Yeremia 31 – AKCB & CCL

Akuapem Twi Contemporary Bible

Yeremia 31:1-40

1“Saa bere no,” Awurade na ose, “Mɛyɛ Israel mmusuakuw no nyinaa Nyankopɔn, na wɔbɛyɛ me nkurɔfo.”

2Nea Awurade se ni:

“Nnipa a wotumi gyinaa wɔ afoa ano no

benya adom wɔ nweatam so;

mede ahomegye bɛbrɛ Israel.”

3Awurade daa ne ho adi kyerɛɛ yɛn kan no na ɔkae se,

“Mede ɔdɔ a ɛnsa da adɔ mo

mede adɔe atwe mo.

4Mede mo besi hɔ bio

na wɔbɛsan de wo, Ɔbabun Israel, asi hɔ.

Wobɛfa wʼakasae bio

na woafi adi ne anigyefo akɔsaw.

5Bio, mobɛyɛ bobe nturo

wɔ Samaria nkoko so;

akuafo no bedua

na wɔadi so aba.

6Da bi bɛba a, awɛmfo bɛteɛ mu

wɔ Efraim nkoko so se,

‘Mommra, momma yɛnforo nkɔ Sion,

nkɔ Awurade yɛn Nyankopɔn nkyɛn.’ ”

7Nea Awurade se ni:

“Momfa ahosɛpɛw nto nnwom mma Yakob;

Monteɛ mu mma amanaman mu kannifo.

Momma wɔnte mo ayeyi na monka se,

Awurade, gye wo nkurɔfo,

Israel nkae no.’

8Hwɛ, mede wɔn befi atifi fam asase so aba

na maboa wɔn ano afi nsase ano.

Wɔn mu bi bɛyɛ anifuraefo, mpakye,

apemfo ne mmea a wɔwɔ awoko mu;

dɔm kɛse bɛsan aba.

9Wɔde osu na ɛbɛba;

wɔbɛbɔ mpae bere a mede wɔn resan aba no.

Mede wɔn bɛfa nsuwa ho;

ɔkwan tamaa a wɔrenhintiw wɔ so,

efisɛ mɛyɛ Israel agya,

na Efraim yɛ me babarima piesie.

10“Muntie Awurade asɛm, mo amanaman;

mommɔ no dawuru wɔ mpoano nsase a ɛwɔ akyirikyiri so se,

‘Nea ɔbɔɔ Israel petee no bɛboaboa wɔn ano

na wahwɛ ne nguankuw so sɛ oguanhwɛfo.’

11Na Awurade begyina mu ama Yakob

na wagye wɔn afi wɔn a

wɔwɔ ahoɔden sen wɔn no nsam.

12Wɔbɛba na wɔde ahurusi ateɛ mu wɔ Sion sorɔnsorɔmmea;

wɔbɛsɛpɛw wɔn ho wɔ akyɛde bebrebe a

efi Awurade hɔ mu,

atoko, nsa foforo ne ngo,

nguantenmma ne anantwi.

Wɔbɛyɛ sɛ turo a wɔagugu so nsu yiye,

na wɔrenni awerɛhow bio.

13Afei mmabaa bɛsaw na wɔn ani agye,

mmerante ne nkwakoraa nso ka ho.

Mɛma wɔn awerɛhow adan anigye;

mɛma wɔn ahotɔ ne ahosɛpɛw de asi awerɛhow anan mu.

14Mɛma asɔfo no nea ehia wɔn ama abu so,

na mama mʼakyɛde bebrebe amee me nkurɔfo,”

Awurade, na ose.

15Sɛɛ na Awurade se:

“Wɔte nne bi wɔ Rama,

awerɛhow ne agyaadwotwa bebree,

Rahel resu ne mma

na ɔmpɛ sɛ wɔkyekye ne werɛ,

efisɛ ne mma nni hɔ bio.”

16Sɛɛ na Awurade se:

“Hyɛ wo ho so na woansu,

mia wʼani na woante nusu,

efisɛ wobetua wʼadwumayɛ so ka,”

Awurade na ose.

“Wɔbɛsan afi atamfo no asase so aba.

17Enti anidaso wɔ hɔ ma wo daakye.”

Awurade na ose.

Wo mma bɛsan aba wɔn ankasa asase so.

18“Ampa ara mate sɛ Efraim resu se,

‘Woteɛteɛɛ me so sɛ nantwi ba a nʼani yɛ den,

na manya ahohyɛso.

Gye me bio, na mɛsan aba,

efisɛ wo ne Awurade, me Nyankopɔn.

19Meman akyi no,

minyaa adwensakra;

na akyiri a minyaa ntease no,

mebɔɔ me koko so.

Mʼanim guu ase na mefɛree,

efisɛ me mmabun mu animguase da so so me.’

20Efraim nyɛ me babarima dɔfo,

ɔba a ɔsɔ mʼani ana?

Ɛwɔ mu, metaa kasa tia no de,

nanso meda so kae no.

Enti me koma pere hwehwɛ no;

mewɔ ayamhyehye ma no,”

sɛɛ na Awurade se.

21“Momfa agyiraehyɛde nsisi akwan ho;

munsisi akwankyerɛ afadum.

Monhyɛ ɔtempɔn no nsow,

ɔkwan a monam so ba.

San wʼakyi, Ɔbabun Israel,

san bra wo nkurow so.

22Wubekyinkyin akosi da bɛn,

Ɔbabea Israel sesafo?

Awurade bɛyɛ ade foforo wɔ asase so,

ɔbea bɛbɔ ɔbarima ho ban.”

23Sɛɛ na Asafo Awurade, Israel Nyankopɔn no se: “Sɛ mesan de wɔn fi nnommum mu ba a, nnipa a wɔwɔ Yuda asase ne nkurow so bɛsan aka saa nsɛm yi se, ‘Awurade nhyira wo, wo yiyeyɛ kuropɔn ne bepɔw kronkron.’ 24Nnipa bɛbɔ mu atena ase wɔ Yuda ne ne nkurow nyinaa so, akuafo ne wɔn a wɔde wɔn nguankuw nenam. 25Mɛma nea wabrɛ no anya ahoɔden foforo, na nea watɔ piti no nso mɛma no amee.”

26Minyanee, na mehwɛɛ me ho hyiae. Medaa hatee.

27“Nna bi reba,” Awurade na ose, “A mede nnipa mma ne mmoa mma bedua Israel ne Yuda fi. 28Sɛnea mehwɛ ma wotutui, wodwiriwii, wobubui, wɔsɛee na wɔde amanehunu bae no, saa ara na mɛhwɛ ama wɔasi na wɔadua,” sɛnea Awurade se ni. 29Saa nna no mu, nnipa renka bio se,

“ ‘Agyanom adi bobe nwennaa,

na mma se afem.’

30Mmom, obiara bewu wɔ ɔno ara bɔne ho; nea obedi bobe nwennaa no ɔno na ne se bɛfem.

31“Bere no reba,” Awurade na ose,

“a me ne Israelfi

ne Yudafi bɛyɛ apam foforo.

32Ɛrenyɛ sɛ apam a

me ne wɔn agyanom yɛe no

bere a misoo wɔn nsa,

dii wɔn anim fii Misraim,

esiane sɛ wobuu mʼapam so,

wɔ bere a na meyɛ okunu ma wɔn no,”

Awurade na ose.

33“Eyi ne apam a me ne Israelfi bɛyɛ saa bere no akyi,”

Awurade na ose.

“Mede me mmara bɛhyɛ wɔn adwene mu,

na makyerɛw wɔ wɔn koma so.

Mɛyɛ wɔn Nyankopɔn,

na wɔbɛyɛ me nkurɔfo.

34Na obiara renkyerɛkyerɛ ne yɔnko bio,

anaa ne nua se, ‘Hu Awurade,’

Efisɛ, wɔn nyinaa behu me,

efi wɔn mu akumaa so, kosi ɔkɛse so,”

Sɛnea Awurade se ni.

“Na mede wɔn amumɔyɛ bɛkyɛ wɔn,

na merenkae wɔn bɔne bio.”

35Sɛɛ na Awurade se,

nea ɔma owia hyerɛn adekyee,

na ɔhyɛ ɔsram ne nsoromma

sɛ wɔnhyerɛn anadwo;

nea ɔkanyan ɛpo

ma nʼasorɔkye bobɔ mu,

Asafo Awurade ne ne din.

36“Saa ahyɛde yi twa mu mʼani so a,”

Awurade na ose,

“ɛno ansa na Israel begyae

ɔmanyɛ wɔ mʼanim.”

37Sɛɛ na Awurade se:

“Sɛ wobetumi asusuw wim ntrɛwmu

na wɔatumi ahwehwɛ asase ase fapem mu a

ɛno de, mɛpo Israel asefo nyinaa,

esiane nea wɔayɛ nyinaa nti,”

Awurade na ose.

38“Nna no reba,” Awurade na ose, “a wɔbɛkyekye kuropɔn yi bio ama me, fi Hananel abantenten kosi Twɔtwɔw so Pon. 39Wɔbɛtwe susuhama no mu, afi hɔ de akosi Gareb koko so, na akɔntɔn akɔ Goa. 40Obon a wɔtow afunu ne nsõ gu mu no nyinaa ne asase a ɛkɔ Kidron bon mu wɔ apuei fam, kosi apɔnkɔ pon no twɔtwɔw so bɛyɛ kronkron ama Awurade. Wɔrentutu na wɔrensɛe kuropɔn no da.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 31:1-40

1“Pa nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “Ndidzakhala Mulungu wa mafuko onse a Israeli, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”

2Yehova akuti,

“Anthu amene anapulumuka ku nkhondo

ndinawakomera mtima mʼchipululu;

pamene Aisraeli ankafuna kupumula.”

3Ine ndinawaonekera ndili chapatali ndipo ndinati,

“Ine ndakukondani ndi chikondi chopanda malire.

Nʼchifukwa chake ndipitiriza kukukondani.

4Ndidzakusamaliraninso, inu anthu a Israeli;

mudzasangalala poyimba tizitoliro tanu,

ndipo mudzapita kukavina nawo

anthu ovina mwachimwemwe.

5Mudzalimanso minda ya mpesa

pa mapiri a Samariya;

alimi adzadzala mphesa

ndipo adzadya zipatso zake.

6Lidzafika tsiku pamene alonda adzafuwula

pa mapiri a Efereimu nati,

‘Tiyeni tipite ku Ziyoni,

kwa Yehova Mulungu wathu.’ ”

7Yehova akuti,

“Imbani mosangalala chifukwa cha Yakobo,

fuwulani chifukwa cha mtundu wopambana mitundu yonse.

Matamando anu amveke, ndipo munene kuti,

‘Yehova wapulumutsa anthu ake

otsala a Israeli.’

8Taonani, ndidzabwera nawo kuchokera ku dziko la kumpoto,

ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.

Anthu osaona, olumala, amayi oyembekezera

ndi amene ali pa nthawi yawo yochira adzabwera nawo pamodzi.

Chidzakhala chikhamu cha anthu obwerera kuno.

9Adzabwera akulira;

koma Ine ndikuwatonthoza mtima, ndidzawaperekeza.

Ndidzawatsogolera ku mitsinje yamadzi

mʼnjira yosalala mmene sadzapunthwamo.

Chifukwa ndine abambo ake a Israeli,

ndipo Efereimu ndi mwana wanga woyamba.

10“Imvani mawu a Yehova inu anthu a mitundu ina;

lalikirani mawuwa kwa anthu a mayiko akutali a mʼmbali mwa nyanja;

‘Iye amene anabalalitsa Israeli adzawasonkhanitsanso

ndipo adzayangʼanira nkhosa zake ngati mʼbusa.’

11Pakuti Yehova wawombola fuko la Yakobo

anawapulumutsa mʼdzanja la anthu owaposa mphamvu.

12Anthuwo adzabwera akuyimba mofuwula pa mapiri a Ziyoni;

adzasangalala ndi zinthu zabwino zochokera kwa Yehova.

Zinthu zabwinozo ndi izi: tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta,

ana ankhosa ndi ana angʼombe.

Iwo adzakhala ngati munda wothiriridwa bwino,

ndipo sadzamvanso chisoni.

13Pamenepo anamwali adzavina ndi kusangalala.

Anyamata ndi okalamba nawonso adzasangalala.

Kulira kwawo ndidzakusandutsa chisangalalo;

ndidzawasangalatsa nʼkuchotsa chisoni chawo.

14Ansembe ndidzawadyetsa chakudya chabwino,

ndipo anthu anga adzakhuta ndi zabwino zanga,”

akutero Yehova.

15Yehova akuti,

“Kulira kukumveka ku Rama,

kulira kwakukulu,

Rakele akulirira ana ake.

Sakutonthozeka

chifukwa ana akewo palibe.”

16Yehova akuti,

“Leka kulira

ndi kukhetsa misozi

pakuti udzalandira mphotho ya ntchito yako,”

akutero Yehova.

“Iwo adzabwerako ku dziko la adani.

17Tsono chiyembekezo chilipo pa zamʼtsogolo,”

akutero Yehova.

“Ana ako adzabwerera ku dziko lawo.

18“Ndithu ndamva Efereimu akubuwula kuti,

‘Ife tinali ngati ana angʼombe osamva.

Koma inu mwatiphunzitsa kumvera.

Mutibweze kuti tithe kubwerera,

chifukwa ndinu Yehova Mulungu wanga.

19Popeza tatembenuka mtima,

ndiye tikumva chisoni;

popeza tazindikira

ndiye tikudziguguda pachifukwa.

Tachita manyazi ndipo tanyazitsidwa

chifukwa tinachimwa paubwana wathu.’

20Kodi Efereimu si mwana wanga wokondedwa,

mwana amene Ine ndimakondwera naye?

Ngakhale nthawi zambiri ndimamudzudzula,

ndimamukumbukirabe.

Kotero mtima wanga ukumufunabe;

ndimamumvera chifundo chachikulu kwambiri,”

akutero Yehova.

21“Muyike zizindikiro za mu msewu;

muyimike zikwangwani.

Yangʼanitsitsani msewuwo,

njira imene mukuyendamo.

Bwerera, iwe namwali wa Israeli,

bwerera ku mizinda yako ija.

22Udzakhala jenkha mpaka liti,

iwe mwana wa mkazi wosakhulupirika?

Yehova walenga chinthu chatsopano pa dziko lapansi; mkazi ndiye tsopano aziteteza mwamuna.”

23Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Ndikadzabwera nawo anthuwa kuchokera ku ukapolo, anthu a mʼdziko la Yuda ndi amene akukhala mʼmizinda yake adzayankhulanso mawu akuti, ‘Yehova akudalitse, iwe malo achilungamo, iwe phiri lopatulika.’ 24Anthu adzakhala ku Yuda ndi ku mizinda yake pamodzi ndi alimi ndi oweta nkhosa. 25Ndidzatsitsimutsa anthu otopa ndipo ndidzadyetsa anthu anjala.”

26Pamenepo ndinadzuka nʼkuyangʼana uku ndi uku. Tulo tanga tinali tokoma.

27“Masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzachulukitsa anthu pamodzi ndi ziweto mʼdziko la Israeli ndi la Yuda. 28Monga momwe ndinasamalira powazula, powagwetsa, powagumula, powawononga ndi powachita zoyipa, momwemonso ndidzasamala powamanga ndi powadzala” akutero Yehova. 29“Mʼmasiku amenewo anthu sadzanenanso kuti,

“Makolo adya mphesa zosapsa,

koma mano a ana ndiye achita dziru.

30Mʼmalo wake, munthu aliyense adzafa chifukwa cha tchimo lake. Iye amene adzadye mphesa zosapsazo ndiye amene mano ake adzachite dziru.”

31“Masiku akubwera,” akutero Yehova,

“pamene ndidzachita pangano latsopano

ndi Aisraeli

ndiponso nyumba ya Yuda.

32Silidzakhala ngati pangano

limene ndinachita ndi makolo awo

pamene ndinawagwira padzanja

nʼkuwatulutsa ku Igupto;

chifukwa anaphwanya pangano langa,

ngakhale ndinali mwamuna wawo,”

akutero Yehova.

33“Ili ndi pangano limene ndidzachita ndi Aisraeli

atapita masiku amenewo,” akutero Yehova.

“Ndidzayika lamulo langa mʼmitima mwawo

ndi kulilemba mʼmaganizo mwawo.

Ine ndidzakhala Mulungu wawo

ndipo iwo adzakhala anthu anga.

34Sipadzafunikanso kuti wina aphunzitse mnzake,

kapena munthu wina kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, ‘Mudziwe Yehova,’

chifukwa onse adzandidziwa Ine,

kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,”

akutero Yehova.

“Ndidzawakhululukira zoyipa zawo

ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”

35Yehova akuti,

Iye amene amakhazikitsa dzuwa

kuti liziwala masana,

amene amalamula kuti mwezi ndi nyenyezi

ziziwala usiku,

amene amavundula nyanja

kuti mafunde akokome,

dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:

36Ngati zimenezi zilekeka pamaso panga, akutero Yehova, pamenepo padzakhala pamathero a fuko la Israeli pamaso panga.

37Yehova akuti,

“Ndidzataya fuko la Israeli chifukwa cha machimo awo.

Ngati patapezeka munthu

amene angathe kupima zakuthambo

nʼkufufuza maziko a dziko lapansi.”

38“Taonani masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene mzinda wa Yehova udzamangidwanso kuyambira ku Nsanja ya Hananeli mpaka ku Chipata cha Ngodya. 39Malire ake adzayambira pamenepo kupita ku phiri la Garebu, nʼkudzakhota kuloza ku Gowa. 40Chigwa chonse mʼmene amatayiramo mitembo ndi phulusa, ndiponso minda yonse kuyambira ku Chigwa cha Kidroni mpaka ku ngodya ya Chipata cha Akavalo mbali ya kummawa, adzakhala malo opatulika a Yehova. Mzindawu sadzawuzulanso kapena kuwuwononga.”