Yobu 13 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 13:1-28

1“Ndaziona ndi maso anga zonsezi,

ndazimva ndi makutu anga ndipo ndazimvetsa.

2Zimene inu mukudziwa, inenso ndimazidziwa;

ineyo sindine munthu wamba kwa inu.

3Koma ine ndikulakalaka nditayankhula ndi Wamphamvuzonse

ndi kukamba mlandu wanga ndi Mulungu.

4Koma inu mukundipaka mabodza;

nonsenu ndinu asingʼanga opanda phindu!

5Achikhala munangokhala chete nonsenu!

Apo mukanachita zanzeru.

6Tsopano imvani kudzikanira kwanga;

imvani kudandaula kwa pakamwa panga.

7Kodi inu mudzayankhula moyipa kuyankhulira Mulungu?

Kodi mudzayankhulira Iyeyo mwachinyengo?

8Kodi mudzaonetsa kuti Iyeyo ngokondera?

Kodi inu mudzamuteteza Mulungu pa mlandu wake?

9Mulungu atayangʼanitsitsa, inu nʼkukupezani wosalakwa?

Kodi inu mungamunamize Iye monga momwe munganamizire munthu?

10Ndithudi, Iye angathe kukudzudzulani

ngati muchita zokondera mseri.

11Kodi ulemerero wake sungakuopseni?

Kodi kuopsa kwake sikungakuchititseni mantha?

12Mawu anu anzeru ali ngati miyambi yopanda tanthauzo;

mawu anu odzitchinjirizira ali ngati mpanda wadothi.

13“Khalani chete ndipo ndilekeni ndiyankhule;

tsono zimene zindichitikire zichitike.

14Chifukwa chiyani ndikuyika moyo wanga pa chiswe

ndi kutengera mʼmanja moyo wangawu?

15Ngakhale Iye andiphe, komabe ndidzamukhulupirira;

ndithu, ndidzafotokoza mlandu wanga pamaso pake.

16Zoonadi, ichi ndiye chidzakhala chipulumutso changa

pakuti palibe munthu wosapembedza amene angafike pamaso pake!

17Mvetserani mosamala mawu anga;

makutu anu amve zimene ndikunena.

18Pakuti tsopano ndawukonzekera mlandu wanga,

ndikudziwa ndipo adzandipeza wolungama.

19Kodi alipo wina amene angatsutsane nane?

ngati zili choncho, ndidzakhala chete ndi kufa.

20“Inu Mulungu, ndipatseni zinthu ziwiri izi,

ndipo pamenepo ine sindidzakubisalirani:

21Muchotse dzanja lanu pa ine,

ndipo muleke kundichititsa mantha ndi kuopsa kwanuko.

22Tsono muyitane ndipo ndidzayankha,

kapena mulole kuti ine ndiyankhule ndipo Inu muyankhe.

23Kodi zolakwa zanga ndi zingati ndipo machimo anga ndi angati?

Wonetseni kulakwa kwanga ndi machimo anga.

24Chifukwa chiyani mukundifulatira

ndi kundiyesa ine mdani wanu?

25Kodi mudzazunza tsamba lowuluka ndi mphepo?

Kodi mudzathamangitsa mungu wowuma?

26Pakuti Inu mwalemba zinthu zowawa zonditsutsa nazo

ndipo mukundipaka machimo a pa ubwana wanga.

27Inu mwamanga miyendo yanga ndi maunyolo.

Mumayangʼanitsitsa mayendedwe anga onse

poyika zizindikiro pamene mapazi anga apondapo.

28“Motero munthu amatha ngati chinthu chofumbwa,

ngati chovala chodyedwa ndi njenjete.