使徒行传 16 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

使徒行传 16:1-40

提摩太加入福音事工

1保罗来到特庇,然后又到路司得。那里有个门徒名叫提摩太,母亲是信主的犹太人,父亲是希腊人。 2路司得以哥念的弟兄姊妹都称赞提摩太3保罗打算带提摩太去传福音。因为当地的犹太人都知道提摩太的父亲是希腊人,保罗就给提摩太行了割礼。 4他们走遍各城,把耶路撒冷的使徒和长老所定下的规条教导当地的门徒遵守。 5这样,众教会在信仰上得到坚固,人数天天都在增加。

马其顿人的呼求

6由于圣灵阻止他们到亚细亚传福音,他们便经过弗吕迦加拉太地区, 7来到每西亚的边界,正要进入庇推尼地区,耶稣的灵又加以拦阻。 8他们就越过每西亚,下到特罗亚9当天晚上,保罗在异象中看见一个马其顿人站在那里恳求他:“请到马其顿来帮助我们!”

10保罗见了这个异象,确信是上帝呼召我们16:10 本书作者路加此时加入保罗的行列,故改用第一人称复数“我们”。马其顿去传福音,就立刻准备动身。 11我们从特罗亚启航,直接驶往撒摩特喇,第二天抵达尼亚坡里12再从那里来到腓立比腓立比马其顿的主要城市,是罗马帝国的殖民地。我们在那里住了几天。 13安息日那天,我们到城外的河边,知道那里有一个祷告的地方,就坐下来,向已经聚集的妇女讲道。 14听众中有个卖紫色布匹的妇人名叫吕底亚,是推雅推喇城的人,向来敬拜上帝。上帝开启她的心,她便留心听保罗讲道。 15吕底亚和家人接受洗礼之后,极力邀请我们,说:“如果你们认为我是真心信主的话,请来我家住。”于是强留我们住下。

保罗和西拉入狱

16一天,我们又去河边那个祷告的地方,途中遇到一个被巫鬼附身的女奴。她用占卜为她的主人们赚了不少钱。 17她跟着保罗和我们大喊大叫:“这些人是至高上帝的奴仆,是来向你们宣讲得救之道的。” 18一连几天,她都这样喊叫。保罗不胜其烦,就转过身来斥责那鬼:“我奉耶稣基督的名命令你从她身上出来!”那鬼立刻从她身上出去了。

19她的主人们眼见财路断绝了,就把保罗西拉揪住,拖到广场去见官长。 20他们在官长面前控告保罗西拉,说:“这些是犹太人,竟扰乱我们的城市, 21宣扬我们罗马人不可接受或实行的风俗。” 22于是,大家都一起攻击他们,官长下令剥掉他们的衣服,杖打他们。 23他们被毒打一顿,又被关进监狱,官长命狱卒严密看守。 24狱卒接到命令后把他们关进内牢,双脚上了枷锁。

25半夜,保罗西拉祷告、唱诗赞美上帝,其他的囚犯都侧耳倾听。 26突然间发生大地震,整座监狱的地基都摇动起来,牢门立刻全开了,囚犯的锁链也都松开了。 27狱卒惊醒后,看见牢门尽开,以为囚犯已经逃走了,就想拔刀自杀。 28保罗见状,大声喝止:“不要伤害自己,我们都在这里!”

29狱卒叫人拿灯过来,冲进内牢,战战兢兢地俯伏在保罗西拉面前。 30狱卒领他们出来后问道:“两位先生,我该怎样做才能得救?”

31他们说:“要信主耶稣,你和你一家就必定得救。” 32于是保罗西拉向狱卒和他全家传讲主的道。 33当晚,狱卒把二人带去,为他们清洗伤口。他一家老小都接受了洗礼。 34他请二人到家里吃饭,他和全家人充满了喜乐,因为都信了上帝。

35第二天早上,官长派差役来,说:“把他们放了。” 36狱卒转告保罗说:“官长下令释放你们,现在你们可以平安地走了。” 37保罗却说:“我们是罗马公民,他们不经审讯就当众打我们,又把我们关进牢里,现在却想偷偷打发掉我们吗?这样不行,叫他们亲自来领我们出去!”

38差役回报官长。官长得知保罗西拉都是罗马公民,非常害怕, 39连忙到狱中向他们道歉,领他们出监,又央求他们离开腓立比40二人离开监狱,来到吕底亚家中,见了弟兄姊妹,劝勉一番之后,便离开了那里。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 16:1-40

Timoteyo Atsagana ndi Paulo ndi Sila

1Paulo anafika ku Derbe ndi Lusitra, kumene kumakhala ophunzira wina dzina lake Timoteyo. Amayi ake anali Myuda wokhulupirira, koma abambo ake anali Mgriki. 2Abale a ku Lusitra ndi Ikoniya anamuchitira iye umboni wabwino. 3Paulo anafuna kumutenga pa ulendo, kotero anachita mdulidwe chifukwa cha Ayuda amene amakhala mʼderalo pakuti onse amadziwa kuti abambo ake anali Mgriki. 4Pamene amayenda mzinda ndi mzinda, amafotokoza zimene atumwi ndi akulu ampingo ku Yerusalemu anagwirizana kuti anthu azitsatire. 5Kotero mipingo inalimbikitsidwa mʼchikhulupiriro ndipo anthu amachulukirachulukirabe tsiku ndi tsiku.

Paulo Awona Masomphenya

6Paulo ndi anzake anadutsa mayiko a Frugiya ndi Galatiya, Mzimu Woyera atawaletsa kulalikira Mawu a Mulungu ku Asiya. 7Atafika ku malire a Musiya, anayesa kulowa ku Bituniya, koma Mzimu wa Yesu sunawalole kutero. 8Ndipo iwo anadutsa Musiya ndipo anapita ku Trowa. 9Nthawi ya usiku Paulo anaona masomphenya, munthu wa ku Makedoniya atayimirira ndi kumupempha kuti, “Bwerani ku Makedoniya, mudzatithandize.” 10Paulo ataona masomphenyawa, tinakonzeka kupita ku Makedoniya, kutsimikiza kuti Mulungu anatiyitana kuti tikalalikire Uthenga Wabwino.

Lidia Atembenuka Mtima ku Filipi

11Kuchokera ku Trowa tinakwera sitima ya pamadzi kupita ku Samotrake ndipo mmawa mwake tinapitirira mpaka ku Neapoli. 12Kuchokera kumeneko tinapita ku Filipi, boma la Aroma ndiponso mzinda waukulu wa dera la Makedoniya. Tinakhala kumeneko masiku owerengeka.

13Pa tsiku la Sabata tinatuluka mu mzindawo kupita ku mtsinje kumene timayembekezera kukapeza malo opempherera. Tinakhala pansi ndipo tinayamba kuyankhula ndi amayi amene anasonkhana pamenepo. 14Mmodzi wa amayi amene amamvetserawo ndi Lidiya amene amagulitsa nsalu zofiira, wochokera ku mzinda wa Tiyatira, ndipo amapembedza Mulungu. Ambuye anatsekula mtima wake kuti amve mawu a Paulo. 15Iye ndi a mʼbanja lake atabatizidwa, anatiyitana kuti tipite ku nyumba yake. Iye anati, “Ngati mwanditenga ine kukhala wokhulupirira mwa Ambuye, bwerani mudzakhale mʼnyumba mwanga.” Ndipo anatiwumiriza ife kwambiri.

Paulo ndi Sila Mʼndende

16Tsiku lina pamene timapita kumalo wopempherera, tinakumana ndi mtsikana wina amene anali ndi mzimu woyipa umene umanena zamʼtsogolo. Iye amapezera ndalama zambiri ambuye ake pa ulosi wake. 17Mtsikanayu anatsatira Paulo ndi ife, akufuwula kuti, “Anthu awa ndi atumiki a Mulungu Wammwambamwamba, amene akukuwuzani inu njira yachipulumutso.” 18Iye anachita izi masiku ambiri. Kenaka Paulo anavutika mu mtima, natembenuka ndipo anati kwa mzimuwo, “Ndikukulamula iwe mʼdzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa iye!” Nthawi yomweyo mzimuwo unatuluka.

19Pamene ambuye a mtsikana uja anazindikira kuti chiyembekezo chawo chopezera ndalama chatha, anagwira Paulo ndi Sila nawakokera ku bwalo la akulu. 20Anawabweretsa iwo kwa oweruza milandu ndipo anati, “Anthu awa ndi Ayuda, iwo akuvutitsa mu mzinda wathu. 21Ndipo akuphunzitsa miyambo imene ife Aroma sitiloledwa kuyilandira kapena kuyichita.”

22Gulu la anthu linatsutsana ndi Paulo ndi Sila, ndipo woweruza milandu analamula kuti avulidwe ndi kumenyedwa. 23Atawakwapula kwambiri anawaponya mʼndende, nalamula woyangʼanira kuti awasunge mosamalitsa. 24Chifukwa cha mawu amenewa woyangʼanira ndende anakawayika mʼchipinda chamʼkati mwa ndende, nawamangirira miyendo yawo mʼzigologolo.

25Koma pakati pa usiku Paulo ndi Sila ankapemphera ndi kuyimba nyimbo zolemekeza Mulungu, ndipo akayidi ena ankamvetsera. 26Mwadzidzidzi kunachitika chivomerezi champhamvu kotero kuti maziko a ndende anagwedezeka. Nthawi yomweyo zitseko zonse za ndende zinatsekuka, ndipo maunyolo a aliyense anamasuka. 27Woyangʼanira ndende uja atadzuka ku tulo, anaona kuti zitseko za ndende zinali zotsekula, ndipo anasolola lupanga lake nafuna kudzipha chifukwa ankaganiza kuti amʼndende athawa. 28Koma Paulo anafuwula kuti, “Usadzipweteke! Tonse tilipo!”

29Woyangʼanira ndendeyo anayitanitsa nyale, nathamangira mʼkati ndipo anadzigwetsa pa mapazi a Paulo ndi Sila akunjenjemera. 30Iye anawatulutsa kunja ndipo anawafunsa kuti, “Amuna inu, ndichite chiyani kuti ndipulumuke?”

31Iwo anayankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka, iwe ndi a mʼbanja lako.” 32Kenaka analalikira mawu a Ambuye kwa iyeyo ndi onse amene anali mʼnyumba mwake. 33Usiku womwewo woyangʼanira ndendeyo anawatenga nakawatsuka mabala awo; ndipo pomwepo iye ndi a mʼbanja lake anabatizidwa. 34Woyangʼanira ndendeyo anapita nawo ku nyumba yake, nakawapatsa chakudya, ndipo banja lonse linadzazidwa ndi chimwemwe chifukwa anakhulupirira Mulungu.

35Kutacha, woweruza milandu uja anatuma asilikali kwa woyangʼanira ndendeyo kukanena kuti, “Amasuleni anthu aja.” 36Woyangʼanira ndendeyo anawuza Paulo kuti, “Woweruza milandu walamula kuti iwe ndi Sila mumasulidwe. Tsopano muzipita. Pitani mumtendere.”

37Koma Paulo anati kwa asilikaliwo: “Iwo anatikwapula pa gulu la anthu asanatiweruze, ngakhale kuti ndife nzika za Chiroma natiponya mʼndende. Kodi tsopano akufuna kutitulutsa mwamseri? Ayi! Asiyeni abwere okha kuti adzatitulutse.”

38Asilikali aja anakafotokozera woweruza milandu ndipo pamene anamva kuti Paulo ndi Sila anali nzika za Chiroma, anachita mantha. 39Iye anabwera kudzawapepesa ndipo anawatulutsa mʼndende, nawapempha kuti achoke mu mzindawo. 40Paulo ndi Sila atatuluka mʼndende, anapita ku nyumba ya Lidiya, kumene anakumana ndi abale nawalimbikitsa. Kenaka anachoka.