Numeri 15 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 15:1-41

Zopereka Zapadera

1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsanilo, 3ndipo mukamadzapereka kwa Yehova, nsembe yotentha pa moto ya ngʼombe kapena nkhosa monga fungo lokoma kwa Yehova, kaya ndi nsembe yopsereza kapena nsembe zina, nsembe yapadera chifukwa cha lumbiro kapena nsembe yoperekedwa mwaufulu kapenanso yoperekedwa pa chikondwerero, 4munthu amene akubweretsa zopereka zake, azikapereka kwa Yehova chopereka chachakudya cholemera kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta wokwana lita imodzi. 5Pamodzi ndi mwana wankhosa aliyense wa nsembe yopsereza kapena nsembe ina, muzikakonzanso lita imodzi la vinyo ngati chopereka cha chakumwa.’ ”

6“Pamodzi ndi nkhosa yayimuna, muzikakonzanso chopereka cha chakudya cholemera makilogalamu awiri a ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita imodzi ndi theka, 7ndi vinyo wokwanira lita imodzi ndi theka ngati chopereka cha chakumwa. Muzikapereka monga nsembe yopereka fungo lokoma kwa Yehova.

8“ ‘Pamene mukukonza mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse: ya lumbiro lapadera kapena nsembe yachiyanjano kwa Yehova, 9pamodzi ndi mwana wangʼombe wamwamunayo muzibweretsa nsembe yachakudya yolemera makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta okwana malita awiri. 10Komanso muzibweretsa vinyo wokwanira malita awiri monga chopereka chachakumwa. Imeneyi idzakhala chopereka chotentha pa moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova. 11Ngʼombe yayimuna iliyonse kapena nkhosa yayimuna iliyonse, mwana wankhosa aliyense kapena mbuzi yayingʼono, zizikonzedwa motere. 12Ngakhale zingachuluke chotani, chitani izi kwa iliyonse ya nyamazo.

13“ ‘Mbadwa iliyonse ya mu Israeli izichita zimenezi pamene ibweretsa nsembe yotentha pa moto kuti ikhale fungo lokoma kwa Yehova. 14Ku mibado yanu yonse ya mʼtsogolo, pamene mlendo kapena wina aliyense wokhala pakati panu apereka chopereka chotentha pa moto kuti chikhale fungo lokoma kwa Yehova, azichita mofanana ndi momwe inu mumachitira. 15Gulu lonse likhale ndi malamulo ofanana a inu kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya kwa mibado imene ikubwera. Inuyo ndi mlendo mudzakhala wofanana pamaso pa Yehova. 16Mudzakhale ndi malamulo ndi miyambo yofanana, inuyo ndi mlendo wokhala pakati panu.’ ”

17Yehova anawuza Mose kuti, 18“Yankhula ndi Aisraeli ndipo unene kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukutengeraniko 19ndipo mukakadya chakudya cha mʼdzikolo, mukapereke gawo lina kwa Yehova monga chopereka. 20Pa buledi wanu woyamba, mukapereke mmodzi monga nsembe, ngati chopereka chochokera ku malo wopunthira tirigu. 21Pa mibado yanu yonse muzidzapereka chopereka ichi kwa Yehova kuchokera ku zakudya zanu zoyamba za mʼnthaka.

Chopereka Chopepesera Machimo Ochita Mosadziwa

22“ ‘Ndipo ngati muchimwa mosadziwa posasunga ena mwa malamulo awa amene Yehova wapereka kwa Mose, 23lina lililonse mwa malamulo a Yehova amene wapereka kwa inu kudzera mwa Mose, kuyambira tsiku limene Yehova anawapereka mpaka mibado ya mʼtsogolo, 24ndipo ngati zimenezi zachitika osati mwadala ndipo gulu lonse silinadziwe, zikatero gulu lonselo lipereke mwana wangʼombe wamwamuna monga nsembe yopsereza kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova pamodzinso ndi chopereka chachakudya ndi chopereka cha chakumwa ndi mbuzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo potsata zimene zinalamulidwa. 25Wansembe apereke nsembe yopepesera machimo a gulu lonse la Aisraeli, ndipo adzakhululukidwa, pakuti linali tchimo lochita mosadziwa. Ndipo chifukwa cha tchimo lawolo, abweretse kwa Yehova nsembe yotentha pa moto ndi nsembe yopepesera machimo. 26Gulu lonse la Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo adzakhululukidwa chifukwa anthu onsewo anachimwa mosadziwa.

27“ ‘Koma ngati munthu mmodzi achimwa mosadziwa, ayenera kubweretsa mbuzi yayikazi ya chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. 28Wansembe apereke nsembe yopepesera machimowo pamaso pa Yehova chifukwa cha munthu yemwe anachimwa mosadziwayo. Nsembe yopepesera tchimo lakelo ikaperekedwa, munthuyo adzakhululukidwa. 29Lamulo lomweli ligwiritsidwe ntchito kwa aliyense wochimwa mosadziwa, kaya ndi mbadwa ya mu Israeli kapena mlendo.

30“ ‘Koma aliyense amene achimwa mwadala, kaya ndi mbadwa kapena mlendo, nachitira chipongwe Yehova, ameneyo achotsedwe ndithu pakati pa anthu ake. 31Popeza wanyoza mawu a Yehova ndi kuphwanya malamulo ake. Munthu ameneyo achotsedwe ndithu, kuchimwa kwake kudzakhala pa iyeyo.’ ”

Wosasunga Sabata Aphedwa

32Aisraeli ali mʼchipululu, munthu wina anapezeka akutola nkhuni tsiku la Sabata. 33Amene anamupeza akutola nkhunizo anabwera naye kwa Mose ndi Aaroni ndi kwa gulu lonse 34ndipo anamutsekera mʼndende chifukwa sankadziwa choti achite naye. 35Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Munthu ameneyu ayenera kuphedwa. Gulu lonse liyenera kumugenda ndi miyala kunja kwa msasa.” 36Choncho gululo linamutengera kunja kwa msasa ndi kumupha pomugenda ndi miyala, monga momwe Yehova analamulira Mose.

Mphonje pa Zovala

37Yehova anawuza Mose kuti, 38“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pa mibado yanu yonse muzisokerera mphonje pa ngodya za zovala zanu ndipo pa ngodya ya mphonje iliyonse azisokererapo chingwe chobiriwira. 39Mudzakhala ndi mphonje zimenezi kuti mukaziona muzikakumbukira malamulo onse a Yehova ndi kuwamvera kuti musamatsatenso zilakolako za mʼmitima mwanu ndi za maso anu. 40Motero mudzakumbukira kumvera malamulo anga ndipo mudzakhala opatulikira a Mulungu wanu. 41Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”

Bibelen på hverdagsdansk

4. Mosebog 15:1-41

Yderligere regler for ofringer

1Herren sagde til Moses: 2„Giv Israels folk denne besked fra mig: Når folket engang kommer ind i det land, jeg vil give dem, 3-5og de ønsker at glæde mig med et ildoffer, hvad enten det er et brændoffer eller et slagtoffer, skal de udvælge offerdyret blandt deres småkvæg eller hornkvæg. Hvert eneste offer—hvad enten det drejer sig om et almindeligt offer, et løfteoffer, et frivilligt offer eller et særligt offer i forbindelse med de årlige festdage—skal bringes sammen med et afgrødeoffer. Hvis det er et lam, de ofrer, skal afgrødeofferet bestå af to liter fint mel blandet med en liter olivenolie. Desuden skal der ofres et drikoffer bestående af en liter vin.

6Hvis de ofrer en vædder, skal det medfølgende afgrødeoffer bestå af fire liter fint mel blandet med godt en liter olivenolie 7og drikofferet skal bestå af godt en liter vin. Duften af dette offer vil glæde mig.

8-9Hvis de ofrer en ung tyr, skal det medfølgende afgrødeoffer bestå af seks liter fint mel blandet med to liter olivenolie, 10og drikofferet skal bestå af to liter vin. Duften af dette offer vil glæde mig.

11-12Det er reglerne for de ofre, der skal følge med, hvad enten offerdyret er en tyr, en vædder, et lam eller et gedekid— 13-14og reglerne er de samme for israelitter som for de fremmede, der bor iblandt dem. 15-16Denne lov skal gælde fremover fra slægt til slægt. Samme lov skal gælde for alle.”

17Herren sagde også dette til Moses: 18„Sig til Israels folk: Når I kommer ind i det land, jeg vil give jer, 19-21skal I ofre en smagsprøve af landets første høst til mig ved at tage noget korn fra tærskepladsen og bage et grovbrød af det. Loven om et offer fra den første høst skal gælde fremover fra slægt til slægt.

22-24Hvis I eller jeres efterkommere som folk betragtet uforvarende kommer til at overtræde de love, som jeg har givet jer gennem Moses indtil nu, skal hele folket, så snart fejltagelsen er opdaget, ofre en ung tyr som brændoffer. Da vil jeg anerkende duften af brændofferet som et lifligt offer, når det ofres sammen med det sædvanlige afgrødeoffer og drikoffer samt et syndoffer bestående af en gedebuk. 25Præsten skal på den måde skaffe soning for hele folket, og da skal de blive tilgivet, fordi der var tale om en fejltagelse, som er rettet, efter at der er ofret et brændoffer og et syndoffer. 26Da skal hele folket få tilgivelse, også de fremmede, der bor iblandt jer, fordi der var tale om uforvarende, kollektiv synd.

27Hvis en enkeltperson uforvarende kommer til at overtræde lovene, skal han ofre en etårs hun-ged som syndoffer; 28og præsten skal skaffe ham soning, hvorefter han er tilgivet. 29Denne lov gælder også de fremmede, der bor iblandt jer.

30-31Men enhver der synder forsætligt—hvad enten han er indfødt israelit eller fremmed—skal udryddes, fordi han har vist ringeagt for mig og mine bud og med vilje overtrådt min lov. Derfor skal han bære sin straf.”

Straffen for at bryde sabbatsloven

32En sabbatsdag, da Israels folk opholdt sig i ørkenen, blev en mand taget på fersk gerning i at gå og samle brænde. 33Manden blev ført til Moses og Aron og de øvrige ledere, 34som fængslede ham, indtil de kunne få en afgørelse fra Herren angående mandens forseelse.

35Da sagde Herren til Moses: „Manden skal føres uden for lejren og stenes til døde af hele folket.” 36Så førte man ham uden for lejren og henrettede ham, som Herren havde befalet.

Om kvaster på kappen

37Herren sagde til Moses: 38„Sig til Israels folk, at de fremover fra slægt til slægt skal gøre det til en vane at sætte kvaster i hjørnerne af deres kapper; kvasterne skal sys i med purpurtråd. 39Hensigten med denne ordning er at minde jer selv om at følge mine befalinger. Hver gang I får øje på kvasten, skal I tænke på at adlyde mig i stedet for at adlyde jeres egne lyster og indskydelser, som I har så let ved at gøre. 40Når I ser kvasten, skal I rette jeres indre blik på mig, så I kommer til at ligne mig i hellighed; 41for jeg er Herren, jeres Gud, der førte jer ud af Egyptens land—ja, jeg er Herren, jeres Gud.”