Yesaya 1 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 1:1-31

1Masomphenya wonena za Yuda ndi Yerusalemu, amene Yesaya mwana wa Amozi, anaona pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.

Anthu Owukira

2Tamverani, miyamba inu! Tchera khutu, iwe dziko lapansi!

Pakuti Yehova wanena kuti,

“Ndinabala ana ndi kuwalera,

koma anawo andiwukira Ine.

3Ngʼombe imadziwa mwini wake,

bulu amadziwa kumene kuli gome la mbuye wake,

koma Israeli sadziwa,

anthu anga samvetsa konse.”

4Haa, mtundu wochimwa,

anthu olemedwa ndi machimo,

obadwa kwa anthu ochita zoyipa,

ana odzipereka ku zoyipa!

Iwo asiya Yehova;

anyoza Woyerayo wa Israeli

ndipo afulatira Iyeyo.

5Chifukwa chiyani mukufuna kuti muzingolangidwabe?

Chifukwa chiyani mukupitirira kukhala mʼmoyo wowukira?

Mutu wanu wonse uli ndi mabala,

mtima wanu wonse wafowokeratu.

6Kuchokera ku phazi mpaka ku mutu

palibe pabwino,

paliponse pali mikwingwirima ndi zilonda,

mabala ali magazi chuchuchu,

mabala ake ngosatsuka, ngosamanga

ndiponso ngosapaka mafuta ofewetsa.

7Dziko lanu lasanduka bwinja,

mizinda yanu yatenthedwa ndi moto;

minda yanu ikukololedwa ndi alendo

inu muli pomwepo,

dziko lanu lasanduka bwinja monga ngati lagonjetsedwa ndi alendo.

8Mwana wamkazi wa Ziyoni watsala yekha

ngati nsanja mʼmunda wampesa,

ngati chisimba mʼmunda wa minkhaka,

ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo.

9Yehova Wamphamvuzonse akanapanda

kutisiyira opulumuka,

tikanawonongeka ngati Sodomu,

tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.

10Imvani mawu a Yehova,

inu olamulira Sodomu;

mverani lamulo la Mulungu wathu,

inu anthu a ku Gomora!

11Yehova akuti, “Kodi ndili nazo chiyani

nsembe zanu zochuluka?”

“Zandikola nsembe zanu zopsereza

za nkhosa zazimuna ndiponso mafuta a nyama zonenepa;

sindikusangalatsidwanso

ndi magazi angʼombe zamphongo ndi a ana ankhosa ndi ambuzi zazimuna.

12Ndani anakulamulirani kuti

mubwere nazo pamaso panga?

Ndani anakuwuzani kuti muzipondaponda mʼmabwalo a nyumba yanga?

13Siyani kubweretsa nsembe zachabechabezo!

Nsembe zanu zofukiza zimandinyansa Ine.

Sindingapirire misonkhano yanu yoyipa,

kapenanso zikondwerero za Mwezi Watsopano ndi Masabata.

14Zikondwerero zanu za Mwezi Watsopano ndi masiku anu opatulika

ndimadana nazo.

Zasanduka katundu wondilemera;

ndatopa kuzinyamula.

15Mukamatambasula manja anu popemphera,

Ine sindidzakuyangʼanani;

ngakhale muchulukitse mapemphero anu,

sindidzakumverani.

Manja anu ndi odzaza ndi magazi;

16sambani, dziyeretseni.

Chotsani pamaso panu

ntchito zanu zoyipa!

Lekani kuchita zoyipa,

17phunzirani kuchita zabwino!

Funafunani chilungamo,

thandizani oponderezedwa.

Tetezani ana amasiye,

muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.”

18Yehova akuti,

“Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu.

Ngakhale machimo anu ali ofiira,

adzayera ngati thonje.

Ngakhale ali ofiira ngati kapezi,

adzayera ngati ubweya wankhosa.

19Ngati muli okonzeka kundimvera

mudzadya zinthu zabwino za mʼdziko;

20koma mukakana ndi kuwukira

mudzaphedwa ndi lupanga.”

Pakuti Yehova wayankhula.

21Taonani momwe mzinda wokhulupirika

wasandukira wadama!

Mzinda umene kale unali wodzaza ndi chiweruzo cholungama;

mu mzindamo munali chilungamo,

koma tsopano muli anthu opha anzawo!

22Siliva wako wasanduka wachabechabe,

vinyo wako wabwino wasungunulidwa ndi madzi.

23Atsogoleri ako ndi owukira,

anthu ogwirizana ndi mbala;

onse amakonda ziphuphu

ndipo amathamangira mphatso.

Iwo sateteza ana amasiye;

ndipo samvera madandawulo a akazi amasiye.

24Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvu,

Wamphamvuyo wa Israeli, akunena kuti,

“Haa, odana nane ndidzawatha,

ndipo ndidzawabwezera ndekha adani anga.

25Ndidzatambasula dzanja langa kuti ndilimbane nawe;

ndidzasungunula machimo ako nʼkuwachotsa,

monga mmene amachotsera dzimbiri ndi mankhwala.

26Ndidzabwezeretsa oweruza ako ngati masiku amakedzana,

aphungu ako ndidzawabwezeretsa ngati poyamba paja.

Kenaka iweyo udzatchedwa

mzinda wolungama,

mzinda wokhulupirika.”

27Ziyoni adzawomboledwa mwa chiweruzo cholungama,

anthu ake olapadi adzapulumutsidwa mwachilungamo.

28Koma owukira ndi ochimwa adzawawonongera pamodzi,

ndipo amene asiya Yehova adzatheratu.

29“Mudzachita nayo manyazi mitengo ya thundu

imene inkakusangalatsani;

mudzagwetsa nkhope chifukwa cha minda

imene munayipatula.

30Mudzakhala ngati mtengo wa thundu umene masamba ake akufota,

mudzakhala ngati munda wopanda madzi.

31Munthu wamphamvu adzasanduka ngati udzu wowuma,

ndipo ntchito zake zidzakhala ngati mbaliwali;

motero zonse zidzayakira limodzi,

popanda woti azimitse motowo.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以賽亞書 1:1-31

1猶大烏西雅約坦亞哈斯希西迦執政期間,亞摩斯的兒子以賽亞看到了以下有關猶大耶路撒冷的異象。

上帝責備叛逆的子民

2諸天啊,請聽!

大地啊,要側耳聽!

耶和華說:

「我把孩子撫育成人,

他們竟然背叛我。

3牛認識主人,

驢也認得主人的槽,

以色列卻不認識,

我的子民卻不明白。」

4唉!你們這罪惡的民族,

惡貫滿盈的百姓,

作惡的子孫,

敗壞的兒女!

你們背棄耶和華,

藐視以色列的聖者,

與祂疏遠。

5你們為什麼一再叛逆?

你們還要受責打嗎?

你們已經頭破血流,

身心疲憊。

6你們已經體無完膚,

從頭到腳傷痕纍纍,

傷口沒有清洗,

沒有包紮,也沒有敷藥。

7你們的土地荒涼,

城邑化為灰燼。

你們親眼目睹自己的田園被外族人侵吞、毀壞、變成不毛之地。

8僅存的錫安1·8 錫安」又稱「耶路撒冷」。城也像葡萄園裡的草棚、

瓜田中的茅舍、

被困無援的孤城。

9若不是萬軍之耶和華讓我們一些人存活,

我們早就像所多瑪蛾摩拉一樣滅亡了。

10你們這些「所多瑪」的首領啊,

要聆聽耶和華的話!

你們這些「蛾摩拉」的百姓啊,

要側耳聽我們上帝的訓誨!

11耶和華說:

「你們獻上許多祭物,對我有什麼用呢?

我厭煩公綿羊的燔祭和肥畜的脂肪,

我不喜歡公牛、羊羔和公山羊的血。

12「你們來敬拜我的時候,

誰要求你們帶著這些來踐踏我的院宇呢?

13不要再帶毫無意義的祭物了。

我憎惡你們燒的香,

厭惡你們的朔日1·13 朔日」即每月初一。、安息日和大會。

你們又作惡又舉行莊嚴的聚會,

令我無法容忍。

14我憎惡你們的朔日及其他節期,

它們成了我的重擔,

令我厭倦。

15你們舉手禱告,我必掩面不理。

即使你們禱告再多,

我也不會聽,

因為你們雙手沾滿鮮血。

16你們要洗淨自己,

停止作惡,

不要讓我再看見你們的惡行。

17你們要學習行善,

追求正義,

幫助受欺壓的,

替孤兒辯護,

為寡婦伸冤。」

18耶和華說:

「來吧,我們彼此理論!

你們的罪雖如猩紅,

也必潔白如雪;

你們的罪雖如緋紅,

也必白如羊毛。

19如果你們願意聽從,

就必享用這地方的美好出產。

20如果你們執意叛逆,

就必喪身刀下。」

這是耶和華親口說的。

21耶路撒冷啊,

你這忠貞的妻子竟變成了妓女!

你從前充滿公平,

是公義之家,

現在卻住著兇手。

22你曾經像銀子,現在卻像渣滓;

曾經像美酒,現在卻像攙了水的酒。

23你的首領是叛逆之徒,

與盜賊為伍,

個個收受賄賂,

貪圖好處,

不為孤兒辯護,

不替寡婦伸冤。

24所以,主——萬軍之耶和華,

以色列的大能者說:

「我要向我的敵人報仇雪恨。

25我必攻擊你,

用鹼煉淨你的渣滓,

除盡你的雜質。

26我必像從前一樣賜你審判官和謀士。

之後,你必被稱為公義之城、

忠信之邑。」

27耶和華必因祂的公正救贖錫安

必因祂的公義拯救城中悔改的人。

28但叛逆之輩和犯罪之徒必遭毀滅,

背棄耶和華的人必滅亡。

29你們必因在橡樹下,

在你們選擇的園子裡祭拜偶像而蒙羞。

30你們必像枯萎的橡樹,

又如無水的園子。

31你們中間有權勢的人必因他們的惡行而遭毀滅,

好像火花點燃枯木,無人能救。