Revelation 5 – NIVUK & CCL

New International Version – UK

Revelation 5:1-14

The scroll and the Lamb

1Then I saw in the right hand of him who sat on the throne a scroll with writing on both sides and sealed with seven seals. 2And I saw a mighty angel proclaiming in a loud voice, ‘Who is worthy to break the seals and open the scroll?’ 3But no-one in heaven or on earth or under the earth could open the scroll or even look inside it. 4I wept and wept because no-one was found who was worthy to open the scroll or look inside. 5Then one of the elders said to me, ‘Do not weep! See, the Lion of the tribe of Judah, the Root of David, has triumphed. He is able to open the scroll and its seven seals.’

6Then I saw a Lamb, looking as if it had been slain, standing at the centre of the throne, encircled by the four living creatures and the elders. The Lamb had seven horns and seven eyes, which are the seven spirits5:6 That is, the sevenfold Spirit of God sent out into all the earth. 7He went and took the scroll from the right hand of him who sat on the throne. 8And when he had taken it, the four living creatures and the twenty-four elders fell down before the Lamb. Each one had a harp and they were holding golden bowls full of incense, which are the prayers of God’s people. 9And they sang a new song, saying:

‘You are worthy to take the scroll

and to open its seals,

because you were slain,

and with your blood you purchased for God

persons from every tribe and language and people and nation.

10You have made them to be a kingdom and priests to serve our God,

and they will reign5:10 Some manuscripts they reign on the earth.’

11Then I looked and heard the voice of many angels, numbering thousands upon thousands, and ten thousand times ten thousand. They encircled the throne and the living creatures and the elders. 12In a loud voice they were saying:

‘Worthy is the Lamb, who was slain,

to receive power and wealth and wisdom and strength

and honour and glory and praise!’

13Then I heard every creature in heaven and on earth and under the earth and on the sea, and all that is in them, saying:

‘To him who sits on the throne and to the Lamb

be praise and honour and glory and power,

for ever and ever!’

14The four living creatures said, ‘Amen’, and the elders fell down and worshipped.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chivumbulutso 5:1-14

Buku la Mwana Wankhosa

1Kenaka ndinaona buku mʼdzanja la wokhala pa mpando waufumu uja. Bukulo linali lolembedwa mbali zonse ndipo linali lomatidwa ndi zomatira zisanu ndi ziwiri. 2Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu akulengeza ndi mawu okweza kuti, “Ndani ali woyenera kumatula zomatira ndi kufutukula bukuli?” 3Koma panalibe ndi mmodzi yemwe kumwamba kapena pa dziko lapansi kapena kunsi kwa dziko lapansi woti afutukule bukulo kapena kuona zamʼkati mwake. 4Ndinalira kwambiri chifukwa panalibe amene anapezeka woyenera kufutukula bukuli kapena kuona zamʼkati mwake. 5Tsono mmodzi mwa akuluakulu aja anati kwa ine, “Usalire! Taona, Mkango wa fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana. Iye angathe kufutukula bukuli ndi kumatula zomatira zisanu ndi ziwirizo.”

6Kenaka ndinaona Mwana Wankhosa akuoneka ngati wophedwa atayimirira pakatikati pa mpando waufumu uja ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Mwana Wankhosayo anali ndi nyanga zisanu ndi ziwiri ndi maso asanu ndi awiri omwe ndi Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu yomwe anayitumiza ku dziko lonse lapansi. 7Iye anabwera natenga buku lija limene linali mʼdzanja lamanja la wokhala pa mpando waufumuyo. 8Ndipo atalitenga, zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu 24 aja anadzigwetsa pansi pamaso pa Mwana Wankhosa. Aliyense wa akuluakuluwo anali ndi zeze ndiponso mbale zagolide zodzaza ndi lubani. Lubaniyo ndi mapemphero a oyera mtima. 9Ndipo ankayimba nyimbo yatsopano yakuti,

“Inu ndinu woyenera kulandira bukuli

ndi kumatula zomatira zake,

chifukwa munaphedwa,

ndipo magazi anu munagulira Mulungu

anthu a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse, ndi mtundu uliwonse.

10Inu munawasandutsa kukhala mtundu waufumu ndi ansembe otumikira Mulungu,

ndipo adzalamulira dziko lapansi.”

11Kenaka nditayangʼananso ndinamva mawu a angelo ambiri, miyandamiyanda kuchulukitsa ndi miyandamiyanda. Anazungulira mpando waufumu pamodzi ndi zamoyo zija ndi akuluakulu aja. 12Ndipo angelowo anayimba ndi mawu ofuwula akuti,

“Mwana Wankhosa amene anaphedwayu

ndi woyenera kulandira ulamuliro, chuma, nzeru, mphamvu, ulemu,

ulemerero ndi mayamiko.”

13Kenaka ndinamva mawu a cholengedwa chilichonse kumwamba, pa dziko lapansi, kunsi kwa dziko lapansi, pa nyanja ndi zonse zili mʼmenemo zikuyimba kuti,

“Kwa wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa,

kukhale mayamiko, ulemu, ulemerero ndi mphamvu

mpaka muyaya!”

14Zamoyo zinayi zija zinati: “Ameni,” ndipo akuluakulu aja anadzigwetsa pansi napembedza.