Yesaya 55 – CCL & NIVUK

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 55:1-13

Kuyitanidwa kwa Womva Ludzu

1“Bwerani, inu nonse amene muli ndi ludzu,

bwerani madzi alipo;

ndipo inu amene mulibe ndalama

bwerani, mudzagule chakudya kuti mudye!

Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka

osalipira ndalama, osalipira chilichonse.

2Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene samadya,

ndipo mukuwononga malipiro anu pa zinthu zimene sizikhutitsa?

Tamverani, mvetsetsani zimene ndikunena kuti mudye zimene zili zabwino;

ndipo mudzisangalatse.

3Tcherani makutu ndipo mubwere kwa Ine;

mvereni Ine, kuti mukhale ndi moyo.

Ndidzachita nanu pangano losatha,

chikondi changa chija chosasinthika ndi chodalirika ndinalonjeza Davide.

4Taonani, ine ndamusankha kuti akhale mboni yanga kwa mitundu ya anthu,

kuti akhale mtsogoleri ndi wolamulira mitundu ya anthu.

5Ndithu inu mudzayitanitsa mitundu ya anthu imene simuyidziwa,

ndipo mitundu ya anthu imene sikudziwani idzabwera ndi liwiro kwa inu.

Izi zidzatero chifukwa Yehova Mulungu wanu,

Woyerayo wa Israeli,

wakuvekani ulemerero.”

6Funafunani Yehova pamene Iye akupezeka.

Mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi.

7Woyipa asiye makhalidwe ake oyipa,

ndipo wosalungama asinthe maganizo ake oyipa.

Abwerere kwa Yehova, ndipo adzamuchitira chifundo,

ndi kwa Mulungu wathu, pakuti adzamukhululukira koposa.

8“Pakuti maganizo anga siwofanana ndi maganizo anu,

ngakhale njira zanu si njira zanga,”

akutero Yehova.

9“Monga momwe mlengalenga muli kutali ndi dziko lapansi,

momwemonso zochita zanga nʼzolekana kutali ndi zochita zanu,

ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.

10Monga mvula ndi chisanu chowundana

zimatsika kuchokera kumwamba,

ndipo sizibwerera komweko

koma zimathirira dziko lapansi.

Ndipo zimameretsa ndi kukulitsa zomera

kenaka nʼkupatsa mlimi mbewu ndi chakudya.

11Ndi mmenenso amachitira mawu ochokera mʼkamwa mwanga.

Sadzabwerera kwa Ine kopanda phindu lake,

koma adzachita zonse zimene ndifuna,

ndipo adzakwaniritsa cholinga chimene ndinawatumira.

12Inu mudzatuluka mu mzindawo mwachimwemwe

ndipo adzakutsogolerani mwamtendere;

mapiri ndi zitunda

zidzakuyimbirani nyimbo,

ndipo mitengo yonse yamʼthengo

idzakuwombereni mʼmanja.

13Mʼmalo mʼmene tsopano muli mitengo ya minga mudzamera mitengo ya payini,

ndipo kumene kuli mkandankhuku kudzamera mchisu.

Zimenezi zidzakhala chikumbutso cha Yehova,

ngati chizindikiro chamuyaya,

chimene sichidzafafanizika konse.”

New International Version – UK

Isaiah 55:1-13

Invitation to the thirsty

1‘Come, all you who are thirsty,

come to the waters;

and you who have no money,

come, buy and eat!

Come, buy wine and milk

without money and without cost.

2Why spend money on what is not bread,

and your labour on what does not satisfy?

Listen, listen to me, and eat what is good,

and you will delight in the richest of fare.

3Give ear and come to me;

listen, that you may live.

I will make an everlasting covenant with you,

my faithful love promised to David.

4See, I have made him a witness to the peoples,

a ruler and commander of the peoples.

5Surely you will summon nations you know not,

and nations you do not know will come running to you,

because of the Lord your God,

the Holy One of Israel,

for he has endowed you with splendour.’

6Seek the Lord while he may be found;

call on him while he is near.

7Let the wicked forsake their ways

and the unrighteous their thoughts.

Let them turn to the Lord, and he will have mercy on them,

and to our God, for he will freely pardon.

8‘For my thoughts are not your thoughts,

neither are your ways my ways,’

declares the Lord.

9‘As the heavens are higher than the earth,

so are my ways higher than your ways

and my thoughts than your thoughts.

10As the rain and the snow

come down from heaven,

and do not return to it

without watering the earth

and making it bud and flourish,

so that it yields seed for the sower and bread for the eater,

11so is my word that goes out from my mouth:

it will not return to me empty,

but will accomplish what I desire

and achieve the purpose for which I sent it.

12You will go out in joy

and be led forth in peace;

the mountains and hills

will burst into song before you,

and all the trees of the field

will clap their hands.

13Instead of the thorn-bush will grow the juniper,

and instead of briers the myrtle will grow.

This will be for the Lord’s renown,

for an everlasting sign,

that will endure for ever.’