Numeri 18 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 18:1-32

Ntchito za Ansembe ndi Alevi

1Yehova anawuza Aaroni kuti, “Iwe, ana ako aamuna ndi banja la abambo ako mudzasenza tchimo la malo wopatulika, koma iwe ndi ana ako aamuna okha mudzasenza tchimo lokhudza unsembe wanu. 2Ubweretse Alevi, abale ako, kuchokera ku fuko la abambo ako kuti azikhala ndi iwe ndi kumakuthandiza pamodzi ndi ana ako amuna pamene mukutumikira mu tenti ya umboni. 3Iwowo azikutumikirani ndipo azichita ntchito zonse za ku tenti, koma asamafike pafupi ndi zipangizo za ku malo opatulika kapena guwa lansembe, kuopa kuti iwo ndi inu mungafe. 4Azikhala ndi inu ndipo azisamalira ntchito yonse ya mu tenti ya msonkhano koma munthu wina aliyense wapadera sayenera kufika pafupi nanu.

5“Inuyo muzisamalira malo wopatulika ndi guwa lansembe, kuti ukali wa Yehova usawagwerenso Aisraeli. 6Ine mwini ndasankha Alevi, abale ako, pakati pa Aisraeli ngati mphatso yako ndipo aperekedwa kwa Yehova kuti azigwira ntchito ku tenti ya msonkhano. 7Koma iwe wekha ndi ana ako aamuna muzitumikira ngati ansembe ndi zina zonse zokhudza pa guwa lansembe ndi za mʼkati mwa malo wopatulika kwambiri. Ndikukupatsani mphatso ya utumiki wa unsembe. Aliyense woyandikira malo wopatulika ayenera kuphedwa.

Zopereka za Ansembe ndi Alevi

8“Kenaka Yehova anati kwa Aaroni, ona, Ine mwini ndikukuyika kuti ukhale woyangʼanira zopereka zobwera kwa Ine; zopereka zonse zopatulika za Aisraeli zimene amapereka kwa ine ndi kuzipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ngati gawo lanu la nthawi zonse. 9Uzilandiranso gawo la zopereka zopatulika kwambiri zomwe sizinawotchedwe pa moto. Kuchokera pa mphatso zonse zimene amabweretsa kwa Ine ngati zopatulika kwambiri, nsembe zachakudya kapena nsembe zopepesera machimo, gawo limenelo ndi lako ndi ana ako aamuna. 10Muzidya zimenezo ngati zinthu zopatulika kwambiri; mwamuna aliyense adyeko. Uzitenge kukhala zopatulika.

11“Izinso ndi zako: chilichonse chopatulidwa kuchokera ku mphatso zoweyula za Aisraeli ndapereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lako la nthawi zonse. Aliyense wa mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa monga mwa mwambo angathe kudyako.

12“Ndikukupatsani mafuta onse abwino kwambiri a olivi ndi vinyo yense watsopano wabwino kwambiri ndi tirigu yense zomwe Aisraeli amapereka kwa Yehova ngati zipatso zoyamba pa zokolola zawo. 13Zipatso zonse zoyamba kucha za mʼdziko lawo zomwe amapereka kwa Yehova zidzakhala zako. Aliyense mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa angathe kudyako.

14“Chilichonse mu Israeli chomwe chapatulidwira Yehova ndi chako. 15Chilichonse choyamba kubadwa kwa munthu kaya nyama, chomwe chaperekedwa kwa Yehova ndi chako. Koma uyenera kuwombola mwana aliyense wamwamuna ndi mwana aliyense woyamba wa nyama zodetsedwa. 16Pamene zili ndi mwezi umodzi wa kubadwa, uziwombole pa mtengo wowombolera wa ndalama zisanu zasiliva, monga mwa ndalama za ku malo wopatulika.

17“Koma usawombole ana oyamba kubadwa a ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi. Iwo ndi opatulika. Uwaze magazi a nyamazi pa guwa lansembe ndi kutentha mafuta ake ngati nsembe yotentha ndi moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova. 18Nyama yake ikhale yanu monga momwe chimakhalira chidale cha nsembe yoweyula ndi ntchafu za miyendo ya kumanja, zonsezi ndi zako. 19Zonse zimene mwazichotsa ku zopereka zoyera zomwe Aisraeli anapereka kwa Yehova ndazipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lanu nthawi zonse. Ili ndi pangano losatha la mchere pamaso pa Yehova kwa iwe ndi ana ako.”

20Ndipo Yehova anati kwa Aaroni, “Iweyo sudzakhala ndi cholowa mʼdziko lawo, ndiponso sudzalandira gawo lililonse pakati pawo. Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisraeli.

21“Taonani, ndawapatsa Alevi chakhumi chonse mu Israeli ngati cholowa chawo chifukwa cha ntchito ya ku tenti ya msonkhano. 22Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo Aisraeli asamapite pafupi ndi tenti ya msonkhano. Ngati atero adzasenza zotsatira za tchimo lawo ndipo adzafa. 23Alevi ndi amene azidzagwira ntchito ya ku tenti ya msonkhano ndipo adzalangidwa chilichonse chikalakwika. Ili ndi lamulo losatha kwa mibado yawo yonse. Iwowo sadzalandira cholowa pakati pa Aisraeli. 24Mʼmalo mwake, ndikuwapatsa Aleviwo chakhumi ngati cholowa chawo chimene Aisraeli amapereka kwa Yehova. Nʼchifukwa chake zokhudza iwo ndinati: ‘Sadzakhala ndi cholowa pakati pa Aisraeli.’ ”

25Yehova anati kwa Mose, 26“Yankhula ndi Alevi ndi kunena nawo kuti, ‘Pamene mulandira chakhumi kuchoka kwa Aisraeli chimene ndimakupatsani ngati cholowa chanu, muyenera kupereka chakhumi cha choperekacho kwa Yehova. 27Chopereka chanucho chidzawerengedwa kwa inu ngati tirigu wochokera kopunthira kapena ngati mphesa zopsinya kuchokera kopsinyira mphesa. 28Mwa njira imeneyi inunso muzipereka chopereka kwa Yehova kuchokera ku chakhumi chanu chilichonse chimene mumalandira kuchokera kwa Aisraeli. Kuchokera ku chakhumicho muziperekako gawo la Yehova kwa Aaroni, wansembe. 29Muyenera kupereka monga gawo la Yehova magawo abwino kwambiri ndi opatulika a chilichonse chimene chapatsidwa kwa inu.’

30“Nena kwa Alevi: ‘Pamene mupereka gawo labwino lopambana zonse, gawo limenelo lidzawerengedwa kwa inu ngati lochokera popunthira tirigu kapenanso kopsinyira mphesa. 31Inu ndi a pa banja panu mungathe kudyera zimenezi paliponse chifukwa ndi malipiro a ntchito yanu ya ku tenti ya msonkhano. 32Popereka gawo labwino kwambirilo simudzapezeka olakwa. Mukatero simudzadetsa zopereka zoyera za Aisraeli, ndipo simudzafa.’ ”

Bibelen på hverdagsdansk

4. Mosebog 18:1-32

Præsternes og levitternes tjeneste

1Da sagde Herren til Aron: „Jeg har overdraget tjenesten ved helligdommen til levitterne. Det er deres ansvar, hvis der sker et lovbrud under tjenesten. Men præstetjenesten er overdraget til dig og dine efterkommere, og sker der noget galt der, er det jer, der bliver krævet til ansvar. 2Levitterne skal hjælpe jer under præstetjenesten foran teltet med pagtens ark. 3Men når de udfører deres arbejde, må de under ingen omstændigheder røre direkte ved nogen af de hellige ting eller ved alteret. Gør de det, skal de dø—og det skal I også. 4Levitterne skal tage sig af åbenbaringsteltet og transportere det omkring, men ingen af de andre israelitter må hjælpe til med det arbejde.

5Det er jer præster, som skal udføre tjenesten i selve helligdommen og ved alteret, så Israels folk ikke igen skal rammes af min vrede ved ikke at respektere præstetjenesten. 6Jeg har udvalgt levitterne til at hjælpe jer under jeres præstetjeneste i åbenbaringsteltet. De er en gave til jer fra Herren. 7Men du og dine efterkommere, som er mine præster, skal alene varetage altertjenesten. Det er kun jer, som har tilladelse til at gå ind bag forhænget til helligdommen, for I er mine præster. Enhver anden, der trænger ind i helligdommen, skal dø.”

Præsternes og levitternes underhold

8Herren sagde videre til Aron: „Jeg giver jer præster jeres del af de offergaver, som folket bringer til mig. Denne ordning skal gælde for altid. 9I må få de dele af de hellige ofre, som ikke skal brændes på alteret, hvad enten det er afgrødeofre, syndofre eller skyldofre. 10I skal spise dem på et helligt sted, men kun mændene må spise dem. 11De offergaver, som svinges foran alteret, skal for altid tilhøre jer og jeres familier. Både mænd, kvinder og børn må spise af disse ofre—med undtagelse af dem, der er urene på det tidspunkt.

12Det samme gælder for de høstofre, som folket bringer til mig—det første og bedste af deres olivenolie, nylavede vin, korn 13og frugter. De ofre må alle jeres familiemedlemmer få del i—med undtagelse af dem, der er urene på det tidspunkt. 14Alt hvad der tilhører mig, tilhører også jer. 15Alt det førstefødte blandt mennesker og dyr tilhører mig, og skal derfor tilhøre jer. Dog skal israelitterne løskøbe de førstefødte sønner og det førstefødte blandt alle urene dyr. 16I stedet for at bringe disse førstefødte sønner og urene dyr som offergaver, skal de en måned efter fødslen løskøbe dem med fem sølvstykker for hver.

17Hvad de førstefødte blandt hornkvæget og småkvæget angår, kan de ikke løskøbes, men de skal ofres til mig. Deres blod skal stænkes på alteret, og deres fedt skal brændes som et lifligt offer til mig. 18Men kødet skal tilhøre jer—ligesom brystet og det højre lårstykke, der svinges foran alteret, tilhører jer. 19Alle de ofre, som folket bringer til mig ved at svinge dem foran alteret, skal tilhøre jer, og I og jeres familier må spise af dem. Dette er en permanent lov, en troskabspagt18,19 På hebraisk en „saltpagt”. mellem mig på den ene side og jer og jeres efterkommere på den anden side.”

20Herren sagde videre til Aron: „I præster må ikke eje jord eller anden ejendom i landet. Hvad der tilhører mig, tilhører også jer. 21Men hvad levitterne angår, skal de modtage betaling for deres arbejde ved åbenbaringsteltet i form af den tiende, Israels folk bringer. De får nemlig heller ikke jord eller ejendom i landet.

22Fra nu af skal israelitterne, med undtagelse af præsterne og levitterne, holde sig på afstand af åbenbaringsteltet. Gør de ikke det, skal de dø. 23Levitterne skal gøre tjeneste ved åbenbaringsteltet og hjælpe præsterne, men de må ikke få del i landets jord. Det skal være en fast ordning som varer fra slægt til slægt. 24I stedet for jord får de den tiende, som israelitterne bringer til mig.”

25Herren sagde videre til Moses: 26„Sig til levitterne, at en tiendedel af den tiende, de modtager fra israelitterne, skal de give videre til mig. 27-30Det bliver deres ‚høstoffer’ og skal i mine øjne regnes på lige fod med de øvrige israelitters høstofre, der betales af det første korn fra tærskepladsen og den første vin, de producerer. Den skal bestå af den bedste del af de tiendegaver, som de modtager fra folket og denne tiende skal de overdrage til Aron som repræsentant for præsterne. 31-32Så længe levitterne sørger for at bringe den bedste del af den tiende, de selv modtager, videre til præsterne, må de spise resten, hvor de vil, sammen med deres familier, uden derved at pådrage sig skyld. Det er deres løn for det arbejde, de udfører ved åbenbaringsteltet. Men hvis de overtræder denne lov, skal de dø.”