Masalimo 107 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 107:1-43

BUKU LACHISANU

Masalimo 107–150

Salimo 107

1Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;

pakuti chikondi chake ndi chosatha.

2Owomboledwa a Yehova anene zimenezi

amene Iyeyo anawawombola mʼdzanja la mdani,

3iwo amene anawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko,

kuchokera kumadzulo ndi kummawa, kuchokera kumpoto ndi kummwera.

4Ena anayendayenda mʼchipululu mopanda kanthu,

osapeza njira yopitira ku mzinda kumene akanakakhazikikako.

5Iwo anamva njala ndi ludzu,

ndipo miyoyo yawo inafowokeratu.

6Pamenepo analirira Yehova mʼmavuto awo

ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo.

7Iye anawatsogolera mʼnjira yowongoka

kupita ku mzinda umene anakakhazikikako.

8Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha

ndi chifukwa cha machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,

9pakuti Iye wapha ludzu la munthu womva ludzu

ndipo wakhutitsa wanjala ndi zinthu zabwino.

10Ena anakhala mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu,

amʼndende ovutika mʼmaunyolo achitsulo,

11pakuti iwowo anawukira mawu a Mulungu

ndi kunyoza uphungu wa Wammwambamwamba.

12Kotero Iye anawapereka kuti agwire ntchito yakalavulagaga;

anagwa pansi ndipo panalibe woti awathandize.

13Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo

ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo.

14Yehova anawatulutsa mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu

ndipo anadula maunyolo awo.

15Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha

ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,

16pakuti Iye amathyola zipata zamkuwa

ndi kudula pakati mipiringidzo yachitsulo.

17Ena anakhala zitsiru chifukwa cha njira zawo zowukira,

ndipo anamva zowawa chifukwa cha mphulupulu zawo.

18Iwo ananyansidwa ndi chakudya chilichonse

ndipo anafika pafupi ndi zipata za imfa.

19Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo

ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awowo.

20Iye anatumiza mawu ake ndi kuwachiritsa;

anawalanditsa ku manda.

21Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha

ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.

22Apereke nsembe yachiyamiko

ndi kufotokoza za ntchito zake ndi nyimbo zachimwemwe.

23Ena anayenda pa nyanja mʼsitima zapamadzi;

Iwo anali anthu amalonda pa nyanja yayikulu.

24Anaona ntchito za Yehova,

machitidwe ake odabwitsa mʼnyanja yakuya.

25Pakuti Iye anayankhula ndi kuwutsa mphepo yamkuntho

imene inabweretsa mafunde ataliatali.

26Sitima za pamadzizo zinatukulidwa mmwamba ndi kutsikira pansi pakuya;

pamene amawonongeka, kulimba mtima kwawo kunasungunuka.

27Anachita chizungulire ndi kudzandira ngati anthu oledzera;

anali pa mapeto a moyo wawo.

28Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo

ndipo Iyeyo anawapulumutsa ku masautso awo.

29Yehova analetsa namondwe,

mafunde a mʼnyanja anatontholetsedwa.

30Anali osangalala pamene kunakhala bata,

ndipo Iye anawatsogolera ku dooko limene amalifuna.

31Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha

ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.

32Akuze Iye mu msonkhano wa anthu

ndi kumutamanda pabwalo la akuluakulu.

33Iye anasandutsa mitsinje kukhala chipululu,

akasupe otuluka madzi kukhala nthaka yowuma,

34ndiponso nthaka yachonde kukhala nthaka yamchere,

chifukwa cha kuyipa kwa amene amakhala kumeneko.

35Anasandutsa chipululu kukhala mayiwe a madzi

ndi nthaka yowuma kukhala akasupe a madzi oyenda;

36kumeneko Iye anabweretsa anthu anjala kuti azikhalako,

ndipo iwo anamanga mzinda woti akhazikikeko.

37Anafesa mbewu mʼminda ndi kudzala mipesa

ndipo anakolola zipatso zochuluka;

38Yehova anawadalitsa, ndipo chiwerengero chawo chinachuluka kwambiri,

ndipo Iye sanalole kuti ziweto zawo zithe.

39Kenaka chiwerengero chawo chinachepa ndipo iwo anatsitsidwa

chifukwa cha mazunzo, mavuto ndi chisoni;

40Iye amene amakhuthulira mʼnyozo pa olemekezeka

anawachititsa kuyendayenda mʼmalo owumawo wopanda njira.

41Koma Iyeyo anakweza anthu osowa kuchoka ku masautso awo

ngati magulu a nkhosa.

42Anthu olungama mtima amaona ndi kusangalala,

koma anthu onse oyipa amatseka pakamwa pawo.

43Aliyense wanzeru asamalitse zinthu zimenezi

ndi kuganizira za chikondi chachikulu cha Yehova.

King James Version

Psalms 107:1-43

1O give thanks unto the LORD, for he is good: for his mercy endureth for ever.

2Let the redeemed of the LORD say so, whom he hath redeemed from the hand of the enemy;

3And gathered them out of the lands, from the east, and from the west, from the north, and from the south.107.3 south: Heb. sea

4They wandered in the wilderness in a solitary way; they found no city to dwell in.

5Hungry and thirsty, their soul fainted in them.

6Then they cried unto the LORD in their trouble, and he delivered them out of their distresses.

7And he led them forth by the right way, that they might go to a city of habitation.

8Oh that men would praise the LORD for his goodness, and for his wonderful works to the children of men!

9For he satisfieth the longing soul, and filleth the hungry soul with goodness.

10Such as sit in darkness and in the shadow of death, being bound in affliction and iron;

11Because they rebelled against the words of God, and contemned the counsel of the most High:

12Therefore he brought down their heart with labour; they fell down, and there was none to help.

13Then they cried unto the LORD in their trouble, and he saved them out of their distresses.

14He brought them out of darkness and the shadow of death, and brake their bands in sunder.

15Oh that men would praise the LORD for his goodness, and for his wonderful works to the children of men!

16For he hath broken the gates of brass, and cut the bars of iron in sunder.

17Fools because of their transgression, and because of their iniquities, are afflicted.

18Their soul abhorreth all manner of meat; and they draw near unto the gates of death.

19Then they cry unto the LORD in their trouble, and he saveth them out of their distresses.

20He sent his word, and healed them, and delivered them from their destructions.

21Oh that men would praise the LORD for his goodness, and for his wonderful works to the children of men!

22And let them sacrifice the sacrifices of thanksgiving, and declare his works with rejoicing.107.22 rejoicing: Heb. singing

23They that go down to the sea in ships, that do business in great waters;

24These see the works of the LORD, and his wonders in the deep.

25For he commandeth, and raiseth the stormy wind, which lifteth up the waves thereof.107.25 raiseth: Heb. maketh to stand

26They mount up to the heaven, they go down again to the depths: their soul is melted because of trouble.

27They reel to and fro, and stagger like a drunken man, and are at their wits’ end. 107.27 are…: Heb. all their wisdom is swallowed up

28Then they cry unto the LORD in their trouble, and he bringeth them out of their distresses.

29He maketh the storm a calm, so that the waves thereof are still.

30Then are they glad because they be quiet; so he bringeth them unto their desired haven.

31Oh that men would praise the LORD for his goodness, and for his wonderful works to the children of men!

32Let them exalt him also in the congregation of the people, and praise him in the assembly of the elders.

33He turneth rivers into a wilderness, and the watersprings into dry ground;

34A fruitful land into barrenness, for the wickedness of them that dwell therein.107.34 barrenness: Heb. saltiness

35He turneth the wilderness into a standing water, and dry ground into watersprings.

36And there he maketh the hungry to dwell, that they may prepare a city for habitation;

37And sow the fields, and plant vineyards, which may yield fruits of increase.

38He blesseth them also, so that they are multiplied greatly; and suffereth not their cattle to decrease.

39Again, they are minished and brought low through oppression, affliction, and sorrow.

40He poureth contempt upon princes, and causeth them to wander in the wilderness, where there is no way.107.40 wilderness: or, void place

41Yet setteth he the poor on high from affliction, and maketh him families like a flock.107.41 from: or, after

42The righteous shall see it, and rejoice: and all iniquity shall stop her mouth.

43Whoso is wise, and will observe these things, even they shall understand the lovingkindness of the LORD.