Psalm 16 – NIRV & CCL

New International Reader’s Version

Psalm 16:1-11

Psalm 16

A miktam of David.

1My God, keep me safe.

I go to you for safety.

2I say to the Lord, “You are my Lord.

Without you, I don’t have anything that is good.”

3I say about God’s people who live in our land, “They are the noble ones.

I take great delight in them.”

4Those who run after other gods

will suffer more and more.

I will not pour out offerings of blood to those gods.

My lips will not speak their names.

5Lord, you alone are everything I need.

You make my life secure.

6I am very pleased with what you have given me.

I am very happy with what I’ve received from you.

7I will praise the Lord. He gives me good advice.

Even at night my heart teaches me.

8I keep my eyes always on the Lord.

He is at my right hand.

So I will always be secure.

9So my heart is glad. Joy is on my tongue.

My body also will be secure.

10You will not leave me in the place of the dead.

You will not let your faithful one rot away.

11You always show me the path of life.

You will fill me with joy when I am with you.

You will make me happy forever at your right hand.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 16:1-11

Salimo 16

Mikitamu ya Davide.

1Ndisungeni Inu Mulungu,

pakuti ine ndimathawira kwa Inu.

2Ndinati kwa Yehova, “Inu ndinu Ambuye anga;

popanda Inu, ine ndilibe chinthu chinanso chabwino.”

3Kunena za oyera mtima amene ali pa dziko,

amenewa ndi olemekezeka, amene ndimakondwera nawo.

4Anthu amene amathamangira kwa milungu ina

mavuto awo adzachulukadi.

Ine sindidzathira nawo nsembe zawo zamagazi

kapena kutchula mayina awo ndi pakamwa panga.

5Yehova, Inu mwandipatsa cholowa changa ndi chikho changa;

mwateteza kolimba gawo langa.

6Malire a malo anga akhala pabwino;

ndithudi, ine ndili cholowa chokondweretsa kwambiri.

7Ine ndidzatamanda Yehova amene amandipatsa uphungu;

ngakhale usiku mtima wanga umandilangiza.

8Ndayika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.

Popeza Iyeyo ali kudzanja langa lamanja,

sindidzagwedezeka.

9Choncho mtima wanga ndi wosangalala ndipo pakamwa panga pakukondwera;

thupi langanso lidzakhala pabwino,

10chifukwa Inu simudzandisiya ku manda,

simudzalola kuti woyera wanu avunde.

11Inu mwandidziwitsa njira ya moyo;

mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu,

ndidzasangalala mpaka muyaya pa dzanja lanu lamanja.