Masalimo 84 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 84:1-12

Salimo 84

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Gititi. Salimo la ana a Kora.

1Malo anu okhalamo ndi okomadi,

Inu Yehova Wamphamvuzonse!

2Moyo wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka,

kufuna mabwalo a Yehova;

Mtima wanga ndi thupi langa zikufuwulira

Mulungu wamoyo.

3Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo,

ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa,

kumene amagonekako ana ake

pafupi ndi guwa lanu la nsembe,

Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.

4Odala amene amakhala mʼNyumba yanu;

nthawi zonse amakutamandani.

Sela

5Odala amene mphamvu yawo ili mwa Inu,

mitima yawo ikufunitsitsa kuyenda mʼmisewu yopita ku Ziyoni.

6Pamene akudutsa chigwa cha Baka,

amachisandutsa malo a akasupe;

mvula ya chizimalupsa imadzazanso mayiwe ake.

7Iwo amanka nakulirakulira mphamvu

mpaka aliyense ataonekera pamaso pa Mulungu mu Ziyoni.

8Imvani pemphero langa, Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse;

mvereni Inu Mulungu wa Yakobo.

Sela

9Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu;

yangʼanani mokoma mtima pa wodzozedwa wanu.

10Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi

kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000;

Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga

kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.

11Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango;

Yehova amapereka chisomo ndi ulemu;

Iye sawamana zinthu zabwino

iwo amene amayenda mwangwiro.

12Inu Yehova Wamphamvuzonse,

wodala ndi munthu amene amakhulupirira Inu.

New Serbian Translation

Псалми 84:1-12

Псалам 84

Хоровођи. Радосница потомака Корејевих. Псалам.

1О, Господе над војскама,

дивно ли је боравиште твоје!

2Чезне ми и копни душа

за двориштем Господњим!

Срце ми и тело кличу живом Богу!

3Крај твојих жртвеника –

о, Господе над војскама,

Царе мој и Боже мој –

птица дом свој нађе

и ластавица гнездо своје,

у које птиће своје стави.

4Како су блажени они што бораве у твом Дому,

они што те славе без престанка. Села

5Како је блажен човек коме је у теби снага,

онај чије срце жели к теби да путује.

6Они што пролазе сузном долином

чине је извором,

благослове јој рана киша носи.

7Путују, и све су силнији,

док се свако не покаже Богу на Сиону.

8О, Господе, Боже над војскама, чуј молитву моју!

Пригни ухо, о, Јаковљев Боже!

9Штит наш погледај, о, Боже,

и запази лице свог помазаника.

10Јер бољи је и један дан у твојим двориштима

него хиљаду других;

боље и да стојим на прагу Дома Бога мога,

него да боравим у шаторима злога.

11Јер Господ Бог је и сунце и штит,

Господ даје и наклоност и част.

Не узима добро беспрекорним људима.

12О, Господе над војскама,

благо сваком ко се у тебе поузда!