Yeremiya 19 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 19:1-15

1Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukagule mʼphika wadothi kwa munthu wowumba. Utenge akuluakulu ena a anthuwa ndi ansembe 2ndipo mupite ku Chigwa cha Hinomu chimene chili pafupi ndi pa chipata cha mapale. Pamenepo ukalengeze mawu amene ndikakuwuze. 3Ukanene kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu a ku Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu. Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti: Tamverani! Ine ndibweretsa mavuto pa malo pano mwakuti aliyense amene adzamve adzadzidzimuka. 4Pakuti anthu andikana Ine ndipo ayipitsa malo ano. Afukiza lubani pa malo ano kwa milungu imene iwo ngakhale makolo awo ngakhalenso mafumu a ku Yuda sanayidziwe. Iwo adzaza malowa ndi magazi a anthu osalakwa. 5Amanga nsanja zopembedzerapo Baala, kuperekapo ana awo kuti akhale nsembe zopsereza kwa Baala, chinthu chimene Ine sindinalamule kapena kuchiyankhula, ngakhalenso kuchiganizira. 6Nʼchifukwa chake taonani, masiku akubwera, akutero Yehova, pamene anthu sadzatchulanso malo ano kuti Tofeti kapena Chigwa cha Hinomu, koma Chophera anthu.

7“ ‘Pamalo pano ndidzasokoneza maganizo a anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Ndidzachititsa kuti adani awo awaphe ku nkhondo. Ndidzawakanthitsa kwa anthu amene akuwazonda. Mitembo yawo ndidzayipereka kwa mbalame za mlengalenga ndi zirombo za kutchire kuti ikhale chakudya chawo. 8Mzinda uno ndidzawusakaza ndi kuwusandutsa chinthu chochititsa mantha ndi chonyansa. Onse odutsamo adzadabwa ndi kupukusa mitu yawo chifukwa cha kuwonongeka kwake. 9Adani awo adzawuzinga mzindawo kufuna kuwapha motero kuti anthu a mʼkatimo adzafika pomadyana wina ndi mnzake. Adzadya ana awo aamuna ndi ana awo aakazi.’

10“Tsono iwe udzaphwanye mtsukowo anthu amene udzapite nawowo akuona, 11ndipo ukawawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti, Ine ndidzaphwanya dziko lino ndi mzinda uno ngati momwe wowumba amaphwanyira mbiya yake ndipo sangathe kuyikonzanso. Adzayika anthu akufa ku Tofeti chifukwa padzasowa malo ena owayika. 12Umu ndi mmene ndidzachitire ndi malo ano pamodzi ndi anthu okhalamo, akutero Yehova. Ndidzasandutsa mzindawu kukhala ngati Tofeti. 13Nyumba za mu Yerusalemu ndi za mafumu a ku Yuda ndidzazisandutsa ngati za ku Tofeti chifukwa ndi nyumba zimene pa madenga ake ankafukiza lubani kwa zolengedwa zamlengalenga ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa milungu ina.’ ”

14Kenaka Yeremiya anabwerako ku Tofeti, kumene Yehova anamutuma kuti akanenere, nakayimirira mʼbwalo la Nyumba ya Yehova ndi kuwawuza anthu kuti, 15“Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti, ‘Tamverani! Ine ndidzabweretsa masautso amene ndinanena aja pa mzinda uno ndi pa mizinda yozungulira, chifukwa anthu ake ndi nkhutukumve ndipo sanamvere mawu anga.’ ”

New Russian Translation

Иеремия 19:1-15

Разбитый кувшин

1Так сказал Господь:

– Пойди и купи у горшечника глиняный кувшин. Возьми с собой кого-нибудь из старейшин народа и из старейшин священников 2и выйди в долину Бен-Гинном, что лежит напротив ворот Черепков. Возвести там слова, которые Я говорю тебе, 3и скажи: «Слушайте слово Господне, цари Иудеи и жители Иерусалима. Так говорит Господь Сил, Бог Израиля: Я нашлю на эту землю беду, от которой у любого, кто услышит, зазвенит в ушах. 4Ведь люди осквернили эту землю и жгли здесь благовония чужим богам, которых не знали ни они сами, ни их отцы, ни цари Иудеи, и залили эту землю невинной кровью. 5Они построили для Баала святилища на возвышенностях, чтобы сжигать своих сыновей ему в жертву – то, о чем Я не приказывал и не говорил, о чем даже не думал. 6И вот, непременно настанут дни, – возвещает Господь, – когда это место больше не будут называть ни Тофетом, ни долиной Бен-Гинном, а долиной Бойни.

7На этом месте Я разрушу19:7 Здесь в еврейском тексте наблюдается игра слов: «бакак» («разрушать») и «бакбук» («кувшин») (ст. 1 и 10). замыслы Иудеи и Иерусалима. Я повергну их мечом перед врагами – руками тех, кто хочет их смерти, – и отдам их трупы в пищу небесным птицам и земным зверям. 8Я опустошу этот город и сделаю его посмешищем; каждый, кто пройдет мимо, ужаснется и будет злорадствовать над всеми его ранами. 9Я накормлю его жителей плотью их сыновей и дочерей, и они станут есть плоть друг друга, находясь в осаде и в нужде, на которую обрекут их враги, желающие их смерти».

10– Разбей кувшин на глазах у тех, кто пришел с тобой, 11и скажи им: «Так говорит Господь Сил: Я разобью этот народ и этот город, как был разбит кувшин горшечника, который уже не склеить. И будут их хоронить в Тофете, пока не останется места». 12Вот что Я сделаю с этим краем и с теми, кто здесь живет, – возвещает Господь. – Я оскверню этот город, как осквернен Тофет19:12 Букв.: «Огненное место». Тофет находился в долине Бен-Гинном, где в жертву аммонитскому богу Молоху приносили детей, сжигая их на костре (см. 4 Цар. 21:6; 23:10), что было строго запрещено израильтянам (см. Лев. 18:21).. 13Дома Иерусалима и дворцы царей Иудеи – все дома, где на крышах жгли благовония всему небесному воинству и лили жертвенные возлияния чужим богам, – будут осквернены, как место Тофет.

14Иеремия вернулся из Тофета, куда Господь посылал его пророчествовать, встал во дворе Господнего дома и возвестил всему народу:

15– Так говорит Господь Сил, Бог Израиля: Я нашлю на этот город и на все его предместья все беды, которые Я им определил, за то, что они были упрямыми и не слушали Моих слов.