Yesaya 18 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 18:1-7

Za Kulangidwa kwa Kusi

1Tsoka kwa anthu a ku Kusi.

Kumeneko kumamveka mkokomo wa mapiko a dzombe.

2Dziko limenelo limatumiza akazembe pa mtsinje wa Nailo,

mʼmabwato amabango amene amayandama pa madzi,

ndikunena kuti, “Pitani, inu amithenga aliwiro,

kwa mtundu wa anthu ataliatali a khungu losalala,

ndi woopedwa ndi anthu.

Akazembe anatumidwa ku dziko la anthu amphamvu ndi logonjetsa anthu ena.

Dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje.”

3Inu nonse anthu a pa dziko lonse,

inu amene mumakhala pa dziko lapansi,

pamene mbendera yakwezedwa pa mapiri

yangʼanani,

ndipo pamene lipenga lilira

mumvere.

4Pakuti Yehova akunena kwa ine kuti,

“Ndili chikhalire ku malo anga kuno, ndidzakhala chete, ndi kumangoyangʼana,

monga momwe dzuwa limawalira nthawi yotentha,

monganso momwe mame amagwera usiku pa nthawi yotentha yokolola.”

5Pakuti, anthu asanayambe kukolola, maluwa atayoyoka

ndiponso mphesa zitayamba kupsa,

Iye adzadula mphukira ndi mipeni yosadzira,

ndipo adzadula ndi kuchotsa nthambi zotambalala.

6Mitembo ya anthu ankhondo adzasiyira mbalame zamʼmapiri zodya nyama

ndiponso zirombo zakuthengo;

mbalame zidzadya mitemboyo nthawi yonse ya chilimwe,

ndipo zirombo zidzayidya pa nthawi yonse yachisanu.

7Pa nthawi imeneyo anthu adzabwera ndi mphatso kwa Yehova Wamphamvuzonse,

zochokera kwa anthu ataliatali ndi osalala,

kuchokera kwa mtundu wa anthu woopedwa ndi anthu apafupi ndi akutali omwe,

mtundu wa anthu amphamvu ndi a chiyankhulo chachilendo,

anthu amene dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje.

Adzabwera nazo mphatso ku Phiri la Ziyoni, ku malo a Dzina la Yehova Wamphamvuzonse.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以賽亞書 18:1-7

關於古實的預言

1古實河那邊、翅膀刷刷作響之地有禍了!

2那裡派出的使節乘蘆葦船行駛在水面上。

迅捷的使節啊,

去身材高大、皮膚光滑、

遠近畏懼、強盛兇悍、

國土河流縱橫的民族那裡吧!

3世上的一切居民啊,

山上豎立旗幟的時候,

你們要看;

號角吹響的時候,你們要聽。

4耶和華對我說:

「我要從我的居所靜靜地觀看,

無聲無息,就像豔陽下的熱氣,

又如夏收時節的露水。」

5在收割之前,

在花已凋謝、葡萄將熟之時,

耶和華必毀滅古實人,

就像用刀削去葡萄樹的嫩枝,

砍掉蔓延的枝條。

6他們的屍首成了山間鷙鳥和田野走獸的食物,

夏天被鷙鳥啄食,

冬天被走獸吞噬。

7那時,這身材高大、皮膚光滑、

遠近畏懼、強盛兇悍、

國土河流縱橫的民族,

必帶著禮物來到錫安山,

獻給萬軍之耶和華。