Masalimo 141 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 141:1-10

Salimo 141

Salimo la Davide.

1Inu Yehova ndikukuyitanani; bwerani msanga kwa ine.

Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu.

2Pemphero langa lifike kwa Inu ngati lubani;

kukweza manja kwanga kukhale ngati nsembe yamadzulo.

3Yehova ikani mlonda pakamwa panga;

londerani khomo la pa milomo yanga.

4Musalole kuti mtima wanga ukokedwere ku zoyipa;

kuchita ntchito zonyansa

pamodzi ndi anthu amene amachita zoyipa;

musalole kuti ndidye nawo zokoma zawo.

5Munthu wolungama andikanthe, chimenecho ndiye chifundo;

andidzudzule ndiye mafuta pa mutu wanga.

Mutu wanga sudzakana zimenezi.

Komabe pemphero langa nthawi zonse ndi lotsutsana ndi ntchito za anthu ochita zoyipa.

6Olamulira awo adzaponyedwa pansi kuchokera pa malo okwera kwambiri,

ndipo anthu oyipa adzaphunzira kuti mawu anga anayankhulidwa bwino.

7Iwo adzati, “Monga momwe nkhuni zimamwazikira akaziwaza,

ndi momwenso mafupa athu amwazikira pa khomo la manda.”

8Koma maso anga akupenyetsetsa Inu Ambuye Wamphamvuzonse;

ndimathawira kwa Inu, musandipereke ku imfa.

9Mundipulumutse ku misampha imene anditchera,

ku makhwekhwe amene anthu oyipa andikonzera.

10Anthu oyipa akodwe mʼmaukonde awo,

mpaka ine nditadutsa mwamtendere.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

詩篇 141:1-10

第 141 篇

求上帝蔭庇

大衛的詩。

1耶和華啊,

我向你呼求,求你快來幫助我;

我向你呼求的時候,求你垂聽。

2願我的禱告如香升到你面前,

願我舉手所獻的禱告如同晚祭。

3耶和華啊,

求你守住我的口,

看住我的嘴。

4耶和華啊,求你不要讓我的心偏向邪惡,

免得我與惡人同流合污;

也不要讓我吃他們的美食。

5我情願受義人出於愛心的責打,

他們的責打是良藥,

我不會逃避。

我要不斷地用禱告抵擋惡人的行徑。

6他們的首領被拋下懸崖的時候,

他們就會知道我所言不虛。

7那些惡人的骨頭散落在墓旁,

好像耕田翻起的土塊。

8主耶和華啊,

我仰望你,我投靠你,

求你不要讓我遭害。

9求你不要使我落入惡人設下的網羅,

不要掉進他們的陷阱。

10願他們作繭自縛,

而我可以安然逃脫。