Miyambo 29 – CCL & TNCV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 29:1-27

1Munthu amene amawumitsabe khosi lake atadzudzulidwa kwambiri,

adzawonongeka mwadzidzidzi popanda chomuchiritsa.

2Anthu olungama akamalamulira mʼdziko anthu amakondwa,

koma ngati dziko lilamulidwa ndi anthu oyipa mtima anthu amadandaula.

3Munthu amene amakonda nzeru amasangalatsa abambo ake,

koma woyenda ndi akazi achiwerewere amasakaza chuma chake.

4Mfumu imalimbitsa dziko poweruza mwachilungamo,

koma mfumu imene imawumiriza anthu kuti ayipatse mphatso imawononga dziko.

5Munthu woshashalika mnzake,

akudziyalira ukonde mapazi ake.

6Munthu woyipa amakodwa ndi machimo ake,

koma wochita chilungamo amayimba lokoma.

7Munthu wolungama amasamalira anthu osauka,

koma woyipa salabadira zimenezi.

8Anthu onyoza atha kuwutsa ziwawa mu mzinda,

koma anthu anzeru amaletsa ukali.

9Ngati munthu wanzeru atsutsana ndi chitsiru,

chitsirucho chimachita phokoso ndi kumangoseka ndipo sipakhala mtendere.

10Anthu okhetsa magazi amadana ndi munthu wangwiro

koma anthu olungama amasamalira moyo wake.

11Munthu wopusa amaonetsa mkwiyo wake,

koma munthu wanzeru amadzigwira.

12Ngati wolamulira amvera zabodza,

akuluakulu ake onse adzakhala oyipa.

13Munthu wosauka ndi munthu wopondereza anzake amafanana pa kuti:

Yehova ndiye anawapatsa maso onsewa.

14Ngati mfumu iweruza osauka moyenera,

mpando wake waufumu udzakhazikika nthawi zonse.

15Ndodo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru

koma mwana womulekerera amachititsa amayi ake manyazi.

16Oyipa akamalamulira zoyipa zimachuluka,

koma anthu olungama adzaona kugwa kwa anthu oyipawo.

17Umulange mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere

ndi kusangalatsa mtima wako.

18Ngati uthenga wochokera kwa Yehova supezeka anthu amangochita zofuna zawo;

koma wodala ndi amene amasunga malamulo.

19Munthu wantchito sangalangizidwe ndi mawu okha basi;

ngakhale awamvetse mawuwo sadzatha kuchitapo kanthu.

20Ngakhale munthu wa uchitsiru nʼkuti ndiponi popeza chikhulupiriro chilipo

kuposa munthu wodziyesa yekha kuti ndi wanzeru poyankhula.

21Ngati munthu asasatitsa wantchito wake kuyambira ali mwana,

potsirizira adzapeza kuti wantchitoyo wasanduka mlowachuma wake.

22Munthu wamkwiyo amayambitsa mikangano,

ndipo munthu waukali amachita zolakwa zambiri.

23Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa,

koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.

24Woyenda ndi munthu wakuba ndi mdani wa moyo wake womwe;

amalumbira koma osawulula kanthu.

25Kuopa munthu kudzakhala ngati msampha,

koma aliyense amene amadalira Yehova adzatetezedwa.

26Anthu ambiri amafunitsitsa kuti wolamulira awakomere mtima,

koma munthu amaweruzidwa mwachilungamo ndi thandizo la Yehova basi.

27Anthu olungama amanyansidwa ndi anthu achinyengo;

koma anthu oyipa amanyansidwa ndi anthu a mtima wowongoka.

Thai New Contemporary Bible

สุภาษิต 29:1-27

1ผู้ที่ถูกตักเตือนบ่อยๆ แต่ยังทำคอแข็งไม่ฟัง

จะแหลกสลายเกินเยียวยาในชั่วพริบตา

2เมื่อคนชอบธรรมเจริญ ผู้คนก็ชื่นชมยินดี

เมื่อคนชั่วขึ้นปกครอง ผู้คนก็โอดครวญ

3ชายที่รักสติปัญญาทำให้พ่อสุขใจ

แต่คนที่คบหาสมาคมกับหญิงโสเภณีก็จะหมดเนื้อหมดตัว

4กษัตริย์สร้างความมั่นคงให้ชาติด้วยความยุติธรรม

แต่กษัตริย์ที่รับสินบน29:4 หรือให้สินบนก็ทำลายชาติ

5ผู้ที่ประจบสอพลอเพื่อนบ้านของตน

ก็กางข่ายไว้ดักเท้าของตน29:5 หรือของเขา

6คนเลวติดกับเพราะบาปของตน

แต่คนชอบธรรมโห่ร้องยินดี

7คนชอบธรรมใส่ใจในความยุติธรรมเพื่อผู้ยากไร้

แต่คนชั่วไม่แยแส

8คนชอบเยาะเย้ยทำให้บ้านเมืองโกลาหล

แต่คนฉลาดทำให้ความโกลาหลสงบลง

9หากคนฉลาดต้องเผชิญหน้ากับคนโง่ในศาล

คนโง่ก็จะโกรธจนตัวสั่น หัวเราะเย้ยหยัน และไม่มีความสงบสุข

10คนกระหายเลือดเกลียดชังคนสุจริต

และหาทางกำจัดผู้ที่เที่ยงธรรม

11คนโง่เขลาระบายความโกรธเต็มที่

แต่คนฉลาดจะสงบนิ่งได้ในที่สุด

12ถ้าผู้ครอบครองฟังความเท็จ

ข้าราชการทุกคนของเขาจะกลายเป็นคนชั่วไปด้วย

13ผู้ยากไร้และผู้กดขี่ข่มเหงก็เหมือนกันอย่างหนึ่ง

คือองค์พระผู้เป็นเจ้าประทานตาที่แลเห็นให้พวกเขาทั้งคู่

14หากกษัตริย์ให้ความเที่ยงธรรมแก่ผู้ยากไร้

ราชบัลลังก์ก็จะยืนยงเสมอ

15ไม้เรียวและการลงโทษจะให้ปัญญา

แต่เด็กที่ถูกปล่อยปละละเลยจะทำให้แม่อับอายขายหน้า

16เมื่อคนชั่วเจริญ บาปก็ทวีขึ้น

แต่คนชอบธรรมจะเห็นความล่มจมของเหล่าคนชั่ว

17จงอบรมสั่งสอนลูกของเจ้า แล้วเขาจะทำให้เจ้ามีสันติสุข

เขาจะทำให้เจ้าชื่นอกชื่นใจ

18ในที่ซึ่งไม่มีการเผยพระวจนะ สังคมก็โกลาหลวุ่นวาย

แต่ความสุขมีแก่ผู้ที่รักษาบทบัญญัติ

19จะอบรมสั่งสอนคนรับใช้ด้วยคำพูดอย่างเดียวไม่ได้

แม้เขาเข้าใจ เขาก็ไม่ยอมทำตาม

20เจ้าเห็นคนที่พูดพล่อยๆ หรือไม่?

ยังมีความหวังสำหรับคนโง่มากกว่าเขา

21การประคบประหงมคนรับใช้ตั้งแต่เด็ก

เขาจะนำความทุกข์โศกมาให้29:21 หรือเขาจะกลายเป็นลูกหรือเขาจะกลายเป็นผู้รับมรดกในที่สุด

22คนขี้โมโหก่อการวิวาท

และคนเลือดร้อนทำบาปมากมาย

23ความหยิ่งผยองทำให้คนเราตกต่ำ

ส่วนผู้ที่จิตใจถ่อมสุภาพได้รับเกียรติ

24ผู้ที่สมคบกับขโมยก็เป็นศัตรูกับตัวเอง

ต้องสาบานในศาลแต่ไม่กล้าเป็นพยาน

25ความกลัวของคนเป็นเพียงกับดัก

แต่ผู้ที่วางใจในองค์พระผู้เป็นเจ้าก็ปลอดภัย

26หลายคนวิ่งเต้นเข้าหาเจ้านาย

แต่คนเราได้รับความยุติธรรมจากองค์พระผู้เป็นเจ้า

27คนอยุติธรรมชิงชังคนชอบธรรม

แต่คนเที่ยงตรงชิงชังคนชั่ว