Псалми 27 – NSP & CCL

New Serbian Translation

Псалми 27:1-14

Псалам 27

Давидов.

1Господ ми је светлост и спасење,

кога да се бојим?

Господ је моја тврђава,

од кога да страхујем?

2Кад на мене навале опаки

да ми тело ждеру,

моји противници и душмани,

они се спотичу и падају.

3Па да и војска крене против мене,

моје се срце неће уплашити.

Да се и рат поведе против мене,

и тада ћу бити пун поуздања.

4Једно тражим од Господа

и за тиме жудим:

да пребивам у Дому Господњем

кроз све дане свог живота;

да посматрам лепоту Господњу,

и савет потражим у његовом Дому.

5Јер он ме склања под сеницу своју

у дан невоље,

скрива ме у скровишту свог шатора,

на стену ме подиже.

6Узвисила се сада моја глава

изнад мојих душмана око мене:

у његовом шатору жртве ћу хвале принети,

певаћу Господу, песмом га славити.

7Чуј, Господе, глас мој,

смилуј ми се, услиши ме!

8Моје ме срце упућује к теби:

„Тражи лице моје.“

Твоје лице тражим, Господе.

9Не криј своје лице од мене,

не изручи гневу слугу свога,

ти си увек био моја помоћ,

не напуштај ме, не остављај ме,

Боже спасења мога.

10Ако ме напусте и отац и мајка,

Господ ће ме примити.

11Учи ме, Господе, своме путу,

равном ме стазом води,

ради мрзитеља мојих.

12Не предај ме вољи мога противника,

јер лажни сведоци устају на мене,

који одишу насиљем.

13Ја верујем да ћу видети доброту Господњу

у земљи живих.

14Чекај на Господа:

буди јак и одважна срца,

и чекај на Господа.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 27:1-14

Salimo 27

Salimo la Davide.

1Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa;

ndidzaopa yani?

Yehova ndi linga la moyo wanga;

ndidzachita mantha ndi yani?

2Pamene anthu oyipa abwera kudzalimbana nane

kudzadya mnofu wanga,

pamene adani anga ndi achiwembu andithira nkhondo,

iwo adzapunthwa ndi kugwa.

3Ngakhale gulu lankhondo lindizinge,

mtima wanga sudzaopa.

Ngakhale nkhondo itayambika kulimbana nane,

ngakhale nthawi imeneyo, ine ndidzalimbika mtima.

4Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova,

ichi ndi chimene ndidzachifunafuna:

kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova

masiku onse a moyo wanga,

ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova,

ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.

5Pakuti pa tsiku la msautso

Iye adzanditeteza mʼmalo ake okhalamo;

adzandibisa mʼkati mwa Nyumba yake

ndi kukhazika ine pamwamba pa thanthwe.

6Kotero mutu wanga udzakwezedwa

kuposa adani anga amene andizungulira;

pa Nyumba yake ndidzapereka nsembe ndi mfuwu wachimwemwe;

ndidzayimba nyimbo kwa Yehova.

7Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu Yehova

mundichitire chifundo ndipo mundiyankhe.

8Mtima wanga ukuti kwa Inu, “Funafuna nkhope yake!”

Nkhope yanu Yehova ndidzayifunafuna.

9Musandibisire nkhope yanu,

musamubweze mtumiki wanu mwamkwiyo;

mwakhala muli thandizo langa.

Musandikane kapena kunditaya,

Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.

10Ngakhale abambo ndi amayi anga anditaya

Yehova adzandisamala.

11Phunzitseni njira yanu Inu Yehova,

munditsogolere mʼnjira yowongoka

chifukwa cha ondizunza.

12Musandipereke ku zokhumba za adani anga,

pakuti mboni zambiri zauka kutsutsana nane

ndipo zikundiopseza.

13Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi;

ndidzaona ubwino wa Yehova

mʼdziko la anthu amoyo.

14Dikirani pa Yehova;

khalani anyonga ndipo limbani mtima

nimudikire Yehova.