Yobu 36 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 36:1-33

1Ndipo Elihu anapitirira kuyankhula nati:

2“Mundilole pangʼono pokha ndipo ndikuonetsani

kuti zilipo zambiri zoti ziyankhulidwe mʼmalo mwa Mulungu.

3Nzeru zanga ndimazitenga kutali;

ndidzaonetsa kulungama kwa Mlengi wanga.

4Ndithudi mawu anga si abodza;

wanzeru zangwiro ali ndi inu.

5“Mulungu ndi wamphamvu, koma sanyoza anthu;

Iye ndi wamphamvu, ndipo ndi wokhazikika pa cholinga chake.

6Salola oyipa kuti akhalebe ndi moyo

koma amapereka ufulu kwa anthu osautsidwa.

7Iye saleka kuyangʼanira anthu olungama;

amawayika kuti alamulire pamodzi ndi mafumu

ndipo amawalemekeza mpaka muyaya.

8Koma ngati anthu amangidwa ndi unyolo,

ndipo akondwa ndi zingwe zamasautso,

9Iye amawafotokozera zomwe anachita,

kuti iwo anachimwa modzikuza.

10Mulungu amawatsekula makutu kuti amve malangizo ake

ndipo amawalamula kuti alape zoyipa zawo.

11Ngati iwo amumvera ndi kumutumikira,

adzatsiriza masiku a moyo wawo mwamtendere,

adzatsiriza zaka zawo mosangalala.

12Koma ngati samvera,

adzaphedwa ndi lupanga

ndipo adzafa osadziwa kanthu.

13“Anthu osapembedza amasunga mkwiyo mu mtima mwawo;

akawalanga, safuwulira kwa Iye kupempha thandizo.

14Amafa akanali achinyamata,

pakati pa amuna achiwerewere a kumalo azipembedzo.

15Koma ovutika, Iye amawapulumutsa pa mavuto awo;

Mulungu amawayankhula mʼmasautso awowo.

16“Iye akukukopani inu kuti muchoke mʼmasautso,

kuti mupite ku malo aakulu kumene kulibe chokutchingani,

kumalo a mpumulo kumene kuli chakudya chabwino kwambiri.

17Koma tsopano inu mwapezeka wopalamula chifukwa cha kuyipa kwanu;

chiweruzo ndi chilungamo chakugwerani.

18Muchenjere kuti wina asakukopeni ndi chuma;

musalole kuti chiphuphu chachikulu chikusocheretseni.

19Kodi chuma chanu

kapena mphamvu zanu zonse

zingakusungeni kotero kuti simungakhale pa masautso?

20Musalakalake kuti usiku ubwere,

pakuti ndiyo nthawi imene anthu adzawonongeka.

21Muchenjere kuti musatembenukire ku uchimo,

chifukwa uchimowo ndiwo unabweretsa kuzunzika kwanu.

22“Taonani, Mulungu ndi wamkulu ndiponso ndi wamphamvu.

Kodi ndi mphunzitsi uti amene angafanane naye?

23Kodi ndani amene anamuwuzapo Mulungu zoti achite,

kapena kumuwuza kuti, ‘Inu mwachita chinthu cholakwa?’

24Kumbukirani kutamanda ntchito zake

zimene anthu amaziyamika mʼnyimbo.

25Anthu onse amaziona ntchitozo;

anthuwo amaziona ali kutali.

26Ndithudi, Mulungu ndi wamkulu, sitimudziwa nʼpangʼono pomwe!

Chiwerengero cha zaka zake nʼchosadziwika.

27“Mulungu ndiye amakweza timadontho tamadzi kuthambo,

timene timasungunuka nʼkukhala mvula;

28mitambo imagwetsa mvulayo

ndipo mvulayo imavumbwa pa anthu mokwanira.

29Kodi ndani amene angadziwe momwe mitambo imayendera,

momwe Iye amabangulira kuchokera kumalo ake?

30Taonani momwe amawalitsira zingʼaningʼani pa malo ake onse,

zimafika ngakhale pansi pa nyanja.

31Umu ndi mmene Iye amalamulira mitundu ya anthu

ndi kuwapatsa chakudya chochuluka.

32Amadzaza manja ake ndi zingʼaningʼani,

ndipo amazilamulira kuti zigwe pamalo pamene Iye akufuna.

33Mabingu ake amalengeza za kubwera kwa mvula yamkuntho;

ngʼombe nazo zimalengeza za kubwera kwake.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

約伯記 36:1-33

1以利戶又說:

2「再給我片刻,容我講明,

我還有話替上帝說。

3我要旁徵博引,

證明我的創造主公義。

4我的話絕非虛言,

知識全備者在你身旁。

5「上帝有大能,但不藐視人,

祂無所不知。

6祂不容惡人活命,

祂為窮苦人伸冤。

7祂時時看顧義人,

使他們與君王同坐寶座,

永遠受尊崇。

8他們若被鎖鏈捆綁,

被苦難的繩索纏住,

9祂就會指明他們的所作所為,

讓他們知道自己狂妄的罪愆。

10祂開啟他們的耳朵,使之受教,

督促他們離開罪惡。

11他們若聽從、事奉祂,

就可一生幸福,安享天年。

12否則,他們必死於刀下,

在無知中滅亡。

13不信上帝的人心存憤怒,

被上帝捆綁也不求救。

14他們盛年喪命,

與廟中的男妓一同夭亡。

15上帝藉苦難拯救受苦的人,

藉患難開通他們的耳朵。

16祂也要引領你脫離困境,

進入廣闊自由之地,

使你享受滿桌佳餚。

17「但惡人應受的審判落在你身上,

你難逃審判和懲罰。

18當心,不可因憤怒而嘲罵,

不可因贖金大就偏離正道。

19難道你呼求、使出渾身力氣,

就能脫離困境嗎?

20不要渴望黑夜來臨——

就是眾民被毀滅的時候。

21當心,不可轉向罪惡,

因你喜歡罪惡勝於苦難。

22看啊,上帝的能力無以倫比。

誰能像祂那樣賜人教誨?

23誰能為祂指定道路?

誰能說祂行事不義?

24人們都歌唱祂的作為,

你也要記得頌揚。

25祂的作為,萬民都已看見,

世人從遠處目睹。

26我們無法明白上帝的偉大,

祂的年歲無法數算。

27祂吸取水滴,

使之在雲霧中化為雨,

28從雲端沛然降下,

滋潤人間。

29誰能明白雲層的鋪展,

及祂幔幕發出的雷聲?

30祂在四圍鋪展閃電,

照亮大海的深處。

31祂藉此治理萬民,

賜下豐富的食物。

32祂手握閃電,

令它射向目標。

33雷聲顯明祂的作為,

就連牲畜也能察覺。