Oweruza 13 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 13:1-25

Kubadwa kwa Samsoni

1Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova, kotero Yehova anawapereka mʼmanja mwa Afilisti kwa zaka makumi anayi.

2Ku Zora kunali munthu wina dzina lake Manowa, wochokera ku fuko la Dani. Mkazi wake analibe ana popeza anali wosabereka. 3Mngelo wa Yehova anaonekera mkaziyo ndipo anati, “Ndinu wosabereka ndipo mulibedi mwana, komabe mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. 4Tsono mudzisamale bwino, osamwa vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa ndiponso musamadye chakudya chilichonse chodetsedwa, 5chifukwa mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo akadzabadwa lumo lisadzapite pa mutu chifukwa mnyamatayo adzakhala Mnaziri, ndiye kuti wopatulika kwa Mulungu kuyambira pa nthawi imene adzakhale ali mʼchiberekero. Ndipo adzayamba ntchito yopulumutsa Israeli mʼmanja mwa Afilisti.”

6Kenaka mayiyo anapita kukawuza mwamuna wake kuti, “Munthu wa Mulungu anabwera kwa ine, ndipo maonekedwe ake anali ngati mngelo wa Mulungu, maonekedwe woopsa kwambiri. Ine sindinamufunse kumene amachokera, ndipo iyeyo sanandiwuzenso dzina lake. 7Koma anandiwuza kuti, ‘Mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. Choncho musamamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa, musamadye chakudya chilichonse choyipitsidwa chifukwa mwanayo adzakhala Mnaziri, wopatulika kwa Mulungu kuyambira pa nthawi imene adzakhale ali mʼchiberekero mpaka tsiku la kufa kwake.’ ”

8Kenaka Manowa anapemphera kwa Yehova kuti, “Chonde Ambuye, lolani munthu wa Mulungu amene munamutuma abwerenso kwa ife kuti adzatiphunzitse zochita ndi mwanayo akadzabadwa.”

9Mulungu anamva pemphero la Manowa, ndipo mngelo wa Mulungu anabweranso kwa mkaziyo nthawi imene anali ku munda, koma Manowa mwamuna wake sanali naye. 10Tsono mkaziyo anathamanga kukawuza mwamuna wake kuti, “Wandionekeranso munthu uja amene anabwera kwa ine tsiku lija.”

11Choncho Manowa ananyamuka namutsatira mkazi wake. Atafika kwa munthuyo anamufunsa kuti, “Kodi ndinu munayankhula ndi mkazi wanga?”

Iye anayankha kuti, “Ndine.”

12Kenaka Manowa anafunsa kuti, “Tiyerekeze kuti mawu anuwa akwaniritsidwadi, ndiye mwanayu azidzakhala bwanji ndipo azidzachita chiyani?”

13Ndipo mngelo wa Yehova uja anamuyankha kuti, “Zonse zimene ndinawawuza akazi anuwa asamale ndipo adzazichitedi. 14Asadzadye chilichonse chochokera ku mphesa. Asadzamwe vinyo kapena choledzeretsa chilichonse, ngakhale kudya chakudya chilichonse chodetsedwa. Zonse zimene ndinawalamula azisunge bwino.”

15Manowa anamuwuza mngelo wa Yehova uja kuti, “Chonde dikirani pangʼono, timati tikukonzereni mwana wambuzi.”

16Mngelo wa Yehova anayankha kuti, “Ngakhale mukundidikiritsa, ine sindidya chakudya chanu. Koma ngati mukonze nsembe yopsereza iperekeni kwa Yehova.” (Manowa nʼkuti asakudziwa kuti munthuyo anali mngelo wa Mulungu).

17Tsono Manowa anapempha mngelo wa Yehova kuti, “Chonde tidziwitseni dzina lanu kuti zikadzachitika zimene mwanenazi ife tidzakulemekezeni?”

18Iye anayankha kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufunsa dzina langa? Dzina laketu ndi lodabwitsa.” 19Ndipo Manowa anatenga mwana wambuzi pamodzi ndi chopereka cha chakudya nakapereka nsembe pa thanthwe kwa Yehova ndipo Yehova anachita zodabwitsa kwa Manowa ndi mkazi wake akuona. 20Pamene malawi a moto amakwera kumwamba kuchoka pa guwa, mngelo wa Yehova uja anakwera kumwamba mʼmalawi a motowo Manowa ndi mkazi wake akuona. Tsono anadzigwetsa pansi naweramitsa mitu yawo pansi. 21Mngelo wa Yehova uja sanaonekerenso kwa Manowa ndi mkazi wake. Choncho Manowa anazindikira kuti anali mngelo wa Yehova.

22Iye anawuza mkazi wake kuti, “Ife tifa basi pakuti taona Mulungu!”

23Koma mkazi wake anamuyankha kuti, “Yehova akanafuna kutipha sakanayilandira nsembe yathu yopsereza ndi chopereka chathu chachakudya chija, ndipo sakanationetsanso zinthu zonsezi kapena kutiwuza zinthu ngati zimenezi nthawi ino.”

24Motero mkaziyo anabereka mwana wa mwamuna, namutcha dzina lake Samsoni. Iye anakula ndipo Yehova anamudalitsa. 25Mzimu wa Yehova unayamba kumulimbikitsa pamene ankakhala ku misasa ya anthu a fuko la Dani, malo amene anali pakati pa Zora ndi Esitaoli.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

士师记 13:1-25

参孙的出生

1以色列人又做耶和华视为恶的事,耶和华就把他们交在非利士人手中四十年。

2琐拉城住了一个支派的人,名叫玛挪亚。他妻子不能生养,没有孩子。 3耶和华的天使向那妇人显现,对她说:“你虽然多年不育,但不久你必怀孕生一个儿子。 4所以,你要留心,不可喝淡酒和烈酒,不可吃不洁之物。 5你必怀孕生一个儿子,你不可为他剃头,因为他一出生就要归给上帝做拿细耳人13:5 拿细耳人”参见民数记6:1-8。他要从非利士人手中拯救以色列人。” 6妇人就去对丈夫说:“有一位上帝的仆人向我显现,他的容貌像上帝的天使,非常可畏。我没有问他从哪里来,他也没有把名字告诉我。 7他对我说,‘你必怀孕生一个儿子,所以不可喝淡酒和烈酒,不可吃不洁之物,因为孩子一出生就要献给耶和华,终生做拿细耳人。’”

8玛挪亚向耶和华祈求说:“主啊,求你再派你的仆人到这里来,教我们怎样照顾要出生的孩子。” 9上帝应允了他的祈求。他妻子正坐在田间的时候,上帝的天使再次向她显现。当时她丈夫玛挪亚不在场。 10她赶忙跑去告诉她丈夫说:“那天来的那人又向我显现了。” 11玛挪亚立刻跟随妻子来到那人面前,问他:“那天跟我妻子说话的就是你吗?”他答道:“是我。” 12玛挪亚问道:“你的话应验以后,我们应该怎样抚养这孩子?他该做什么?” 13耶和华的天使说:“你的妻子必须谨记我的一切吩咐。 14她不可吃葡萄树所结的果实,淡酒和烈酒都不可喝,不可吃任何不洁之物。她必须遵行我的一切吩咐。”

15玛挪亚说:“请你留下来,我们要预备一只山羊羔给你吃。” 16当时,玛挪亚仍然不知道那人是耶和华的天使。天使说:“我就是留下来也不会吃你预备的食物。如果你预备燔祭,就把它献给耶和华吧!” 17玛挪亚说:“请告诉我你的名字,当一切应验的时候,我们好向你表达敬意。” 18耶和华的天使说:“何必问我的名字呢?我的名字奇妙难测。” 19于是,玛挪亚就把一只山羊羔和素祭放在磐石上,献给耶和华。就在这时候,天使在玛挪亚和他妻子面前行了一件奇妙的事: 20火焰从祭坛上升起的时候,耶和华的天使也在祭坛的火焰中升上去了。玛挪亚夫妇见状,便俯伏在地。

21耶和华的天使后来没再向玛挪亚和他妻子显现,玛挪亚才知道他是耶和华的天使。 22玛挪亚对妻子说:“我们必死无疑,因为我们看见了上帝。” 23他妻子却说:“如果耶和华要杀我们,祂就不会接受我们的燔祭和素祭了,也不会让我们看见这些事并告诉我们这些话了。”

24后来玛挪亚的妻子生了个儿子,她给孩子取名叫参孙。这孩子渐渐长大,耶和华赐福给他。 25当他在琐拉以实陶之间的玛哈尼·但的时候,耶和华的灵开始感动他。