Nehemiah 10 – KJV & CCL

King James Version

Nehemiah 10:1-39

1Now those that sealed were, Nehemiah, the Tirshatha, the son of Hachaliah, and Zidkijah,10.1 those…: Heb. at the sealings10.1 the Tirshatha: or, the governor 2Seraiah, Azariah, Jeremiah, 3Pashur, Amariah, Malchijah, 4Hattush, Shebaniah, Malluch, 5Harim, Meremoth, Obadiah, 6Daniel, Ginnethon, Baruch, 7Meshullam, Abijah, Mijamin, 8Maaziah, Bilgai, Shemaiah: these were the priests. 9And the Levites: both Jeshua the son of Azaniah, Binnui of the sons of Henadad, Kadmiel; 10And their brethren, Shebaniah, Hodijah, Kelita, Pelaiah, Hanan, 11Micha, Rehob, Hashabiah, 12Zaccur, Sherebiah, Shebaniah, 13Hodijah, Bani, Beninu. 14The chief of the people; Parosh, Pahath-moab, Elam, Zatthu, Bani, 15Bunni, Azgad, Bebai, 16Adonijah, Bigvai, Adin, 17Ater, Hizkijah, Azzur, 18Hodijah, Hashum, Bezai, 19Hariph, Anathoth, Nebai, 20Magpiash, Meshullam, Hezir, 21Meshezabeel, Zadok, Jaddua, 22Pelatiah, Hanan, Anaiah, 23Hoshea, Hananiah, Hashub, 24Hallohesh, Pileha, Shobek, 25Rehum, Hashabnah, Maaseiah, 26And Ahijah, Hanan, Anan, 27Malluch, Harim, Baanah.

28¶ And the rest of the people, the priests, the Levites, the porters, the singers, the Nethinims, and all they that had separated themselves from the people of the lands unto the law of God, their wives, their sons, and their daughters, every one having knowledge, and having understanding; 29They clave to their brethren, their nobles, and entered into a curse, and into an oath, to walk in God’s law, which was given by Moses the servant of God, and to observe and do all the commandments of the LORD our Lord, and his judgments and his statutes;10.29 by: Heb. by the hand of 30And that we would not give our daughters unto the people of the land, nor take their daughters for our sons: 31And if the people of the land bring ware or any victuals on the sabbath day to sell, that we would not buy it of them on the sabbath, or on the holy day: and that we would leave the seventh year, and the exaction of every debt.10.31 every…: Heb. every hand

32Also we made ordinances for us, to charge ourselves yearly with the third part of a shekel for the service of the house of our God; 33For the shewbread, and for the continual meat offering, and for the continual burnt offering, of the sabbaths, of the new moons, for the set feasts, and for the holy things, and for the sin offerings to make an atonement for Israel, and for all the work of the house of our God. 34And we cast the lots among the priests, the Levites, and the people, for the wood offering, to bring it into the house of our God, after the houses of our fathers, at times appointed year by year, to burn upon the altar of the LORD our God, as it is written in the law: 35And to bring the firstfruits of our ground, and the firstfruits of all fruit of all trees, year by year, unto the house of the LORD: 36Also the firstborn of our sons, and of our cattle, as it is written in the law, and the firstlings of our herds and of our flocks, to bring to the house of our God, unto the priests that minister in the house of our God: 37And that we should bring the firstfruits of our dough, and our offerings, and the fruit of all manner of trees, of wine and of oil, unto the priests, to the chambers of the house of our God; and the tithes of our ground unto the Levites, that the same Levites might have the tithes in all the cities of our tillage. 38And the priest the son of Aaron shall be with the Levites, when the Levites take tithes: and the Levites shall bring up the tithe of the tithes unto the house of our God, to the chambers, into the treasure house. 39For the children of Israel and the children of Levi shall bring the offering of the corn, of the new wine, and the oil, unto the chambers, where are the vessels of the sanctuary, and the priests that minister, and the porters, and the singers: and we will not forsake the house of our God.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nehemiya 10:1-39

1Amene anasindikiza chidindo anali awa:

Nehemiya, bwanamkubwa uja, mwana wa Hakaliya.

Zedekiya, 2Seraya, Azariya, Yeremiya

3Pasuri, Amariya, Malikiya,

4Hatusi, Sebaniya, Maluki,

5Harimu, Meremoti, Obadiya,

6Danieli, Ginetoni, Baruki,

7Mesulamu, Abiya, Miyamini

8Maziya, Biligai ndi Semaya

Awa anali ansembe.

9Alevi anali awa:

Yesuwa mwana wa Azaniya, Binuyi wa fuko la Henadadi, Kadimieli,

10ndi abale awo awa: Sebaniya,

Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani,

11Mika, Rehobu, Hasabiya,

12Zakuri, Serebiya, Sebaniya,

13Hodiya, Bani ndi Beninu.

14Atsogoleri a anthu anali awa:

Parosi, Pahati-Mowabu, Elamu, Zatu, Bani,

15Buni, Azigadi, Bebai,

16Adoniya, Bigivai, Adini,

17Ateri, Hezekiya, Azuri,

18Hodiya, Hasumu, Bezayi

19Harifu, Anatoti, Nebayi,

20Magipiyasi, Mesulamu, Heziri

21Mesezabeli, Zadoki, Yaduwa

22Pelatiya, Hanani, Ananiya,

23Hoseya, Hananiya, Hasubu

24Halohesi, Piliha, Sobeki,

25Rehumu, Hasabiya, Maaseya,

26Ahiya, Hanani, Anani,

27Maluki, Harimu ndi Baana.

28Ife otsalafe, ndiye kuti ansembe, Alevi, alonda a ku Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu, onse amene anadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina kuti atsate malamulo a Yehova, pamodzi ndi akazi athu, ana athu ndi onse amene ali ndi nzeru, 29tikuphatikana ndi abale athu wolemekezeka, ndipo tikulonjeza molumbira kuti tidzayenda motsata malamulo a Mulungu amene anapereka kudzera mwa Mose mtumiki wa Mulungu. Tilonjeza kumvera ndi kutsata bwino mawu onse, miyambo yonse ndi malangizo onse a Yehova. Yehova atilange ngati sitidzachita zimenezi.

30“Ife tikulonjeza kuti sitidzapereka ana athu aakazi kuti akwatiwe ndi amuna a mayiko ena kapena kutenga ana awo aakazi kuti akwatiwe ndi ana athu aamuna.

31“Ngati anthu a mitundu ina abwera ndi zinthu za malonda, monga tirigu, kudzagulitsa pa tsiku la Sabata, sitidzawagula pa tsiku la Sabata kapena pa tsiku lina lililonse loyera. Pa chaka chilichonse cha chisanu ndi chiwiri tidzagoneka munda wosawulima ndipo tidzafafaniza ngongole zonse.

32“Tikulonjezanso molumbira kuti chaka ndi chaka tizipereka magalamu anayi a siliva kuti zithandize ntchito ya ku Nyumba ya Mulungu wathu. 33Ndalamayi izithandiza kulipirira buledi wa pa tebulo, chopereka cha chakudya cha nthawi zonse, zopereka zopsereza za nthawi zonse, zopereka za pa tsiku la Sabata, za pachikondwerero cha Mwezi Watsopano, za pa masiku a chikondwerero osankhika, zopereka za zinthu zopatulika, zopereka za nsembe yopepesera machimo a Aisraeli ndi ntchito ina iliyonse ya ku Nyumba ya Mulungu.

34“Ife ansembe, Alevi ndi anthu onse, tachita maere kuti tidziwe pamene banja lathu lililonse lidzabweretsa ku nyumba ya Mulungu wathu pa nthawi yoyikika ya chaka zopereka za nkhuni zoyaka pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo.”

35“Tilonjezanso kuti tidzabwera ndi zipatso zoyamba kucha za mʼminda yathu ndi zipatso zoyamba kucha za mtengo uliwonse wa zipatso chaka ndi chaka kuti tidzapereke ku Nyumba ya Mulungu wathu.”

36“Tidzabweranso nawo ku Nyumba ya Mulungu, kwa ansembe amene amatumikira ku Nyumba ya Mulungu ana athu aamuna oyamba kubadwa ndi ana angʼombe oyamba kubadwa monga zalembedwera mu Malamulo. Tidzaperekanso ana oyamba kubadwa a ziweto zathu ndi ana ankhosa oyamba kubadwa.”

37“Ndiponso ku zipinda za Nyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe tidzaperekanso mtanda wathu wa buledi wa ufa ndi mphatso zina monga zipatso za mtengo uliwonse, vinyo ndi mafuta. Tidzaperekanso kwa alevi chakhumi cha mbewu zathu pakuti alevi ndiwo amasonkhanitsa chakhumi mʼmidzi yathu yonse. 38Wansembe, mdzukulu wa Aaroni azikhala pamodzi ndi Alevi pamene akulandira chakhumi. Ndipo Alevi azibwera ndi chakhumicho ku nyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda zosungiramo chuma.” 39Choncho Israeli, kuphatikiza zidzukulu za Alevi, azipititsa zopereka za tirigu, vinyo ndi mafuta ku zipinda zosungiramo katundu wopatulika, komanso kokhala ansembe amene akutumikira pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu ndi anthu oyimba nyimbo.

“Kwambiri ife sitidzaleka kusamala Nyumba ya Mulungu.”