歷代志上 29 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

歷代志上 29:1-30

為建殿而獻的禮物

1大衛王又對全體會眾說:「我兒所羅門是上帝特別揀選的,但他還年輕,缺乏經驗。建殿的工程浩大,因為這殿不是為人造的,乃是為耶和華上帝造的。 2我已竭盡所能為我上帝的殿預備了製作金器、銀器、銅器、鐵器和木器所需的金銀銅鐵及木頭,還有大量的瑪瑙、鑲嵌用的寶石、彩石、大理石及其他貴重的石頭。 3而且,我因為愛慕我上帝的殿,除了預備以上物品外,還把自己珍藏的金銀獻上,用來建造我上帝的殿。 4我獻上一百噸俄斐金、二百四十噸純銀,用來貼殿牆, 5供匠人製作金器銀器。今天,有誰樂意向耶和華奉獻?」

6結果,各族長、以色列各支派的首領、千夫長、百夫長和負責王室事務的官員都樂意奉獻, 7他們為上帝的殿奉獻了一百七十噸金子,三百四十噸銀子,六百二十噸銅,三千四百噸鐵。 8有寶石的人都把寶石交到耶和華殿的庫房,由革順耶歇保管。 9因為他們誠心誠意地把東西獻給上帝,百姓歡喜不已,大衛王也非常歡喜。

大衛頌讚耶和華

10大衛在會眾面前頌讚耶和華,說:「我們先祖以色列的上帝耶和華啊,你永永遠遠當受頌讚! 11耶和華啊,偉大、權能、榮耀、尊貴和威嚴都是你的,天上地下的一切都是你的。耶和華啊,國度是你的,你是萬有的主宰。 12富貴和尊榮都從你而來,你掌管一切,你手中有權能和力量,能使人尊大、強盛。 13我們的上帝啊,我們稱頌你,讚美你榮耀的名。

14「我算什麼,我的人民算什麼,怎麼配向你奉獻?因為萬物都從你而來,我們只是把從你那裡得來的獻給你。 15我們在你面前只是客旅,是寄居的,像我們祖先一樣;我們在世的日子就像影子一樣轉瞬即逝。 16我們的上帝耶和華啊,我們為你的聖名建造殿宇所預備的這一切財物都是從你那裡來的,都屬於你。 17我的上帝啊,我知道你洞察人心,喜愛正直的人。我懷著正直的心甘願獻上這一切,我也看見你這裡的子民甘心樂意地將財物獻給你。 18我們祖先亞伯拉罕以撒以色列的上帝耶和華啊!求你使你的子民常存這樣的心志,使他們的心忠於你。 19求你賜給我兒所羅門忠誠的心,以遵行你的誡命、法度和律例,用我預備的材料全力建造殿宇。」

20大衛對全體會眾說:「你們要頌讚你們的上帝耶和華。」於是,全體會眾頌讚他們祖先的上帝耶和華,向耶和華和王俯伏下拜。

所羅門被立為王

21次日,他們向耶和華獻祭。他們代表全以色列獻上一千頭公牛、一千隻公綿羊、一千隻羊羔作燔祭,同時還獻上奠祭及許多其他祭。 22那一天,他們在耶和華面前歡歡喜喜地吃喝。

他們再次擁立大衛的兒子所羅門做王,在耶和華面前膏立他做首領,又膏立撒督做祭司。 23於是,所羅門登上了耶和華所賜的王位,接替他父親大衛做王。他凡事亨通,以色列眾人都服從他, 24眾首領、勇士以及大衛王的眾子都效忠於他。 25耶和華使所羅門倍受以色列人尊崇,賜他君王的威嚴,超過在他之前的所有以色列王。

大衛去世

26耶西的兒子大衛是全以色列的王, 27他在以色列執政共四十年:在希伯崙執政七年,在耶路撒冷執政三十三年。 28大衛年紀老邁,享盡富貴尊榮後,壽終正寢。他兒子所羅門繼位。 29大衛王一生的事蹟都記在撒母耳先見、拿單先知和迦得先見的史記上。 30書中記述了他的政績和英勇事蹟,以及他和以色列及列國所遭遇的事。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 29:1-30

Zopereka Zomangira Nyumba ya Mulungu

1Kenaka, mfumu Davide inati kwa gulu lonse: “Mwana wanga Solomoni amene Mulungu wamusankha ndi wamngʼono ndipo sadziwa zambiri. Ntchitoyi ndi yayikulu chifukwa nyumba yaufumuyi si ya munthu, koma ndi ya Yehova Mulungu. 2Ine ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu zinthu zanga zonse, golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva ndi zitsulo zopangira zinthu zazitsulo, mkuwa wopangira zinthu zamkuwa ndi matabwa opangira zinthu zamatabwa komanso miyala yokongola ya onikisi yokongoletsera, miyala ya maonekedwe osiyanasiyana, ndi miyala yonse yosalala ndi miyala ya marabulo, zonsezi ndapereka zochuluka. 3Kupatulapo izi, ine modzipereka ku Nyumba ya Mulungu wanga, tsopano ndikupereka chuma changachanga cha golide ndi siliva ku Nyumba ya Mulungu wanga, kuwonjezera pa zimene ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu woyerayu: 4Matani 100 agolide (golide wa ku Ofiri) ndi matani 240 a siliva woyengeka bwino wokutira makoma a nyumba, 5zinthu zagolide ndi zinthu zasiliva, ndiponso zinthu zonse zimene anthu aluso adzagwiritse ntchito. Tsopano ndani amene akufuna kudzipatulira yekha kwa Yehova lero?”

6Tsono atsogoleri a mabanja, akuluakulu a mafuko a Israeli, olamulira asilikali 1,000, ndi olamulira asilikali 100, ndiponso akuluakulu onse amene amayangʼanira ntchito ya mfumu anapereka mwaufulu. 7Iwo anapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu matani 170 a golide, matani 340 a siliva, matani 620 a mkuwa ndi matani 3,400 a chitsulo. 8Aliyense amene anali ndi miyala yokongola anayipereka ku nyumba yosungiramo chuma cha Nyumba ya Yehova ndipo amene ankayangʼanira anali Yehieli Mgeresoni. 9Anthu anakondwa chifukwa cha kupereka mwaufulu kwa atsogoleri awo, pakuti anapereka kwa Yehova mwaufulu ndiponso ndi mtima wonse. Nayenso mfumu Davide anakondwera kwambiri.

Pemphero la Davide

10Davide anatamanda Yehova pamaso pa gulu lonse, ponena kuti,

“Mutamandidwe Inu Yehova

Mulungu wa kholo lathu Israeli

kuchokera muyaya mpaka muyaya.

11Wanu, Inu Yehova ndi ukulu ndi mphamvu,

ulemerero ndiponso ufumu ndi kukongola.

Pakuti zinthu zonse zakumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu.

Wanu, Inu Yehova ndi ufumu;

Inu ndinu wokwezeka ndipo ndinu mtsogoleri wa zonse.

12Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu;

Inu ndinu wolamulira zinthu zonse.

Mʼdzanja lanu muli nyonga ndi mphamvu,

kukweza ndi kupereka nyonga kwa onse.

13Tsopano Mulungu wathu, ife tikukuthokozani

ndi kutamanda dzina lanu laulemerero.

14“Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndani, kuti tikupatsani mowolowamanja motere? Zinthu zonse zimachokera kwa Inu, ndipo ife takupatsani zomwe zimachokera mʼdzanja lanu. 15Ife ndife anthu osadziwika ndiponso alendo pamaso panu, monga analili makolo athu. Masiku anthu pa dziko lapansi ali ngati chithunzithunzi, wopanda chiyembekezo. 16Inu Yehova Mulungu wathu, zinthu zonse zimene tapereka kumangira Nyumba yanu zachokera mʼdzanja lanu ndipo zonsezi ndi zanu. 17Mulungu wanga, ine ndikudziwa kuti mumayesa mtima ndipo mumakondwera ndi anthu angwiro. Zinthu zonsezi ndapereka mwaufulu ndi cholinga chabwino. Ndipo tsopano ndaona ndi chimwemwe momwe anthu anu amene ali pano akuperekera mwaufulu kwa Inu. 18Inu Yehova Mulungu wa makolo athu Abrahamu, Isake ndi Israeli, mukhazikitse chofuna ichi mʼmitima ya anthu anu kwamuyaya, ndipo mukhazikitse mtima wokhulupirika kwa Inu. 19Ndipo mumupatse mwana wanga Solomoni mtima wodzipereka kwathunthu kwa Inu kuti asunge malamulo anu, zofuna ndi malangizo anu. Achite chilichonse pomanga nyumba yaufumu imene ine ndayipezera zofunika zonse.”

20Kenaka mfumu Davide inati kwa gulu lonse, “Tamandani Yehova Mulungu wanu.” Kotero onse anatamanda Yehova, Mulungu wa makolo awo ndipo anawerama pansi ndi kugona chafufumimba pamaso pa Yehova ndi mfumu.

Solomoni Avomerezedwa Monga Mfumu

21Mmawa mwake anthu anapereka nsembe zosiyanasiyana ndi nsembe zopsereza kwa Yehova; ngʼombe zamphongo 1,000, nkhosa zamphongo 1,000 ndi ana ankhosa 1,000, pamodzi ndi nsembe yachakumwa ndi nsembe zina zambiri zoperekera Aisraeli onse. 22Tsiku limeneli, iwo anadya ndi kumwa mosangalala pamaso pa Yehova ndipo anavomereza Solomoni mwana wa Davide kukhala mfumu yawo kachiwiri.

Anamudzoza pamaso pa Yehova kukhala wolamulira wawo ndipo Zadoki anadzozedwa kukhala wansembe. 23Ndipo Solomoni ankakhala pa mpando waufumu wa Yehova monga mfumu mʼmalo mwa Davide abambo ake. Iye analemera ndipo Aisraeli onse ankamumvera. 24Akuluakulu onse a ankhondo ndi anthu amphamvu, pamodzinso ndi ana onse aamuna a mfumu Davide, analonjeza kumvera mfumu Solomoni.

25Yehova anamukweza kwambiri Solomoni pamaso pa Aisraeli onse ndi kumupatsa ulemerero waufumu umene sunapatsidwepo kwa mfumu ina iliyonse ya Israeli.

Imfa ya Davide

26Davide mwana wa Yese anali mfumu ya Aisraeli onse. 27Iye analamulira Israeli kwa zaka makumi anayi; zaka zisanu ndi ziwiri ali ku Hebroni ndi zaka 33 ali ku Yerusalemu. 28Iye anamwalira atakalamba kwambiri, atakhala ndi moyo wautali, chuma ndi ulemu. Solomoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

29Tsono zonse zimene mfumu Davide anachita, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mneneri Samueli, mʼbuku la mneneri Natani ndi mʼbuku la mneneri Gadi, 30pamodzi ndi tsatanetsatane wa mbiri ya ulamuliro wake ndi mphamvu zake, ndi zonse zomwe zinamuzungulira iye ndi Israeli ndiponso mafumu a mayiko ena onse.