Revelation 6 – NIVUK & CCL

New International Version – UK

Revelation 6:1-17

The seals

1I watched as the Lamb opened the first of the seven seals. Then I heard one of the four living creatures say in a voice like thunder, ‘Come!’ 2I looked, and there before me was a white horse! Its rider held a bow, and he was given a crown, and he rode out as a conqueror bent on conquest.

3When the Lamb opened the second seal, I heard the second living creature say, ‘Come!’ 4Then another horse came out, a fiery red one. Its rider was given power to take peace from the earth and to make people kill each other. To him was given a large sword.

5When the Lamb opened the third seal, I heard the third living creature say, ‘Come!’ I looked, and there before me was a black horse! Its rider was holding a pair of scales in his hand. 6Then I heard what sounded like a voice among the four living creatures, saying, ‘A kilogram of wheat for a day’s wages,6:6 Greek a denarius and three kilograms of barley for a day’s wages,6:6 Greek a denarius and do not damage the oil and the wine!’

7When the Lamb opened the fourth seal, I heard the voice of the fourth living creature say, ‘Come!’ 8I looked, and there before me was a pale horse! Its rider was named Death, and Hades was following close behind him. They were given power over a quarter of the earth to kill by sword, famine and plague, and by the wild beasts of the earth.

9When he opened the fifth seal, I saw under the altar the souls of those who had been slain because of the word of God and the testimony they had maintained. 10They called out in a loud voice, ‘How long, Sovereign Lord, holy and true, until you judge the inhabitants of the earth and avenge our blood?’ 11Then each of them was given a white robe, and they were told to wait a little longer, until the full number of their fellow servants, their brothers and sisters,6:11 The Greek word for brothers and sisters (adelphoi) refers here to believers, both men and women, as part of God’s family; also in 12:10; 19:10. were killed just as they had been.

12I watched as he opened the sixth seal. There was a great earthquake. The sun turned black like sackcloth made of goat hair, the whole moon turned blood red, 13and the stars in the sky fell to earth, as figs drop from a fig-tree when shaken by a strong wind. 14The heavens receded like a scroll being rolled up, and every mountain and island was removed from its place.

15Then the kings of the earth, the princes, the generals, the rich, the mighty, and everyone else, both slave and free, hid in caves and among the rocks of the mountains. 16They called to the mountains and the rocks, ‘Fall on us and hide us6:16 See Hosea 10:8. from the face of him who sits on the throne and from the wrath of the Lamb! 17For the great day of their6:17 Some manuscripts his wrath has come, and who can withstand it?’

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chivumbulutso 6:1-17

Kutsekulidwa kwa Zimatiro Zisanu ndi Chimodzi

1Ndinaona pamene Mwana Wankhosa anatsekula chomatira choyamba cha zomatira zisanu ndi ziwiri zija. Ndipo ndinamva chimodzi mwa zamoyo zinayi zija chikunena liwu lomveka ngati bingu kuti, “Bwera!” 2Nditayangʼana patsogolo pake ndinaona kavalo woyera! Wokwerapo wake anali ndi uta ndipo anapatsidwa chipewa chaufumu, ndipo anatuluka kupita kukagonjetsa anthu ena.

3Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachiwiri, ndinamva chamoyo chachiwiri chija chikuti, “Bwera!” 4Pamenepo kavalo wina wofiira anatulukira. Wokwerapo wake anapatsidwa mphamvu yochotsa mtendere pa dziko lapansi ndi kuchititsa anthu kuti aziphana wina ndi mnzake. Iyeyu anapatsidwa lupanga lalikulu.

5Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu chikuti, “Bwera!” Nditayangʼana patsogolo panga ndinaona kavalo wakuda! Wokwerapo wake anali ndi masikelo awiri mʼmanja mwake. 6Ndinamva ngati liwu kuchokera pakati pa zamoyo zinayi zija likuti, “Kilogalamu imodzi ya tirigu mtengo ndi malipiro a tsiku limodzi ndipo makilogalamu atatu a barele mtengo wake ndi malipiro a tsiku limodzi koma usawononge mafuta ndi vinyo!”

7Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachinayi, ndinamva chamoyo chachinayi chija chikunena kuti, “Bwera!” 8Nditayangʼana patsogolo panga ndinaona kavalo wotuwa! Wokwerapo wake dzina lake linali Imfa ndipo Hade inali kumutsatira pambuyo pake. Anapatsidwa ulamuliro pa gawo limodzi la magawo anayi a dziko lapansi kuti aphe ndi lupanga, njala, mliri, ndi zirombo zakuthengo za mʼdziko lapansi.

9Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachisanu, ndinaona kunsi kwa guwa lansembe kunali mizimu ya anthu amene anaphedwa chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi chifukwa chochitira umboni. 10Iwo anafuwula kuti, “Mudzawaleka mpaka liti, Inu Ambuye wamkulu, woyera ndi woona, osawaweruza anthu okhala mʼdziko lapansi ndi kulipsira magazi athu?” 11Pamenepo aliyense wa anthuwo anapatsidwa mwinjiro woyera ndipo anawuzidwa kuti adikire pangʼono kufikira chiwerengero cha anzawo ndi abale awo amene anayeneranso kuphedwa ngati iwo, chitakwanira.

12Ndinayangʼanitsitsa pamene ankatsekula chomatira chachisanu ndi chimodzi. Ndipo panachitika chivomerezi champhamvu. Dzuwa linada ngati chiguduli chopanga ndi bweya wambuzi wakuda. Mwezi wonse unafiira ngati magazi, 13ndipo nyenyezi zakuthambo zinagwa pa dziko lapansi ngati muja zimagwera nkhuyu zotsalira mu mtengo mphepo yamphamvu ikawomba. 14Thambo linachoka ngati amayalulira mphasa ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zinachotsedwa pa malo pake.

15Kenaka, mafumu a pa dziko lapansi, ana a mafumu, atsogoleri a ankhondo, olemera, amphamvu, kapolo aliyense, ndi mfulu aliyense anakabisala kumapanga ndi pakati pa matanthwe a ku mapiri. 16Iwo anafuwulira mapiri ndi matanthwe kuti, “Tigwereni ndi kutivundikira kuti asatione wokhala pa mpando waufumuyo ndi kupulumuka ku mkwiyo wa Mwana Wankhosa! 17Pakuti tsiku lalikulu la mkwiyo wawo lafika ndipo ndi ndani angathe kulimbapo?”