Yobu 14 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 14:1-22

1“Munthu wobadwa mwa amayi

amakhala masiku owerengeka ndipo ndi odzaza ndi mavuto okhaokha.

2Amaphuka ngati duwa ndipo kenaka amafota;

amathawa ngati mthunzi ndipo sakhalitsa.

3Kodi munthu wotereyo nʼkumuyangʼanitsitsa?

Kodi mungamubweretse pamaso panu kuti mumuzenge mlandu?

4Ndani angatulutse chabwino mʼchoyipa?

Palibe ndi mmodzi yemwe!

5Masiku a munthu ndi odziwikiratu;

munakhazikitsa chiwerengero cha miyezi yake

ndipo munamulembera malire amene sangathe kuwalumpha.

6Choncho Inu mumufulatire ndipo mumuleke apumule

kufikira atakondwera nawo moyo ngati munthu waganyu.

7“Mtengo uli nacho chiyembekezo:

ngati wadulidwa, udzaphukiranso

ndipo nthambi zake sizidzaleka kuphukira.

8Mizu yake ingathe kukalamba mʼnthaka

ndipo chitsa chake nʼkuwola pa dothi,

9koma pamene chinyontho chafika udzaphukira

ndipo udzaphuka nthambi ngati mtengo wanthete.

10Koma munthu amafa nayikidwa mʼmanda,

amapuma mpweya wotsiriza ndipo kutha kwake nʼkomweko.

11Monga madzi amaphwera mʼnyanja

kapena monga mtsinje umaphwera nuwuma,

12momwemonso munthu amagona ndipo sadzukanso;

mpaka zamlengalenga zidzathe, anthu sadzauka

kapena kudzutsidwa ku tulo tawo.

13“Aa, Inu mukanangondibisa mʼmanda

ndi kundiphimba kuti ndisaoneke mpaka mkwiyo wanu utapita!

Achikhala munandiyikira nthawi,

kuti pambuyo pake mundikumbukirenso.

14Munthu akafa, kodi adzakhalanso ndi moyo?

Masiku anga onse a moyo wovutikawu

ndidzadikira mpaka itafika nthawi yomasulidwa.

15Inu mudzandiyitane ndipo ndidzakuyankhani;

inu mudzafunitsitsa kuona cholengedwa chimene munachipanga ndi manja anu.

16Ndithudi pamenepo mudzayangʼana mayendedwe anga

koma simudzalondola tchimo langa.

17Zolakwa zanga zidzakulungidwa mʼthumba;

inu mudzaphimba tchimo langa.

18“Koma monga phiri limakokolokera ndi kuswekasweka

ndipo monga thanthwe limasunthira kuchoka pa malo ake,

19monganso madzi oyenda amaperesera miyala

ndipo madzi othamanga amakokololera nthaka,

momwemonso Inu mumawononga chiyembekezo cha munthu.

20Inu mumamugonjetsa kamodzinʼkamodzi ndipo munthuyo nʼkutheratu;

Inu mumasintha maonekedwe a nkhope yake ndipo mumamutaya kutali.

21Ana ake akamalemekezedwa, iyeyo sazidziwa zimenezo;

akamachititsidwa manyazi iye saziona zimenezo.

22Iye amangomva zowawa za mʼthupi lake

ndipo amangodzilirira yekha mwini wakeyo.”