Yeremiya 15 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 15:1-21

1Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Ngakhale Mose ndi Samueli akanayima pamaso panga kupempherera anthu awa, Ine sindikanawachitira chisoni. Achotseni ndipo ndisawaonenso! Aleke apite! 2Ndipo ngati akufunsa iwe kuti, ‘Kodi tipite kuti?’ uwawuze kuti, ‘Yehova akuti,

“ ‘Oyenera kufa adzafa;

oyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga;

oyenera kufa ndi njala adzafa ndi njala;

oyenera kupita ku ukapolo adzapita ku ukapolo.’

3“Ine ndidzawatumizira mitundu inayi ya zinthu zowononga,” akutero Yehova, “lupanga lowapha, agalu owaluma, mbalame zamumlengalenga ndiponso zirombo zoti ziwadye ndi kuwawononga. 4Ndidzawasandutsa kukhala chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a dziko lapansi chifukwa cha zimene Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda anachita mu Yerusalemu.

5“Kodi adzakumvera chisoni ndani, Yerusalemu?

Kodi adzakulira ndani?

Kodi ndani amene adzapatuka kufunsa za moyo wako?

6Inu mwandikana Ine,” akutero Yehova.

“Inu mukubwererabe mʼmbuyo.

Choncho Ine ndidzakukanthani.

Ndatopa ndi kukuchitirani chifundo.

7Ine ndidzakubalalitsani kukuchotsani mʼmizinda ya mʼdzikomo

monga mmene amachitira ndi mankhusu popeta ndi lichero.

Anthu anga ndinawaliritsa ndi kuwawononga

chifukwa sanasinthe makhalidwe awo oyipa.

8Ndinachulukitsa amayi awo amasiye

kupambana mchenga wa kunyanja.

Amayiwo ndinawawonongera ana awo aamuna

dzuwa lili pamutu.

Mwadzidzidzi ndinawagwetsera

kuwawa mtima ndi mantha.

9Mayi wa ana asanu ndi awiri wakomoka

ndipo akupuma wefuwefu.

Dzuwa lake lalowa ukanali usana;

anamuchititsa manyazi ndipo wathedwa nzeru.

Otsala ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo

kuti awaphe ndi lupanga,”

akutero Yehova.

10Kalanga ine, amayi pakuti munandibereka ine,

munthu amene ndikutsutsana ndi kulimbana ndi anthu pa dziko lonse!

Ine sindinakongoze kapena kukongola kanthu,

komatu aliyense akunditemberera.

11Yehova anati,

“Ndithudi, Ine ndidzakulanditsa kuti upeze bwino.

Ndithudi, adani ako adzakupempha pa nthawi ya tsoka

ndi ya mavuto awo.

12“Palibe munthu amene angathe kudula chitsulo,

makamaka chitsulo chochokera kumpoto chosakaniza ndi mkuwa.

13Anthu ako ndi chuma chako

ndidzazipereka kwa ofunkha popanda malipiro,

chifukwa cha machimo anu onse

a mʼdziko lanu lonse.

14Ndidzakusandutsani akapolo a adani anu

mʼdziko limene inu simulidziwa,

chifukwa mkwiyo wanga wayaka ngati moto

umene udzakutenthani.”

15Ine ndinati, “Inu Yehova, mumadziwa zonse;

kumbukireni ndi kundisamalira.

Ndilipsireni anthu ondizunza.

Ndilezereni mtima musandilande moyo wanga.

Onani momwe ndi kuvutikira chifukwa cha Inu.

16Munandiyankhula ndipo mawu anu ndinawalandira bwino.

Mawu anu anandipatsa chimwemwe ndipo mtima wanga unasangalala.

Paja ine, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse,

ndimadziwika ndi dzina lanu.

17Sindinakhale nawo mʼgulu la anthu amadyera,

sindinasangalale nawo anthu amenewo.

Ndinakhala ndekha chifukwa choti dzanja lanu linali pa ine

ndipo munadzaza mu mtima mwanga ndi mkwiyo.

18Nanga nʼchifukwa chiyani mavuto anga sakutha?

Bwanji chilonda changa sichikupola?

Kodi inu mudzakhala ngati mtsinje wowuma nthawi yachilimwe,

kapena ngati kasupe wopanda madzi?”

19Tsono Yehova anandiyankha kuti,

“Ukabwerera kwa Ine, ndidzakulandiranso

ndipo udzakhalanso mtumiki wanga.

Ngati udzayankhula mawu oyenera osati achabechabe,

udzakhalanso mneneri wanga.

Anthu adzabwera kwa iwe

ndipo sipadzafunika kuti iwe upite kwa iwo.

20Ndidzakusandutsa ngati khoma lolimba

ngati mkuwa kwa anthu awa.

Adzalimbana nawe

koma sadzakugonjetsa,

pakuti Ine ndili nawe

kukulanditsa ndi kukupulumutsa,”

akutero Yehova.

21“Ndidzakupulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa

ndipo ndidzakuwombola kwa anthu ankhanza.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

耶利米書 15:1-21

猶大的厄運

1耶和華對我說:「就算摩西撒母耳站在我面前求情,我也不會憐憫這些百姓。你把他們從我面前趕走吧! 2如果他們問你,『我們該去哪裡,』你就告訴他們,耶和華這樣說,

『該死的死,

該被殺的被殺,

該遭饑荒的遭饑荒,

該被擄的被擄。』

3「我要讓他們遭受四種禍患——刀殺、狗撕、鳥啄、獸吞。這是耶和華說的。 4因為猶大希西迦的兒子瑪拿西耶路撒冷的所作所為,我要使他們的遭遇令天下萬國驚懼。

5耶路撒冷啊,誰會同情你?

誰會為你悲哀?

誰會駐足向你問安?

6你背棄我,遠離我,

因此我要伸手攻擊你,毀滅你,

不再憐憫你。

這是耶和華說的。

7我要在這片土地上的各城門口用簸箕簸散我的子民,

使他們喪掉兒女;

我要滅絕他們,

因為他們不思悔改。

8我要使他們的寡婦比海沙還多,

使毀滅者在午間突然奪取青年的性命,

以致母親們陷入痛苦、驚恐中。

9生過七個孩子的母親心力枯竭,奄奄一息。

她羞愧難當,

她的希望突然破滅,

猶如白晝突然變成黑夜。

我必使其餘的人喪身在敵人刀下。

這是耶和華說的。」

耶利米訴苦

10母親啊,我真不幸,因為你生了我這個跟全猶大爭論、激辯的人。我沒有向人借貸,也沒有借貸給人,然而人人都咒罵我。 11耶和華說:「我必拯救你,我必使仇敵在災禍、困難來臨時哀求你。 12誰能折斷來自北方之敵的鐵拳銅臂呢? 13因為你們境內罪惡氾濫,我要使敵人任意搶掠你們的財寶, 14把你們擄到陌生的地方。我的怒火要燒滅你們。」

15耶和華啊,你知道我的遭遇。

求你顧念我,眷顧我,

報應迫害我的人。

求你不要取我的性命,

因為你不輕易發怒,

你知道我為了你忍受辱罵。

16萬軍之上帝耶和華啊,

我把你的話視為甘飴,

它們是我心中的快樂和喜悅,

因為我屬於你的名下。

17我沒有與作樂的人為伍,

沒有與他們同樂。

你要我獨坐一處,

他們的罪惡使我怒氣填胸。

18為什麼我的痛楚無休無止?

為什麼我的創傷無法醫治?

難道你要像一條時斷時流的小溪讓我無法依靠嗎?

19耶和華對我說:

「如果你回心轉意,

我就讓你重新事奉我。

如果你說有益的話,

不說無益的話,

就可以做我的發言人,

百姓便會歸向你,

但你不可受他們的影響。

20我要使你成為堅固的銅牆,

他們要攻擊你,卻不能勝過你,

因為我與你同在,我會保護你,

拯救你。

這是耶和華說的。

21我要把你從惡人手中救出,

從殘暴之徒的權勢下贖回。」