使徒行传 15 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

使徒行传 15:1-41

耶路撒冷会议

1有几个从犹太下来的人教导弟兄们说:“你们若不照着摩西的规条接受割礼,就不能得救。” 2保罗巴拿巴为这件事与他们激烈地辩论,最后大家决定派保罗巴拿巴和几个当地的信徒上耶路撒冷去跟使徒和长老讨论这件事。

3于是教会为他们送行。他们经过腓尼基撒玛利亚,沿途报告外族人悔改信主的消息,弟兄姊妹都大受鼓舞。 4他们到了耶路撒冷,受到教会、使徒和长老的接待,并详述了上帝借他们所做的一切事。 5有几个信了主的法利赛人站起来说:“外族的信徒必须接受割礼,而且还要遵守摩西的律法。”

6使徒和长老们聚集商议这个问题。 7经过许多辩论之后,彼得站起来对大家说:“弟兄们,你们都知道,上帝早已在你们当中拣选我去向外族人传道,让他们也可以听到福音并信主。 8洞悉人心的上帝把圣灵赐给他们,正如赐给我们一样,以表明祂也接纳外族人。 9上帝对他们和我们一视同仁,祂因他们的信心而洁净了他们的心灵。 10现在你们为什么要试探上帝,把我们祖先和我们不能负的重担强加在这些门徒身上? 11我们相信,他们和我们一样都是靠主耶稣的恩典得救。”

12众人都沉默不语,继续听巴拿巴保罗叙述上帝借着他们在外族人中所行的神迹奇事。 13他们报告完了,雅各站起来说:“弟兄们,请听我说。 14刚才西门讲述了上帝当初如何眷顾外族人,从他们当中拣选人归在祂的名下。 15这完全与众先知的话相符,正如圣经上说,

16“‘此后,我要回来重建已倾覆的大卫王朝,

将它从废墟中重建、恢复,

17好叫其余的百姓,

就是凡归在我名下的外族人都寻求主。’

这是上帝说的, 18祂从亘古就显明了这事。

19“所以,我认为不应该为难那些信上帝的外族人。 20我们只须写信吩咐他们远避被偶像玷污之物,不可淫乱,不可吃血和勒死的牲畜。 21因为自古以来,在各城都有人宣讲摩西的律法,每逢安息日,都有人在会堂里诵读。”

给外族信徒的信

22最后,使徒、长老和全教会都决定从他们当中选派代表,随保罗巴拿巴安提阿。他们选了别号巴撒巴犹大西拉,这两位都是教会的领袖。 23他们带去的书信这样说:“安提阿叙利亚基利迦的外族弟兄姊妹,你们的弟兄——众使徒和长老向你们问安!

24“听说有几个人从我们这里去了你们那里,教导你们必须接受割礼并遵守摩西的律法15:24 有古卷无“教导你们必须接受割礼并遵守摩西的律法。”。他们的言论使你们大感困惑。其实我们从来没有授权他们这样做。 25所以我们一致决定选派代表,随我们敬爱的巴拿巴保罗去你们那里。 26他们二人为我们主耶稣基督的缘故已将生死置之度外。 27我们选派犹大西拉两位代表跟他们一起去,向你们报告我们的决定。 28因为圣灵和我们都认为不应把重担加在你们身上。但请务必注意以下几件事, 29要远避祭拜偶像的事,不可吃血,不可吃勒死的牲畜,不可淫乱。你们一一遵守这些事就好了。祝平安!”

30他们奉命下到安提阿,召集众人,交付书信。 31众人读过这封信之后,都因信中劝勉的话而欢喜。 32犹大西拉也是先知,他们讲了许多勉励、坚立弟兄姊妹的话。 33住了些日子后,安提阿的弟兄姊妹以平安的祝福为他们送行,让他们回耶路撒冷复命。 34西拉决定留在那里。15:34 有古卷无“但西拉决定留在那里”。 35保罗巴拿巴则继续留在安提阿,与许多人一起教导、传扬上帝的道。

保罗与巴拿巴分手

36过了一些日子,保罗巴拿巴说:“我们回到曾传过福音的各城镇去探望弟兄姊妹吧,好知道他们的情况。” 37巴拿巴想要带约翰·马可同去, 38保罗坚持不带他同行,因为他在旁非利亚离开了他们,没有和他们一起做工。

39二人激烈地争执起来,僵持不下,只好分道扬镳。巴拿巴约翰·马可一同乘船去塞浦路斯40保罗则选了西拉同行,弟兄姊妹把他们交托在主的恩典中。 41保罗走遍了叙利亚基利迦,巩固当地的各教会。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 15:1-41

Msonkhano wa ku Yerusalemu

1Anthu ena ochokera ku Yudeya anafika ku Antiokeya ndipo amaphunzitsa abale kuti, “Ngati simuchita mdulidwe potsata mwambo wa Mose, simungapulumuke.” 2Zimenezi zinachititsa Paulo ndi Barnaba kuti atsutsane nawo kwambiri. Kotero Paulo ndi Barnaba anasankhidwa pamodzi ndi abale ena kuti apite ku Yerusalemu kukaonana ndi atumwi ndi akulu ampingo kukakambirana za nkhaniyi. 3Mpingo unawaperekeza, ndipo pamene amadutsa ku Foinike ndi Samariya, iwo anafotokoza momwe a mitundu ina anatembenukira mtima. Nkhani imeneyi inakondweretsa kwambiri abale onse. 4Atafika ku Yerusalemu, iwo analandiridwa ndi mpingo, pamodzi ndi atumwi ndiponso akulu ampingo. Paulo ndi Barnaba anawafotokozera zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo.

5Kenaka, okhulupirira ena amene kale anali a gulu la Afarisi anayimirira ndipo anati, “Anthu a mitundu ina ayenera kuchita mdulidwe ndi kusunga malamulo a Mose.”

6Atumwi ndi akulu ampingo anasonkhana kuti akambirane za nkhaniyi. 7Atakambirana kwambiri Petro anayimirira, ndipo anawayankhula nati: “Abale, mukudziwa kuti masiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu kuti anthu a mitundu ina amve kuchokera pakamwa panga mawu a Uthenga Wabwino ndi kukhulupirira. 8Mulungu amene amadziwa mtima wa munthu, Iye anaonetsa kuti anawalandira powapatsa Mzimu Woyera, monga momwe anachita kwa ife. 9Iye sanasiyanitse pakati pa ife ndi iwo, pakuti anayeretsa mitima yawo mwachikhulupiriro. 10Tsopano, chifukwa chiyani mukuyesa Mulungu poyika goli mʼkhosi la ophunzira, limene ngakhale ife kapena makolo athu sangathe kulisenza? 11Osatero! Ife tikukhulupirira kuti tinapulumutsidwa mwachisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu, monga iwonso anachitira.”

12Gulu lonse linakhala chete pamene amamvetsera Barnaba ndi Paulo akuwawuza za zizindikiro zodabwitsa zimene Mulungu anazichita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mwa iwo. 13Iwo atatha kuyankhula, Yakobo anayankhula nati: “Abale, tandimverani. 14Simoni watifotokozera mmene Mulungu poyamba paja anaonetsa kukhudzidwa kwake pomwe anatenga anthu a mitundu ina kukhala ake. 15Mawu a aneneri akuvomereza zimenezi, monga kwalembedwa kuti,

16“ ‘Zitatha izi Ine ndidzabwerera

ndipo ndidzamanganso nyumba ya Davide imene inagwa.

Ndidzakonzanso malo amene anagumuka,

ndi kuyimanganso,

17kuti anthu otsalawo afunefune Ambuye,

ndi anthu onse a mitundu ina amene atchedwa ndi dzina langa,

akutero Ambuye, amene amachita zinthu zimenezi

18zinaululidwa kuyambira kalekale.’

19“Chifukwa chake, ine ndikuweruza kuti tisamavute anthu a mitundu ina amene atembenuka mtima kutsata Mulungu. 20Koma tiwalembere iwo, kuwawuza kuti asadye chakudya choperekedwa kwa mafano, apewenso dama, asadyenso nyama zochita kupotola kapena kudya magazi. 21Pakuti malamulo a Mose akhala akulalikidwa mu mzinda uliwonse, kuyambira kalekale ndipo amawerengedwa mʼMasunagoge tsiku la Sabata.”

Kalata Yopita kwa Anthu a Mitundu ina

22Pamenepo atumwi ndi akulu ampingo, pamodzi ndi mpingo onse, anagwirizana zosankha anthu ena pakati pawo kuti awatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Bamaba. Iwo anasankha Yudasi, wotchedwa Barsaba ndi Sila, anthu awiri amene anali atsogoleri pakati pa abale, 23kuti akapereke kalata yonena kuti,

Kuchokera kwa atumwi ndi akulu ampingo, abale anu,

Kwa anthu a mitundu ina okhulupirira a ku Antiokeya, Siriya ndi Kilikiya:

Tikupereka moni.

24Ife tamva kuti anthu ena ochokera pakati pathu, amene sitinawatume anakusokonezani maganizo ndi kukuvutitsani ndi zimene amakuwuzani. 25Tsono ife tagwirizana kuti, tisankhe anthu ena ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi abale athu okondedwa Paulo ndi Barnaba, 26anthu amene anapereka moyo wawo chifukwa cha dzina la Ambuye athu Yesu Khristu. 27Nʼchifukwa chake, tikutumiza Yudasi ndi Sila kuti adzachitire umboni ndi mawu a pakamwa pawo za zimene ife talemba. 28Pakuti zinakomera Mzimu Woyera ndiponso ife kuti tisakusenzetseni katundu wina, kupatula zoyenera zokhazi: 29Mupewe kudya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano, musadye magazi, kapena nyama yopha mopotola ndiponso musachite dama. Mudzachita bwino mukapewa zimenezi.

Tsalani bwino.

30Anthu aja anatumidwa ndipo anafika ku Antiokeya, kumene anasonkhanitsa mpingo pamodzi napereka kalatayo. 31Anthuwo anawerenga kalatayo ndipo abalewo anakondwa chifukwa cha mawu ake achirimbikitso. 32Yudasi ndi Sila amene analinso aneneri, ananena zambiri zowalimbikitsa ndi kuwapatsa mphamvu abalewo. 33Atakhala kumeneko kwa kanthawi, abale aja anatsanzikana nawo mwamtendere kuti abwerere kwa amene anawatuma. 34Koma Sila anasankha kuti akhale komweko. 35Koma Paulo ndi Barnaba anatsalira ku Antiokeya kumene iwo pamodzi ndi ena ambiri anaphunzitsa ndi kulalikira Mawu a Ambuye.

Paulo Asiyana ndi Barnaba

36Patapita masiku ena Paulo anati kwa Barnaba, “Tiyeni tibwerere kuti tikaone abale ku mizinda yonse imene tinalalika Mawu a Ambuye ndipo tikaone mmene akuchitira.” 37Barnaba anafuna kutenga Yohane, wotchedwanso Marko, kuti apite nawo. 38Koma Paulo anaganiza kuti sichinali cha nzeru kumutenga Yohane chifukwa iye anawathawa ku Pamfiliya ndipo sanapitirire nawo pa ntchito. 39Iwo anatsutsana kwambiri kotero kuti anapatukana. Barnaba anatenga Marko ndipo anakwera sitima ya pamadzi kupita ku Kupro. 40Paulo anasankha Sila. Abale atawapempherera kwa Ambuye kuti alandire chisomo, ananyamuka. 41Iye anadutsa ku Siriya ndi ku Kilikiya kupita akulimbikitsa mipingo.