Yesaya 16 – CCL & CARSA

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 16:1-14

1Anthu a ku Mowabu

atumiza mphatso za ana ankhosa onenepa,

kuchokera ku Sela kudutsa chipululu

mpaka kukafika ku phiri la Ziyoni.

2Monga momwe mbalame zimawulukira uku ndi uku

akazimwaza mʼchisa,

momwemonso akazi a ku Mowabu

akuyendayenda ku madooko a Arinoni.

3Amowabu aja anawuza a ku Yuda kuti,

“Tiwuzeni chochita, gamulani zoti tichite.

Inu mutiteteze kwa adani anthu.

Mukhale ngati mthunzi wathu dzuwa lili pa liwombo.

Mutibise,

musatipereke ife othawa nkhondo kwa adani athu.

4Lolani kuti anthu othawa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu;

mukhale populumukira pawo kwa wowonongayo.”

Nthawi idzafika ndipo wozunzayo sadzakhalaponso,

kuwononga kudzaleka;

waukaliyo adzachoka mʼdzikomo.

5Mpando waufumu udzakhazikitsidwa mwachikondi;

mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika.

Iyeyo poweruza adzatsata chilungamo

ndipo adzalimbikitsa kuchita zachilungamo.

6Tinamva kuti Mowabu anadzikuza kwambiri.

Kunyada kwawo

ndi kunyogodola kwawo ndi kudzitama kwawo,

zonse ndi zopanda phindu.

7Nʼchifukwa chake Amowabu akulira kwambiri;

iwo akulirira dziko lawo.

Akubuma momvetsa chisoni

chifukwa cha makeke a mphesa a ku Kiri Hareseti.

8Minda ya ku Hesiboni yauma,

minda ya mpesa ya ku Sibina yaguga.

Atsogoleri a mitundu ina anapondaponda

minda ya mpesa wabwino,

imene nthambi zake zinakafika ku Yazeri,

mpaka kutambalalira ku chipululu.

Mizu yake inakafika

mpaka ku tsidya la nyanja.

9Kotero Ine ndikulira, monga mmene akulirira anthu a ku Yazeri,

chifukwa cha minda ya mpesa ya ku Sibima.

Inu anthu a ku Hesiboni, inu anthu a ku Eleali,

ndikukunyowetsani ndi misozi!

Mwalephera kupeza zokolola,

chifukwa cha nkhondo imene inawononga zokolola zonse.

10Chimwemwe ndi chisangalalo zalekeka ku minda yanu ya zipatso;

palibe amene akuyimba kapena kufuwula mʼminda ya mpesa;

palibe amene akupsinya vinyo ku malo opsinyira mphesa,

pakuti ndathetsa kufuwula.

11Chifukwa chake moyo wanga ukulira ngati pangwe kulirira Mowabu,

mtima wanga ukubuwula chifukwa cha Kiri Hareseti.

12Ngakhale anthu a ku Mowabu

apite ku malo awo achipembedzo

koma amangodzitopetsa ndi kutaya nthawi chabe

chifukwa sizidzatheka.

13Awa ndi mawu amene Yehova wayankhula kale zokhudza Mowabu. 14Koma tsopano Yehova akuti, “Zisanathe zaka zitatu, potsata mʼmene munthu waganyu amawerengera, ulemerero wa Mowabu udzakhala utatheratu ndipo anthu ake ambiri adzakhala atawonongeka, ndipo opulumuka ake adzakhala ochepa ndi ofowoka.”

Священное Писание (Восточный перевод), версия с «Аллахом»

Исаия 16:1-14

1Посылайте ягнят в дань

правителям Иудеи,

из Селы16:1 Села – столица Эдома. через пустыню

на гору Сион.

2Как бьющая крыльями птица,

выброшенная из гнезда, –

женщины-моавитянки

у бродов Арнона.

3– Дай нам совет,

прими решение.

Пусть твоя тень среди полудня,

как ночь, нас укроет.

Спрячь изгнанников,

не выдавай скитальцев.

4Дай моавским изгнанникам остаться у тебя,

стань им убежищем от губителя.

Когда притеснителю придёт конец,

прекратится опустошение

и в стране сгинут расхитители,

5тогда верностью утвердится престол,

и воссядет на него в истине правитель –

правитель из дома Давуда, –

ищущий справедливость,

спешащий творить праведность.

6Слышали мы о гордости Моава,

о его непомерной гордости и тщеславии,

о его гордости и наглости,

но пуста его похвальба.

7Поэтому плачут моавитяне,

все вместе оплакивают Моав.

Плачьте, сражённые горем,

вспоминая прекрасные лепёшки с изюмом16:7 Лепёшки с изюмом – этот деликатес, приготовлявшийся из измельчённого изюма в особых случаях (см. 2 Цар. 6:19), возможно, использовался в обрядах поклонения Баалу как средство, возбуждающее чувственность (см. Песн. 2:5; Ос. 3:1). из Кир-Харесета.

8Засохли поля Хешбона

и виноградные лозы Сивмы.

Вожди народов растоптали лучшие лозы,

что некогда тянулись до Иазера,

простирались к пустыне.

Побеги их расширялись

и достигали Мёртвого моря.

9И я плачу, как плачет Иазер,

о лозах Сивмы.

О, Хешбон и Элеале,

орошу вас слезами!

Над твоими созревшими плодами,

над твоим поспевшим зерном

стихли крики радости.

10Веселье и радость ушли из садов,

никто не поёт, не шумит в виноградниках

и в давильнях не топчет вино,

и радости шумной положен конец.

11Плачет сердце моё о Моаве, как арфа,

и душа – о Кир-Харесете.

12Если Моав явится

и станет изводить себя в капище,

если он придёт в своё святилище молиться,

то не будет от этого прока.

13Таково слово, которое Вечный сказал о Моаве в прошлом. 14Но теперь Вечный говорит:

– Ровно через три года, как если бы батрак отсчитывал дни до конца срока своей работы, слава Моава и всё множество его народа погибнут, а уцелевшие будут малочисленны и слабы.