Mlaliki 8 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mlaliki 8:1-17

1Ndani angafanane ndi munthu wanzeru?

Ndani angadziwe kutanthauzira zinthu?

Nzeru imabweretsa chimwemwe pa nkhope ya munthu

ndipo imasintha maonekedwe ake awukali.

Za Kumvera Mfumu

2Ine ndikuti, mvera lamulo la mfumu, chifukwa unalumbira pamaso pa Mulungu. 3Usafulumire kuchoka pamaso pa mfumu. Usawumirire chinthu choyipa, pakuti mfumu idzachita chilichonse chomwe imasangalatsidwa nacho. 4Popeza mawu a mfumu ali ndi mphamvu, ndani anganene kwa mfumuyo kuti, “Kodi mukuchita chiyani?”

5Aliyense amene amamvera lamulo lake sadzapeza vuto lililonse,

ndipo munthu wanzeru amadziwa nthawi yoyenera ndi machitidwe ake.

6Pakuti pali nthawi yoyenera ndiponso machitidwe a chinthu chilichonse,

ngakhale kuti mavuto ake a munthu amupsinja kwambiri.

7Popeza palibe munthu amene amadziwa zamʼtsogolo,

ndani angamuwuze zomwe zidzachitika mʼtsogolo?

8Palibe munthu amene ali ndi mphamvu yolamulira mpweya wa moyo kuti athe kuwusunga,

choncho palibe amene ali ndi mphamvu pa tsiku la imfa yake.

Nkhondo sithawika; tsono anthu ochita zoyipa,

kuyipa kwawoko sikudzawapulumutsa.

9Zonsezi ndinaziona pamene ndinalingalira mu mtima mwanga, zonse zimene zimachitika pansi pano. Ilipo nthawi imene ena amalamulira anzawo mwankhanza. 10Kenaka, ndinaona anthu oyipa akuyikidwa mʼmanda, iwo amene ankalowa ndi kumatuluka mʼmalo opatulika ndipo ankatamandidwa mu mzindawo pamene ankachita zimenezi. Izinso ndi zopandapake.

11Pamene chigamulo cha anthu opalamula mlandu chikuchedwa, mitima ya anthu imadzaza ndi malingaliro ochita zolakwa. 12Ngakhale munthu woyipa apalamule milandu yambirimbiri, nʼkumakhalabe ndi moyo wautali, ine ndikudziwa kuti anthu owopa Mulungu zinthu zidzawayendera bwino, omwe amapereka ulemu pamaso pa Mulungu. 13Koma popeza oyipa saopa Mulungu zinthu sizidzawayendera bwino, ndipo moyo wawo sudzakhalitsa monga mthunzi.

14Palinso chinthu china chopanda phindu chomwe chimachitika pa dziko lapansi: anthu olungama amalangidwa ngati anthu osalungama. Pamene oyipa amalandira zabwino ngati kuti ndi anthu abwino. 15Nʼchifukwa chake ndikuti munthu azikondwerera moyo, pakuti munthu alibe chinanso chabwino pansi pano choposa kudya, kumwa ndi kumadzikondweretsa. Akamatero, munthuyo adzakhala ndi chimwemwe pa ntchito yake masiku onse a moyo wake amene Mulungu wamupatsa pansi pano.

16Pamene ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe nzeru ndi kuonetsetsa ntchito za munthu pa dziko lapansi, osapeza tulo usana ndi usiku, 17pamenepo ndinaona zonse zimene Mulungu anazichita. Palibe munthu amene angathe kuzimvetsa zonse zimene zimachitika pansi pano. Ngakhale munthu ayesetse kuzifufuza, sangathe kupeza tanthauzo lake. Ngakhale munthu wanzeru atanena kuti iye amadziwa, sangathe kuzimvetsetsa zinthuzo.

Bibelen på hverdagsdansk

Prædikerens Bog 8:1-17

1Hvem vil ikke gerne have visdom? Hvem vil ikke gerne kunne finde en løsning på problemerne? Visdom gør et menneske mere forstående og mindre hård.

Adlyd Gud og kongen

2Adlyd kongens befalinger, som du er forpligtet til over for Gud. 3Gør ikke oprør mod kongen, for han straffer dem, der er ulydige imod ham. 4Bag kongens befaling er der myndighed og magt, og ingen vover at sætte spørgsmålstegn ved hans beslutning. 5Den, der adlyder hans befalinger, kan færdes trygt, og den vise ved, at når tiden er inde, vil retfærdigheden ske fyldest. 6Der kommer et tidspunkt, hvor dommen afsiges, for menneskenes ondskab tynger dem ned. 7Ingen kender fremtiden, og hvem kan vide, hvornår dommens time kommer?

8Ingen er herre over vinden, så de kan spærre den inde, og ingen er herre over, hvornår de skal dø. Ingen slipper for militærtjeneste under en krig, og den gudløse slipper heller ikke for sin dom.

De gode og de onde

9Jeg har tænkt dybt over verdens tilstand, hvor det ene menneske har magt til at undertrykke det andet. 10Jeg har set onde mennesker færdes hjemmevant i helligdommen og blive rost ude i byen til trods for al deres ondskab. Ja, selv ved deres begravelse blev de rost til skyerne. Hvor meningsløst! 11Hvis en forbrydelse ikke straffes med det samme, får mennesker mod til at fortsætte med deres ondskab. 12Selv om en ond person begår 100 forbrydelser, og det lykkes ham at undgå straf, så er jeg dog overbevist om, at de gudfrygtige er bedre stillet, netop fordi de frygter Gud. 13Men de onde går det ikke godt. De oplever ikke livets aften, hvor skyggerne bliver lange, for de frygter ikke Gud.

14Endnu en uretfærdighed er udbredt på jorden: Det sker, at ulykker rammer de gode i stedet for de onde, og at de onde får den belønning, som de gode havde fortjent. Er det ikke meningsløst? 15Derfor kan man lige så godt nyde livet, så længe man har det. Spis, drik og vær glad. På den måde får man dog nogen trøst midt i det hårde liv, Gud har givet menneskene på denne jord.

16Da jeg søgte efter visdom, iagttog jeg dag og nat, hvad mennesker foretog sig på jorden. 17Jeg så, at Guds værk var så stort, at ingen kan fatte det, uanset hvor ihærdigt de prøver at forstå det. De, der påstår at være kloge nok til at fatte det, har ikke forstået noget som helst.