Yobu 27 – CCL & NIRV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 27:1-23

1Ndipo Yobu anapitiriza kuyankhula kwake:

2“Ndithu pali Mulungu wamoyo, amene wakana kundiweruza molungama,

Wamphamvuzonse, amene wawawitsa mtima wanga,

3nthawi zonse pamene ndili ndi moyo,

mpweya wa Mulungu uli mʼmphuno mwanga,

4pakamwa panga sipadzatuluka mawu oyipa,

lilime langa silidzayankhula zachinyengo.

5Sindidzavomereza kuti inu mukunena zoona;

mpaka imfa yanga, sindidzataya ungwiro wanga.

6Ndidzasunga chilungamo changa ndipo sindidzalola kuti chindichokere;

chikumbumtima changa sichidzanditsutsa nthawi yonse ya moyo wanga.

7“Mdani wanga akhale ngati woyipa,

wondiwukira akhale ngati munthu wosalungama!

8Nanga chiyembekezo cha munthu wosapembedza nʼchiyani pamene aphedwa,

pamene Mulungu achotsa moyo wake?

9Kodi Mulungu amamva kulira kwake

pamene zovuta zamugwera?

10Kodi adzapeza chikondwerero mwa Wamphamvuzonse?

Kodi adzapemphera kwa Mulungu nthawi zonse?

11“Ndidzakuphunzitsani za mphamvu ya Mulungu ndipo

sindidzabisa njira za Wamphamvuzonse.

12Inu mwadzionera nokha zonsezi.

Nanga bwanji mukuyankhula zopanda pake?

13“Pano pali chilango chimene Mulungu amasungira woyipa,

cholowa chimene munthu wankhanza amalandira kuchokera kwa Wamphamvuzonse.

14Angakhale ana ake achuluke chotani adzaphedwa ndi lupanga ndipo

zidzukulu zake zidzasowa zakudya.

15Amene adzatsalireko adzafa ndi mliri,

ndipo akazi awo amasiye sadzawalira.

16Ngakhale aunjike siliva ngati fumbi,

ndi kukundika zovala ngati mchenga,

17zimene wasungazo wolungama ndiye adzavale,

ndipo anthu osalakwa ndiwo adzagawane siliva wakeyo.

18Nyumba imene akuyimanga ili ngati mokhala kadziwotche,

ili ngati msasa umene mlonda amamanga.

19Amapita kokagona ali wolemera koma kutha kwake nʼkomweko;

akatsekula maso ake, chuma chake chonse chapita.

20Zoopsa zimamukokolola ngati madzi achigumula;

mphepo yamkuntho imamunyamula usiku.

21Mphepo ya kummawa imamuwulutsa ndipo iye saonekanso ndipo

imamuchotsa pamalo pake.

22Imakuntha pa iye osamuchitira chisoni,

pamene akuyesa kuthawa mphamvu zake mwaliwiro.

23Mphepoyo imamuwomba ndithu

ndipo kuchokera pamalo pake imamuopseza.”

New International Reader’s Version

Job 27:1-23

Job’s Final Reply to His Friends

1Job continued to speak. He said,

2“God hasn’t treated me fairly.

The Mighty One has made my life bitter.

You can be sure that God lives.

And here’s something else you can be sure of.

3As long as I have life

and God gives me breath,

4my mouth won’t say evil things.

My lips won’t tell lies.

5I’ll never admit you people are right.

Until I die, I’ll say I’m telling the truth.

6I’ll continue to say I’m right.

I’ll never let go of that.

I won’t blame myself as long as I live.

7“May my enemies suffer like sinful people!

May my attackers be punished like those who aren’t fair!

8What hope do ungodly people have when their lives are cut short?

What hope do they have when God takes away their lives?

9God won’t listen to their cry

when trouble comes on them.

10They won’t take delight in the Mighty One.

They’ll never call out to God.

11“I’ll teach all of you about God’s power.

I won’t hide the things the Mighty One does.

12You have seen those things yourselves.

So why do you continue your useless talk?

13“Here’s what God does to sinful people.

Here’s what those who are mean receive from the Mighty One.

14All their children will be killed by swords.

They’ll never have enough to eat.

15A plague will kill those who are left alive.

The widows of sinful men

won’t even weep over their own children.

16Sinners might store up silver like dust

and clothes like piles of clay.

17But people who do what is right will wear those clothes.

People who haven’t done anything wrong

will divide up that silver.

18The house an evil person builds is like a moth’s cocoon.

It’s like a hut that’s made by someone on guard duty.

19Sinful people lie down wealthy, but their wealth is taken away.

When they open their eyes, everything is gone.

20Terrors sweep over them like a flood.

A storm takes them away during the night.

21The east wind carries them off, and they are gone.

It sweeps them out of their houses.

22It blows against them without mercy.

They try to escape from its power.

23It claps its hands and makes fun of them.

It hisses them out of their houses.”