Yeremiya 30 – CCL & NVI-PT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 30:1-24

Kubwezeretsedwa kwa Israeli

1Yehova anawuza Yeremiya kuti, 2“Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, ‘Lemba mʼbuku mawu onse amene ndakuwuza. 3Nthawi ikubwera pamene ndidzachotse anthu anga, Israeli ndi Yuda kuchokera ku ukapolo ndi kuwabwezera dziko limene ndinapatsa makolo awo,’ akutero Yehova.”

4Nawa mawu amene Yehova anayankhula ndi anthu a ku Israeli ndi Yuda: 5“Yehova akuti:

“Ndamva kulira chifukwa cha nkhawa,

ndamva kulira kwa mantha popeza palibe mtendere.

6Tsono khalani pansi ndi kudzifunsa kuti:

Kodi munthu wamwamuna angathe kubereka mwana?

Nanga nʼchifukwa chiyani ndikuona munthu aliyense wamwamuna

atagwira manja ake pa mimba pake ngati mayi pa nthawi yake yochira?

Chifukwa chiyani nkhope iliyonse ili yakugwa?

7Mayo ine! Tsiku limeneli ndi lalikulu kwambiri!

Sipadzakhala lina lofanana nalo.

Idzakhala nthawi ya masautso kwa Yakobo,

koma adzapulumuka ku masautsowo.”

8Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Pa tsiku limenelo,

ndidzathyola goli la ukapolo mʼkhosi mwawo

ndipo ndidzadula zingwe zowamanga;

Aisraeli sadzakhalanso akapolo a alendo.

9Mʼmalo mwake, adzatumikira Yehova Mulungu wawo

ndiponso Davide mfumu yawo,

amene ndidzawasankhira.

10“ ‘Tsono usachite mantha, iwe mtumiki wanga Yakobo;

usade nkhawa, iwe Israeli,’

akutero Yehova.

‘Ndithu ndidzakupulumutsa kuchokera ku dziko lakutali,

zidzukulu zako kuchokera ku dziko la ukapolo wawo.

Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala modekha pa mtendere,

ndipo palibe amene adzamuchititsa mantha.

11Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani,’

akutero Yehova.

‘Ngakhale ndidzawononga kotheratu mitundu yonse ya anthu

kumene ndinakubalalitsirani,

koma inu sindidzakuwonongani kotheratu.

Sindidzakulekani kuti mukhale osalangidwa.

Koma ndidzakulangani mwachilungamo.’ ”

12Yehova akuti,

“Chilonda chanu nʼchosachizika,

bala lanu ndi lonyeka.

13Palibe amene angathe kukutetezani pa mlandu wanu,

palibe chiyembekezo choti inu nʼkuchira,

palibe mankhwala ochiritsa inu.

14Abwenzi anu onse akuyiwalani;

sasamalanso za inu.

Ndakukanthani ngati mmene mdani akanachitira.

Ndipo ndakulangani mwa nkhanza,

chifukwa machimo anu ndi ambiri,

ndipo kulakwa kwanu ndi kwakukulu.

15Chifukwa chiyani mukulira nacho chilonda chanu?

Bala lanu silingapole ayi.

Ine ndakuchitani zimenezi chifukwa machimo anu ndi ambiri

ndipo kulakwa kwanu nʼkwakukulu.

16“Tsono onse amene anakuwonongani, nawonso adzawonongedwa;

adani anu onse adzapita ku ukapolo.

Iwo amene anafunkha zinthu zanu, zinthu zawo zidzafunkhidwanso;

onse amene anakusakazani nawonso adzasakazidwa.

17Ndidzachiza matenda anu

ndi kupoletsa zilonda zanu,

akutero Yehova,

‘chifukwa mukutchedwa anthu otayika.

Amati, ndi anthu a ku Ziyoni awa amene alibe wowasamala.’ ”

18Yehova akuti,

“Ndidzabwera nalo banja la Yakobo ku dziko lawo

ndipo ndidzachitira chifundo malo ake okhalamo;

mzinda wa Yerusalemu udzamangidwanso pa bwinja pake,

nyumba yaufumu idzamangidwanso pa malo pake penipeni.

19Anthuwo adzayimba nyimbo zoyamika Yehova

ndipo kudzamveka phokoso lachisangalalo.

Ndidzawachulukitsa,

ndipo chiwerengero chawo sichidzatsika;

ndidzawapatsa ulemerero,

ndipo sadzanyozedwanso.

20Ana awo adzakhalanso monga mmene analili kale,

ndipo gulu lawo ndidzalikhazikitsa pamaso panga;

ndidzalanga onse owazunza.

21Mtsogoleri wawo adzakhala mmodzi mwa iwo.

Wodzawalamulira adzachokera pakati pawo.

Choncho ndidzawakokera kufupi ndi Ine ndipo iye adzandiyandikira.

Ndani angalimbe mtima payekha kuyandikana nane

popanda kuyitanidwa?”

akutero Yehova.

22“Choncho inu mudzakhala anthu anga,

ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu.”

23Taonani ukali wa Yehova wowomba

ngati mphepo ya mkuntho.

Mphepo ya namondwe

ikuwomba pa mitu ya anthu oyipa.

24Mkwiyo woopsa wa Yehova sudzachoka

mpaka atakwaniritsa zolinga

za mu mtima mwake.

Mudzamvetsa zimenezi

masiku akubwerawo.

Nova Versão Internacional

Jeremias 30:1-24

A Restauração de Israel

1Esta é a palavra que veio a Jeremias da parte do Senhor: 2“Assim diz o Senhor, o Deus de Israel: Escreva num livro todas as palavras que eu falei a você. 3Certamente vêm os dias”, diz o Senhor, “em que mudarei a sorte do meu povo, Israel e Judá, e os farei retornar à terra que dei aos seus antepassados, e eles a possuirão”, declara o Senhor.

4Estas são as palavras que o Senhor falou acerca de Israel e de Judá: 5“Assim diz o Senhor:

“Ouvem-se gritos de pânico,

de pavor e não de paz.

6Pergunte e veja: Pode um homem dar à luz?

Por que vejo, então, todos os homens

com as mãos no estômago,

como uma mulher em trabalho de parto?

Por que estão pálidos todos os rostos?

7Como será terrível aquele dia!

Sem comparação!

Será tempo de angústia para Jacó;

mas ele será salvo.

8“Naquele dia”, declara o Senhor dos Exércitos,

“quebrarei o jugo que está sobre o pescoço deles

e arrebentarei as suas correntes;

não mais serão escravizados pelos estrangeiros.

9Servirão ao Senhor, ao seu Deus,

e a Davi, seu rei, que darei a eles.

10“Por isso, não tema, Jacó, meu servo!

Não fique assustado, ó Israel!”,

declara o Senhor.

“Eu o salvarei de um lugar distante,

e os seus descendentes, da terra do seu exílio.

Jacó voltará e ficará em paz e em segurança;

ninguém o inquietará.

11Porque eu estou com você e o salvarei”, diz o Senhor.

“Destruirei completamente todas as nações

entre as quais eu o dispersei;

mas a você não destruirei completamente.

Eu o disciplinarei, como você merece.

Não o deixarei impune”.

12Assim diz o Senhor:

“Seu ferimento é grave,

sua ferida, incurável.

13Não há quem defenda a sua causa;

não há remédio para a sua ferida, que não cicatriza.

14Todos os seus amantes esqueceram-se de você;

eles não se importam com você.

Eu a golpeei como faz um inimigo;

dei a você um castigo cruel,

porque é grande a sua iniquidade

e numerosos são os seus pecados.

15Por que você grita por causa do seu ferimento,

por sua ferida incurável?

Fiz essas coisas a você

porque é grande a sua iniquidade

e numerosos são os seus pecados.

16“Mas todos os que a devoram serão devorados;

todos os seus adversários irão para o exílio.

Aqueles que a saqueiam serão saqueados;

eu despojarei todos os que a despojam.

17Farei cicatrizar o seu ferimento

e curarei as suas feridas”, declara o Senhor,

“porque a você, Sião, chamam de rejeitada,

aquela por quem ninguém se importa”.

18Assim diz o Senhor:

“Mudarei a sorte das tendas de Jacó

e terei compaixão das suas moradas.

A cidade será reconstruída sobre as suas ruínas

e o palácio no seu devido lugar.

19Deles virão ações de graça e o som de regozijo.

Eu os farei aumentar e eles não diminuirão;

eu os honrarei e eles não serão desprezados.

20Seus filhos serão como nos dias do passado,

e a sua comunidade será firmada diante de mim;

castigarei todos aqueles

que os oprimem.

21Seu líder será um entre eles;

seu governante virá do meio deles.

Eu o trarei para perto e ele se aproximará de mim;

pois quem se arriscaria a aproximar-se de mim?”,

pergunta o Senhor.

22“Por isso vocês serão o meu povo,

e eu serei o seu Deus”.

23Vejam, a tempestade do Senhor!

Sua fúria está à solta!

Um vendaval vem

sobre a cabeça dos ímpios.

24A ira do Senhor não se afastará

até que ele tenha completado os seus propósitos.

Em dias vindouros

vocês compreenderão isso.