Yesaya 38 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 38:1-22

Kudwala kwa Hezekiya

1Nthawi imeneyo Mfumu Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya mwana wa Amozi anapita kukamuona ndipo anati “Yehova akuti: Konza bwino nyumba yako, pakuti ukufa; suchira.”

2Hezekiya anatembenuka nayangʼana kukhoma, napemphera kwa Yehova kuti, 3“Inu Yehova, kumbukirani momwe ndayendera pamaso panu mokhulupirika ndi modzipereka ndipo ndakhala ndikuchita zabwino pamaso panu.” Ndipo Hezekiya analira mosweka mtima.

4Ndipo Yehova analamula Yesaya kuti: 5“Pita kwa Hezekiya ndipo ukamuwuze kuti, ‘Yehova, Mulungu wa kholo lake Davide akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona; ndidzakuwonjezera zaka 15 pa moyo wako. 6Ndipo ndidzakupulumutsa, iwe pamodzi ndi mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya, Ine ndidzawuteteza mzindawu.

7“ ‘Ichi ndi chizindikiro cha Yehova kwa iwe kutsimikiza kuti Yehova adzachita zimene walonjeza: 8Chithunzithunzi chimene dzuwa likuchititsa pa makwerero a Ahazi ndidzachibweza mʼmbuyo makwerero khumi.’ ” Ndipo chithunzithunzi chinabwerera mʼmbuyo makwerero khumi.

9Ndakatulo ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda imene analemba atadwala ndi kuchira:

10Ine ndinaganiza kuti

ndidzapita ku dziko la akufa

pamene moyo ukukoma.

11Ndinaganiza kuti, “Sindidzaonanso Yehova,

mʼdziko la anthu amoyo,

sindidzaonanso mtundu wa anthu

kapena kukhala pamodzi ndi amene amakhala pa dziko lapansi lino.

12Nyumba yanga yasasuka

ndipo yachotsedwa.

Ngati tenti ya mʼbusa mwapindapinda moyo wanga,

ngati munthu wowomba nsalu;

kuyambira usana mpaka usiku mwakhala mukundisiya.

13Ndinkalira kupempha chithandizo usiku wonse mpaka mmawa;

koma Inu Yehova munaphwanya mafupa anga ngati mkango,

ndipo mwakhala mukundisiya.

14Ndinkalira ngati namzeze kapena chumba,

ndinkabuwula ngati nkhunda yodandaula.

Maso anga anatopa nʼkuyangʼana mlengalenga.

Inu Ambuye, ine ndili mʼmavuto bwerani mudzandithandize!”

15Koma ine ndinganene chiyani?

Yehova wayankhula nane, ndipo Iye ndiye wachita zimenezi.

Chifukwa cha kuwawa kwa mtima wanga,

ine ndidzayenda modzichepetsa masiku amoyo wanga onse.

16Ambuye, masiku anga ali mʼmanja mwanu.

Mzimu wanga upeza moyo mwa Inu.

Munandichiritsa ndi

kundikhalitsa ndi moyo.

17Ndithudi, ine ndinamva zowawa zotere

kuti ndikhale ndi moyo;

Inu munandisunga

kuti ndisapite ku dzenje la chiwonongeko

chifukwa mwakhululukira

machimo anga onse.

18Pakuti akumanda sangathe kukutamandani,

akufa sangayimbe nyimbo yokutamandani.

Iwo amene akutsikira ku dzenje

sangakukhulupirireni.

19Amoyo, amoyo okha ndiwo amakutamandani,

monga mmene ndikuchitira ine lero lino;

abambo amawuza ana awo za

kukhulupirika kwanu.

20Yehova watipulumutsa.

Tiyeni tiyimbe ndi zoyimbira za zingwe

masiku onse a moyo wathu

mʼNyumba ya Yehova.

21Yesaya anati, “Anthu atenge mʼbulu wankhunyu ndipo apake pa chithupsacho ndipo Hezekiya adzachira.”

22Hezekiya nʼkuti atafunsa kuti, “Kodi chizindikiro chako nʼchiyani chotsimikiza kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova?”

Bibelen på hverdagsdansk

Esajasʼ Bog 38:1-22

Kong Hizkijas sygdom og helbredelse

1Senere blev Hizkija alvorligt syg og lå for døden. Da kom profeten Esajas til ham og sagde: „Gør dig klar til at dø, for Herren siger, du ikke bliver rask igen.”

2Esajas gik derefter sin vej, og Hizkija vendte ansigtet mod væggen. 3„Åh, Herre,” tryglede han, „husk dog på, hvordan jeg altid har bestræbt mig på at adlyde dig og behage dig i alt, hvad jeg har foretaget mig.” Og han græd højt.

4-5„Gå tilbage til Hizkija,” sagde Herren til Esajas. „Sig til ham: Herren, din forfar Davids Gud, har hørt din bøn og set dine tårer. Jeg vil give dig endnu 15 år at leve i, 6og jeg vil frelse både dig og Jerusalem fra assyrerkongen!”

21Esajas sagde så til kongens tjenere, at de skulle lægge et figenplaster på det syge sted, for så ville kongen blive rask.38,21 De to vers er flyttet op, hvor de ifølge 2.Kong. 20,7-8 oprindeligt hørte hjemme. 22Hizkija spurgte Esajas: „Hvilket tegn får jeg på, at Herren virkelig vil helbrede mig, så jeg kan gå op til Herrens hus?”