malamulo ndi malemba akuluakulu.”

Matemberero Kuchokera ku Phiri la Ebala

9Kenaka Mose ndi ansembe, amene ndi Alevi anati kwa Aisraeli onse, “Khalani chete Aisraeli inu ndipo mumvetsere! Tsopano inu ndinu anthu a Yehova Mulungu wanu. 10Muzimvera Yehova Mulungu wanu ndi kutsata malamulo ake ndi malangizo ake omwe ndikukupatsani lero lino.”

11Tsiku lomwelo Mose analamula anthu kuti:

12Mukawoloka Yorodani, mafuko awa akayimirire pa Phiri la Gerizimu ndi kudalitsa anthu: Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Yosefe ndi Benjamini. 13Ndipo mafuko awa akayimirire pa Phiri la Ebala ndi kutchula matemberero: Rubeni, Gadi, Aseri, Zebuloni, Dani ndi Nafutali.

14Alevi adzayankhula mokweza kwa Aisraeli onse kuti:

15“Ndi wotembereredwa munthu amene asema chifanizo kapena kupanga fano, ndi kuchiyika mobisa, pakuti chimenechi ndi chinthu chodetsedwa pamaso pa Yehova, ntchito za manja a anthu.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

16“Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira ulemu abambo ake kapena amayi ake.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

17“Ndi wotembereredwa munthu amene amasuntha mwala wa malire wa mnzake.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

18“Ndi wotembereredwa munthu amene amasocheretsa munthu wosaona pa msewu.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

19“Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira chilungamo mlendo, ana amasiye kapena mkazi wamasiye.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

20“Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mkazi wa abambo ake pakuti iye sachitira ulemu pogona pa abambo ake.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

21“Ndi wotembereredwa munthu amene achita chigololo ndi nyama ya mtundu uli wonse.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

22“Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake kapena mwana wamkazi wa amayi ake.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

23“Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi apongozi ake.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

24“Ndi wotembereredwa munthu amene apha mnzake mwachinsinsi.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

25“Ndi wotembereredwa munthu amene alandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

26“Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita kapena sasunga mawu a malamulo awa.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

New Russian Translation

Второзаконие 27:1-26

Жертвенник на горе Гевал

1Моисей и старейшины Израиля повелели народу:

– Исполняйте все повеления, которые я даю вам сегодня. 2Когда вы перейдете через Иордан в землю, которую Господь, ваш Бог, дает вам, тогда поставьте большие камни и покройте их известью. 3Напишите на них все слова этого Закона, когда переправитесь, чтобы войти в землю, которую Господь, ваш Бог, дает вам, землю где течет молоко и мед, как Господь, Бог ваших отцов, и обещал вам. 4А когда вы перейдете через Иордан и установите эти камни на горе Гевал, как я повелеваю вам сегодня, покройте их известью. 5Построй там жертвенник Господу, твоему Богу, жертвенник из камней. Не обрабатывай эти камни железным орудием. 6Построй жертвенник Господу, твоему Богу, из нетесаных27:6 Букв.: «цельных». камней и приноси на нем всесожжения Господу, твоему Богу. 7Приноси там жертвы примирения, ешь их и веселись в присутствии Господа, твоего Бога. 8Напиши четко и ясно все слова этого Закона на камнях, которые ты установишь.

Проклятия с горы Гевал

9Затем Моисей и священники из левитов сказали всему Израилю:

– Молчи и слушай, Израиль! Теперь ты стал народом Господа, твоего Бога. 10Слушайся Господа, твоего Бога, и исполняй все Его повеления и установления, которые я даю тебе сегодня.

11В тот же день Моисей повелел народу:

12– Когда вы перейдете через Иордан, вот какие роды встанут на горе Гаризим, чтобы благословить народ: Симеон, Левий, Иуда, Иссахар, Иосиф и Вениамин. 13А эти роды встанут на горе Гевал, чтобы произносить проклятия: Рувим, Гад, Асир, Завулон, Дан и Неффалим.

14Левиты будут возвещать всему народу Израиля громким голосом:

15«Проклят человек, который сделает изваянного или литого идола – вещь, отвратительную Господу, работу рук ремесленника, и поставит его в тайнике».

И весь народ пусть скажет: «Аминь!»27:15 Аминь – еврейское слово, которое переводится как «да, верно, воистину так» или «да будет так».

16«Проклят человек, который оскорбит отца или мать».

И весь народ пусть скажет: «Аминь!»

17«Проклят человек, который передвинет межевой камень ближнего своего».

И весь народ пусть скажет: «Аминь!»

18«Проклят человек, который собьет слепого с пути».

И весь народ пусть скажет: «Аминь!»

19«Проклят человек, который откажет в правосудии чужеземцу, сироте или вдове».

И весь народ пусть скажет: «Аминь!»

20«Проклят человек, который переспит с женой своего отца, потому что он позорит постель своего отца27:20 Букв.: «открывает край одежды своего отца».».

И весь народ пусть скажет: «Аминь!»

21«Проклят человек, который совокупится с животным».

И весь народ пусть скажет: «Аминь!»

22«Проклят человек, который ляжет со своей сестрой, дочерью своего отца или своей матери».

И весь народ пусть скажет: «Аминь!»

23«Проклят человек, который переспит со своей тещей».

И весь народ пусть скажет: «Аминь!»

24«Проклят человек, который тайно убьет другого».

И весь народ пусть скажет: «Аминь!»

25«Проклят человек, который берет взятку, чтобы убить невиновного».

И весь народ пусть скажет: «Аминь!»

26«Проклят человек, который не исполняет слов этого Закона и не следует им».

И весь народ пусть скажет: «Аминь!»