Mlaliki 3 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mlaliki 3:1-22

Chilichonse Chili ndi Nthawi

1Chinthu chilichonse chili ndi nthawi yake,

ndi nyengo yake yomwe anayika Mulungu:

2Nthawi yobadwa ndi nthawi yomwalira,

nthawi yodzala ndi nthawi yokolola.

3Nthawi yakupha ndi nthawi yochiritsa,

nthawi yogwetsa ndi nthawi yomanga.

4Nthawi yomva chisoni ndi nthawi yosangalala,

nthawi yolira maliro ndi nthawi yovina.

5Nthawi yotaya miyala ndi nthawi yokundika miyala,

nthawi yokumbatirana ndi nthawi yoleka kukumbatirana.

6Nthawi yofunafuna ndi nthawi yoleka kufunafuna,

nthawi yosunga ndi nthawi yotaya.

7Nthawi yongʼamba ndi nthawi yosoka,

nthawi yokhala chete ndi nthawi yoyankhula.

8Nthawi yokondana ndi nthawi yodana,

nthawi ya nkhondo ndi nthawi ya mtendere.

9Kodi wantchito amapeza phindu lanji pa ntchito yake yolemetsa? 10Ine ndinaona chipsinjo chimene Mulungu anayika pa anthu. 11Iye anapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthawi yake. Anayika nzeru zamuyaya mʼmitima ya anthu; komabe anthuwo sangathe kuzindikira zomwe Mulungu wachita kuyambira pa chiyambi mpaka chimaliziro. 12Ine ndikudziwa kuti palibenso kanthu kabwino kwa anthu kopambana kusangalala ndi kuchita zabwino pamene ali ndi moyo. 13Ndi mphatso ya Mulungu kwa munthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ndi ntchito zake zolemetsa. 14Ndikudziwa kuti chilichonse chimene Mulungu amachita chidzakhala mpaka muyaya; palibe zimene zingawonjezedwe kapena kuchotsedwa. Mulungu amazichita kuti anthu azimuopa.

15Chilichonse chimene chilipo chinalipo kale,

ndipo chimene chidzakhalapo chinalipo poyamba;

Mulungu amabwezanso zakale zimene zinapita kuti zichitikenso.

16Ndipo ndinaona chinthu chinanso pansi pano:

ku malo achiweruzo, kuyipa mtima kuli komweko,

ku malo achilungamo, kuyipa mtima kuli komweko.

17Ndinalingalira mu mtima mwanga kuti;

“Mulungu adzaweruza

olungama pamodzi ndi oyipa omwe,

pakuti anayika nthawi yochitikira chinthu chilichonse,

nthawi ya ntchito iliyonse.”

18Ndinalingaliranso kuti, “Kunena za anthu, Mulungu amawayesa ndi cholinga choti awaonetse kuti iwo ali ngati nyama. 19Zimene zimachitikira munthu, zomwezonso zimachitikira nyama; chinthu chimodzi chomwecho chimachitikira onse: Monga munthu amafa momwemonso nyama imafa. Zonsezi zimapuma mpweya umodzimodzi omwewo; munthu saposa nyama. Zonsezi ndi zopandapake. 20Zonse zimapita kumodzimodzi; zonsezi zimachokera ku fumbi, ndipo zimabwereranso ku fumbi komweko. 21Kodi ndani amene amadziwa ngati mzimu wa munthu umakwera kumwamba, ndipo mzimu wa nyama umatsikira kunsi kwa dziko?”

22Kotero ndinaona kuti palibe chinthu chabwino kwa munthu kuposa kuti munthu azisangalala ndi ntchito yake, pakuti ichi ndiye chake chenicheni. Pakuti ndani amene angamubweretse kuti adzaone zimene zidzamuchitikira iye akadzamwalira?

Bibelen på hverdagsdansk

Prædikerens Bog 3:1-22

Tid til alt

1Alt i livet har sin egen tid:

2Tid til at fødes og tid til at dø,

tid til at plante og tid til at høste,

3tid til at dræbe og tid til at læge,

tid til at bryde ned og tid til at bygge op,

4tid til at græde og tid til at le,

tid til at sørge og tid til at danse,

5tid til at dænge sten på en mark3,5 Jf. 2.Kong. 3,25. og tid til at samle dem,

tid til at omfavne og tid til ikke at omfavne,

6tid til at finde og tid til at miste,

tid til at gemme og tid til at kassere,

7tid til at flænge og tid til at lappe,

tid til tavshed og tid til tale,

8tid til at elske og tid til at hade,

tid til krig og tid til fred.

Gud er suveræn

9Hvad har man så ud af alt sit slid? 10Gud har givet menneskene mange ting at beskæftige sig med. 11Alt har han skabt, så det har sin tid og tjener hans plan. Men skønt han har lagt evigheden i vores hjerter, fatter vi dog ikke hans plan og virke fra begyndelsen til enden. 12Derfor er det bedste, man kan gøre, at glæde sig og nyde livet, så længe det er muligt, 13for det at spise og drikke og finde tilfredsstillelse i sit arbejde er en Guds gave.

14Jeg ved, at hvad Gud gør, står ikke til at ændre. Man kan hverken lægge noget til eller trække noget fra. Hans hensigt er, at vi skal have ærefrygt for ham.

15Hvad der sker nu, er allerede sket før, og hvad der sker i fremtiden, er også sket før. Gud lader historien gentage sig.

16Jeg lagde også mærke til, at der var gudløshed og ondskab, hvor der burde være retfærdighed og godhed, 17og jeg sagde til mig selv: „Når tiden er inde, vil Gud dømme de gode såvel som de onde.” 18-19Gud lader verden gå sin gang for at lade os forstå, at den samme skæbne venter både mennesker og dyr: Alle indånder de den samme luft, og alle skal de dø en dag. Mennesket er i det stykke ikke bedre stillet end et dyr, for begges liv synes at være uden formål. 20Alle ender samme sted, for af jord er de kommet, og til jord skal de blive. 21Hvem ved, om menneskets ånd går opad, og dyrets ånd går nedad?

22Jeg fandt altså, at det bedste for et menneske er at glæde sig ved sit arbejde. Ingen af os kan vide, hvad der sker efter døden.