Yeremiya 39 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 39:1-18

Kugonjetsedwa kwa Yerusalemu

1Mzinda wa Yerusalemu anawulanda motere: Mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anabwera ndi gulu lake lonse kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu ndipo anawuzinga mzindawo. 2Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi wachinayi wa chaka cha khumi ndi chimodzi cha Zedekiya, malinga a mzindawo anabowoledwa. 3Pamenepo akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni anabwera nakakhala pa Chipata Chapakati. Akuluwo ndi awa: Nerigali-Sarezeri, Samugara Nebo, Sarisekimu mkulu wa nduna, Nerigali-Sarezeri winanso mlangizi wa mfumu ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni. 4Zedekiya mfumu ya Yuda pamodzi ndi ankhondo ake atawaona, anathawa mu mzindawo usiku podzera ku munda wa mfumu, kudutsa chipata cha pakati pa makoma awiri. Anathawira ku Araba.

5Koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola ndi kumupeza Zedekiyayo mʼchigwa cha ku Yeriko. Anamugwira napita naye kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ku Ribula mʼdziko la Hamati kumene anagamula mlandu wake. 6Ku Ribulako, mfumu ya ku Babuloni inapha ana aamuna a Zedekiya iyeyo akuona. Inaphanso anthu olemekezeka onse a ku Yuda. 7Kenaka inakolowola maso a Zedekiya ndi kumumanga ndi maunyolo a mkuwa nʼkupita naye ku Babuloni.

8Ababuloni anatentha nyumba ya mfumu ndi nyumba za anthu, ndiponso anagwetsa malinga a Yerusalemu. 9Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo a mfumu, anatenga ukapolo anthu onse otsala mu mzindamo kupita nawo ku Babuloni, pamodzi ndi amene anadzipereka kale kwa iye. 10Koma Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo anasiya mʼdziko la Yuda anthu ena osauka, amene analibe chilichonse; ndipo anawapatsa minda ya mpesa ndi minda inanso.

11Tsono Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni inatuma mawu kwa Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda ankhondo a mfumu za Yeremiya. Iye anati: 12“Mutenge, umusamale bwino, ndipo usamuvute koma umuchitire zimene afuna.” 13Choncho Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda, Nebusazibani mkulu wa nduna, Nerigali-Sarezeri mlangizi wamkulu wa mfumu ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni 14anatuma anthu nakamutulutsa Yeremiya mʼbwalo la alonda. Anakamupereka kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti amutumize ku nyumba yake. Ndipo Yeremiya anakhala pakati pa abale ake.

15Yeremiya ali mʼndende ku bwalo la alonda, Yehova anayankhula naye: 16“Pita ukamuwuze Ebedi-Meleki, Mkusi, kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Zidzachitikadi zimene ndinanena zokhudza mzinda uno; ndipo zidzakhala zoyipa osati zabwino ayi. Zimenezi zidzachitika pa nthawi yake iwe ukuona. 17Koma ndidzakupulumutsa pa tsiku limenelo, akutero Yehova; sudzaperekedwa kwa anthu amene umawaopa. 18Ndithu ndidzakupulumutsa; sudzaphedwa pa nkhondo koma udzapulumuka, chifukwa wadalira Ine, akutero Yehova.’ ”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

耶利米書 39:1-18

耶路撒冷淪陷

1猶大西底迦執政第九年十月,巴比倫尼布甲尼撒率領全軍包圍耶路撒冷2西底迦執政第十一年四月九日,耶路撒冷淪陷。 3尼甲·沙利薛三甲·尼波撒西金和另一個尼甲·沙利薛巴比倫王的所有將領都進城坐在中門。 4猶大西底迦和所有軍兵見勢不妙,便在夜間穿過御花園,從兩城牆中間的門逃往亞拉巴5迦勒底的軍隊追上來,在耶利哥的平原擒住西底迦,把他帶到哈馬利比拉去見巴比倫尼布甲尼撒,接受審判。 6巴比倫王在利比拉當著西底迦的面殺了他的眾子和猶大所有的貴族, 7並且挖去他的雙眼,把他用銅鏈鎖著帶到巴比倫8迦勒底人放火焚燒王宮和民居,拆毀耶路撒冷的城牆。 9護衛長尼布撒拉旦把城中的餘民以及投降的人都擄到巴比倫10卻讓那些一貧如洗的窮人留在猶大,將葡萄園和田地分給他們。

耶利米獲釋

11至於耶利米巴比倫尼布甲尼撒吩咐護衛長尼布撒拉旦12「你好好照顧耶利米,切不可傷害他。他有什麼要求,你都要滿足。」 13於是,護衛長尼布撒拉旦尼布沙斯班尼甲·沙利薛巴比倫王的所有將領, 14便派人把耶利米從護衛兵的院子提出來,讓沙番的孫子、亞希甘的兒子基大利帶他回家。從此,耶利米就生活在百姓當中。

15耶利米被監禁在護衛兵院子裡的時候,耶和華對他說: 16「你去告訴古實以伯·米勒以色列的上帝——萬軍之耶和華說,『看啊,我必照我說的使這城遭受災禍,得不到祝福。你必親眼看見這一切發生。』 17耶和華說,『但那時,我必拯救你,使你不致落在你所懼怕的人手中。 18我必拯救你,使你保全性命,不致喪身刀下,因為你信靠我。這是耶和華說的。』」